Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinkafuna Kukhala Ngati Mwana wa Yefita

Ndinkafuna Kukhala Ngati Mwana wa Yefita

Ndinkafuna Kukhala Ngati Mwana wa Yefita

Yosimbidwa ndi Joanna Soans

Ndili mwana ndinkalakalaka kwambiri n’takhala ngati mwana wa Yefita. Dikirani ndifotokoze zimene ndinkaganiza komanso zimene zinachitika pamapeto pake kuti ndikhaledi ngati mwana wa Yefita.

M’CHAKA cha 1956, ndinapita kumsonkhano waukulu wa Mboni za Yehova kwa nthawi yoyamba. Msonkhanowu unachitikira mumzinda wa Bombay (umene panopa umatchedwa Mumbai), m’dziko la India, ndipo unasintha moyo wanga. Nkhani yonena za mwana wa Yefita imene ndinamva kumsonkhanowo inandikhudza kwambiri.

Mwina munawerenga m’Baibulo nkhani ya mwana wamkazi wa Yefita. Mtsikanayu anavomera kuti sadzakwatiwa ndipo n’kutheka kuti anachita zimenezi asanakwanitse zaka 20. Zimenezi zinathandiza bambo ake kuti akwaniritse lonjezo lawo. Choncho mtsikanayu sanakwatiwedi ndipo ankatumikira Yehova panyumba yake kapena kuti pachihema, moyo wake wonse.​—Oweruza 11:28-40.

Mumtima mwanga ndinkafunitsitsa n’takhala ngati mtsikana ameneyu. Koma ndinakumana ndi vuto lalikulu chifukwa chikhalidwe cha kwathu ku India pa nthawiyo sichinkalola kuti munthu akhale wosakwatiwa.

Banja Lathu

Ine ndinali mwana wachisanu m’banja la ana 6 ndipo ndinabadwira ku Udipi, mzinda umene uli m’mphepete mwa nyanja, kumadzulo kwa dziko la India. Makolo anga anali a Benjamin ndi a Marcelina Soans. Chinenero chathu ndi Chitulu, chimene chimalankhulidwa ndi anthu pafupifupi 2 miliyoni. Komabe, mofanana ndi anthu ambiri ku Udipi, kusukulu tinkaphunzira chinenero cha Chikannada.

Anthu a m’dera limeneli amakhulupirira kuti m’pofunika kwambiri kuti munthu akwatiwe ndi kubereka ana. Ndipo kuyambira ndili mwana sindinamvepo mawu achitulu otanthauza “kusakwatiwa,” “kusungulumwa,” kapena “kufuna kwambiri kupita kumudzi.” Zinkangokhala ngati anthu a m’derali zimenezi sizinkawachitikira. Mwachitsanzo, m’banja lathu tinkakhala ndi agogo athu akuchimuna ndi akuchikazi, amalume, azakhali, ndi achibale ena ambirimbiri.

Pa chikhalidwe chathu, ana ankaonedwa kuti ndi akuchikazi. Choncho mbumba yonse inkakhala yakuchikazi ndipo ana aakazi ankalandira mbali yaikulu ya chuma cha banja. Kwa anthu ena achitulu, mtsikana akakwatiwa ankapitiriza kukhala ndi mayi ake, ndipo mwamuna wake ndi amene ankachoka kwawo n’kukakhala kuchikamwini.

Koma banja lathu litalowa chipembedzo chinachake chachikhristu, tinkachita zinthu zina mosiyana ndi anthu ena. Madzulo alionse agogo anga aamuna ankatsogolera banja lonse polambira. Iwo ankapemphera komanso kuwerenga mokweza Baibulo lachitulu. Akamatsegula Baibulo lawo limene linali long’ambikang’ambika kuti atiwerengere, ndinkangoona ngati akutsegula bokosi limene lili ndi zinthu zamtengo wapatali, ndipo ndinkasangalala kwambiri. Ndinachita chidwi ndi lemba la Salimo 23:1 limene limati: “Yehova ndi M’busa wanga. Sindidzasowa kanthu.” Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova ameneyu ndani, ndipo n’chifukwa chiyani akutchedwa m’busa?’

Maso Anga Anatseguka

Titakumana ndi mavuto azachuma chifukwa cha nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, tinasamukira mumzinda wa Bombay, umene unali pamtunda wa makilomita oposa 900 kuchokera kumudzi kwathu. Kumeneko anthu awiri a Mboni za Yehova anabwera kudzacheza ndi bambo mu 1945, ndipo anawapatsa kabuku kofotokoza za m’Baibulo. Bambo anachita chidwi kwambiri ndi kabukuka moti anakawerenga nthawi yomweyo ndipo anasangalala kwambiri ndi uthenga wake. Kenako anayamba kuuza anthu ena olankhula Chikannada zimene anawerengazo. Pofika kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1950, kagulu kakang’ono ka ophunzira Baibulo ku Bombay, kanakula n’kukhala mpingo woyamba wa Mboni za Yehova wa anthu olankhula Chikannada mumzindawu.

Bambo ndi mayi anatiphunzitsa anafe kuti tiziphunzira Baibulo mwakhama ndiponso kuti tiziphunzitsa ena mogwira mtima. Tsiku lililonse ankapeza mipata yopemphera nafe komanso kuphunzira nafe. (Deuteronomo 6:6, 7; 2 Timoteyo 3:14-16) Tsiku lina ndikuwerenga Baibulo, maso anga anatseguka chifukwa ndinaphunzira mfundo yakuti Yehova ali ngati m’busa chifukwa amatsogolera, kudyetsa ndi kuteteza anthu amene amamulambira.​—Salimo 23:1-6; 83:18.

Yehova Wandigwira Dzanja

Ine ndinabatizidwa utangodutsa msonkhano wosaiwalika uja, umene unachitika ku Bombay mu 1956. Patangopita miyezi 6, ndinakhala mlaliki wa nthawi zonse, potengera chitsanzo cha mchimwene wanga Prabhakar. Ngakhale kuti ndinkafunitsitsa kuuza ena choonadi cha m’Baibulo, ndinkachita mantha kwambiri ndikayamba kuuza anthu za chikhulupiriro changa, moti malovu ankauma m’kamwa mwanga. Ndinkachita chibwibwi ndipo ndinkanjenjemera polankhula moti ndinkadziuza kuti, ‘Sindingakwanitse kugwira ntchito imeneyi, pokhapokha ngati Yehova atandithandiza.’

Yehova anandithandizadi chifukwa kunabwera amishonale awiri ochokera ku Canada. Mayina awo anali Homer ndi Ruth McKay. Banja limeneli linaphunzitsidwa kusukulu ya Mboni za Yehova yophunzitsa amishonale imene inachitika m’chaka cha 1947 mumzinda wa New York, m’dziko la United States. Tinganene kuti iwo anandigwira dzanja pamene ndinkavutika kulalikira nditangoyamba kumene utumiki wanga. Mwachitsanzo, Ruth anandithandiza chifukwa nthawi zonse ankayeserera nane ulaliki wa khomo ndi khomo. Iye ankadziwa bwino kwambiri njira zothetsera mantha anga mu utumiki. Ndikamanjenjemera ankandigwira dzanja n’kundiuza kuti: “Usadandaule mlongo, tiye tikayese panyumba inayo.” Mawu ake olimbikitsawo ankandithandiza kuti ndilimbe mtima.

Tsiku lina ndinauzidwa kuti ndizilalikira limodzi ndi Elizabeth Chakranarayan, yemwe anali wachikulire komanso wodziwa kuphunzitsa Baibulo mwaluso. Nditangomva zimenezi ndinadzifunsa kuti: ‘Ndidzakwanitsa bwanji kukhala ndi mlongo wamkulu kwambiri chonchi kuposa ine?’ Koma nditayamba kugwira naye ntchito, ndinazindikira kuti iye ndi munthu amene ndinkafunikiradi.

“Sikuti Tilidi Tokhatokha”

Dera lathu loyamba kukachita utumiki wa nthawi zonse linali mzinda wotchuka wa Aurangabad, umene uli pamtunda wa makilomita pafupifupi 400, kum’mawa kwa mzinda wa Bombay. Posakhalitsa tinazindikira kuti a Mboni tinalipo awiri okha mumzindawo, momwe munali anthu pafupifupi 1 miliyoni. Komanso ndinkafunikira kuphunzira chinenero cha Chimarathi, chimene anthu ambiri amalankhula mumzindawo.

Nthawi zina ndinkasungulumwa, moti ndinkalira chifukwa ndinkangodziona ngati mwana wamasiye. Koma Elizabeth ankandilimbikitsa chifukwa ankandilankhula ngati mayi wanga. Iye ankandiuza kuti: “Nthawi zina tingasungulumwe, koma sikuti tilidi tokhatokha. N’zoona kuti anzako komanso achibale ako ali kutali, koma Yehova ali nawe pafupi nthawi zonse. Uzimuona Yehova ngati mnzako, ndipo kusungulumwa kwako konse kudzatheratu.” Malangizo amenewo akundithandizabe mpaka pano.

Ndalama zoyendera zikatithera, tinkayenda wapansi mtunda wa makilomita 20 tsiku lililonse, kaya ndi nthawi yafumbi, yamatope, yotentha kapena yozizira. Nthawi yotentha, kunkatentha kwambiri mpaka kufika 40 digiri seshasi. Ndipo m’nyengo yamvula, m’malo ambiri amene tinkalalikiramo munkakhala matope kwa miyezi yambiri. Komabe, vuto lalikulu kwa ife chinali chikhalidwe cha anthu, osati nyengo.

M’derali akazi sankalankhula ndi amuna poyera pokhapokha ngati anali apachibale, ndipo zinali zachilendo kuti akazi aziphunzitsa amuna. Choncho anthu ankatinyoza ndi kutichitira zinthu zachipongwe. Kwa miyezi 6 yoyambirira, tinkangochita awiriwiri misonkhano ya mlungu ndi mlungu. Kenako anthu achidwi anayamba kubwera kumisonkhanoyi. Posakhalitsa gululi linayamba kukula ndipo ena anayamba kulalikira nafe limodzi mu utumiki wakumunda.

“Pitiriza Kukulitsa Luso Lako”

Patapita pafupifupi zaka ziwiri ndi hafu, anatitumiza ku Bombay. Kumeneko Elizabeth anapitiriza kuchita upainiya, koma ine ndinapemphedwa kuti ndizithandizana ndi bambo anga, amene ankagwira okhaokha ntchito yomasulira mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’chinenero cha Chikannada. Bambowo anasangalala kwambiri kuti ndizikawathandiza, chifukwa analinso ndi maudindo ambiri kumpingo.

Mu 1966, makolo anga anaganiza zobwerera kumudzi kwathu ku Udipi. Pamene bambo ankachoka ku Bombay, anandiuza kuti: “Pitiriza kukulitsa luso lako mwana wanga. Pomasulira uzigwiritsa ntchito mawu osavuta kumva ndipo uzilemba zomveka bwino. Usamadzidalire kwambiri, ukhale wodzichepetsa ndipo uzidalira Yehova.” Amenewa ndi malangizo omaliza amene bambo anandipatsa chifukwa anamwalira atangobwerera ku Udipi. Mpaka pano, ndikuyesetsa kutsatira malangizo amenewa pa ntchito yanga yomasulira mabuku.

“Kodi Sufuna Kukwatiwa?”

Makolo a ku India amapezeratu munthu woti adzakwatirane ndi mwana wawo, potsatira mwambo wawo. Iwo amachita zimenezi anawo ali aang’ono kwambiri ndipo akadzakwatirana amawalimbikitsa kuti abereke ana. Choncho kawirikawiri anthu ankandifunsa kuti: “Kodi sufuna kukwatiwa? Adzakusamalire ndani ukadzakalamba? Kodi susungulumwa?”

Nthawi zina mafunso amenewa, omwe anthu ankandifunsa mobwerezabwereza, ankandipweteka. Ngakhale kuti sindinkaonetsera poyera kuti zikundipweteka, ndikangopeza mpata wokhala ndekha ndinkamuuza Yehova zonse zimene zili mumtima mwanga. Ndinkalimba mtima ndikaganizira mfundo yakuti iye saona kuti ndine woperewera chifukwa chakuti sindinakwatiwe. Chimene chinandithandiza kuti ndipitirize kutumikira Mulungu popanda chosokoneza chilichonse, n’chakuti ndinkaganizira za mwana wa Yefita komanso Yesu. Onsewa sanali pa banja ndipo anali odzipereka kwambiri pochita chifuniro cha Mulungu.​—Yohane 4:34.

Mphatso Yochokera kwa Yehova

Ine ndi Elizabeth tinakhala mabwenzi enieni kwa zaka pafupifupi 50, ndipo iye anamwalira mu 2005 ali ndi zaka 98. Elizabeth sankathanso kuona bwino pa zaka zotsirizira za moyo wake ndipo ankalephera kuwerenga Baibulo. Choncho tsiku lililonse ankangokhalira kupemphera kwa Mulungu mochokera pansi pa mtima ndipo ankachita zimenezi pafupifupi tsiku lonse. Nthawi zina ndinkaganiza kuti akukambirana malemba ndi munthu wina m’chipinda chake, koma kenako ndinkapeza kuti amalankhula ndi Yehova. Kwa iye Mulungu anali munthu weniweni ndipo ankangokhala ngati ali naye pafupi nthawi zonse. Ine ndaphunzira kuti imeneyi ndi njira yokhalira wolimba potumikira Mulungu, ngati mmene mwana wa Yefita anachitira. Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chondipatsa mlongo wachikulireyu, yemwe ankandiphunzitsa pamene ndinali mwana komanso ankandilimbikitsa pa mavuto anga onse.​—Mlaliki 4:9, 10.

Ndapeza madalitso ambiri potumikira Yehova ngati mmene mwana wa Yefita anachitira. Kukhala wosakwatiwa komanso kutsatira malangizo a m’Baibulo kwandithandiza kukhala moyo wosangalala ndi wopindulitsa popitiriza “kutumikira Ambuye nthawi zonse popanda chododometsa.”​—1 Akorinto 7:35.

[Chithunzi patsamba 28]

Bambo anga akukamba nkhani ya onse ku Bombay m’ma 1950

[Chithunzi patsamba 28]

Ine ndi Elizabeth. Iye anamwalira patapita masiku ochepa

[Chithunzi patsamba 29]

Tikuitanira anthu kudzamvera nkhani ya m’Baibulo ku Bombay mu 1960

[Chithunzi patsamba 29]

Ndili ndi anzanga amene ndikugwira nawo ntchito yomasulira mabuku