Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Natani Anali Wokhulupirika Ndipo Ankalimbikitsa Kulambira Koona

Natani Anali Wokhulupirika Ndipo Ankalimbikitsa Kulambira Koona

Natani Anali Wokhulupirika Ndipo Ankalimbikitsa Kulambira Koona

Si zophweka kudzudzula munthu wolemekezeka akalakwitsa zinthu, ndi kumuthandiza kuti asinthe. Kodi inuyo mungapereke uphungu kwa munthu amene anapha munthu wina chifukwa chofuna kuti cholakwa chake chisadziwike?

Mfumu Davide ya ku Isiraeli inachita chigololo ndi Bateseba ndipo iye anakhala ndi pakati. Pofuna kuti tchimo lake lisadziwike, Davide anakonza zoti mwamuna wa Bateseba aphedwe ndipo kenako anadzamukwatira. Kwa miyezi yambiri, Davide anabisa tchimo lake ndipo mosakayikira anangopitiriza kugwira ntchito yake monga mfumu. Koma Yehova sanalole kuti tchimoli lisadziwike. Iye anatumiza mneneri wake Natani kuti akathandize Davide.

Kuchita zimenezi sikunali kophweka. Mukanakhala inuyo kodi mukanatani? Chifukwa choti anali wokhulupirika kwa Yehova komanso ankatsatira kwambiri mfundo zake, Natani anakakambirana ndi Davide za machimo ake. Kodi akanachita bwanji zimenezi kuti Davideyo afike pokhutira n’kuvomereza kuti ayenera kulapa?

MPHUNZITSI WALUSO

Panopa mungachite bwino kupatula nthawi n’kuwerenga 2 Samueli 12:1-25. Tayerekezani kuti ndinu Natani ndipo mwakumana ndi Davide n’kuyamba kumuuza nkhani yakuti: “Panali amuna awiri amene anali kukhala mumzinda umodzi. Wina anali wolemera ndipo wina anali wosauka. Munthu wolemera uja anali ndi nkhosa ndi ng’ombe zambiri. Koma munthu wosauka uja anali ndi kamwana ka nkhosa kamodzi kokha kakakazi kamene anagula. Iye anali kusunga kamwana ka nkhosako ndipo kanali kukula pamodzi ndi ana ake. Munthuyo anali kudya ndi kumwa nako pamodzi ndipo kanali kugona pachifuwa chake. Kwa iye kanali ngati mwana wake wamkazi. Patapita nthawi, kwa munthu wolemera uja kunabwera mlendo. Koma munthu wolemerayo sanatenge zina mwa nkhosa zake ndi ng’ombe zake kuti akonzere mlendo amene anabwera kwawoyo. M’malomwake, anatenga kamwana ka nkhosa kakakazi ka munthu wosauka uja ndi kukonzera munthu amene anabwera kwawoyo kuti adye.”​—2 Sam. 12:1-4.

Davide yemwe anakhalapo m’busa, anakhulupirira kuti nkhaniyi yachitikadi. Katswiri wina anati: “N’kutheka kuti Natani ankabwera kwa Davide kudzamupempha kuti athandize anthu ovutika omwe analibe owathandiza ndipo panopa Davide ankaganiza kuti Natani akuchita zimenezo.” Kaya zimenezi ndi zoona, Natani ayenera kuti anafunika kukhala wokhulupirika kwa Mulungu komanso wolimba mtima kuti akalankhule ndi mfumu. Zimene Natani analankhulazi zinakwiyitsa kwambiri Davide moti anati: “Ndithu, pali Yehova Mulungu wamoyo, munthu wochita zimenezi ayenera kufa.” Ndiyeno atatero Natani ananena mosapita m’mbali kuti: “Munthu ameneyo ndiwe!”​—2 Sam. 12:5-7.

N’chifukwa chiyani Natani anakambirana ndi Davide m’njira imeneyi? Zimakhala zovuta kwa munthu amene ali pa chibwenzi ndi wina ndipo akumukonda kwambiri kuti aziona zinthu bwinobwino. Tonsefe timafunanso kudziikira kumbuyo ngati tachita zinthu zinazake zokayikitsa. Koma fanizo la Natani linachititsa kuti Davide adzidzudzule yekha mosazindikira. Mfumuyi inaona kuti munthu amene Natani anamufotokoza uja anachita zoipa kwambiri. Davide atakwiya ndi zimenezi, Natani anamuululira kuti munthuyo ndi Davideyo. Tsopano Davide anatha kuona kuopsa kwa tchimo lake. Izi zinachititsa kuti akhale ndi maganizo abwino komanso kuti alandire uphungu. Iye anavomereza kuti zimene anachita ndi Bateseba ‘zinanyozetsa’ Yehova ndipo analandira uphungu umene anapatsidwa.​—2 Sam. 12:9-14; onaninso mawu apamwamba a Salimo 51.

Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Tikamaphunzira Baibulo ndi anthu, cholinga chathu chizikhala kuwathandiza kuti azindikire okha mfundo yoyenera. Natani ankalemekeza kwambiri Davide choncho anakambirana naye mosamala kwambiri. Natani ankadziwa kuti mumtima mwake Davide ankakonda chilungamo. Choncho mneneriyu anagwiritsa ntchito fanizo lomwe lingafike pamtima munthu wokonda chilungamo. Nafenso tikhoza kuthandiza anthu ofuna choonadi kumvetsa maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingawathandize kumvetsa mmene Yehova amaonera zinthu pogwiritsa ntchito mfundo zimene iwowo amayesetsa kuyendera. Komanso tiyenera kuchita zimenezi popanda kulankhula ngati ndife abwino kapena olungama kuposa iwowo. M’malo mofotokoza za m’maganizo mwathu, tiyenera kugwiritsa ntchito Baibulo powathandiza kudziwa chabwino ndi choipa.

Koposa zonse, kukhulupirika kwa Mulungu ndi kumene kunathandiza kuti Natani athe kudzudzula mfumu yamphamvuyi. (2 Sam. 12:1) Nafenso tiyenera kukhala okhulupirika choncho kuti tizitsatira mfundo zolungama za Yehova.

ANKALIMBIKITSA KULAMBIRA KOYERA

Zikuoneka kuti Natani ndi Davide ankagwirizana kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti Davide anatchula mwana wake dzina lakuti Natani. (1 Mbiri 3:1, 5) M’Baibulo timayamba kumva za Natani pa nthawi imene anali ndi Davide. Onse ankakonda Yehova. Mfumuyi iyenera kuti inkakhulupirira kuti Natani ndi wanzeru choncho inamuululira kuti ikufuna kumanga kachisi wa Yehova. Davide anati: “‘Tsopano taona, ine ndikukhala m’nyumba ya mitengo ya mkungudza, pamene likasa la Mulungu woona likukhala m’chihema chansalu.’ Pamenepo Natani anauza mfumu kuti: ‘Chitani chilichonse chimene chili mumtima mwanu, chifukwa Yehova ali nanu.’”​—2 Sam. 7:2, 3.

Popeza Natani ankalambira Yehova mokhulupirika, analimbikitsa Davide kuti amange nyumba yoyamba yoti azilambiriramo Mulungu padziko lapansi. Koma zikuoneka kuti pa nthawiyi, Natani anangonena maganizo ake m’malo monena zinthu m’dzina la Yehova. Ndiyeno usiku womwewo Mulungu anauza mneneriyu kuti akanene kwa mfumuyo uthenga wosiyana ndi umene ananena poyamba. Anakamuuza kuti samanga kachisi wa Yehova. Munthu woti adzamange kachisiyu anali mwana wa Davide. Koma Natani ananenanso kuti Mulungu akuchita pangano ndi Davide lakuti mpando wake wachifumu “udzakhazikika mpaka kalekale.”​—2 Sam. 7:4-16.

Maganizo a Mulungu anasiyana ndi zimene Natani ananena zokhudza kumanga kachisi. Izi zitachitika, mneneri wodzichepetsayu sananyinyirike, m’malomwake anagonjera ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Yehova. Apatu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha zimene tiyenera kuchita ngati Mulungu akutiwongolera pa nkhani inayake. Zimene Natani anachita pambuyo pa nkhani imeneyi zikusonyeza kuti ubwenzi wake ndi Mulungu unali wabwinobe. Ndipotu zikuoneka kuti Yehova anauzira Natani ndi Gadi, yemwe anali wamasomphenya, kuti alimbikitse Davide kukhazikitsa anthu 4,000 oti azidzaimbira Yehova pakachisi.​—1 Mbiri 23:1-5; 2 Mbiri 29:25.

ANATETEZA UFUMU

Natani ankadziwa kuti Solomo ndi amene anayenera kutenga ufumu wa Davide. Koma Davide atakalamba, Adoniya anafuna kulanda ufumu. Natani atadziwa zimenezi, anachita zinthu mwanzeru komanso mokhulupirika. Poyamba, anauza Bateseba kuti akumbutse Davide lumbiro lake lakuti mwana wawo Solomo ndi amene ayenera kukhala mfumu. Kenako Natani anapita kwa Davide kukamufunsa ngati wavomereza zoti Adoniya akhale mfumu. Davide ataona kuti nkhaniyi yafika povuta, anauza Natani ndi anthu ena okhulupirika kuti adzoze Solomo kukhala mfumu komanso alengeze zoti Solomoyo ndi mfumu. Apa zokhumba za Adoniya zinalephereka.​—1 Maf. 1:5-53.

WOLEMBA MBIRI WODZICHEPETSA

Zikuoneka kuti Natani ndi Gadi ndi amene analemba 1 Samueli chaputala 25 mpaka 31 komanso buku lonse la 2 Samueli. Pofotokoza za nkhani zouziridwa zimene zili m’mabuku amenewa, Baibulo limati: “Nkhani zokhudza Davide mfumu, zoyambirira ndi zomalizira, zinalembedwa pakati pa mawu a Samueli wamasomphenya, Natani mneneri, ndiponso pakati pa mawu a Gadi wamasomphenya.” (1 Mbiri 29:29) Zikuonekanso kuti Natani ndi amene analemba “nkhani zina zokhudza Solomo.” (2 Mbiri 9:29) Zonsezi zikusonyeza kuti Davide atamwalira, Natani ayenera kuti anapitirizabe kuthandiza pa zinthu zina zokhudza nyumba yachifumu.

N’kutheka kuti zinthu zambiri zokhudza Natani zimene timawerenga m’Baibulo zinalembedwa ndi Natani yemweyo. Koma iye sanalembe zinthu zina ndipo mfundo imeneyi ikutiphunzitsa khalidwe lina la Natani. Zikuoneka kuti iye anali wolemba mbiri wodzichepetsa. Iye sankafuna kutchuka. Buku lina lomasulira Baibulo limanena kuti iye amapezeka m’Mawu ouziridwa “popanda mawu omufotokoza kapena mzere wa makolo ake.” Sitidziwa mbiri ya moyo wa Natani komanso ya makolo ake.

ANALI WOKHULUPIRIKA KWA YEHOVA

Mfundo zochepa zokhudza Natani zimene timawerenga m’Baibulo zimatithandiza kudziwa kuti iye anali wodzichepetsa koma wamphamvu poonetsetsa kuti chifuniro cha Mulungu chikuchitika. Yehova Mulungu anamupatsa ntchito zovuta kwambiri kuti agwire. Muyenera kuganizira kwambiri makhalidwe abwino a Natani monga kukhala wokhulupirika kwa Mulungu komanso kulemekeza kwambiri zofuna za Mulungu. Yesetsani kutengera makhalidwe amenewa.

Sikuti mungapemphedwe kukapereka uphungu kwa mfumu imene yachita chigololo kapena kukalepheretsa mapulani a anthu oukira. Koma Mulungu akhoza kukuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika komanso muzitsatira mfundo zake zolungama. Mukhozanso kuphunzitsa choonadi molimba mtima koma mosamala ndiponso kulimbikitsa kulambira koyera.

[Chithunzi patsamba 25]

Pofuna kuteteza ufumu, Natani analankhula ndi Bateseba mosamala kwambiri