Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yandikirani Mulungu

“Zinthu Zakale Sizidzakumbukiridwanso”

“Zinthu Zakale Sizidzakumbukiridwanso”

NTHAWI zina kukumbukira zinthu n’kwabwino. Mwachitsanzo, timasangalala tikakumbukira zinthu zabwino zimene tinachita ndi anthu amene timawakonda. Koma nthawi zina tikakumbukira zinthu zakale, timavutika maganizo. Kodi pali zinthu zina zimene zinakuchitikirani, zomwe mukazikumbukira zimakuvutitsani maganizo? Ngati zili choncho, mwina mumadzifunsa kuti, ‘Kodi zinthu zimenezi zidzatheka kuziiwala?’ Tingapeze yankho lolimbikitsa la funso limeneli m’mawu amene mneneri Yesaya analemba.​—Werengani Yesaya 65:17.

Yehova wakonza zoti anthufe tisadzavutikenso maganizo chifukwa chokumbukira zinthu zoipa zimene zinatichitikira. Iye adzachita zimenezi pochotsa zoipa zonse. Kodi Yehova adzachotsa bwanji zoipa zonse? Adzachotsa dziko loipali komanso mavuto onse ndipo adzabweretsa dziko lopanda mavuto. Kudzera mwa Yesaya, Yehova akulonjeza kuti: “Ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Kumvetsa bwino lonjezo limeneli kungatithandize kukhala ndi chiyembekezo.

Kodi kumwamba kwatsopano n’chiyani? Baibulo lingatithandize kupeza yankho la funso limeneli. Choyamba, nkhani yokhudza kumwamba kwatsopano inatchulidwanso ndi anthu ena awiri amene analemba nawo Baibulo ndipo anthu awiri onsewa ankanena zokhudza mmene dzikoli lidzasinthire. (2 Petulo 3:13; Chivumbulutso 21:1-4) Chachiwiri, m’Baibulo mawu akuti “kumwamba” amaimira ulamuliro kapena boma. (Yesaya 14:4, 12; Danieli 4:25, 26) Choncho, kumwamba kwatsopano kukutanthauza boma latsopano limene lidzakwanitse kubweretsa chilungamo padziko lapansili. Pali boma limodzi lokha limene lingathe kuchita zimenezi lomwe ndi Ufumu wa Mulungu womwe Yesu anatiphunzitsa kuti tizipemphera kuti ubwere. Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba ndipo udzachititsa kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lonse lapansi.​—Mateyu 6:9, 10.

Nanga kodi dziko lapansi latsopano n’chiyani? Tiyeni tikambirane mfundo ziwiri za m’Malemba zimene zingatithandize kupeza yankho. Choyamba, m’Baibulo mawu akuti “dziko” nthawi zina amatanthauza anthu osati dziko lenilenili. (Salimo 96:1; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.) Chachiwiri, Baibulo linalosera kuti mu ulamuliro wa Mulungu, anthu okhulupirika adzaphunzira chilungamo ndipo chilungamocho chidzafalikira padziko lonse lapansi. (Yesaya 26:9) Choncho, mawu akuti dziko lapansi latsopano akunena za anthu omwe azidzagonjera ulamuliro wa Mulungu komanso mfundo zake zolungama.

Kodi tsopano mwayamba kuona zimene Yehova adzachite potithandiza kuti tisadzakumbukirenso zinthu zoipa zimene zinatichitikira? Posachedwapa iye akhazikitsa ulamuliro wolungama ndipo kudzera mu ulamuliro umenewu, adzakwaniritsa lonjezo lake lonena za kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. * Mu ulamuliro umenewo, Mulungu adzachotsa mavuto onse amene amachititsa kuti tizikumbukira zinthu zoipa zimene zinatichitikira. Anthu okhulupirika adzasangalala kwambiri ndi moyo ndipo tsiku lililonse azidzachita zinthu zoti akazikumbukira, zizidzawasangalatsa.

Nanga bwanji ngati masiku ano tikuvutika maganizo chifukwa chokumbukira zinthu zimene zinatichitikira? Yehova akupitiriza kutilonjeza kudzera mwa Yesaya kuti: “Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.” Mavuto alionse amene tingakumane nawo m’dziko lakaleli, m’kupita kwanthawi adzaiwalika. Kodi inuyo mukulakalaka kudzakhalapo pa nthawi imene zimenezi zidzachitike? Ngati ndi choncho, mungachite bwino kuphunzira mmene mungayandikirire Mulungu amene analonjeza zinthu zosangalatsa zimenezi.

Mavesi amene mungawerenge mu March:

Yesaya 63-66Yeremiya 1-16

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kuti mudziwe zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu komanso zimene udzachite posachedwapa, werengani mutu 3, 8, ndi 9 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Yehova wakonza zoti anthufe tisadzavutikenso maganizo chifukwa chokumbukira zinthu zoipa zimene zinatichitikira ndipo adzachita zimenezi pochotsa zoipa zonse