Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Usadalire Luso Lako Lomvetsa Zinthu”

“Usadalire Luso Lako Lomvetsa Zinthu”

“Usadalire Luso Lako Lomvetsa Zinthu”

“Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu.”​—MIY. 3:5.

1, 2. (a) Kodi ndi mavuto ati amene tingakumane nawo? (b) Kodi pamene takumana ndi mavuto, pamene tikufuna kusankha zinthu kapena pamene tikulimbana ndi mayesero, tiyenera kudalira ndani ndipo n’chifukwa chiyani?

ABWANA a Cynthia * akufuna kuchepetsa anthu amene amagwira ntchito pakampani yawo ndipo anthu angapo achotsedwa kale. Cynthia akuopa kuti basi watsala ndi iyeyo. Kodi ntchito ikatha, zinthu zimuthera bwanji? Kodi ndalama azidzazipeza kuti? Mlongo wina dzina lake Pamela akufuna kusamukira kudera lina kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Kodi iye apitekodi? Mnyamata wina dzina lake Samuel ali ndi vuto lina. Iye ankaonera zithunzi zolaula ali wamng’ono. Panopa ali ndi zaka za m’ma 20 ndipo akuona kuti amalakalakabe kuonera zithunzi zolaula. Kodi angachite chiyani kuti alimbane ndi mayesero amenewa?

2 Kodi mumadalira ndani mukakumana ndi mavuto, mukamafuna kusankha zinthu zofunika kapena mukamalimbana ndi mayesero? Kodi mumadalira nzeru zanu kapena ‘mumatulira Yehova nkhawa zanu’? (Sal. 55:22) Baibulo limati: “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.” (Sal. 34:15) Choncho kukhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse ndi chinthu chofunika kwambiri ndipo sitiyenera kudalira luso lathu lomvetsa zinthu.​—Miy. 3:5.

3. (a) Kodi kukhulupirira Yehova kumaphatikizapo chiyani? (b) N’chiyani chingachititse ena kuti azidalira luso lawo lomvetsa zinthu?

3 Kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse kumaphatikizapo kuchita zinthu mmene iye akufunira komanso mogwirizana ndi chifuniro chake. Kuti zimenezi zitheke, timafunika kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima, n’kumamupempha kuti atitsogolere. Komabe, anthu ambiri zimawavuta kudalira Yehova pa chilichonse. Mwachitsanzo mlongo wina dzina lake Lynn ananena kuti: “Kudalira Yehova pa chilichonse n’chimodzi mwa zinthu zimene zimandivuta kwambiri kuchita. Ine ndi bambo anga sitigwirizana kwenikweni. Nawonso mayi anga sankasamala za mmene ndikumvera ndipo sankachita nane chidwi. Choncho ndinangozolowera kudzichitira zinthu ndekha.” Chifukwa cha zimene Lynn wakhala akukumana nazo kuyambira ali mwana, amaona kuti n’zovuta kudalira anthu ena ndi mtima wonse. Anthu ena amayamba kudzidalira chifukwa cha luso linalake limene ali nalo ndiponso chifukwa cha zimene akwanitsa kuchita pa moyo. Chifukwa chodzidalira, mkulu mu mpingo angayambe kusamalira nkhani za mpingo koma asanayambe wapemphera kwa Mulungu.

4. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?

4 Yehova amafuna kuti tiziyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene tamupempha ndiponso mogwirizana ndi chifuniro chake. Ndiyeno tingatani kuti tisadalire nzeru ndi luso lathu pochita zimene tamupemphazo? Kodi tiyenera kusamala ndi zinthu ziti pamene tikusankha zochita? Nanga n’chifukwa chiyani pemphero lili lofunika pamene tikulimbana ndi mayesero? M’nkhani ino tikambirana zitsanzo zingapo za m’Malemba zimene zingatithandize kuyankha mafunso amenewa.

Tikakumana ndi Mavuto

5, 6. Kodi Hezekiya anatani ataopsezedwa ndi mfumu ya Asuri?

5 Baibulo limafotokoza za Mfumu Hezekiya ya Yuda kuti: “Hezekiya anapitiriza kumamatira Yehova. Sanasiye kum’tsatira, koma anapitiriza kusunga malamulo amene Yehova analamula Mose.” Kunena zoona, “iye anadalira Yehova Mulungu wa Isiraeli.” (2 Maf. 18:5, 6) Pa nthawi ina, Mfumu Senakeribu ya Asuri inatumiza Rabisake ndi nthumwi zina limodzi ndi gulu lalikulu la asilikali ku Yerusalemu. Kodi Hezekiya anatani izi zitachitika? Gulu la asilikali a Asuri linali litalanda kale mizinda ingapo ya Yuda ndipo pa nthawiyi cholinga cha Senakeribu chinali kulanda Yerusalemu. Ndiyeno Hezekiya anapita kunyumba ya Yehova n’kuyamba kupemphera kuti: “Inu Yehova Mulungu wathu, chonde tipulumutseni m’manja mwake, kuti maufumu onse a padziko lapansi adziwe kuti inu Yehova, inu nokha ndiye Mulungu.”​—2 Maf. 19:14-19.

6 Hezekiya anachita zinthu mogwirizana ndi pemphero lake. Asanapite kukapemphera kukachisi, iye anauza anthu ake kuti asayankhe chilichonse pa mawu onyoza a Rabisake. Hezekiya anatumizanso anthu kuti apite kwa mneneri Yesaya kukafunsa malangizo. (2 Maf. 18:36; 19:1, 2) Apatu Hezekiya anachita zinthu zolondola. Iye sanayese kuthana ndi vutolo pogwiritsa ntchito njira yotsutsana ndi cholinga cha Yehova. Sanapemphe thandizo ku Iguputo kapena ku mitundu ina yowazungulira. Komanso sanadalire luso lake lomvetsa zinthu, m’malomwake anakhulupirira Yehova. Ndiyeno mngelo wa Yehova anapha asilikali 185,000 a Senakeribu. Izi zinachititsa kuti Senakeribu ‘achokeko’ n’kubwerera ku Nineve.​—2 Maf. 19:35, 36.

7. Kodi tingatonthozedwe bwanji ndi mapemphero amene Hana komanso Yona anapereka?

7 Hana, yemwe anali mkazi wa Mlevi wina dzina lake Elikana, anali ndi vuto loti sankabereka. Izi zinkamudetsa nkhawa kwambiri koma iyenso anadalira Yehova. (1 Sam. 1:9-11, 18) Mneneri Yona anapulumutsidwa m’mimba mwa chinsomba pambuyo popemphera. Iye ananena kuti: “Pamene ndinali m’masautso ndinaitana Yehova, ndipo anandiyankha. Ndinafuula kupempha thandizo ndili m’Manda akuya. Ndipo inu munamva mawu anga.” (Yona 2:1, 2, 10) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti kaya vuto lathu likule bwanji, tikhoza kupempha Yehova kuti ‘atikomere mtima.’​—Werengani Salimo 55:1, 16.

8, 9. Kodi mapemphero amene Hezekiya, Hana komanso Yona anapereka akusonyeza kuti nkhawa yawo yaikulu inali chiyani, ndipo tikuphunzira chiyani?

8 Zitsanzo za Hezekiya, Hana ndiponso Yona zimatiphunzitsa chinthu china chimene tiyenera kukumbukira tikamapemphera za vuto limene tili nalo. Anthu atatu onsewa anavutika maganizo pamene anakumana ndi mavuto. Komabe mapemphero awo amasonyeza kuti sankangodziganizira okha n’kumafufuza njira zopulumukira ku mavutowo. Iwo ankaganizira kwambiri za dzina la Mulungu, kumulambira ndiponso kuchita chifuniro chake. Hezekiya zinamupweteka kwambiri ataona mmene anthu ankanyozera dzina la Yehova. Hana analonjeza kuti mwana amene ankamufunitsitsayo, adzamupereka kuti azikatumikira kuchihema ku Silo. Yona ananenanso kuti: “Zimene ndalonjeza ndidzazikwaniritsa.”​—Yona 2:9.

9 Tikamapempha Mulungu kuti atithandize kuthana ndi vuto linalake, tiyenera kuonanso bwino zolinga zathu. Kodi timangofuna kuti vutolo lithe basi, kapena timaganiziranso za Yehova ndi cholinga chake? Nthawi zina, tikakumana ndi vuto tikhoza kumangoganizira za vutolo basi n’kuiwala zinthu zauzimu. Tikamapemphera, tiyenera kuganizira kwambiri za Yehova, kuyeretsedwa kwa dzina lake ndiponso za mmene adzasonyezere kuti ndi woyenera kulamulira. Tikatero tidzakhalabe osangalala ngakhale vutolo litamapitirira. Mwina Mulungu akhoza kuyankha mapemphero athuwo pongotithandiza kupirira vuto lathulo.​—Werengani Yesaya 40:29; Afilipi 4:13.

Pamene Tikufuna Kusankha Zochita

10, 11. Kodi Yehosafati anachita chiyani atakumana ndi vuto loti sankadziwa kuti athana nalo bwanji?

10 Kodi inuyo mumatani mukafuna kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu? Kodi mumayamba mwasankha zochita kenako n’kupempha Yehova kuti adalitse zimene mwasankhazo? Taganizirani zimene Yehosafati, yemwe anali mfumu ya Yuda, anachita ataukiridwa ndi Amowabu ndi Aamoni. Iye ndi anthu ake sakanatha kulimbana ndi anthu amenewa. Kodi Yehosafati anatani?

11 Baibulo limati: “Yehosafati atamva zimenezi anachita mantha ndipo anatsimikiza mumtima mwake kuti afunefune Yehova.” Ndiyeno analengeza kuti Ayuda onse asale kudya ndipo anawasonkhanitsa pamodzi kuti “afunsire kwa Yehova.” Kenako Yehosafati anaimirira pakati pa mpingo wa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu n’kupemphera. Iye anachonderera Yehova kuti: “Inu Mulungu wathu kodi simuwaweruza? Ifeyo patokha tilibe mphamvu zotha kulimbana ndi khamu lalikulu limene likubwera kudzamenyana nafeli ndipo sitikudziwa chochita, koma maso athu ali pa inu.” Mulungu woona anamva pemphero la Yehosafati ndipo anawapulumutsa mozizwitsa. (2 Mbiri 20:3-12, 17) Tikamasankha zochita, makamaka zimene zingakhudze moyo wathu wauzimu, tiyenera kudalira kwambiri Yehova osati luso lathu lomvetsa zinthu.

12, 13. Kodi Mfumu Davide inapereka chitsanzo chotani pa nkhani yosankha zochita?

12 Kodi tingachite chiyani ngati takumana ndi vuto lomwe tikuona kuti n’losavuta kuthana nalo chifukwa choti mwina m’mbuyomu tinakumana nalonso? Zimene zinachitikira Mfumu Davide zikhoza kutithandiza kupeza yankho labwino. Pa nthawi ina, Aamaleki anaukira mzinda wa Zikilaga, n’kutenga akazi, ana ndiponso anthu ena a Davide. Iye anapemphera kwa Yehova kuti: “Kodi ndithamangitse gulu la achifwambali?” Pamenepo Yehova anamuyankha kuti: “Inde athamangitse chifukwa uwapezadi ndi kulanditsa zinthu zimene afunkha.” Davide anamvera zimene anauzidwazi ndipo “analanditsa zonse zimene Aamaleki anatenga.”​—1 Sam. 30:7-9, 18-20.

13 Patapita nthawi ndithu kuchokera pamene Aamaleki anachita zimenezi, Afilisiti anaukiranso Aisiraeli. Davide anapempheranso kwa Yehova ndipo anapatsidwa yankho lomveka bwino. Mulungu anati: “Pita, ndipereka ndithu Afilisitiwa m’manja mwako.” (2 Sam. 5:18, 19) Pasanapite nthawi yaitali, Afilisitiwo anabweranso kudzamenyana ndi Davide. Kodi Davide anatani pa nthawiyi? Mwina akanaganiza kuti: ‘Aa izi si zijazi. Ndipita ndikathane nawo adani a Mulungu amenewa ngati mmene ndinachitira m’mbuyomu.’ Kodi Davide anatero kapena anafunsanso malangizo kwa Yehova? Davide sanadalire zimene anachita m’mbuyomo koma anapempheranso kwa Yehova. Pa nthawiyi analandira malangizo osiyana ndi oyamba aja. (2 Sam. 5:22, 23) Iye ayenera kuti anasangalala kwambiri kuti anayamba wafunsa kaye maganizo a Yehova. Ifenso tikakumana ndi vuto limene tinakumananso nalo m’mbuyomu, tiyenera kusamala kuti tisamadalire zimene tinachita kale n’kumaganiza kuti tikhoza kuthana nalo patokha.​—Werengani Yeremiya 10:23.

14. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yoswa ndi amuna aakulu a Isiraeli anachita ndi anthu a ku Gibeoni?

14 Chifukwa chakuti tonse ndife anthu opanda ungwiro, aliyense kuphatikizapo akulu, ayenera kusamala kuti asasiye kuyendera malangizo a Yehova posankha zochita. Taganizirani zimene Yoswa yemwe analowa m’malo mwa Mose limodzi ndi amuna aakulu a Isiraeli anachita pa nthawi imene anthu a ku Gibeoni ananamizira kuti akuchokera kutali kwambiri. Iwo asanafunsire kwa Yehova, anagwirizana nawo za mtendere ndipo anachita nawo pangano kuti asawaphe. Ngakhale kuti Yehova anadzagwirizana ndi zimene anachita, iye anaonetsetsa kuti cholakwa chawo chimenechi chilembedwe m’Malemba kuti tiphunzirepo kanthu.​—Yos. 9:3-6, 14, 15.

Tikamalimbana ndi Mayesero

15. N’chifukwa chiyani pemphero lili lofunika tikamalimbana ndi mayesero?

15 Popeza tili ndi “chilamulo cha uchimo” m’ziwalo zathu, tiyenera kuyesetsa kwambiri kulimbana ndi mtima wofuna kuchita machimo. (Aroma 7:21-25) N’zotheka kupambana nkhondo imeneyi. Koma kodi tingapambane bwanji? Yesu anauza otsatira ake kuti kupemphera n’kofunika kwambiri kuti tilimbane ndi mayesero. (Werengani Luka 22:40.) Ngakhale kuti tikhoza kumaganizirabe zolakwika pambuyo poti tapemphera, tiyenera ‘kupemphabe kwa Mulungu’ kuti atipatse nzeru zoti tithane ndi vutolo. Tikatero, iye adzatipatsa mowolowa manja komanso mosatonza. (Yak. 1:5) Yakobo analembanso kuti: “Kodi pali wina amene akudwala [mwauzimu] pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo amupempherere ndi kumupaka mafuta m’dzina la Yehova. Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo.”​—Yak. 5:14, 15.

16, 17. Ngati munthu akufuna thandizo kuti alimbane ndi mayesero, kodi nthawi yoyenera kupemphera ndi iti?

16 N’zoona kuti pemphero n’lothandiza tikamakumana ndi mayesero koma tiyenera kudziwa nthawi imene tiyenera kupemphera. Taganizirani za mnyamata wotchulidwa pa Miyambo 7:6-23. Pa nthawi ya madzulo kuli kachisisira, iye anali kuyenda mumsewu wolowera kumene kunkakhala mkazi wachiwerewere. Iye anatengeka ndi zimene mkaziyo ankachita komanso mawu ake okopa ndipo anayamba kumulondola ngati ng’ombe yamphongo yopita kokaphedwa. N’chifukwa chiyani mnyamata ameneyu ankapita kumeneko? Chifukwa chakuti anali “wopanda nzeru mumtima mwake.” Izi zikutanthauza kuti sankadziwa zambiri ndipo zikuoneka kuti ankalimbana ndi mtima wofuna kuchita zoipa. (Miy. 7:7) Kodi ndi nthawi iti pamene pemphero likanamuthandiza kwambiri? N’zoona kuti kupemphera kuti alimbane ndi mayesero pa nthawi iliyonse imene wakumana nawo kukanamuthandiza. Komabe nthawi yabwino kwambiri kupemphera inali pamene ankaganiza zoyamba kudutsa msewu umenewowo.

17 Masiku ano, munthu akhoza kumalimbana ndi vuto loonera zolaula. Koma bwanji ngati amapita dala pamalo ena pa Intaneti amene akudziwa kuti pamakhala zithunzi kapena mavidiyo olaula? Kodi sangafanane ndi mnyamata wotchulidwa pa Miyambo chaputala 7? Zimenezitu zingakhale zangozi kwambiri. Kuti munthu apewe kuonera zolaula ayenera kupemphera kwa Yehova asanayambe kufufuza zinthu pa Intaneti.

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani kulimbana ndi mayesero kuli kovuta ndipo tingatani kuti tigonjetse mayesero? (b) Kodi mwatsimikiza kuchita chiyani?

18 Kulimbana ndi mayesero kapena kusiya zizolowezi zoipa n’kovuta. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zilakolako za thupi zimalimbana ndi mzimu, mzimunso umalimbana ndi thupi.” Choncho ‘zinthu zimene timafuna kuchita sitizichita.’ (Agal. 5:17) Kuti tithane ndi vuto limeneli, tiyenera kupemphera ndi mtima wonse tikangoyamba kuganizira zoipa kenako n’kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene tapemphazo. Kumbukirani kuti “palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene amagwera anthu ena.” Choncho Yehova angakuthandizeni kuti mukhale okhulupirika kwa iye.​—1 Akor. 10:13.

19 Kaya takumana ndi vuto lalikulu, kaya tikufuna kusankha zochita kapena kulimbana ndi mayesero, Yehova watipatsa mphatso yamtengo wapatali kwambiri. Mphatso imeneyi ndi pemphero. Tikamapemphera timasonyeza kuti timadalira Mulungu. Tiyenera kupitiriza kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake woyera umene umatitsogolera komanso kutipatsa mphamvu. (Luka 11:9-13) Choncho tiyeni nthawi zonse tizikhulupirira Yehova ndipo tisamadalire luso lathu lomvetsa zinthu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Mayinawa asinthidwa.

Kodi Mukukumbukira?

• Pa nkhani yodalira Yehova, kodi tikuphunzira chiyani kwa Hezekiya, Hana ndi Yona?

• Kodi zimene Davide ndi Yoswa anachita zikusonyeza bwanji kuti tiyenera kusamala kwambiri tikamasankha zochita?

• Kodi ndi nthawi iti kwenikweni imene tiyenera kupemphera kuti tilimbane ndi mayesero?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi ndi nthawi iti imene tiyenera kupemphera kuti tilimbane ndi mayesero?