Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinsinsi cha Banja Losangalala

Yesetsani Kuti Banja Lanu Lizikonda Zinthu Zauzimu

Yesetsani Kuti Banja Lanu Lizikonda Zinthu Zauzimu

Frederick *: “Ine ndi mkazi wanga Leanne titangokwatirana kumene, ndinkafuna kuti tiziphunzira limodzi Baibulo. Ndinkafunitsitsa kuti pa nthawi imene tikuphunzira, maganizo ake onse azikhala pa zimene tikuphunzirazo. Koma Leanne sankakhazikika maganizo. Ndikafunsa funso, iye ankangoyankha kuti inde kapena ayi basi. Zimene ankachita pa phunziro lathu sizinkagwirizana ndi zimene ndinkafuna.”

Leanne: “Pamene tinkakwatirana ndi Frederick n’kuti ndili ndi zaka 18. Nthawi zambiri tinkaphunzirira limodzi Baibulo koma pa phunziro lililonse Frederick ankakonda kunena zomwe ndimalakwitsa komanso zomwe akufuna ndisinthe kuti ndikhale mkazi wabwino. Zimenezi zinkandikhumudwitsa kwambiri.”

KODI mukuganiza kuti Frederick ndi Leanne sankagwirizana chifukwa chiyani? Zolinga zawo zinali zabwino ndipo onse ankakonda Mulungu. Komanso onse ankaona kuti ayenera kumaphunzirira limodzi Baibulo. Koma m’malo moti kuphunzirira limodzi kuwathandize kukhala ogwirizana, kunkachititsa kuti azisiyana maganizo. Ngakhale kuti ankaphuzirira limodzi Baibulo, n’kutheka kuti iwo sankaona zinthu moyenera.

Kodi Akhristu ayenera kumaona bwanji zinthu? Kodi n’chifukwa chiyani anthu okwatirana ayenera kuyesetsa kuti azikonda zinthu zauzimu? Kodi ndi mavuto ati amene angakumane nawo, nanga angawathetse bwanji?

Kodi Akhristu Ayenera Kumaona Bwanji Zinthu?

Baibulo limanena kuti anthu amaona zinthu mosiyanasiyana. (Yuda 18, 19) Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anafotokoza kusiyana kwa pakati pa munthu amene amatsatira mfundo za Mulungu ndi munthu wokonda zinthu zakuthupi. Paulo ananena kuti anthu amene amakonda zinthu zakuthupi, amaganizira kwambiri za iwowo osati za anthu ena. M’malo moyesetsa kutsatira mfundo za Mulungu pa moyo wawo, amangochita zinthu zimene iwowo akuganiza kuti n’zoyenera.​—1 Akorinto 2:14; Agalatiya 5:19, 20.

Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene amaona zinthu mwauzimu, amaona kuti mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino n’zofunika kwambiri. Iwo amaona kuti Yehova Mulungu ndi Bwenzi lawo ndipo amayesetsa kutsanzira makhalidwe ake. (Aefeso 5:1) Chotero, iwo amakhala achikondi, okoma mtima ndiponso sakhala aukali pochita zinthu ndi ena. (Ekisodo 34:6) Komanso anthu otere amamvera Mulungu ngakhale pamene kumverako kungachititse kuti akumane ndi mavuto ena. (Salimo 15:1, 4) Darren, amene amakhala ku Canada ndipo wakhala m’banja kwa zaka 35 ananena kuti: “Ine ndimaona kuti munthu amene amakonda zinthu zauzimu, nthawi zonse amaganizira mmene zonena komanso zochita zake zingakhudzire ubwenzi wake ndi Mulungu.” Mkazi wake Jane ananena kuti: “Ndimaona kuti mkazi amene amakonda zinthu zauzimu ndi amene amayesetsa tsiku ndi tsiku kuti akhale ndi makhalidwe amene mzimu woyera wa Mulungu umatulutsa.”​—Agalatiya 5:22, 23.

Komatu si munthu wapabanja yekha amene amayenera kukulitsa mtima wokonda zinthu zauzimu. Baibulo limaphunzitsa kuti munthu aliyense ali ndi udindo wophunzira za Mulungu ndi kumutsanzira.​—Machitidwe 17:26, 27.

N’chifukwa Chiyani Anthu Okwatirana Ayenera Kuyesetsa Kuti Azikonda Zinthu Zauzimu?

Kodi n’chifukwa chiyani anthu okwatirana ayenera kuyesetsa kuti azikonda zinthu zauzimu? Taganizirani chitsanzo ichi: Anthu awiri agula munda ndipo akufuna kulima ndiwo zamasamba. Mmodzi akuganiza zoti abzale mbewu, pamene winayo akuona kuti adzabzale nthawi ina m’tsogolo. Wina akuganiza kuti athire mbewuzo feteleza pomwe wina akutsutsa kuti mbewuzo sizikufunikira feteleza. Wina amakonda kulimira mbewuzo tsiku lililonse koma winayo amakonda kungokhala n’kumaonerera mnzakeyo akugwira ntchito. Potsirizira pake anthuwo angapeze ndiwo zamasamba, komabe sizingakhale zambiri poyerekeza ndi zimene akanapeza akanakhala kuti anagwirizana zochita kenako n’kumagwirira ntchito limodzi kuti zimene akufunazo zitheke.

Mwamuna ndi mkazi wake ali ngati anthu amenewa. Ngati munthu mmodzi atayesetsa kumakonda zinthu zauzimu, banja lawo likhoza kukhala lolimba. (1 Petulo 3:1, 2) Komabe banjalo lingakhale lolimba kuposa pamenepo ngati onse awiri agwirizana kuti azitsatira mfundo za Mulungu pa moyo wawo ndipo akuyesetsa kuthandizana potumikira Mulungu. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Awiri amaposa mmodzi.” Chifukwa chiyani? “Chifukwa amapeza mphoto yabwino pa ntchito yawo imene amaigwira mwakhama. Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.”​—Mlaliki 4:9, 10.

Muyenera kuti mukulakalaka kuti inu ndi mkazi kapena mwamuna wanu muzikonda zinthu zauzimu. Koma kungolakalaka kokha, sikungathandize kuti zimenezi zitheke. Tiyeni tikambirane mavuto awiri amene mungakumane nawo komanso mmene mungawathetsere.

VUTO LOYAMBA: Tikulephera kupeza nthawi.

Sue, yemwe wangokwatiwa kumene, ananena kuti: “Mwamuna wanga amakanditenga kuntchito 7 koloko madzulo. Tikafika kunyumba timapeza ntchito zambirimbiri zikutidikira. Mtima wathu umalakalaka titakhala pansi limodzi n’kumaphunzira za Mulungu koma thupi limafuna kupuma chifukwa chotopa.”

Zimene mungachite: Khalani okonzeka kusintha ndipo muzichita zinthu mogwirizana. Sue ananena kuti: “Ine ndi mwamuna wanga tinagwirizana kuti tizidzuka m’mawa kwambiri kuti tiziwerenga Baibulo ndi kukambirana zimene tawerengazo tisanapite kuntchito. Mwamuna wanga amandithandizanso kugwira ntchito zina zapakhomo n’cholinga choti tizipeza mpata wokambirana.” Kodi zimenezi zawathandiza bwanji? Ed, yemwe ndi mwamuna wake wa Sue, ananena kuti: “Ndaona kuti kuyesetsa kuphunzirira zinthu zauzimu limodzi nthawi zonse, kwatithandiza kuti tizipeza njira zothetsera mavuto amene timakumana nawo komanso kwatithandiza kuti tisamakhale ndi nkhawa kwambiri.”

Kuwonjezera pa kulankhulana, n’zofunikanso kwambiri kuti tsiku lililonse muzipeza nthawi yopempherera limodzi. Kodi zimenezi zingakuthandizeni bwanji? Ryan, yemwe wakhala m’banja kwa zaka 16 ananena kuti: “Zaka za m’mbuyomu, ine ndi mkazi wanga tinali ndi mavuto ambiri m’banja mwathu. Koma tinayamba kumapemphera limodzi madzulo aliwonse, n’kumamufotokozera Mulungu mavuto athu. Ndikuona kuti kupemphera limodzi kwatithandiza kuthetsa mavuto athu komanso kuti tiyambirenso kusangalala m’banja mwathu.”

TAYESANI IZI: Yesetsani kuti madzulo a tsiku lililonse muzipeza nthawi yokambirana zinthu zabwino zimene mwakumana nazo ndipo mukufuna kuthokoza Mulungu chifukwa cha zimenezi. Komanso kambiranani za mavuto amene mukukumana nawo amene mukuona kuti ndi ofunika kuti Mulungu akuthandizeni. Chenjezo: Imeneyi si nthawi yoti muyambe kuuza mnzanuyo zinthu zimene amalakwitsa. M’malomwake, mukamapemphera tchulani za mavuto amene mukufuna kuwathetsera limodzi monga banja. Tsiku lotsatira, yesetsani kuchita zinthu zogwirizana ndi zimene munatchula m’pemphero zija.

VUTO LACHIWIRI: Timasiyana pa nkhani yophunzira.

Tony ananena kuti: “Ine zimandikanika kuti ndikhale pansi n’kumaphunzira.” Mkazi wa Tony, dzina lake Natalie, ananena kuti: “Ndimakonda kuwerenga komanso kulankhula zimene ndaphunzira. Koma nthawi zina ndimaona kuti mwamuna wanga amamangika nane tikamaphunzira limodzi nkhani za m’Baibulo.”

Zimene mungachite: Muzithandizana m’malo mochita zinthu mwampikisano komanso muzipewa kuweruzana. Muzilimbikitsana komanso kuyamikirana wina akachita bwino. Tony ananena kuti: “Mkazi wanga amakonda kucheza nkhani za m’Baibulo moti nthawi zina ndimafika potopa nazo. Poyamba sindinkafuna kuti ndizikambirana naye nkhani za m’Baibulo. Komabe, Natalie amandithandiza kwambiri. Panopa timakambirana nkhani zauzimu kawirikawiri ndipo ndazindikira kuti palibe chifukwa choti ndizimangika. Masiku ano ndimasangalala kukambirana naye nkhani za m’Baibulo ndipo zimenezi zathandiza kuti banja lathu lizikhala losangalala komanso lamtendere.”

Mabanja ambiri aona kuti kuphunzira limodzi Baibulo mlungu uliwonse kwathandiza kuti zinthu ziziwayendera bwino. Komabe, chenjezo ndi lakuti: Mukawerenga malangizo enaake a m’Baibulo, muzifotokoza mmene inuyo mungagwiritsire ntchito malangizowo osati mmene mnzanuyo angawagwiritsire ntchito. (Agalatiya 6:4) Ngati muli ndi mavuto a m’banja muzikambirana zimenezo nthawi ina, osati pamene mukuphunzira Baibulo. N’chifukwa chiyani tikutero?

Taganizirani izi: Pamene mukudya limodzi ndi banja lanu, kodi mungayambe kutsuka ndi kumanga bala lamafinya? N’zodziwikiratu kuti simungatero, chifukwa kuchita zimenezi kungapangitse kuti aliyense asiye kudya. Yesu anayerekezera kuphunzira za Mulungu komanso kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kudya. (Mateyu 4:4; Yohane 4:34) Pophunzira Baibulo, mukakhala ndi chizolowezi chofotokoza mavuto omwe ali m’maganizo mwanu, mnzanuyo sangafunenso kumaphunzira zinthu zauzimu. N’zoona kuti muyenera kukambirana mavuto a m’banja, komabe ndi bwino kupeza nthawi ina yokambirana mavutowo.​—Miyambo 10:19; 15:23.

TAYESANI IZI: Lembani makhalidwe awiri kapena atatu a mwamuna kapena mkazi wanu amene amakusangalatsani kwambiri. Ndiyeno ulendo wina mukamadzakambirana nkhani zauzimu zokhudza makhalidwe amenewa, mudzamuuze mnzanuyo kuti mumayamikira kwambiri mmene iye amasonyezera makhalidwewo.

Mumakolola Zimene Mwafesa

Ngati mutayesetsa monga banja kuti muzikonda zinthu zauzimu, banja lanu lidzakhala lamtendere komanso losangalala. Ndipotu Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”​—Agalatiya 6:7.

Frederick ndi Leanne, omwe tawatchula kumayambiriro kwa nkhani ino aja, anazindikira kuti mfundo ya m’Baibulo imeneyi ndi yoona. Tsopano iwo akhala m’banja kwa zaka 45 ndipo aona kuti kupirira kumathandiza. Frederick anati: “Poyamba ndinkaimba mlandu mkazi wanga kuti safuna tizikambirana. Koma patapita nthawi ndinazindikira kuti nanenso ndiyenera kuchita khama kuti vutoli lithe.” Leanne anati: “Chimene chinatithandiza kwambiri pa nthawi yovutayi, ndi choti tonse timakonda Yehova Mulungu. Kwa zaka zambiri takhala tikuphunzira Baibulo ndiponso kupemphera limodzi. Ndikuona kuti Frederick akuyesetsa kusonyeza makhalidwe achikhristu ndipo zimenezi zachititsa kuti ndizimukonda kwambiri.”

^ ndime 3 Mayinawa tawasintha.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi ndi liti pamene ineyo ndi mwamuna kapena mkazi wanga tinapemphera limodzi?

  • Kodi ndingachite chiyani kuti mkazi kapena mwamuna wanga azikhala womasuka kukambirana nane nkhani za m’Baibulo?