Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

ESITERE anayesetsa kudzilimbitsa mtima pamene ankalowa m’bwalo la nyumba ya mfumu ku Susani. Kulowa m’nyumba imeneyi siinali nkhani yamasewera. Nyumbayi inali ndi ziboliboli zamitundu yambirimbiri. Ziboliboli zina zinali zooneka ngati ng’ombe zokhala ndi mapiko ndipo zina ngati anthu oponya mivi ndi uta. Nyumbayi inalinso ndi makoma a njerwa okhala ndi zithunzi za mikango, zipilala za miyala yosema ndiponso ziboliboli zina zochititsa chidwi kwambiri. Kuwonjezera pamenepa, nyumbayi anaimanga pamalo okwera kwambiri pafupi ndi mapiri a Zagros ndipo inayang’ana kumene kunali mtsinje wa Choaspes. Zinthu zonsezi zinkapangitsa aliyense wofika panyumbayi kuzindikira kuti wafika pakhomo pa munthu wolemekezeka kwambiri. Esitere ankapita kukaonana ndi munthu ameneyo, yemwe ankadzitcha kuti “mfumu yaikulu.” Mfumu imene Esitere ankapita kukakumana nayoyi inali Ahasiwero yemwe analinso mwamuna wake.

Koma Ahasiwero sanali munthu woti mtsikana aliyense wachiyuda wokhulupirika angalakelake atakhala mwamuna wake. * Iye sankatsatira chitsanzo chabwino cha anthu ngati Abulahamu, amene anatsatira malangizo a Mulungu modzichepetsa omuuza kuti amvere zimene mkazi wake Sara ankamuuza. (Genesis 21:12) Mfumuyo sinkadziwa chilichonse chokhudza Yehova, Mulungu amene Esitere ankamulambira, komanso Chilamulo chake. Koma malamulo amene Ahasiwero ankadziwa anali malamulo a Aperisiya, kuphatikizapo lamulo loletsa zimene Esitere ankafuna kuchita. Kodi Esitere ankafuna kuchita chiyani? Panali lamulo lonena kuti munthu aliyense wopita kukaonekera pamaso pa mfumu ya Perisiya asanaitanidwe ndi mfumuyo, ayenera kuphedwa. Esitere sanaitanidwe, koma pa nthawiyi amapita kukaonekera kwa mfumuyo. N’kutheka kuti mmene ankayandikira bwalo lamkati lomwe linali pamalo poonekera kwa mfumu, ankangoona kuti basi kwake kwatha.​—Esitere 4:11; 5:1.

Kodi n’chifukwa chiyani Esitere anaika moyo wake pachiswe chonchi? Ndipo kodi tingaphunzire chiyani pa chikhulupiriro cha mtsikana ameneyu? Choyamba tiyeni tione chimene chinachititsa kuti Esitere akhale mfumukazi ku Perisiya.

Anali “Wokongola Kwambiri”

Esitere anali mwana wamasiye ndipo Baibulo silinena zambiri za makolo ake omwe anamutchula dzina lachiheberi lakuti Hadasa. Dzinali limatanthauza “mtengo wa mchisu,” womwe umakhala ndi maluwa okongola oyera. Makolo a Esitere atamwalira, wachibale wake wina dzina lake Moredekai anamuchitira chifundo ndipo anamutenga n’kumakhala naye. Esitere anali mlongo wake wa Moredekai (mwana wa m’bale wa bambo ake), komabe Moredekai anali wamkulu kwambiri poyerekeza ndi Esitere. Moredekai anatenga Esitere n’kumakhala naye kunyumba kwake ndipo ankamusamalira ngati mwana wake weniweni.​—Esitere 2:5-7, 15.

Moredekai ndi Esitere anali akapolo ochokera ku Yuda ndipo ankakhala mumzinda wa Susani womwe unali likulu la Ufumu wa Perisiya. Iwo ayenera kuti ankakumana ndi mavuto ambiri chifukwa cha chipembedzo chawo komanso Chilamulo chimene ankayesetsa kuchitsatira. Mosakayikira Esitere anayamba kumukonda kwambiri Moredekai pamene ankamuphunzitsa za Yehova, yemwe ndi Mulungu wachifundo amene analanditsa anthu Ake m’mavuto osiyanasiyana ndipo anali kudzalanditsanso anthu ake. (Levitiko 26:44, 45) N’zodziwikiratu kuti Esitere ndi Moredekai ankakondana kwambiri komanso ankakhulupirirana.

Zikuoneka kuti Moredekai anali ndi udindo winawake m’nyumba ya mfumu ku Susani ndipo nthawi zambiri ankakhala pakhomo la mpanda wa nyumbayo limodzi ndi atumiki ena a mfumu. (Esitere 2:19, 21; 3:3) Sitikudziwa kuti Esitere ankakonda kupanga chiyani ali wamng’ono, komabe zikuoneka kuti ankasamalira bwino Moredekai ndi nyumba yawo. N’kutheka kuti nyumba imeneyi inali tsidya lina la mtsinje, osati mbali imene kunali nyumba yachifumu ija. Iye ayenera kuti ankakonda kupita kumsika wa ku Susani kumene anthu ankagulitsa zinthu zosiyanasiyana zopangidwa ndi golide, siliva, ndiponso zinthu zina. Pa nthawi imeneyi, Esitere sankadziwa kuti m’tsogolo adzakhala ndi zinthu ngati zimenezi zambirimbiri.

Mfumukazi Ilowedwa M’malo

Tsiku lina nkhani inali m’kamwam’kamwa mumzinda wa Susani yonena za zomwe zinachitika kunyumba ya mfumu. Ahasiwero anakonzera akuluakulu aboma phwando lalikulu la zakudya zapamwamba ndiponso vinyo. Phwandoli lili mkati, mfumuyo inaganiza zoitana mkazi wake wokongola, Vasiti, yemwe ankadyera kwina ndi azimayi anzake. Koma Vasiti anakana kubwera. Chifukwa chokwiya komanso kuchita manyazi ndi zimenezi, mfumu inafunsa alangizi ake chilango chimene ingam’patse Vasiti. Malinga ndi zimene alangiziwo ananena, mfumu inalengeza kuti iye sakhalanso mfumukazi ndipo apeza mkazi wina woti alowe m’malo mwake. Anthu ogwira ntchito kunyumba kwa mfumu anayamba kufufuza atsikana okongola m’dziko lonselo kuti pa atsikana amenewo, mfumu idzasankhepo mkazi wake.​—Esitere 1:1–2:4.

Moredekai ayenera kuti ankanyadira komanso kuda nkhawa poona kuti Esitere akukula ndipo tsopano wayamba kuoneka bwino kwambiri. Baibulo limati: “Mtsikanayu anali wooneka bwino ndi wokongola kwambiri.” (Esitere 2:7) Kukongola n’kwabwino komabe munthu wokongola amakhala wosiririka ngati alinso wanzeru ndiponso wodzichepetsa. Ngati munthu wokongola alibe makhalidwe amenewa, amakhala wonyada komanso amakhala ndi makhalidwe ena oipa. (Miyambo 11:22) Tikukhulupirira kuti inunso mukuvomereza kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Ndiye popeza Esitere anali wokongola, kodi kukongolako kunamuthandiza kapena kunamupangitsa kuti akhale munthu woipa? Yankho la funso limeneli linadziwika patapita nthawi.

Atumiki a mfumuwo anaona kuti Esitere anali m’gulu la atsikana okongola ndipo anamutenga kuchoka m’manja mwa Moredekai kupita kunyumba ya mfumu, yomwe inali tsidya lina la mtsinje. (Esitere 2:8) Ziyenera kuti zinali zovuta kwambiri pamene Esitere ankasiyana ndi Moredekai popeza iwo ankakondana kwambiri ndipo ankangokhala ngati mwana ndi bambo ake. Moredekai ayenera kuti sankafuna kuti mwana wakeyu adzakwatiwe ndi munthu wosalambira Yehova, ngakhale munthuyo atakhala mfumu, koma pamene zinthu zinafikapa sakanatha kuletsa. Esitere ayenera kuti asanatengedwe anamvetsera mwatcheru malangizo onse amene Moredekai anamupatsa. Mmene ankapita kunyumba yachifumu ku Susani, ayenera kuti anali ndi mafunso ambirimbiri mumtima mwake. Iye sankadziwa kuti zikamuthera bwanji.

Ankakondedwa “Ndi Aliyense Womuona”

Esitere anayamba kukhala kunyumba yosiyana kwambiri ndi kwawo ndipo zonse kumeneko zinali zachilendo kwa iye. Iye ankakhala ndi “atsikana ambiri” amene anatengedwa kuchokera kumbali zonse za Ufumu wa Perisiya. N’zoonekeratu kuti atsikana amenewa anali osiyana kwambiri zikhalidwe, zilankhulo komanso mmene ankaonera zinthu. Atsikana amenewa ankayang’aniridwa ndi munthu wina, dzina lake Hegai. Kwa chaka chathunthu iwo ankapakidwa mafuta onunkhira komanso ankawakongoletsa m’njira zosiyanasiyana. (Esitere 2:8, 12) Moyo ngati umenewu ukanatha kusokoneza atsikanawo mosavuta. Maganizo awo onse akanakhala pa kudzikongoletsa ndipo zikanachititsa kuti ayambe kunyada komanso kukhala ndi mtima wampikisano. Kodi kukhala pamalo oterewa kunamukhudza bwanji Esitere?

Moredekai ankamudera nkhawa kwambiri Esitere. Baibulo limanena kuti tsiku lililonse iye ankafika kumalo kumene Esitere ankakhala, n’cholinga chakuti adziwe mmene alili. (Esitere 2:11) Akamva zokhudza Esitere, mwina kuchokera kwa anthu amene ankagwira ntchito pamalopa, mosakayikira iye ankasangalala kwambiri ndipo ankanyadira chifukwa chokhala ndi mwana wotere. Chifukwa chiyani?

Zinali choncho chifukwa chakuti Hegai anasangalala kwambiri ndi Esitere moti ankamukomera mtima pa zinthu zambiri. Iye anapatsa Esitere atsikana 7 oti azimutumikira ndiponso anamupatsa malo abwino kwambiri m’nyumba ya akaziyo. Nkhaniyi imanenanso kuti: “Pa nthawi imeneyi Esitere anali kukondedwa ndi aliyense womuona.” (Esitere 2:9, 15) Kodi anthu ankamukonda chonchi Esitere chifukwa chakuti anali wokongola basi? Ayi, panali zinthu zina zimene zinachititsa kuti azikondedwa.

Mwachitsanzo Baibulo limati: “Esitere sananene za mtundu wa anthu ake kapena za abale ake, pakuti Moredekai anali atamulamula kuti asanene kalikonse.” (Esitere 2:10) Moredekai anali atalangiza Esitere kuti asaulule zoti anali Myuda. Mosakayikira, iye anachita zimenezi chifukwa chodziwa kuti anthu a m’banja lachifumu ambiri sankasangalala ndi Ayuda. Moredekai ayenera kuti anasangalala kwambiri kuona kuti ngakhale kuti Esitere ankakhala kwina, anapitirizabe kumumvera komanso kuchita zinthu mwanzeru.

Nawonso achinyamata a masiku ano akhoza kusangalatsa makolo awo komanso anthu amene akuwalera. Akakhala ndi achinyamata anzawo, angakane kuchita zinthu zoipa n’kupitirizabe kuchita zinthu zogwirizana ndi mfundo zimene akuona kuti ndi zolondola. Iwo angachite zimenezi ngakhale pamene ali ndi anthu osaganiza bwino, akhalidwe loipa kapenanso aukali. Akamachita zimenezi, mofanana ndi Esitere, amasangalatsa mtima wa Atate wawo wakumwamba.​—Miyambo 27:11.

Ndiyeno nthawi itakwana yoti Esitere akaonekere kwa mfumu, anapatsidwa ufulu woti anene chilichonse chimene akufuna kuti am’patse, mwina kuti awonjezere kudzikongoletsa. Koma iye anatsatira malangizo a Hegai ndipo sanapemphe chilichonse chowonjezera pa zimene Hegai anatchula. (Esitere 2:15) Ayenera kuti anadziwa kuti kukongola pakokha sikungachititse kuti mfumuyo imusankhe. Ankadziwa kuti mtima wodzichepetsa ndiye wofunika kwambiri. Koma kodi zimenezi zinali zoona?

Nkhaniyi imati: “Mfumu inakonda kwambiri Esitere kuposa akazi ena onse, moti mfumu inakondwera naye ndipo inamusonyeza kukoma mtima kosatha kuposa anamwali ena onse. Pamenepo mfumu inamuveka duku lachifumu kumutu kwake ndi kumusandutsa mfumukazi m’malo mwa Vasiti.” (Esitere 2:17) Esitere anakhala mfumukazi yatsopano ndipo anali mkazi wa mfumu yamphamvu kwambiri padziko lonse pa nthawiyo. Iye ayenera kuti anavutika kuti azolowere moyo watsopanowu. Koma kodi udindo umenewu unamupangitsa kuti ayambe kunyada?

Ayi, Esitere anapitirizabe kumvera Moredekai, yemwe anamulera ngati bambo ake. Iye sanaulule zoti anali Myuda. Komanso pamene Moredekai anatulukira chiwembu chimene anthu anakonza choti aphe Ahasiwero, Esitere anamvera zimene Moredekai anamuuza ndipo anachenjeza mfumu za nkhaniyi. Izi zinachititsa kuti chiwembucho chilephereke. (Esitere 2:20-23) Iye anapitirizabe kukhala wodzichepetsa ndiponso womvera ndipo zimenezi zinasonyeza kuti ankakhulupirira Mulungu wake. Masiku ano anthu ambiri saona kuti kumvera ndi khalidwe labwino chifukwa amaona kuti palibe vuto ndi kusamvera kapena kuchita zinthu mosatsatira malamulo. Koma anthu amene amakhulupiriradi Mulungu amaona kuti kumvera ndi khalidwe lamtengo wapatali ngati mmene Esitere ankaonera.

Chikhulupiriro cha Esitere Chinayesedwa

Mfumu inakweza pa udindo munthu wina dzina lake Hamani kuti akhale nduna yake yaikulu. Zimenezi zinachititsa kuti Hamani akhale mlangizi wake wamkulu ndiponso wachiwiri kwa mfumuyo. Komanso mfumu inalamula kuti munthu aliyense akaona Hamani azimuweramira. (Esitere 3:1-4) Zinali zovuta kwa Moredekai kuti atsatire lamulo limeneli. Iye ankadziwa kuti ayenera kumvera mfumu koma osati pa zinthu zomwe zingakwiyitse Mulungu. Hamani anali “Mwagagi.” Zimenezi zikutanthauza kuti anali mbadwa ya Agagi, mfumu ya Aamaleki, yomwe inaphedwa ndi Samueli, mneneri wa Mulungu. (1 Samueli 15:33) Aamaleki anali anthu oipa kwambiri moti anadzipanga okha kukhala adani a Yehova ndi Aisiraeli. Mulungu ankanyansidwa ndi mtundu wonse wa Aamaleki. * (Deuteronomo 25:19) Ndiye kodi Myuda wokhulupirika akanagwadira bwanji Mwamaleki? Moredekai sakanachita zimenezo. Masiku anonso amuna ndi akazi okhulupirika amalolera kuika moyo wawo pachiswe potsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Machitidwe 5:29.

Hamani anakwiya koopsa ndi Moredekai. Koma ankaona kuti kupha Moredekai yekha sikunali kokwanira. Iye ankafuna kufafaniza anthu onse a mtundu wa Moredekai. Hamani anauza mfumu zinthu zoipa n’cholinga chakuti mfumuyo ione kuti Ayuda ndi anthu oipa. Iye sanawatchule dzina koma anangonena kuti ndi mtundu wa anthu osafunika “umene ukupezeka paliponse ndipo ukudzipatula pakati pa anthu.” Iye ananenanso kuti anthu amenewa samvera malamulo a mfumu ndipo ndi adani oopsa. Hamani analonjeza kuti apereka ndalama zambiri zoti zigwiritsidwe ntchito polipirira zonse zofunika kuti Ayuda onse amene anali mu ufumuwo aphedwe. * Ahasiwero anapatsa Hamani mphete yake yodindira kuti adinde lamulo lililonse lokhudza nkhaniyi limene akufuna kukhazikitsa.​—Esitere 3:5-10.

Pasanapite nthawi anatumiza anthu okwera pamahatchi kumadera onse a ufumuwo kuti akapereke uthenga woti Ayuda onse aphedwa. Taganizirani mmene Ayuda amene anali ku Yerusalemu anamvera atamva uthenga umenewu. Iwo anali atabwerera ku ukapolo ku Babulo ndipo ankamanganso mzinda wa Yerusalemu womwe pa nthawiyi unali wosatetezeka chifukwa unalibe mpanda. N’kutheka kuti Moredekai atamva nkhani yomvetsa chisoni imeneyi anaganizira za anthu amenewa komanso anzake ndi abale ake amene ankakhala ku Susani. Chifukwa chothedwa nzeru, Moredekai anang’amba zovala zake, kuvala chiguduli n’kudzola phulusa ndipo anayamba kulira mofuula pakati pa mzindawo. Koma Hamani anali atangokhala n’kumamwa vinyo ndi mfumu ku Susani. Zoti Ayuda ndiponso anzawo anali achisoni kwambiri chifukwa cha uthenga umene iyeyo anatumiza, sizinkamukhudza n’komwe.​—Esitere 3:12–4:1.

Moredekai anaona kuti ayenera kuchitapo kanthu. Koma kodi akanatani pamenepa? Esitere atamva za Moredekai anamutumizira zovala, koma iye anakana kutonthozedwa. N’kutheka kuti kwa nthawi yaitali iye ankadabwa kuti n’chifukwa chiyani Yehova Mulungu analola kuti mwana wake Esitere akhale mkazi wa mfumu yosalambira Yehova. Koma tsopano chifukwa chimene Mulungu analolera kuti zimenezi zichitike chinayamba kuoneka. Moredekai anatumiza uthenga kwa Mfumukazi Esitere, womupempha kuti akachonderere mfumu kuti isinthe maganizo. Pamenepa Esitere anafunika kulimba mtima kuti ateteze “anthu a mtundu wake.”​—Esitere 4:4-8.

Esitere ayenera kuti anachita mantha kwambiri atamva uthengawo. Pamenepa chikhulupiriro chake chinayesedwa. Zimene Esitere anayankha Moredekai zinasonyeza kuti anali ndi mantha kwambiri. Iye anakumbutsa Moredekai za lamulo loletsa kukaonekera kwa mfumu usanaitanidwe lija, chifukwa zimenezi zingachititse kuti uphedwe. Munthu ankapulumuka pokhapokha ngati mfumu yamuloza ndi ndodo yake yagolide. Ndipo akaganizira zimene zinachitikira Vasiti atakana kukaonekera kwa mfumu, Esitere ankaona kuti ngakhale kuti ndi mkazi wa mfumu, n’kutheka kuti mfumuyi singamuchitire chifundo. Esitere anauza Moredekai kuti panali patatha masiku 30 asanaitanidwe kuti akaonekere kwa mfumu. Zimenezi ziyenera kuti zinachititsa Esitere kuyamba kukayikira ngati mfumuyi, yomwe sinkachedwa kupsa mtima, inkamukondabe. *​—Esitere 4:9-11.

Moredekai anayankhanso Esitere ndi mawu amphamvu kuti chikhulupiriro chake chilimbe. Anamutsimikizira kuti ngati sangachitepo kanthu, chipulumutso cha Ayuda chichokera kwina. Koma kodi lamulo loti Ayuda aphedwe likanayamba kugwira ntchito Esitere akanapulumuka? Apa Moredekai anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova, yemwe sangalole kuti anthu ake onse awonongedwe kapena kulola kuti malonjezo ake asakwaniritsidwe. (Yoswa 23:14) Kenako Moredekai anafunsa Esitere kuti: “Ndani akudziwa? Mwina iwe wakhala mfumukazi kuti uthandize pa nthawi ngati imeneyi.” (Esitere 4:12-14) Moredekai ankakhulupirira Mulungu wake, Yehova, ndi mtima wonse. Kodi ifenso timatero?​—Miyambo 3:5, 6.

Anali ndi Chikhulupiriro Cholimba Moti Sanaope Kufa

Apa Esitere anafunika kusankha zochita mwamsanga. Iye anatumiza uthenga kwa Moredekai womudziwitsa kuti iyeyo asala kudya kwa masiku atatu ndipo anapemphanso Moredekaiyo ndi Ayuda ena kuti nawonso asale kudya pa nthawiyo. Uthengawu unalinso ndi mawu osonyeza chikhulupiriro komanso kulimba mtima, amene anthu ambiri akhala akuwanena kwa zaka zambiri. Mawu ake ndi akuti: “Ngati n’kufa, ndife.” (Esitere 4:15-17) Pa masiku atatu amenewa Esitere ayenera kuti ankapemphera mochokera pansi pa mtima kuposa mmene ankachitira masiku ena onse. Ndiyeno tsiku loti akaonane ndi mfumu litakwana, iye anavala zovala zachifumu zokongola kwambiri kuti akaoneke bwino pamaso pa mfumuyo.

Monga tafotokozera kumayambiriro kwa nkhaniyi, Esitere ananyamuka ulendo wopita kunyumba ya mfumu. N’zachidziwikire kuti anali ndi nkhawa komanso ankapemphera chamumtima. Iye anafika pabwalo la nyumba ya mfumu ndipo anamuona Ahasiwero atakhala pampando wake wachifumu. N’kutheka kuti ankayang’anitsitsa nkhope ya Ahasiwero, yemwe anali watsitsi lanzindo ndiponso ankadulira mwaluso kwambiri ndevu zake. Esitere ayenera kuti ankafuna kuona ngati mfumuyo yakwiya kapena ayi. Ngati panapita nthawi mfumuyo isanamuone, ndiye kuti ankangoona kuchedwa chifukwa anali ndi nkhawa. Koma kenako mfumuyo inamuona. Mfumuyo iyenera kuti inadabwa kwambiri itamuona komabe nkhope yake inayamba kuoneka kuti sanakwiye ndi kubwera kwake ndipo inaloza Esitere ndi ndodo yake yagolide.​—Esitere 5:1, 2.

Ahasiwero anamvetsera zimene Esitere ankafuna kumuuza. Pamenepa Esitere anasonyeza kulimba mtima. Anasonyezanso kuti ali kumbali ya Mulungu komanso anthu a mtundu wake. Zimene anachitazi zinasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba ndipo ndi chitsanzo chabwino kwa atumiki onse a Mulungu mpaka pano. Koma ichi chinali chiyambi chabe. Kodi iye akanatani kuti apangitse mfumu kukhulupirira kuti Hamani, mlangizi wake yemwe ankamukonda zedi, anali woipa kwambiri ndipo anali atakonza chiwembu? Kodi iye anachita chiyani kuti apulumutse anthu a mtundu wake? Mafunso amenewa tidzawakambirana m’nkhani ina yomwe idzatuluke m’tsogolo muno.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Anthu ambiri amakhulupirira kuti Ahasiwero anali Sasita Woyamba, amene analamulira Ufumu wa Perisiya kumayambiriro kwa zaka za m’ma 400 B.C.E.

^ ndime 24 Hamani ayenera kuti anali m’gulu la Aamaleki ochepa kwambiri omwe analipobe pa nthawiyi, chifukwa anthu “otsala” a mtundu umenewu anali ataphedwa kale m’nthawi ya Mfumu Hezekiya.​—1 Mbiri 4:43.

^ ndime 25 Hamani analonjeza kupereka matalente 10,000 asiliva ndipo masiku ano ndalama zimenezi ndi zokwana madola mamiliyoni ambiri. Ngati Ahasiwero analidi Sasita Woyamba, ndiye kuti anakopeka kwambiri ndi ndalama zimene Hamani analonjezazi. Sasita anawononga ndalama zambiri pa nkhondo yomenyana ndi Agiriki, yomwe iye analuza. Iye ayenera kuti anamenya nkhondo imeneyi asanakwatire Esitere.

^ ndime 28 Sasita Woyamba ankadziwika kuti anali munthu wosachedwa kupsa mtima. Mwachitsanzo, katswiri wina wa ku Greece wolemba mbiri yakale, dzina lake Herodotus, analemba zinthu zina zimene Sasita anachita pamene ankamenyana ndi Agiriki. Mfumuyi inalamula kuti panyanja ya Hellespont pamangidwe mlatho pogundaniza mabwato. Mphepo yamkuntho itaphwasula mlathowo, Sasita analamula kuti anthu amene anamanga mlathowo adulidwe mitu. Iye analamulanso asilikali ake kuti alange nyanjayo mwa kukwapula madzi kwinaku akuwerenga mokweza mawu olalata. Pa nkhondo yomweyi, munthu wina wolemera atapempha kuti mwana wake asalowe usilikali, Sasita analamula kuti mwanayo adulidwe pakati ndipo mtembo wake uikidwe poonekera kuti anthu ena atengerepo phunziro.

[Chithunzi patsamba 19]

Moredekai ankasangalala kwambiri ndipo ankanyadira chifukwa cha khalidwe la Esitere

[Chithunzi patsamba 20]

Esitere ankadziwa kuti kudzichepetsa ndiponso nzeru ndi zofunika kwambiri kuposa kukongola

[Chithunzi patsamba 22, 23]

Esitere anaika moyo wake pachiswe n’cholinga chakuti ateteze anthu a Mulungu