Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ansembe Achifumu Amene Adzapindulitse Anthu Onse

Ansembe Achifumu Amene Adzapindulitse Anthu Onse

“Inu ndinu ‘fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera.’”​—1 PET. 2:9.

1. N’chifukwa chiyani “chakudya chamadzulo cha Ambuye” chimatchedwanso kuti Chikumbutso, ndipo kodi cholinga chake n’chiyani?

M’CHAKA cha 33 C.E., madzulo a pa Nisani 14, Yesu Khristu ndi atumwi ake 12 anachita mwambo wachiyuda wa Pasika komaliza. Yesu atachotsa Yudasi Isikariyoti, yemwe anadzamupereka, anayambitsa mwambo umene anautcha “chakudya chamadzulo cha Ambuye.” (1 Akor. 11:20) Mwambowu umatchedwanso Chikumbutso cha imfa ya Khristu chifukwa chakuti Yesu ananena kawiri kuti, “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (1 Akor. 11:24, 25) Mboni za Yehova padziko lonse zimachita mwambo umenewu chaka chilichonse pomvera lamulo limeneli. Malinga ndi kalendala ya Baibulo, m’chaka cha 2012, Nisani 14 lidzakhala Lachinayi pa April 5 dzuwa litalowa.

2. Kodi Yesu anati chiyani zokhudza mkate ndi vinyo zimene anagwiritsa ntchito pa nthawi ya chakudya chamadzulo?

2 Luka, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anafotokoza m’mavesi awiri zimene Yesu anachita ndiponso kulankhula pa mwambowu. Iye anati: “Anatenga mkate. Atayamika anaunyemanyema n’kuwapatsa, ndipo anati: ‘Mkate uwu ukuimira thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.’ Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu atadya chakudya chamadzulocho. Iye anati: ‘Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa chifukwa cha inu.’” (Luka 22:19, 20) Kodi atumwiwo akanadziwa bwanji tanthauzo la mawu amenewa?

3. Kodi atumwi anadziwa bwanji tanthauzo la mawu a Yesu onena za mkate ndi vinyo?

3 Popeza kuti iwo anali Ayuda, ankadziwa bwino kwambiri za nsembe za nyama zimene ansembe ankapereka kukachisi wa Mulungu ku Yerusalemu. Nsembe zina zinkaperekedwa kuti ayanjidwe ndi Yehova ndipo zambiri mwa nsembezi zinkaperekedwa kuti machimo awo akhululukidwe. (Lev. 1:4; 22:17-29) Choncho atumwiwo anamvetsa bwino pamene Yesu anati adzapereka thupi ndi magazi ake ‘chifukwa cha iwo.’ Iye anali kutanthauza kuti adzapereka moyo wake wangwiro monga nsembe. Imeneyi inali nsembe yamtengo wapatali kwambiri kuposa nsembe za nyama.

4. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga”?

4 Nanga bwanji za mawu a Yesu akuti: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga”? Atumwiwa ankadziwa za ulosi wonena za pangano latsopano wopezeka pa Yeremiya 31:31-33. (Werengani.) Mawu a Yesuwa anasonyeza kuti akukhazikitsa pangano latsopano limene lilowe m’malo pangano la Chilamulo limene Yehova anakhazikitsa ndi mtundu wa Isiraeli kudzera mwa Mose. Kodi pali mgwirizano pakati pa mapangano awiriwa?

5. Kodi pangano la Chilamulo linapatsa Aisiraeli chiyembekezo chotani?

5 Zolinga za mapangano awiriwa zinali zogwirizana. Pamene ankakhazikitsa pangano la Chilamulo, Yehova anauza mtunduwu kuti: “Ngati mudzalabadiradi mawu anga ndi kusunga pangano langa, pamenepo mudzakhaladi chuma changa chapadera pakati pa anthu ena onse, chifukwa dziko lonse lapansi ndi langa. Inuyo mudzakhala ufumu wanga wa ansembe ndi mtundu wanga woyera.” (Eks. 19:5, 6) Kodi mawu amenewa anatanthauza chiyani kwa Aisiraeli?

LONJEZO LAKUTI PADZAKHALA ANSEMBE ACHIFUMU

6. Kodi pangano la Chilamulo linathandiza kuti lonjezo liti lidzakwaniritsidwe?

6 Aisiraeli ankadziwa tanthauzo la mawu oti “pangano” chifukwa chakuti Yehova anali atachita mapangano ndi makolo awo Nowa ndi Abulahamu. (Gen. 6:18; 9:8-17; 15:18; 17:1-9) Monga mbali ya pangano lake ndi Abulahamu, Yehova anamulonjeza kuti: “Kudzera mwa mbewu yako, mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso.” (Gen. 22:18) Yehova anachita pangano la Chilamulo pofuna kukwaniritsa lonjezo limeneli. Kudzera m’pangano limeneli, Aisiraeli akanakhala ‘chuma chapadera cha Yehova pakati pa anthu ena onse.’ Kodi cholinga chake chinali chotani? Kuti akhale ‘ufumu wake wa ansembe.’

7. Kodi mawu akuti ‘ufumu wa ansembe’ akutanthauza chiyani?

7 Aisiraeli ankadziwa za mafumu ndi ansembe. Koma ndi Melekizedeki yekha amene anali mfumu komanso wansembe pa nthawi imodzi movomerezedwa ndi Yehova. (Gen. 14:18) Tsopano Yehova anapereka mwayi kwa Aisiraeli wokhala ‘ufumu wa ansembe.’ Monga mmene Malemba anasonyezera pambuyo pake, iwo anali ndi mwayi woti ansembe achifumu onse asankhidwe kuchokera mu mtundu wawo. Ansembe achifumu ndi amene adzakhala mafumu komanso ansembe.​—1 Pet. 2:9.

8. Kodi ansembe osankhidwa ndi Mulungu ankagwira ntchito yotani?

8 Mfumu imalamulira. Koma kodi wansembe amagwira ntchito yotani? Lemba la Aheberi 5:1 limafotokoza kuti: “Mkulu wa ansembe aliyense wotengedwa mwa anthu amaikidwa kuti achite utumiki wa Mulungu m’malo mwa anthu, kuti azipereka mphatso ndi nsembe zophimba machimo.” Choncho wansembe wosankhidwa ndi Yehova ankaimira anthu ochimwa powaperekera nsembe zosiyanasiyana komanso kuchonderera Mulungu kuti awakhululukire machimo. M’njira ina, wansembe ankaimira Yehova pophunzitsa anthu chilamulo cha Mulungu. (Lev. 10:8-11; Mal. 2:7) Choncho wansembe wosankhidwa ndi Mulungu ankagwira ntchito yogwirizanitsanso anthu ndi Mulungu.

9. (a) Kodi chinafunika n’chiyani kuti Aisiraeli akhale ndi mwayi wotulutsa ‘ufumu wa ansembe’? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anakonza zoti mu Isiraeli mukhale ansembe? (c) N’chiyani chinalepheretsa Aisiraeli kutulutsa ‘ufumu wa ansembe’ pa nthawi imene anali m’pangano la Chilamulo?

9 Pangano la chilamulo linapatsa Aisiraeli mwayi wotulutsa ansembe achifumu amene akanathandiza “anthu ena onse.” Koma zimenezi zikanatheka pokhapokha ngati akanalabadira mawu a Mulungu ndi kusunga pangano lake. Kodi zikanatheka kuti Aisiraeli alabadiredi mawu a Yehova? Inde akanayesetsa kutero. Kodi akanatha kuchita zimenezi mosaphonyetsa kalikonse? Ayi. (Aroma 3:19, 20) Chifukwa cha zimenezi, Yehova anakonza zoti pakhale ansembe mu Isiraeli. Iwo sankakhala mafumu koma ankapereka nsembe zanyama chifukwa cha machimo a anthu. (Lev. 4:1–6:7) Izi zikuphatikizapo machimo amene ansembewo ankachita. (Aheb. 5:1-3; 8:3) Yehova ankalandira nsembe zoterezi koma sikuti zinkachotseratu machimo a operekawo. Ansembe amene anaikidwa motsatira pangano la Chilamulo sakanatha kugwirizanitsa bwinobwino Aisiraeli okhulupirika ndi Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “N’kosatheka kuti magazi a ng’ombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.” (Aheb. 10:1-4) Chifukwa cholephera kutsatira Chilamulo, Aisiraeli anatembereredwa. (Agal. 3:10) Zinali zosatheka kuti atumikire anthu onse monga ansembe achifumu.

10. Kodi pangano la Chilamulo linali ndi cholinga chotani?

10 Kodi lonjezo la Yehova loti padzakhala ‘ufumu wa ansembe’ linangopita pachabe? Ayi. Ngati akanayesetsabe kumvera, iwo akanakhala ndi mwayi umenewu koma osati potsatira Chilamulo. N’chifukwa chiyani tikutero? (Werengani Agalatiya 3:19-25.) Chilamulo chinkathandiza anthu amene ankachitsatira mokhulupirika kuti asayambe kulambira konyenga. Chinkathandizanso Ayuda kuzindikira kuti ndi ochimwa ndiponso kuti ankafunikira nsembe yoposa imene mkulu wa ansembe ankapereka. Chilamulo chinali mtsogoleri wowafikitsa kwa Khristu, kapena kuti Mesiya, ndipo mayina awiri onsewa amatanthauza “Wodzozedwa.” Ndiyeno pamene Mesiya anafika, anayambitsa pangano latsopano limene Yeremiya ananeneratu. Onse amene anakhulupirira ndi kutsatira Khristu anakhala mbali ya pangano limeneli. Zimenezi zikutanthauza kuti anadzakhaladi ‘ufumu wa ansembe.’ Tiyeni tione mmene zinachitikira.

PANGANO LATSOPANO LINACHITITSA KUTI PAKHALE ANSEMBE ACHIFUMU

11. Kodi Yesu anakhala bwanji maziko a ansembe achifumu?

11 M’chaka cha 29 C.E., Yesu wa ku Nazareti anaonekera monga Mesiya. Ali ndi zaka 30 anabatizidwa. Apa anasonyeza kuti anali wofunitsitsa kuchita chifuniro chapadera cha Yehova. Yehova anamutchula kuti “Mwana wanga wokondedwa” ndipo anamudzoza ndi mzimu woyera osati mafuta. (Mat. 3:13-17; Mac. 10:38) Pa nthawiyi, Yesu anadzozedwa kuti akhale Mkulu wa Ansembe kwa anthu onse omukhulupirira ndiponso Mfumu yawo yam’tsogolo. (Aheb. 1:8, 9; 5:5, 6) Iye anakhala maziko a ansembe achifumu enieni.

12. Kodi nsembe ya Yesu inachititsa kuti zinthu ziti zitheke?

12 Monga Mkulu wa Ansembe, ndi nsembe yotani imene Yesu anapereka yomwe inaphimbiratu machimo amene okhulupirira anatengera kwa makolo athu oyambirira? Monga mmene anasonyezera pokhazikitsa mwambo wokumbukira imfa yake, iye anapereka moyo wake wangwiro monga nsembe. (Werengani Aheberi 9:11, 12.) Kuchokera pa nthawi imene anabatizidwa mu 29 C.E., Yesu monga Mkulu wa Ansembe anakumana ndi mayesero osiyanasiyana ndiponso kuphunzira zinthu zambiri mpaka pamene anaphedwa. (Aheb. 4:15; 5:7-10) Ataukitsidwa n’kubwerera kumwamba anakapereka nsembe yake kwa Yehova. (Aheb. 9:24) Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu amatha kuchonderera Yehova kuti akhululukire onse amene amasonyeza chikhulupiriro mu nsembe yake. Iye amathandizanso anthuwo kutumikira Mulungu ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Aheb. 7:25) Nsembe yake inachititsa kuti pangano latsopano likhazikitsidwe mwalamulo.​—Aheb. 8:6; 9:15.

13. Kodi anthu amene ali m’pangano latsopano ali ndi chiyembekezo chotani?

13 Anthu amene ali m’pangano latsopanoli nawonso amadzozedwa ndi mzimu woyera. (2 Akor. 1:21) Poyamba, m’panganoli munali Ayuda okhulupirika koma kenako anthu a mitundu ina analowanso m’panganoli. (Aef. 3:5, 6) Kodi amene ali m’pangano latsopano ali ndi chiyembekezo chotani? Machimo awo amakhululukidwa kotheratu. Yehova analonjeza kuti: “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yer. 31:34) Chifukwa chakuti Yehova amafafaniza machimo awo, iwo amayenerera kukhala ‘ufumu wa ansembe.’ Polankhula za Akhristu odzozedwa amenewa, Petulo analemba kuti: “Inu ndinu ‘fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera, kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri’ a amene anakuitanani kuchoka mu mdima kulowa m’kuwala kwake kodabwitsa.” (1 Pet. 2:9) Pamenepa Petulo anagwira mawu a Yehova amene anauza Aisiraeli powapatsa Chilamulo. Ndipo iye anawagwiritsa ntchito pofotokoza za Akhristu amene ali m’pangano latsopano.​—Eks. 19:5, 6.

ANSEMBE ACHIFUMU AMENE AKUTHANDIZA ANTHU ONSE

14. Kodi ansembe achifumu amatumikira kuti?

14 Kodi anthu a m’pangano latsopanoli amatumikira kuti? Iwo monga gulu amatumikira padziko lapansi monga ansembe kuimira Yehova polengeza kwa anthu makhalidwe ake abwino kwambiri komanso kupereka chakudya chauzimu. (Mat. 24:45; 1 Pet. 2:4, 5) Iwo akafa n’kuukitsidwa amakhala oyenera kukatumikira ndi Khristu kumwamba monga mafumu ndiponso ansembe. (Luka 22:29; 1 Pet. 1:3-5; Chiv. 1:6) Potsimikizira zimenezi, mtumwi Yohane anaona masomphenya a zolengedwa zauzimu zili pafupi ndi mpando wachifumu wa Yehova kumwamba. Iwo ankaimbira “Mwanawankhosa” “nyimbo yatsopano” n’kumanena kuti: “Ndi magazi anu, munagula anthu kuti atumikire Mulungu. Anthu ochokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse. Ndipo munawasandutsa mafumu ndi ansembe a Mulungu wathu, moti adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.” (Chiv. 5:8-10) Ponena za olamulira amenewa, m’masomphenya ake ena Yohane ananena kuti: “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.” (Chiv. 20:6) Iwo limodzi ndi Khristu ndiwo ansembe achifumu amene adzapindulitse anthu onse.

15, 16. Kodi ansembe achifumu adzabweretsa madalitso otani kwa anthu?

15 Kodi a 144,000 adzabweretsa madalitso otani padziko lapansi? Lemba la Chivumbulutso chaputala 21 limawafotokoza monga mzinda wakumwamba, Yerusalemu Watsopano amene amatchedwanso “mkazi wa Mwanawankhosa.” (Chiv. 21:9) Mavesi 2 mpaka 4 amanena kuti: “Ndinaonanso mzinda woyera, Yerusalemu Watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wokongoletsedwera mwamuna wake. Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: ‘Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.’” Amenewatu ndi madalitso osaneneka. Imfa ikadzangochotsedwa ndiye kuti misozi, kulira ndi zopweteka zidzathera pomwepo. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu okhulupirika adzakhala angwiro ndiponso adzagwirizananso ndi Mulungu.

16 Popitiriza kufotokoza madalitso amene ansembe achifumu adzabweretse, lemba la Chivumbulutso 22:1, 2 limati: “Anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo, ukuyenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa. Mtsinjewo unali kudutsa pakati pa msewu waukulu wa [Yerusalemu Watsopano]. Kumbali iyi ya mtsinjewo ndi kumbali inayo, kunali mitengo ya moyo yobala zipatso zokolola maulendo 12, ndipo inali kubala zipatso mwezi uliwonse. Masamba a mitengoyo anali ochiritsira mitundu ya anthu.” Chifukwa cha mtsinje ndi mitengo ya moyo yophiphiritsira imeneyi, mitundu yonse ya anthu idzachiritsidwa kotheratu ku uchimo umene tinatengera kwa Adamu. Ndithudi zinthu ‘zakale zidzapita.’

ANSEMBE ACHIFUMU AMALIZA NTCHITO YAWO

17. Kodi ansembe achifumu adzakhala atakwanitsa kuchita chiyani pomadzatha zaka 1,000?

17 Pofika kumapeto kwa zaka 1,000 za utumiki wawo, ansembe achifumu adzakhala atathandiza anthu onse kukhala angwiro. Ndiyeno Khristu monga Mkulu wa Ansembe komanso Mfumu adzapereka anthu angwirowa kwa Yehova. (Werengani 1 Akorinto 15:22-26.) Pamenepo ansembe achifumu adzakhala atamaliza ntchito yawo.

18. Pambuyo poti ansembe achifumu amaliza ntchito yawo, kodi Yehova adzawapatsa ntchito yotani?

18 Ndiyeno pambuyo pa zimenezi, kodi Yehova adzawapatsa ntchito yotani anzake a Khristu amenewa? Lemba la Chivumbulutso 22:5 limati iwo “adzalamulira monga mafumu kwamuyaya.” Kodi azidzalamulira ndani? Baibulo silinena chilichonse za nkhani imeneyi. Koma adzakhalabe amtengo wapatali kwa Yehova. Popeza adzakhala ndi moyo wosafa komanso adzakhala ndi luso lotha kuthandiza anthu opanda ungwiro, Yehova adzawagwiritsabe ntchito monga mafumu kuti akwaniritse zolinga zake kwamuyaya.

19. Kodi anthu amene adzapezeke pa Chikumbutso adzakumbutsidwa za chiyani?

19 Tidzakumbutsidwa ziphunzitso za m’Baibulo zimenezi pochita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Lachinayi pa April 5, 2012. Akhristu odzozedwa ochepa omwe adakali padziko lapansi ndi amene adzadye zizindikiro za mkate wopanda chofufumitsa ndi vinyo wofiira kusonyeza kuti ali m’pangano latsopano. Zizindikiro zoimira nsembe ya Khristu zimawakumbutsa mwayi wapadera komanso udindo umene ali nawo pokwaniritsa cholinga cha Mulungu chamuyaya. Tiyeni tonse tidzapezeke pa mwambo umenewu posonyeza kuyamikira makonzedwe a Yehova Mulungu potipatsa ansembe achifumu amene adzapindulitse anthu onse.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 29]

Ansembe achifumu adzabweretsa madalitso osatha kwa anthu