Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Woyera, Woyera, Woyera Ndiye Yehova”

“Woyera, Woyera, Woyera Ndiye Yehova”

Yandikirani Mulungu

“Woyera, Woyera, Woyera Ndiye Yehova”

KODI mutafuna kumufotokoza Yehova Mulungu ndi mawu amodzi, amene angafotokozedi mmene iye alili komanso umunthu wake, mungagwiritse ntchito mawu ati? Kale m’zaka za m’ma 700 B.C.E., mneneri Yesaya anaonetsedwa masomphenya, ndipo anamva zolengedwa zauzimu zikutamanda Yehova ndi mtima wonse. Zolengedwazo zinkagwiritsa ntchito mawu amodzi amene amamufotokoza bwino Yehova. Mawu ake anali akuti “woyera.” Zimene Yesaya anamva ndi kuonazo ziyenera kutichititsa mantha komanso kutithandiza kwambiri kuyandikira Yehova. Pamene tikukambirana lemba la Yesaya 6:1-3, muziyerekezera kuti inuyo munalipo pa nthawiyo.

Kodi Yesaya anaona zotani? Yesaya akutiuza kuti: “Ine ndinaona Yehova atakhala pampando wachifumu wolemekezeka umene unali pamalo okwezeka.” (Vesi 1) Apa sikuti Yesaya ankaonadi Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chifukwa maso aumunthu sangathe kuona zamoyo zauzimu. Ndipo Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” (Yohane 1:18) Zimene Yesaya ankaonazi ndi masomphenya chabe. * Komabe, masomphenyawo anali ooneka bwino zedi ndipo Yesaya ankaona ngati akuona zenizeni, moti anachita mantha kwambiri ngati kuti akuonadi Yehova weniweniyo.

Kenako Yesaya anaona zinthu zapadera kwambiri, zimene mwina palibe munthu wina amene anakhalapo ndi mwayi woziona m’masomphenya. Iye analemba kuti: “Pamwamba pake [pa Yehova] panali aserafi. Mserafi aliyense anali ndi mapiko 6. Mapiko awiri anaphimbira nkhope yake, awiri anaphimbira mapazi ake ndipo awiri anali kuulukira.” (Vesi 2) Aserafi ndi zolengedwa zauzimu za udindo waukulu kwambiri. Ndipo pa anthu onse amene analemba nawo Baibulo, Yesaya yekha ndi amene anatchula za aserafi. Aserafi amakhala okonzeka nthawi zonse kuti apite kukachita chilichonse chimene Yehova angawauze. M’masomphenyawa, Yesaya anawaona ataphimba nkhope ndi mapazi awo posonyeza kupereka ulemu ndi ulemerero kwa Yehova. Aserafi ali ndi mwayi wapadera woimirira pamaso pake ndi kum’tumikira.

Yesaya anachita mantha kwambiri, osati ndi zomwe anaona zokha, komanso ndi zimene anamva. Aserafiwo anayamba kuimba nyimbo mokweza kwambiri monga gulu loimba lakumwamba. Yesaya analemba kuti: “Aliyense anali kuuza mnzake kuti: ‘Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova wa makamu.’” (Vesi 3) Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “woyera,” amatanthauza waukhondo komanso wopanda chodetsa chilichonse. Kuwonjezera pamenepa, mawuwa amatanthauzanso “kusakhudzana ngakhale pang’ono ndi uchimo ndiponso kuupeweratu.” M’nyimbo imene mwina aserafiwo ankaimba mosalekeza komanso movomerezana, iwo anagwiritsa ntchito mawu akuti “woyera” katatu konse. Aserafiwo anachita zimenezi potsindika mfundo yakuti Yehova ndi woyera kwambiri, moti alibiretu chodetsa chilichonse. (Chivumbulutso 4:8) Motero, kukhala woyera ndi khalidwe lake lapadera limene limamusiyanitsa ndi zinthu zonse. Inde, Yehova ndi wosadetsedwa, woyera, ndiponso wopanda cholakwa chilichonse.

Kudziwa mfundo yakuti Yehova ndi woyera, kuyenera kutithandiza kwambiri kuti timuyandikire. N’chifukwa chiyani zili choncho? Mosiyana ndi anthu olamulira amene nthawi zina amasintha n’kuyamba kuchita zinthu mwachinyengo ndiponso mwankhanza, Yehova alibiretu uchimo ngakhale pang’ono. Khalidwe lake loyera ndi umboni wotitsimikizira kuti nthawi zonse iye adzapitiriza kukhala Tate wabwino, Wolamulira wachilungamo ndiponso Woweruza wopanda tsankho. Choncho, tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti Mulungu, yemwe ndi woyera kwambiri, sadzatikhumudwitsa.

Mavesi amene mungawerenge mu December:

Yesaya 1–23

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Buku la Insight on the Scriptures limafotokoza kuti: “Kale munthu akakhala maso koma n’kuona masomphenya ochokera kwa Mulungu, zikuoneka kuti masomphenyawo ankakhazikika m’maganizo ndi mumtima mwake. Kenako munthuyo ankatha kukumbukira masomphenyawo n’kuwalemba kapena kuwafotokoza m’mawu akeake.”​—Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 26]

Kudziwa mfundo yakuti Yehova ndi woyera kuyenera kutithandiza kwambiri kuti timuyandikire