Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena

Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena

MTIMA wa Esitere unkagunda kwambiri pamene ankayandikira pomwe mfumu inakhala. Yerekezerani kuti mukumuona akulowa m’nyumba yachifumu, yomwe inali ku Susani ku Perisiya ndipo anthu onse akukhala chete moti Esitere akutha kumva kaphokoso ka mapazi ake komanso ka zovala zake zachifumu. Nyumba yachifumuyi inali yaikulu kwambiri ndipo makoma ake anamangidwa mochititsa chidwi. Komanso inali yokongoletsedwa ndi matabwa a mkungudza ochokera ku Lebanoni. Koma Esitere sanachite chidwi kwambiri ndi zimenezi. Maso ake onse anali pa mfumu chifukwa ankadziwa kuti zimene mfumuyo ingachite zingachititse kuti iye aphedwe kapena ayi.

Mfumuyo inamuyang’anitsitsa pamene ankayandikira ndipo inamuloza ndi ndodo yake yachifumu yagolide. Zimene mfumu inachitazi zingaoneke ngati nkhani yaing’ono koma zinali zofunika kwambiri chifukwa zinachititsa kuti Esitere asaphedwe chifukwa cha mlandu umene wapalamula. Mlandu wake unali woti iye wakaonekera pamaso pa mfumuyo asanaitanidwe. Atafika pamene panali mfumuyo, Esitere anagwira pamwamba pa ndodoyo posonyeza kuyamikira.​—Esitere 5:1, 2. *

Ahasiwero ankachita kuonekeratu kuti anali wolemera kwambiri komanso mfumu yamphamvu. Akatswiri amaphunziro amanena kuti zovala za mafumu a ku Perisiya a nthawi imeneyo zinali zapamwamba kwambiri moti panopa mtengo wake ukhoza kukhala madola mamiliyoni ambiri. Koma ngakhale zinali choncho, Esitere anaona kuti Ahasiwero ankamukondabe. Ahasiwero anati: “Chavuta n’chiyani Mfumukazi Esitere, ndipo ukufuna kupempha chiyani? Ngakhale utapempha hafu ya ufumuwu, ipatsidwa kwa iwe.”​—Esitere 5:3.

Zimene Esitere anachitazi, pokaonekera kwa mfumu ndi cholinga choti akateteze anthu a mtundu wake ku chiwembu chofuna kuwapha onse, zinasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro komanso anali wolimba mtima. Koma ngakhale kuti zinatheka kuonana ndi mfumuyi, panali padakali zinthu zina zovuta zoti achite. Iye anafunika kufotokoza momveka bwino kwa mfumu yomva zake zokhayi kuti izindikire kuti mlangizi wake amene inkamudalira kwambiri, anali atainamiza n’cholinga choti ilamule zoti anthu a mtundu wa Esitere aphedwe. Kodi Esitere akanachita bwanji zimenezi, ndipo tingaphunzirepo chiyani pa chikhulupiriro chake?

Anasankha Mwanzeru “Nthawi Yolankhula”

Kodi Esitere akanangofikira kufotokozera mfumuyo nkhani imene wabwerera pamaso pa anthu onse ogwira ntchito m’nyumba ya mfumuyo? Kuchita zimenezi kukanachititsa manyazi mfumuyo komanso kukanachititsa Hamani kuyamba kudziikira kumbuyo. Ndiyeno kodi Esitere akanatani? Zaka zambiri izi zisanachitike, mfumu yanzeru Solomo inauziridwa ndi Mulungu kulemba kuti: “Chilichonse chili ndi nthawi yake, . . . Nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” (Mlaliki 3:1, 7) Tikukhulupirira kuti Moredekai, munthu wokhulupirika yemwe analera Esitere ngati mwana wake weniweni, ankamuphunzitsa mtsikanayu mfundo zimenezi. Choncho Esitere ankadziwa kufunika kosankha bwino “nthawi yolankhula.”

Esitere anati: “Ngati zingakukomereni mfumu, lero inu ndi Hamani mubwere kuphwando limene ine ndakukonzerani.” (Esitere 5:4) Mfumu inagwirizana nazo ndipo inaitana Hamani kuti abwere kuphwandoko. Pamenepatu Esitere analankhula mwanzeru. Iye anamusungira mwamuna wake ulemu ndipo anaona kuti imeneyi sinali nthawi yabwino yofotokoza nkhawa imene anali nayo.

N’zachidziwikire kuti Esitere anakonza phwandolo mosamala kwambiri ndipo anaonetsetsa kuti chakudya chaphikidwa mogwirizana ndi zimene mwamuna wake amakonda. Anakonza zoti paphwandolo pakhalenso vinyo n’cholinga choti anthuwo asangalale. (Salimo 104:15) Paphwandolo Ahasiwero anasangalala kwambiri ndipo anafunsanso Esitere kuti anene pempho lake. Kodi imeneyi inali nthawi yabwino yoti Esitere alankhule?

Esitere anaonabe kuti imeneyi sinali nthawi yabwino ndipo anaitaniranso mfumuyo ndi Hamani kuphwando lina tsiku lotsatira. (Esitere 5:7, 8) Kodi n’chifukwa chiyani anadikirabe mpaka tsiku lotsatira? Musaiwale kuti, malinga ndi zimene mfumu inalamula, anthu onse a mtundu wa Esitere anayenera kuphedwa. Choncho, pozindikira kuopsa kwa nkhaniyi, Esitere anafunika kuonetsetsa kuti pempho lake walinena nthawi yabwino. Motero iye anadikirabe ndipo zimenezi zinachititsa kuti mwamuna wake aone kuti amamulemekeza kwambiri.

Kuleza mtima ndi khalidwe lofunika kwambiri ngakhale kuti ndi anthu ochepa chabe amene ali nalo. Esitere anali ndi nkhawa komanso ankafunitsitsa kulankhulana ndi mfumu, komabe anadikira nthawi yoyenera. Tingaphunzire zambiri pa chitsanzo chakechi, popeza tonsefe nthawi zina timaona zinthu zina zolakwika ndipo timalakalaka zitakonzedwa. Tikafuna kupempha munthu waudindo kuti akonze zinthu zinazake zomwe zalakwika, tiyenera kutengera chitsanzo cha Esitere. Lemba la Miyambo 25:15 limati: “Kuleza mtima kumanyengerera mtsogoleri wa asilikali, ndipo lilime lofatsa likhoza kuthyola fupa.” Tikaleza mtima mpaka nthawi yoyenera ndipo kenako n’kufotokoza maganizo athu modekha, ngati mmene Esitere anachitira, tikhoza kukopa anthu ovuta kwambiri amene tingawayerekezere ndi fupa. Kodi Yehova Mulungu anadalitsa Esitere chifukwa chochita zinthu moleza mtima komanso mwanzeru chonchi?

Kuleza Mtima Kunathandiza Kuti Chilungamo Chichitike

Kuleza mtima kwa Esitere, kunathandiza kuti zinthu zambiri zitheke. Hamani anachoka paphwando loyamba lija “ali wokondwa komanso akusangalala kwambiri mumtima mwake” poona kuti umenewu ndi umboni wakuti mfumu komanso mkazi wake akusangalala naye kwambiri. Koma pamene Hamani ankadutsa pachipata cha mfumu, anaona Moredekai, Myuda yemwe ankakana kumuweramira uja. Sikuti Moredekai ankalephera kuweramira Hamani chifukwa chopanda ulemu, koma chifukwa cha chikumbumtima chake komanso ankadziwa mmene zimenezi zingakhudzire ubwenzi wake ndi Yehova Mulungu. Komabe Hamani “anamukwiyira kwambiri” Moredekai.​—Esitere 5:9.

Hamani anafotokozera mkazi wake komanso anzake zoti Moredekai akumakana kumuweramira. Iwo anamuuza kuti akonze mtengo wotalika kuposa mamita 22 ndipo akapemphe chilolezo kwa mfumu kuti apachikepo Moredekai. Hamani anagwirizana nazo ndipo nthawi yomweyo anakonzetsa mtengowo.​—Esitere 5:12-14.

Usiku wa tsiku limenelo, mfumu inavutika. Baibulo limanena kuti: “Mfumu inasowa tulo.” Zitatero, inauza anthu kuti aiwerengere mokweza buku limene ankalembamo zochitika za mu ufumuwo. Zimene anawerengazo zinaphatikizapo lipoti lokhudza chiwembu chofuna kupha Ahasiweroyo. Mfumu inakumbukira nkhaniyo ndiponso kuti anthu amene anakonza chiwembuwo anagwidwa n’kuphedwa. Koma kodi Moredekai, yemwe anaulula chiwembucho, anamuchitira chiyani? Mfumuyo itafunsa ngati Moredekai anachitiridwa chilichonse, inauzidwa kuti palibe chimene anachitiridwa.​—Esitere 6:1-3.

Mokwiya, mfumuyo inafunsa ngati pali nduna iliyonse pafupi yoti aitume kuchita zimene anaiwalazo. Nduna imene inali pafupi inali Hamani. Zikuoneka kuti Hamani ndi amene anayambirira kufika kunyumba ya mfumuyo chifukwa ankafuna kukapempha chilolezo choti aphe Moredekai. Koma iye asanapemphe zimenezi, mfumuyo inamufunsa zomwe angachitire munthu amene mfumu ikukondwera naye. Hamani anaganiza kuti munthu wake ndi iyeyo. Choncho iye anakonza zoti munthuyo achitiridwe zinthu zapamwamba kwambiri. Iye anauza mfumuyo kuti munthuyo avekedwe zovala zachifumu, akwezedwe pahatchi imene mfumu imakwera ndipo mmodzi wa akalonga olemekezeka a mfumu amuyendetse kuzungulira mzinda wonse wa Susani n’kumanena mawu otamanda munthuyo mofuula. Taganizirani mmene nkhope ya Hamani inaonekera atamva kuti munthu woyenera kupatsidwa ulemuyo anali Moredekai. Ndipotu munthu amene mfumuyo inamulamula kuti azikafuula zotamanda Moredekai anali Hamani yemweyo.​—Esitere 6:4-10.

Mokakamizika, Hamani anachitabe zimene anauzidwazo ndipo atamaliza, anabwerera kunyumba kwake mofulumira komanso atakhumudwa kwambiri. Mkazi wake ndi anzake anamuuza kuti pamenepa zaonekeratu kuti sizimuthera bwino ndipo iye sapambana pa nkhondo yake yolimbana ndi Moredekai.​—Esitere 6:12, 13.

Chifukwa chakuti Esitere anadikiranso tsiku lina asanauze mfumu pempho lake, zimenezi zinachititsa kuti Hamani achite zinthu zomwe zinamubweretsera yekha mavuto. N’kutheka kuti Yehova Mulungu ndi amene anachititsa kuti mfumu isowe tulo. (Miyambo 21:1) N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amatilimbikitsa ‘kuyembekezera moleza mtima.’ (Mika 7:7) Tikamayembekezera kuti Mulungu atithandize pa mavuto athu, tidzaona kuti iye amapeza njira yabwino yothetsera mavuto yoposa imene ifeyo tikanatsatira.

Analankhula Molimba Mtima

Esitere anaona kuti si bwino kuti mfumuyo izingodikirabe kuti aiuza zotani. Choncho, paphwando lotsatira, iye anaona kuti ayenera kufotokoza zonse. Koma kodi akanayambira pati? Mwamwayi, mfumuyo inamufunsanso kuti afotokoze pempho lake. (Esitere 7:2) Esitere anaona kuti tsopano imeneyi ndi “nthawi yolankhula.”

N’kutheka kuti Esitere anapemphera chamumtima kwa Mulungu wake asanauze mfumu mawu awa: “Ngati mungandikomere mtima mfumu, ndipo ngati zingakukomereni, ndikupempha kuti mupulumutse moyo wanga komanso kuti musawononge anthu a mtundu wanga.” (Esitere 7:3) Onani kuti iye anasonyeza kuti ankalemekeza zimene mfumuyo ingalamule malinga ndi zomwe iyoyo yaona kuti n’zoyenera. Zimene Esitere anachitazi zinasonyeza kuti iye anali wosiyana kwambiri ndi Vasiti, mkazi wakale wa mfumuyi, amene anachititsa manyazi mfumuyi mwadala. (Esitere 1:10-12) Komanso, Esitere sananyoze mfumuyi chifukwa chokhulupirira zinthu zabodza zimene Hamani anaiuza. M’malomwake, iye anapempha mfumuyo kuti imuteteze kuti asaphedwe.

Pempho limeneli linadabwitsa kwambiri mfumuyo komanso inaona kuti iyeneradi kuchitapo kanthu. Ndipotu palibe amene angalekerere kuti mkazi wake aphedwe. Esitere anapitiriza kufotokoza kuti: “Ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti tiwonongedwe, tiphedwe ndi kufafanizidwa. Ngati tikanagulitsidwa kukhala akapolo aamuna ndi akapolo akazi ndikanakhala chete. Koma musalole kuti tsoka limeneli lichitike chifukwa liwonongetsa zinthu zambiri za mfumu.” (Esitere 7:4) Onani kuti Esitere anafotokoza zokhudza chiwembucho momveka bwino koma ananenanso kuti zikanakhala kuti iwo anangokhala akapolo chabe, iye sakanadandaula chilichonse. Komano popeza kuti kupha mtundu wonse kukanawonongetsa zinthu zambiri za mfumu, iye anaona kuti si bwino kungokhala chete.

Chitsanzo cha Esitere chikutiphunzitsa njira yabwino yofotokozera maganizo athu mogwira mtima. Ngati mukufuna kufotokoza vuto linalake kwa munthu amene mumam’konda kapena kwa munthu waudindo, kuchita zinthu moleza mtima, mwaulemu, komanso kutchula vutolo mosapita m’mbali, kungakuthandizeni kwambiri.​—Miyambo 16:21, 23.

Ndiyeno Ahasiwero anafunsa kuti: “Ndani wachita zimenezi, ndipo ali kuti munthu amene wadzikuza ndi kuchita zinthu zoterezi?” Yerekezerani kuti mukuona Esitere akuloza n’kuyankha kuti: “Munthu wake ndi uyu, Hamani, mdani ndiponso munthu woipa.” Hamani anangoti kukamwa yasaa ndipo anagwidwa ndi mantha aakulu. N’kutheka kuti nkhope ya mfumu inafiira chifukwa cha mkwiyo itazindikira kuti Hamani, mlangizi wake amene inkamukhulupirira, anali ataipusitsa n’kuichititsa kusainira lamulo limene likanachititsa kuti mkazi wake wokondedwa aphedwe. Mfumuyi inachoka paphwandoli n’kupita kumunda wamaluwa kuti mtima wake ukakhale m’malo.​—Esitere 7:5-7.

Hamani, yemwe pa nthawiyi anali atadziwika kuti anali munthu woipa, anagwada pafupi ndi mapazi a mfumukazi n’kuyamba kuichonderera kwambiri. Ndiyeno pamene mfumu inalowanso m’nyumba muja n’kuona Hamani ali pafupi ndi Esitere, inakwiya kwambiri chifukwa inaona ngati Hamani akufuna kugwiririra Esitereyo m’nyumba mwake momwe. Apa zinaonekeratu kuti Hamani sapulumuka. Hamani anachotsedwa m’nyumbamo atamuphimba nkhope. Kenako nduna ina ya mfumu inauza mfumu za mtengo waukulu uja, umene Hamani ankafuna kupachikapo Moredekai. Ahasiwero atangomva zimenezi, analamula kuti Hamani akapachikidwe pamtengowo.​—Esitere 7:8-10.

Masiku ano m’dzikoli kupanda chilungamo kuli ponseponse. Choncho pakakhala nkhani inayake imene sinayende mwachilungamo, n’zosavuta kuyamba kuganiza kuti chilungamo cha nkhaniyo sichidzadziwika. Kodi inunso munayamba mwaganizapo choncho? Koma monga taonera, Esitere sanataye mtima ndipo anakhalabe ndi chikhulupiriro choti Mulungu amuthandiza. Nthawi yoti alankhule itakwana, iye analankhula molimba mtima komanso analankhula chilungamo chokhachokha. Ankakhulupirira kuti Yehova amuthandiza kuti chilungamo chioneke. Nafenso tizichita chimodzimodzi. Yehova sanasinthe, iye amathabe kuchititsa kuti anthu oipa agwere mumsampha wotchera okha ngati mmene zinachitikira ndi Hamani.​—Salimo 7:11-16.

Anaimira Yehova ndi Anthu Ake

Tsopano mfumu inadziwa kuti Moredekai, yemwe anaipulumutsa kwa anthu amene ankafuna kuipha, analinso bambo a Esitere womulera. Ahasiwero anapatsa Moredekai udindo umene unali wa Hamani, wokhala nduna yaikulu. Komanso anapatsa Esitere nyumba ya Hamani ndi chuma chake chonse ndipo Esitereyo anauza Moredekai kuti aziyang’anira zinthuzo.​—Esitere 8:1, 2.

Esitere akanakhala kuti sankaganizira anthu ena, akanangosiyira nkhaniyi pomwepo podziwa kuti iyeyo ndi Moredekai zawo zinali zitayenda. Koma pa nthawiyi n’kuti lamulo la Hamani lija, lonena kuti Ayuda onse aphedwe, likulengezedwabe m’madera onse a ufumuwo. Hamani anachita Puri kapena kuti maere kuti adziwe tsiku loyenera kudzachita chiwembu chimenechi. Mwina maere amene anachitawo anali okhudzana ndi zamizimu. (Esitere 9:24-26) Ngakhale kuti kunali kudakali miyezi ingapo kuti tsikulo lifike, Esitere ndi Moredekai anafunika kuchitapo kanthu mwamsanga. Koma kodi iwo akanatani kuti Ayuda asaphedwe?

Kachiwirinso, chifukwa choganizira anthu ena, Esitere anaika moyo wake pachiswe n’kukaonekeranso pamaso pa mfumu asanaitanidwe. Pa nthawiyi iye analira ndi kuchonderera mwamuna wake kuti asinthe chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda. Koma mu ulamuliro wa Aperisiya, mfumu ikakhazikitsa lamulo silinkasinthidwa. (Danieli 6:12, 15) Choncho, mfumu inapatsa mphamvu Esitere ndi Moredekai yoti akhazikitse malamulo ena atsopano. Zitatero, panaperekedwa lamulo lopatsa Ayuda ufulu wodziteteza. Anthu okwera pamahatchi anatumizidwa m’zigawo zonse za ufumuwo kuti akalengeze nkhani yabwinoyi kwa Ayuda. Apa tsopano mitima ya Ayuda inakhala m’malo. (Esitere 8:3-16) Ayuda a m’zigawo zonse za ufumuwo ayenera kuti anayamba kukonzekera nkhondo, zimene sakanachita zikanakhala kuti lamulo latsopanoli silinakhazikitsidwe. Komabe, Ayuda sakanapambana pa nkhondoyi popanda thandizo la Yehova. Koma kodi “Yehova wa makamu” anawathandiza?​—1 Samueli 17:45.

Tsiku limene Hamani anakhazikitsa lija litakwana, anthu a Mulungu anali atakonzeka kumenya nkhondo. Akuluakulu ena a boma analinso kumbali ya Ayuda popeza zinali zitamveka kuti Moredekai, yemwe anali Myuda, anali ataikidwa kukhala nduna yaikulu. Yehova anathandiza kwambiri anthu ake kuti apambane. Iye anaonetsetsa kuti adani onse a anthu ake agonjetsedwa kuti asadzachitirenso zoipa anthu akewo. *​—Esitere 9:1-6.

Komabe, Moredekai sakanakhala wotetezeka kuyang’anira nyumba ya Hamani pamene ana 10 a Hamaniyo anali adakali moyo. Choncho iwonso anaphedwa. (Esitere 9:7-10) Pamenepatu ulosi wina wa m’Baibulo unakwaniritsidwa. Mulungu anali atalosera kuti Aamaleki onse adzawonongedwa chifukwa iwo anasonyeza kuti anali adani oopsa a anthu ake. (Deuteronomo 25:17-19) Ana a Hamani ndi amene anali omalizira enieni kuphedwa pa anthu a mtundu woipa umenewu.

Ngakhale kuti Esitere anali wachitsikana, anachita mbali yake pa nkhani yovuta ngati imeneyi. Iye analemba nawo malamulo okhudza nkhondo komanso kupha anthu oipa. Komatu kuchita zimenezi sinali nkhani yamasewera. Koma zimenezi zinayenera kuchitika ndithu chifukwa zinali zogwirizana ndi chifuniro cha Yehova choti anthu ake asawonongedwe. Mesiya wolonjezedwa, yemwe ndi njira yokhayo yopulumutsira mtundu wonse wa anthu, anali kudzabadwa kudzera mu mtundu wa Isiraeli. (Genesis 22:18) Atumiki a Mulungu masiku ano amadziwa kuti Yesu, yemwe ndi Mesiya, atabwera padziko lapansi, analamula otsatira ake onse kuti asamamenyenso nkhondo.​—Mateyu 26:52.

Komabe Akhristu amamenya nkhondo yauzimu. Kuposa ndi kale lonse, panopa Satana akufunitsitsa kuwononga chikhulupiriro chathu mwa Yehova Mulungu. (2 Akorinto 10:3, 4) Chitsanzo cha Esitere ndi chofunika kwambiri kwa ife. Nafenso tiyenera kusonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro mwa kulankhula mwanzeru, kuchita zinthu moleza mtima, kukhala olimba mtima komanso kuyesetsa kuthandiza anthu a Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mu nkhani yoyamba, tinaona kuti Esitere yemwe anali mwana wamasiye, analeredwa ndi Moredekai yemwe anali mwana wa m’bale wa bambo ake. Koma Moredekai anali wamkulu kwambiri poyerekeza ndi Esitere. Kenako Esitere anasankhidwa kuti akhale mkazi wa Ahasiwero mfumu ya ku Perisiya. Hamani, yemwe anali mlangizi wa mfumu, anakonza chiwembu choti aphe Moredekai limodzi ndi Ayuda onse. Moredekai anauza Esitere kuti apite kwa mfumu kukapempha kuti Ayuda asaphedwe.​—Onani nkhani yakuti “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo​—Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu,” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2011.

^ ndime 32 Mfumu inalola kuti Ayuda amenyenso nkhondo tsiku lotsatira n’cholinga chakuti amalize kugonjetsa adani awo. (Esitere 9:12-14) Mpaka pano, chaka chilichonse Ayuda amakumbukirabe kupambana kumeneku pa chikondwerero chotchedwa Purimu. Mwambowu anaupatsa dzina limeneli potengera dzina la maere amene Hamani anachita aja.

[Bokosi patsamba 28]

Mafunso Okhudza Esitere

N’chifukwa chiyani Moredekai analola Kuti Esitere akwatiwe ndi munthu wosalambira Mulungu?

Zimene akatswiri ena a maphunziro amanena zoti Moredekai analola kuti Esitere akwatiwe ndi mfumu n’cholinga chakuti iyeyo apeze udindo, zilibe umboni. Iye anali Myuda wokhulupirika choncho sakanalola ukwati umenewu n’cholinga chongofuna udindo. (Deuteronomo 7:3) Nkhani zina zonena za chikhalidwe cha Ayuda zimasonyeza kuti Moredekai anayesetsa kulepheretsa kuti zimenezi zisachitike. N’kutheka kuti zinali zovuta kwambiri kwa Moredekai ndi Esitere kutsutsa zimenezi chifukwa chakuti iwo anali alendo m’dzikolo komanso wolamulira wadzikolo anali wosamva za ena, yemwenso ankapatsidwa ulemu waukulu ngati mulungu. Koma patapita nthawi, zinadziwika kuti Yehova analola kuti Esitere akwatiwe ndi mfumu n’cholinga choti agwiritse ntchito Esitereyo poteteza anthu ake.​—Esitere 4:14.

N’chifukwa chiyani m’buku la Esitere mulibe dzina lenileni la Mulungu lakuti Yehova?

Zikuoneka kuti buku la Esitere linalembedwa ndi Moredekai. N’kutheka kuti lisanatengedwe kupitanso ku Yerusalemu, bukuli linkasungidwa limodzi ndi mabuku ena a ku Perisiya onena za zochitika za kumeneko. Akanati agwiritse ntchito dzina la Yehova m’bukuli, zikanachititsa kuti anthu omwe ankalambira milungu ya ku Perisiya aliwononge. Kaya sanagwiritse ntchito dzina la Mulungu pa chifukwa chimenechi kapena ayi, zikuoneka kuti Yehova anathandiza kuti zinthu zikhale mmene zinakhaliramu. Chochititsa chidwi n’chakuti, ngakhale kuti dzina la Mulungu silinalembedwe mochita kuonekeratu m’bukuli, zikuoneka kuti m’chinenero choyambirira chachiheberi, analemba mawu mwanjira yoti chilembo choyamba kapena chomaliza cha mawu ena otsatizana chikhale chimodzi mwa zilembo zimene zimaimira dzina la Mulungu.

Kodi n’zoona kuti buku la Esitere silimafotokoza mbiri yakale molondola?

Anthu ena amanena kuti bukuli silimafotokoza mbiri yakale molondola. Komabe, akatswiri ena anapeza kuti munthu amene analemba buku la Esitere ankadziwa zinthu zambiri zokhudza ufumu wa Perisiya. Ankadziwanso mmene zinthu za kumeneko zinkamangidwira komanso chikhalidwe cha m’dzikolo. N’zoona kuti mabuku akale samatchula chilichonse chokhudza Mfumukazi Esitere, koma palinso anthu ena a m’banja lachifumu amene satchulidwa m’mabuku akale. Kuwonjezera pamenepa, mabuku ena a mbiri yakale amasonyeza kuti ku Susani kunali nduna ina yotchedwa Mardukâ, yomwe inkagwira ntchito kunyumba ya mfumu pa nthawi imene zinthu zomwe zinalembedwa m’buku la Esitere zinkachitika. Dzina lakuti Mardukâ ndi lachiperesiya ndipo ndi lofanana ndi dzina lakuti Moredekai.

[Bokosi patsamba 29]

Ulosi Unakwaniritsidwa

Zimene Esitere ndi Moredekai anachita pomenyera nkhondo anthu a Mulungu zinakwaniritsa ulosi wina wa m’Baibulo. Zaka zoposa 1,200 izi zisanachitike, Yehova anauzira munthu wokhulupirika Yakobo kuti alosere zinthu zokhudza mmodzi mwa ana ake. Iye anati: “Benjamini adzapitiriza kukhadzula ngati mmbulu. M’mawa adzadya nyama imene wagwira, ndipo madzulo adzagawa zimene wafunkha.” (Genesis 49:27) “M’mawa,” kapena kuti kumayambiriro kwa mafumu achiisiraeli, mbadwa zina za Benjamini zimene zinkamenyera nkhondo anthu a Mulungu zinaphatikizapo Mfumu Sauli komanso asilikali ena amphamvu. “Madzulo,” kapena kuti kumapeto kwa mafumuwa, Esitere ndi Moredekai, omwe anali a fuko la Benjamini, anapambananso pa nkhondo yolimbana ndi adani a Yehova. Tinganenenso kuti iwo anagawa zimene anafunkha chifukwa chuma chonse cha Hamani chinakhala chawo.

[Chithunzi patsamba 25]

Esitere anayamikira kwambiri mfumu itamuchitira chifundo

[Chithunzi pamasamba 26, 27]

Esitere analimba mtima n’kutchula zinthu zoipa zimene Hamani anakonza

[Chithunzi pamasamba 28, 29]

Esitere ndi Moredekai anatumiza lamulo latsopano kwa Ayuda onse a mu Ufumu wa Perisiya