Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yandikirani Mulungu

“Ine, Yehova Mulungu Wako, Ndagwira Dzanja Lako Lamanja”

“Ine, Yehova Mulungu Wako, Ndagwira Dzanja Lako Lamanja”

TAYEREKEZANI kuti mwana wina ndi bambo ake akufuna kuwoloka msewu wodutsa magalimoto ambiri. Mwanayo akuchita mantha kuwoloka msewuwo koma bambo ake akumuuza kuti: “Bwera ndikugwire dzanja.” Kodi mukuganiza kuti mwanayo angamve bwanji? N’zosakayikitsa kuti mantha ake onse angathe ndipo angamve kuti ndi wotetezeka. Kodi nthawi zina mumalakalaka munthu wina atakugwirani dzanja n’kumakutsogolerani pa nthawi imene mukukumana ndi mavuto? Ngati ndi choncho, mawu amene Yesaya analemba angakulimbikitseni kwambiri.​—Werengani Yesaya 41:10, 13.

Yesaya ndi amene analemba mawu a Mulungu amenewa ndipo ankauza Aisiraeli. Ngakhale kuti Mulungu ankaona mtundu wa Isiraeli ngati ‘chuma chake chapadera,’ mtunduwu unali utazunguliridwa ndi adani ambiri. (Ekisodo 19:5) Kodi Aisiraeli ankayenera kuchita mantha? Yehova anagwiritsa ntchito Yesaya kuuza Aisiraeli mawu olimbikitsa. Pamene tikukambirana mawu amenewa, tisaiwale kuti mawuwa akugwiranso ntchito kwa atumiki a Mulungu masiku ano.​—Aroma 15:4.

Yehova ananena kuti: “Usachite mantha.” (Vesi 10) Mulungu anali ndi chifukwa chomveka ponena mawu amenewa. Yehova anafotokoza chifukwa chake anthu ake sayenera kuchita mantha. Iye ananena kuti: “Pakuti ndili nawe.” Yehova samakhala patali ndi anthu ake n’kumangodikira nthawi imene anthu akewo akufunikira thandizo. Iye amafuna kuti anthu ake adziwe kuti ali nawo limodzi ndipo ndi wokonzeka nthawi zonse kuwathandiza. Kodi zimenezi sizolimbikitsa?

Yehova anauzanso atumiki ake mawu ena olimbikitsa akuti: “Usayang’ane uku ndi uku mwamantha.” (Vesi 10) Mawu achiheberi amene anawagwiritsa ntchito pamenepa amanena za munthu amene “amangoti maso mwazumwazu kuti aone ngati kukubwera chinthu choopsa.” Yehova anafotokoza chifukwa chake anthu ake safunikira kuyang’ana uku ndi uku mwamantha. Iye anati: “Ine ndine Mulungu wako.” Koma pali chifukwa chinanso chimene atumiki a Yehova sayenera kuchitira mantha. Chifukwa chake n’chakuti Yehova ndi “Wam’mwambamwamba” komanso “Wamphamvuyonse.” (Salimo 91:1) Choncho, palibe chifukwa choti atumiki a Yehova azichitira mantha chifukwa Yehova, Mulungu wawo, ndi wamphamvuyonse.

Ndiye kodi atumiki a Yehova akanayembekezera kuti iye awachitira chiyani? Iye anawalonjeza kuti: “Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.” (Vesi 10) Iye ananenanso kuti: “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja.” (Vesi 13) Kodi n’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukamva mawu amenewa? Buku lina linanena kuti: “Mavesi awiri amenewa akutipangitsa kuganizira za bambo ndi mwana wake. Sikuti [bambo] amangodikirira kuti athandize mwana wake zinthu zikavuta. Nthawi zonse iye amaonetsetsa kuti ali ndi mwanayo.” Ndi mmenenso Yehova amachitira. Iye nthawi zonse amaonetsetsa kuti ali ndi anthu ake ngakhale pa nthawi imene iwo angaone kuti ndi yovuta kwambiri pa moyo wawo.​—Aheberi 13:5, 6.

Masiku ano, atumiki a Yehova angalimbikitsidwe kwambiri ndi mawu amene takambiranawa amene Yesaya analemba. ‘M’nthawi yovuta’ ino, nthawi zina tingaone kuti mavuto atikulira. (2 Timoteyo 3:1) Komabe sitiyenera kulimbana ndi mavuto amenewa patokha chifukwa Yehova ndi wokonzeka kutigwira dzanja kuti atithandize. Popeza timamudalira monga bambo wathu, tingagwire dzanja lake lamphamvu tili ndi chidaliro chonse kuti atitsogolera m’njira yoyenera komanso atithandiza pa nthawi iliyonse imene tikufunika thandizo.​—Salimo 63:7, 8.

Mavesi amene mungawerenge mu January:

Yesaya 24 mpaka 42