Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?

Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?

Phunzirani Zimene Mawu A Mulungu Amanena

Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi kukwatirana motsatira malamulo kumathandiza bwanji kuti banja likhale losangalala?

Yehova, yemwe ndi Mulungu wachimwemwe, ndi amene anayambitsa ukwati. Anthu akakwatirana motsatira malamulo, amakhala osangalala chifukwa amadziwa kuti ali ndi mnzawo wapamtima komanso amaona kuti ana awo ndi otetezeka chifukwa aleredwa ndi makolo onse awiri. Kodi Mulungu amauona bwanji ukwati? Mulungu amafuna kuti mwamuna ndi mkazi akakwatirana azikhala limodzi kwa moyo wawo wonse. Amafunanso kuti ukwati wawo uzikhala wolembetsedwa ku boma. (Luka 2:1-5) Mulungu amafunanso kuti aliyense m’banjamo azikhala wokhulupirika kwa mnzake. (Aheberi 13:4) Yehova amalola Mkhristu kuthetsa banja lake n’kukwatiranso kapena kukwatiwanso pokhapokha ngati mwamuna kapena mkazi wake wachita chigololo.​—Werengani Mateyu 19:3-6, 9.

2. Kodi mwamuna ndi mkazi wake ayenera kumakhala motani?

Yehova analenga mwamuna ndi mkazi n’cholinga chakuti azithandizana m’banja. (Genesis 2:18) Monga mutu wa banja, mwamuna ayenera kupezera anthu a m’banja lake zosowa komanso kutsogolera banjalo pophunzira zinthu zokhudza Mulungu. Ayenera kusonyeza chikondi chodzimana kwa mkazi wake. Mwamuna ndi mkazi wake ayenera kukondana komanso kulemekezana. Popeza aliyense ndi wopanda ungwiro, anthu okwatirana afunika kuphunzira kukhululukirana kuti banja lawo likhale losangalala.​—Werengani Aefeso 4:31, 32; 5:22-25, 33; 1 Petulo 3:7.

3. Ngati banja silikuyenda bwino, kodi ndi bwino kungolithawa?

Ngati mukuona kuti zinthu sizikuyenda bwino pakati pa inu ndi mkazi kapena mwamuna wanu, yesetsani kuchitirana zinthu mwachikondi. (1 Akorinto 13:4, 5) Mawu a Mulungu salimbikitsa kuti m’banja mukakhala mavuto njira yabwino ndi kungopatukana. Komabe, ngati pali mavuto aakulu kwambiri, Mkhristu angasankhe kupatukana ndi mnzakeyo ngati akuona kuti kuchita zimenezi n’kothandiza.​—Werengani 1 Akorinto 7:10-13.

4. Ananu, kodi Mulungu amafuna kuti muzichita chiyani?

Yehova amafuna kuti muzikhala osangalala. Iye amapereka malangizo abwino kwambiri okuthandizani kuti muzikhala osangalala pamene muli achinyamata. Mulungu amafuna kuti mupindule ndi nzeru za makolo anu komanso zinthu zimene iwo akumana nazo pa moyo. (Akolose 3:20) Yehova amaona ndiponso amayamikira zonse zimene mumachita pomvera makolo anu.​—Werengani Mlaliki 11:9–12:1; Mateyu 19:13-15; 21:15, 16.

5. Makolonu, kodi mungatani kuti ana anu azikhala osangalala?

Muyenera kuyesetsa kuwapezera chakudya, pokhala ndiponso zovala. (1 Timoteyo 5:8) Komano kuti ana anu azikhala osangalala, muyeneranso kuwaphunzitsa kukonda Mulungu ndiponso kutengera chitsanzo chake. (Aefeso 6:4) Ngati inuyo mumakonda Mulungu, ana anu angatengere chitsanzo chanu. Mukamalangiza ana anu pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, mungawathandize kwambiri anawo kuti aziona zinthu moyenera.​—Werengani Deuteronomo 6:4-7; Miyambo 22:6.

Zimakhala zothandiza kwambiri kwa ana mukamawalimbikitsa komanso kuwayamikira. Ana amafunikanso kupatsidwa chilango akalakwitsa. Zimenezi zingathandize kuti azipewa makhalidwe omwe angachititse kuti azikhala osasangalala. (Miyambo 22:15) Koma si bwino kupatsa mwana chilango chokhwima kwambiri kapena kumulanga mwankhanza.​—Werengani Akolose 3:21.

A Mboni za Yehova ali ndi mabuku osiyanasiyana othandiza kwa makolo ndi ana. Mfundo za m’mabuku amenewa ndi zochokera m’Baibulo.​—Werengani Salimo 19:7, 11.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 14 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.