Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Nthawi Imene Sitiyenera Kugona

Nthawi Imene Sitiyenera Kugona

MWINA ukudziwa kuti ukakhala kusukulu suyenera kugona. Ana ambiri amagona akakhala m’kalasi. Koma kuti uphunzire umafunika kukhala maso. Mwinanso umapita kumisonkhano kukaphunzira mfundo za m’Baibulo.

Kodi ukuganiza kuti ungatani kuti usamagone ukakhala m’kalasi kapena ku misonkhano?​ * Chinthu china chimene chingakuthandize ndi kuyesetsa kumagona nthawi yabwino. Komanso kugona pang’ono masana kukhoza kukuthandiza. Tiye tione zimene tingaphunzire pa zimene zinachitikira mnyamata wina amene anagona pamene mtumwi Paulo ankakamba nkhani usiku. Tiye tiwerenge Machitidwe chaputala 20, vesi 7 mpaka 12 kuti tione zimene zinachitika.

Paulo ankachezera mpingo wina womwe unali mumzinda wa Torowa. Mzinda umenewu unali m’mbali mwa nyanja. Baibulo limati Paulo “anali kunyamuka m’mawa wake” pa ngalawa. Choncho, “anatenga nthawi yaitali akulankhula mpaka pakati pa usiku.” Kenako nkhaniyo imati: “Paulo ali mkati mokamba nkhani, mnyamata wina dzina lake Utiko amene anakhala pawindo, anagona tulo tofa nato.” Kodi ukudziwa zimene zinachitika kenako?​

Utiko “anagwa pansi kuchokera panyumba yachitatu yosanja.” Nthawi yomweyo Paulo ndi anthu ena anathamanga kutsika pansi. Iwo anapeza Utiko atafa. Kodi ukuganiza kuti anthu onse amene anali pamalopo anamva bwanji?​— Baibulo limanena kuti Paulo ananyamula Utiko ndi kumukumbatira. Pasanapite nthawi, Paulo anafuula mokondwera kuti: ‘Musadandaule, ali bwino.’ Mulungu anali ataukitsa Utiko.

Kodi zimene zinamuchitikira Utiko zikutiphunzitsa chiyani zokhudza Mulungu?​— Chinthu chimodzi chimene tikuphunzirapo ndi chakuti Yehova, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba, angathe kuukitsa anthu akufa, kuphatikizapo ana. Yehova amadziwa zimene zimakuchitikira ndipo amakukonda kwambiri kuposa mmene makolo ako amakukondera. Yesu ali padziko lapansili, ananyamula ana n’kuwadalitsa ndipo zimenezi zinasonyeza kuti Atate wakenso amakonda ana. Yesu anaukitsanso ana, kuphatikizapo kamtsikana ka zaka 12.

Kodi ukumva bwanji chifukwa chodziwa kuti Atate wako wakumwamba amakukonda?​— Kudziwa zimenezi kumatipangitsa kuti nafenso tizikonda Yehova komanso kuti tizimvera zonse zimene amanena. Kodi ukudziwa zimene tingachite posonyeza kuti timamukonda?​— Tikhoza kusonyeza kuti timamukonda mwa kuuza anthu kuti timamukonda. Yesu ananena kuti: “Ndimakonda Atate.” Komatu Yesu sankangonena kuti amakonda Mulungu. Iye ankachitanso zinthu zosonyeza kuti amakondadi Mulungu.

Yesu ankamvera Mulungu. Iye anati: “Ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse.” Choncho, nafenso kuti tikondweretse Yehova komanso Mwana wake, Yesu, tiyenera kuyesetsa kusagona pa nthawi imene tikufunikira kukhala maso.

^ ndime 4 Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana, mukapeza mzera muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.