Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi N’chifukwa Chiyani Mulungu Anauza Abulahamu Kuti Apereke Mwana Wake Nsembe?

Kodi N’chifukwa Chiyani Mulungu Anauza Abulahamu Kuti Apereke Mwana Wake Nsembe?

▪ Buku la Genesis limanena kuti Yehova Mulungu anauza Abulahamu kuti apereke mwana wake Isaki nsembe. (Genesis 22:2) Anthu ena amene amawerenga Baibulo samvetsa chifukwa chake Mulungu anachita zimenezi. Mwachitsanzo, pulofesa wina dzina lake Carol, ananena kuti: “Nditangomva nkhani imeneyi koyamba ndili mwana, ndinadabwa kwambiri kuti ndi Mulungu wotani amene angamuuze munthu kuti achite zimenezi?” Ngakhale kuti m’pomveka munthu kukhala ndi maganizo amenewa, tingachite bwino kuganizira mfundo zina zokhudza nkhaniyi.

Choyamba, ganizirani zimene Yehova sanachite. Iye sanamusiye Abulahamu kuti aperekedi nsembe mwana wakeyo, ngakhale kuti Abulahamuyo anali wokonzeka kutero. Komanso kuchokera nthawi imeneyi Mulungu sanapemphenso munthu wina aliyense kuti achite zimenezi. Yehova amafuna kuti anthu onse amene amamulambira, kuphatikizapo ana, azikhala ndi moyo wautali komanso wabwino.

Chachiwiri, Baibulo limasonyeza kuti Yehova anali ndi cholinga chapadera popempha Abulahamu kuti apereke nsembe Isaki. Mulungu ankadziwa kuti pambuyo pa zaka zambiri, adzalola kuti Mwana wake, * Yesu, atifere. (Mateyu 20:28) Yehova anafuna kutithandiza kumvetsa mmene imfa imeneyi idzamukhudzire. Popempha Abulahamu kuti apereke mwana wake nsembe, Mulungu anapereka chitsanzo cha nsembe imene iye adzapereke. N’chifukwa chiyani tikutero?

Taganizirani mawu amene Yehova anauza Abulahamu. Iye anati: “Tenga Isaki mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiriyo, ndipo . . . ukamupereke nsembe yopsereza.” (Genesis 22:2) Onani kuti ponena za Isaki, Yehova ananena kuti mwana wako “amene umamukonda kwambiriyo.” Yehova ankadziwa kuti Isaki anali munthu wofunika kwambiri kwa Abulahamu. Choncho ankadziwanso mmene iye ankakondera Mwana wake, Yesu. Ndipotu Yehova amakonda kwambiri Yesu moti kawiri konse analankhula ali kumwamba ndipo anamutcha kuti, “Mwana wanga wokondedwa.”​—Maliko 1:11; 9:7.

Komanso dziwani kuti pamene Yehova ankauza Abulahamu kuti apereke nsembe mwana wake, anagwiritsa ntchito mawu osonyeza kumupempha. N’zodziwikiratu kuti Abulahamu atamva pempho limeneli anamva chisoni kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi mmene Yehova anamvera pamene ankaona Mwana wake wokondedwa akuzunzidwa kenako n’kuphedwa. Pa nthawi imeneyi, Yehova anamva ululu kwambiri. Ziyenera kuti aka kanali koyamba komanso komaliza kuti Yehova amve ululu woterewu.

Choncho, ngakhale kuti tingaganize zoti zimene Yehova anapempha Abulahamu kuchita zinali zovuta, tiyenera kukumbukiranso kuti iye sanalole munthu wokhulupirika ameneyu kuti aperekedi mwana wakeyo nsembe. Pamene Yehova analetsa Abulahamu kuti asaphe Isaki, anathandiza Abulahamuyo kuti asakhale ndi chisoni chimene kholo limakhala nacho mwana wake akafa. Koma Yehova sanalepheretse imfa ya “Mwana wake koma anamupereka m’malo mwa ife tonse.” (Aroma 8:32) N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti mwana wake aphedwe zomwe zinali zinthu zopweteka kwambiri? Iye anachita zimenezi n’cholinga choti “tipeze moyo.” (1 Yohane 4:9) Nkhani ya Abulahamuyi imatithandiza kumvetsa chikondi chachikulu chimene Mulungu ali nacho pa anthufe. Kodi zimenezi sizingatichititse kuti nafenso tizimukonda kwambiri? *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Baibulo siliphunzitsa kuti Mulungu anabereka Yesu kudzera mwa mkazi. M’malomwake Yehova analenga munthu wauzimu ameneyu, yemwe patapita nthawi anamutumiza padziko lapansi ndipo anabadwa kwa namwali wotchedwa Mariya. Choncho popeza kuti Mulungu ndi amene analenga Yesu, mpake kuti iye amatchedwa Atate wa Yesu.

^ ndime 8 Kuti mudziwe zambiri zokhudza kufunika kwa imfa ya Yesu komanso mmene tingasonyezere kuti timayamikira zimene Mulungu anachita, werengani mutu 5 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?