Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi n’zoona kuti m’nthawi ya Yesu anthu ankaimba zitoliro pa maliro?

Baibulo limasonyeza kuti anthu ankaimba zitoliro pa zikondwerero zosiyanasiyana. (1 Mafumu 1:40; Yesaya 5:12; 30:29) Limanenanso kuti zitoliro zinkaimbidwa pa mwambo wa maliro. Pa zipangizo zonse zoimbira, zitoliro zokha n’zimene zimatchulidwa kuti zinkaimbidwa pa maliro. Uthenga Wabwino wa Mateyu umanena kuti wolamulira wina wachiyuda anapempha Yesu kuti akachiritse mwana wake wamkazi amene anali atatsala pang’ono kufa. Koma pamene Yesu ankafika kunyumba kwa wolamulirayo, “anaona oliza zitoliro komanso khamu la anthu likubuma” popeza mwanayo anali atafa kale.​—Mateyu 9:18, 23.

Kodi zomwe Mateyu analemba zokhudza zimene zinkachitika pa maliro n’zolondola? Katswiri wina womasulira Baibulo, dzina lake William Barclay, ananena kuti: “Kale m’mayiko ambiri monga Roma, Girisi, Foinike, Asuri komanso Palesitina, anthu ankaimba zitoliro pakachitika maliro kapena pakachitika tsoka linalake.” Buku lina lotchedwa Talmud limanena kuti, m’nthawi ya atumwi Myuda aliyense, ngakhale atakhala wosauka, ankayesetsa kuti pa maliro a mkazi wake pakhale anthu aganyu awiri oti aziimba zitoliro komanso pakhale mzimayi woti azilira. Wolemba mbiri wina wa m’nthawi ya atumwi, dzina lake Flavius Josephus, analemba kuti mu 67 C.E., uthenga utafika ku Yerusalemu woti Aroma agonjetsa mzinda wa Jotapata ku Galileya komanso kuti anthu ambiri a mumzindawu aphedwa, anamfedwa “ambiri anaitana anthu oti aziimba zitoliro pa maliro a abale awo.”

Kodi anthu amene anapachikidwa limodzi ndi Yesu anapalamula mlandu wotani?

Baibulo limanena kuti anthu amenewa anali “achifwamba.” (Mateyu 27:38; Maliko 15:27) Mabuku ena otanthauzira mawu a m’Baibulo amafotokoza kuti Baibulo likamanena za munthu wopalamula, limagwiritsa ntchito mawu ogwirizana ndi mlandu umene munthuyo anapalamula. Mawu achigiriki akuti kleptes amanena za munthu woba mwakabisira moti anthu sadziwa kuti ndi wakuba. Mawu amenewa amagwirizana ndi zimene Yudasi Isikariyoti ankachita. Iye ankaba ndalama za ophunzira a Yesu zimene zinkaponyedwa m’bokosi. (Yohane 12:6) Koma mawu akuti lestes nthawi zambiri amanena za munthu amene amaba mwauchifwamba ndipo mawuwa anganenenso za munthu woukira boma kapena wopha munthu. Anthu amene anapachikidwa limodzi ndi Yesu anali a m’gulu limeneli. Ndipotu Baibulo limanena kuti mmodzi mwa anthu amenewa ananena kuti: “Tikulandiriratu zonse zotiyenera malinga ndi zimene tinachita.” (Luka 23:41) Zimenezi zikusonyeza kuti mlandu wa anthu amenewa sunali kuba kokha.

Mawu amene anawagwiritsa ntchito ponena za mlandu wa Baraba analinso ofanana ndi mawu amene anawagwiritsa ntchito ponena za mlandu wa anthu amenewa. (Yohane 18:40) Umboni wakuti Baraba sanali ndi mlandu wakuba wokha ndi zimene lemba la Luka 23:19 limanena. Lembali limanena kuti iye “anaponyedwa m’ndende chifukwa cha kuukira boma kumene kunachitika mumzindawo, komanso chifukwa chopha munthu.”

Choncho ngakhale kuti anthu amene anapachikidwa limodzi ndi Yesu anali akuba, n’kuthekanso kuti iwo anali oukira boma kapena opha anthu. Kaya anthu amenewa anali oukira boma kapena opha anthu, Baibulo limanena kuti bwanamkubwa wachiroma dzina lake Pontiyo Pilato anawaweruza kuti ndi oyenera kuphedwa mwa kupachikidwa.