Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Kodi Mmene Ndililimu Ndingakwanitse Kulalikira?’

‘Kodi Mmene Ndililimu Ndingakwanitse Kulalikira?’

‘Kodi Mmene Ndililimu Ndingakwanitse Kulalikira?’

Padziko lonse tili ndi zitsanzo za abale ndi alongo okhulupirika amene amalalikira ngakhale kuti ali ndi vuto la matenda. Dalia, yemwe amakhala mumzinda wa Vilnius womwe ndi likulu la Lithuania, ndi chitsanzo chabwino pa nkhaniyi.

Dalia ndi mlongo yemwe ali ndi zaka za m’ma 30. Iye anabadwa ndi matenda enaake owononga ubongo. Matendawa apha ziwalo zake ndiponso achititsa kuti azilephera kulankhula bwino. Chifukwa cha zimenezi, anthu a m’banja lake okha ndi amene amatha kulankhula naye bwinobwino. Iye amakhala ndi mayi ake omwe dzina lawo ndi a Galina amene amamusamalira. Ngakhale kuti Dalia amavutika kwambiri ndi matendawa ndiponso amakhala ndi nkhawa, komabe iye amaona zinthu moyenera. N’chifukwa chiyani tikutero?

Mayi ake anafotokoza kuti: “M’chaka cha 1999, wachibale wathu dzina lake Apolonija anabwera kudzacheza nafe. Iye anali wa Mboni za Yehova ndipo ankalidziwa bwino Baibulo. Choncho Dalia anayamba kum’funsa mafunso. Posapita nthawi Dalia anayamba kuphunzira Baibulo. Nthawi zina ndinkakhala nawo pa phunziroli kuti ndizimveketsa bwino zimene Dalia akulankhula. Ndinaona kuti zimene anali kuphunzira zinkamuthandiza kwambiri. Ndiye nanenso ndinapempha kuti ndiziphunzira Baibulo.”

Dalia atayamba kumvetsetsa choonadi cha m’Baibulo, panali funso limodzi limene linali kumuvutitsa maganizo kwambiri. Tsiku lina iye anafunsa Apolonija kuti: “Kodi munthu wolumala ngati ine ndingakwanitse kulalikira?” (Mat. 28:19, 20) Apolonija anamuyankha momukhazika mtima pansi kuti: “Usadandaule, Yehova adzakuthandiza.” Ndipo Yehova anamuthandizadi.

Ndiye kodi Dalia amalalikira bwanji? Iye amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, alongo amamuthandiza kulemba makalata okhala ndi uthenga wa m’Baibulo. Choyamba iye amafotokozera alongowo zimene akufuna kuti zilembedwe m’kalatayo. Kenako alongowo amalemba zimene wafotokozazo. Dalia amalalikiranso potumiza mauthenga pa foni yake yam’manja. Kunja kukacha bwino, abale ndi alongo amamutenga kupita naye kukalalikira kumalo amene anthu amakonda kuchezerako ndiponso mumsewu.

Dalia ndi amayi ake akupitirizabe kukula mwauzimu. Iwo anadzipereka kwa Yehova ndipo anabatizidwa mu November 2004. Mu September 2008, ku Vilnius kunapangidwa kagulu ka anthu olankhula Chipolishi. Popeza kuti kaguluka kanali ndi ofalitsa Ufumu ochepa, Dalia ndi mayi ake anapita kukathandiza nawo kulalikira. Dalia anafotokoza kuti: “M’miyezi ina ndimadandaula ndikakhala kuti sindinapite kokalalikira. Koma ndikapemphera kwa Yehova, ndimangoona munthu wina akundiuza kuti adzanditenga kuti tipitire limodzi mu utumiki.” Kodi mlongo wathu wokondedwayu, amamva bwanji chifukwa cha matenda akewa? Iye anafotokoza kuti: “Matendawa apha ziwalo zanga koma sanaphe maganizo anga. Ndine wosangalala kwambiri kuti ndimatha kuuza anthu ena za Yehova.”