Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

Baibulo Limasintha Anthu

KODI n’chiyani chinathandiza mtsikana wina yemwe anakula movutika kwambiri kuti ayambe kukhala wosangalala? Nanga n’chiyani chinachititsa mwamuna wina yemwe anali woukira boma komanso wachiwawa kuti asinthe n’kuyamba kukhala mwamtendere ndi anthu ndiponso kuyamba kulalikira uthenga wabwino? Werengani nkhani zotsatirazi kuti mupeze mayankho a mafunso amenewa.

“Ndinkalakalaka kupeza anthu amene angamandikonde.”​—INNA LEZHNINA

CHAKA CHOBADWA: 1981

DZIKO: RUSSIA

POYAMBA: NDINAKULA MOVUTIKA KWAMBIRI

KALE LANGA: Ndinabadwa ndi vuto losamva ndipo makolo anganso ali ndi vuto lomweli. Poyamba zinthu zinkayenda bwino m’banja lathu. Koma nditakwanitsa zaka 6, banja la bambo ndi mayi anga linatha. Ngakhale kuti ndinali wamng’ono, ndinkadziwa mavuto amene amabwera banja likatha ndipo zinkandipweteka kwambiri. Zitatere, ine ndi mayi tinasamukira mumzinda wa Chelyabinsk ndipo bambo ndi mchimwene wanga wamkulu anatsala mumzinda wa Troitsk. Patapita nthawi mayi anakwatiwanso. Bambo anga ondipezawa ankakonda kuledzera ndipo nthawi zambiri ankawamenya mayi komanso ineyo.

Mu 1993, mchimwene wanga wamkulu anamira m’madzi. Aliyense m’banja lathu anakhudzidwa kwambiri ndi imfa imeneyi. Pofuna kuiwala imfayi, mayi anga anayamba kumwa mowa ndipo nawonso anayamba kundizunza. Ndinayamba kufufuza zimene zingandithandize kuti ndizikhala wosangalala. Ndinkalakalaka kupeza anthu amene angamandikonde. Choncho, ndinayamba kupita kumatchalitchi osiyanasiyana n’cholinga choti mwina ndikalimbikitsidwe, koma palibe tchalitchi chimene chinandithandiza.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Ndili ndi zaka 13, mnzanga wina wa m’kalasi mwathu, yemwe anali wa Mboni za Yehova, ankandiuza nkhani zosiyanasiyana za m’Baibulo. Ndinkasangalala kwambiri ndi nkhani za anthu ngati Nowa ndi Yobu, omwe anatumikira Mulungu ngakhale pa nthawi yovuta. Pasanapite nthawi ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni komanso kupezeka pa misonkhano yawo.

Zimenezi zinandithandiza kuti ndidziwe mfundo zambiri za m’Baibulo. Ndinachita chidwi nditadziwa dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Ndinachitanso chidwi kwambiri nditadziwa kuti Baibulo linalosera molondola za zinthu zimene zikuchitika ‘m’masiku otsiriza’ ano. (2 Timoteyo 3:1-5) Komanso ndinasangalala kwambiri nditaphunzira zoti akufa adzauka chifukwa ndinadziwa kuti ndidzamuonanso mchimwene wanga amene anamwalira uja.​—Yohane 5:28, 29.

Komabe, si anthu onse amene anasangalala nditayamba kuphunzira ndi a Mboni. Mayi komanso bambo anga ondipeza ankadana kwambiri ndi Mboni za Yehova. Iwo ankandikakamiza kuti ndisiye kuphunzira Baibulo. Koma ndinkasangalala kwambiri ndi zimene ndinkaphunzirazo ndipo ndinatsimikiza mtima kuti sindisiya.

Zinali zovuta kupirira zimene makolo anga ankandichitira pofuna kuti ndisiye kuphunzira Baibulo. Chinthu chinanso chomvetsa chisoni chinali imfa ya mchimwene wanga wamng’ono amene anamira m’madzi titapitira limodzi ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Koma a Mboni anandithandiza kwambiri pa nthawi yonse yovutayi. Anthu amenewa ankandikonda kwambiri, ndipo zimenezi n’zimene ndinkalakalaka kuyambira kalekale. Zimenezi zinandichititsa kuzindikira kuti chimenechi ndi chipembedzo choona. Choncho, mu 1996 ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Ndinakwatiwa ndi mwamuna wabwino dzina lake Dmitry ndipo takhala m’banja kwa zaka 6. Panopa ine ndi mwamuna wanga tikutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova yomwe ili mumzinda wa St. Petersburg. Masiku ano makolo anga sadananso kwambiri ndi chipembedzo changa.

Ndimayamikira kwambiri kuti ndamudziwa Yehova ndipo kumutumikira kwachititsa kuti moyo wanga ukhale waphindu.

“Ndinali ndi mafunso ambiri omwe ankandisowetsa mtendere.”​—RAUDEL RODRÍGUEZ RODRÍGUEZ

CHAKA CHOBADWA: 1959

DZIKO: CUBA

POYAMBA: NDINALI WOUKIRA BOMA

KALE LANGA: Ndinabadwira mumzinda wa Havana, m’dziko la Cuba, ndipo ndinakulira m’dera la anthu osauka. M’misewu ya m’derali munkachitika zachiwawa kawirikawiri. Ndili mnyamata, ndinayamba kukonda masewera osiyanasiyana omenyana.

Kusukulu ndinkakhoza bwino ndipo makolo anga anandilimbikitsa kuti ndipite ku yunivesite. Ndili ku yunivesiteko ndinayamba kuona kuti zinthu sizikuyenda bwino m’dziko lathu choncho ndinaona kuti m’pofunika kusintha ulamuliro. Chifukwa cha zimenezi ndinaganiza zoukira boma. Tsiku lina, ine ndi mnzanga wina wa m’kalasi mwathu tinamenya wapolisi wina n’cholinga choti timulande mfuti, moti wapolisiyo anavulala kwambiri m’mutu. Zimenezi zinachititsa kuti ine ndi mnzangayo timangidwe ndipo tinauzidwa kuti tiphedwa powomberedwa ndi mfuti. Pa nthawi imeneyi n’kuti ndili ndi zaka 20 zokha.

Ndili ndekha m’chipinda chimene ananditsekera, ndinkakonzekera zimene ndidzachite pa nthawi yowomberedwayo. Ndinkafuna kuti ndisadzaoneke wamantha. Komabe, pa nthawiyi ndinali ndi mafunso ambiri amene ankandisowetsa mtendere. Ndinkadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani padzikoli pamachitika zinthu zambiri zopanda chilungamo? Kodi mmenemu ndi mmene moyo uyenera kukhalira basi?’

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Patapita nthawi, chilango chathu chija chinasinthidwa ndipo m’malo mophedwa anatilamula kukhala m’ndende kwa zaka 30. Pa nthawi imeneyi m’pamene ndinakumana ndi a Mboni za Yehova amene anamangidwa chifukwa cha chipembedzo chawo. Ndinachita chidwi ndi anthu amenewa chifukwa anali olimba mtima komabe ankachita zinthu mwamtendere. Ngakhale kuti iwo anamangidwa osalakwa, sankaoneka okhumudwa kapena olusa.

A Mboni anandiphunzitsa kuti Mulungu anali ndi cholinga polenga anthu. Anandisonyeza kuchokera m’Baibulo kuti Mulungu adzasandutsa dziko lapansili kukhala paradaiso ndipo simudzakhala zinthu zopanda chilungamo komanso anthu ophwanya malamulo. Anandiphunzitsanso kuti dziko lapansili lidzakhala lopanda mavuto alionse ndipo lidzadzaza ndi anthu abwino okhaokha omwe adzapatsidwe mwayi wokhala ndi moyo wosatha.​—Salimo 37:29.

Ndinkasangalala kwambiri ndi zimene ndinkaphunzira ndi a Mboni koma ndinkaona kuti sindingathe kukhala ndi makhalidwe abwino ngati iwowo. Ndinkaona kuti sindingathe kusalowerera ndale kapena kutembenuzira tsaya lina kwa munthu amene wandimenya. Motero ndinaganiza zomangowerenga Baibulo pandekha. Nditawerenga Baibulo lonse, ndinazindikira kuti a Mboni za Yehova okha ndi amene amachita zinthu ngati Akhristu oyambirira.

Kuchokera pa zimene ndinaphunzira m’Baibulo, ndinazindikira kuti ndiyenera kusintha zinthu zambiri pa moyo wanga. Mwachitsanzo, ndinafunika kusintha kalankhulidwe kanga chifukwa ndinkakonda kutukwana. Ndinafunikanso kusiya kusuta fodya komanso kulowerera nkhani zandale. Kuchita zimenezi sikunali kophweka koma Yehova anandithandiza ndipo m’kupita kwa nthawi ndinasinthadi.

Chinthu china chimene chinandivuta kwambiri kusintha chinali khalidwe langa losachedwa kupsa mtima. Mpaka pano ndimapempherabe kwa Mulungu kuti andithandize kukhala wougwira mtima. Malemba a m’Baibulo monga la Miyambo 16:32 andithandiza kwambiri. Lembali limati: “Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu, ndipo munthu wolamulira mtima wake amaposa munthu wogonjetsa mzinda.”

M’chaka cha 1991, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Ndinabatizidwira m’chibeseni chachikulu kundende komweko. M’chaka chotsatira, ineyo ndi akaidi ena tinamasulidwa ndipo anatitumiza ku Spain chifukwa kumeneko kunali achibale athu. Nditangofika ku Spain, ndinayamba kusonkhana ndi a Mboni za Yehova. A Mboni anandilandira ndi manja awiri ndipo zinangokhala ngati tinadziwana kalekale. Iwo anandithandizanso kupeza zochita zoti zizindithandiza pa moyo wanga.

PHINDU LIMENE NDAPEZA: Panopa ndine munthu wosangalala ndipo ndikutumikira Mulungu limodzi ndi mkazi wanga komanso ana athu awiri aakazi. Ndimasangalalanso kuti nthawi yambiri ndimakhala ndikuthandiza anthu ena kuphunzira Baibulo. Nthawi zina ndimakumbukira ndili mnyamata nditatsala pang’ono kuphedwa ndipo ndimayamikira phindu limene ndapeza kuchokera nthawi imeneyo. Ndimayamikira kuti panopa ndili moyo komanso ndili ndi chiyembekezo. Ndimayembekezera nthawi imene dzikoli lidzakhale Paradaiso ngati mmene Mulungu analonjezera. Pa nthawi imeneyo zinthu zonse zizidzachitika mwachilungamo ndipo “imfa sidzakhalaponso.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

“Ndinachita chidwi nditadziwa dzina la Mulungu”

[Chithunzi patsamba 20]

Ine ndi mwamuna wanga timasangalala kuphunzitsa m’chinenero chamanja anthu osamva