Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Mkhristu angachotsedwe mu mpingo chifukwa cha chizolowezi choonera zolaula?

▪ Inde, zimenezi zingachitike. N’chifukwa chake tiyenera kupewa nkhani kapena zithunzi zolaula za mtundu uliwonse, zomwe zingapezeke m’magazini, m’mafilimu komanso zimene zimapezeka pa Intaneti.

Masiku ano zolaula zili ponseponse. Intaneti yachititsa kuti zolaula zizipezeka kwambiri kuposa kale ndipo anthu amene amaonera akuchulukirachulukira. Anthu ena achinyamata ndi achikulire omwe aonapo mwangozi zithunzi zolaula pa Intaneti. Koma ena amaonera kapena kuwerenga dala zimenezi pa nthawi imene ali okhaokha m’nyumba kapena kuntchito. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kusamala kwambiri ndi zinthu zolaula?

Tingaone chifukwa chachikulu mu chenjezo limene Yesu anapereka lakuti: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” (Mat. 5:28) Kwa anthu amene ali m’banja, kugonana kumakhala koyenera ndiponso kosangalatsa. (Miy. 5:15-19; 1 Akor. 7:2-5) Koma si mmene zilili ndi zolaula chifukwa amaonetsa kugonana kwachisawawa kumene kumapangitsa munthu kukhala ndi maganizo oipa amene Yesu anachenjeza. Kunena mosapita m’mbali, kuwerenga kapena kuonera zolaula n’kosemphana ndi malamulo a Mulungu onena kuti: “Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.”​—Akol. 3:5.

Koma bwanji ngati Mkhristu waonera zolaula kamodzi kapena kawiri? Zimenezi zingafanane ndi zinthu zoopsa zimene zinachitikira wamasalimo Asafu. Iye analemba kuti: “Koma ine phazi langa linangotsala pang’ono kupatuka, mapazi anga anangotsala pang’ono kuterereka.” N’zosatheka Mkhristu kukhala ndi chikumbumtima choyera komanso kukhala pa mtendere ndi Mulungu ngati nthawi inayake ankaonera zithunzi zolaula, za amuna kapena akazi amaliseche kapena za anthu akuchita chiwerewere. Nayenso Asafu sanali pa mtendere. Iye anati: “Ndinali kukumana ndi masoka tsiku lililonse, ndipo m’mawa uliwonse ndinali kudzudzulidwa.”​—Sal. 73:2, 14.

Mkhristu amene wakumana ndi vuto limeneli ayenera kudziwa kuti akufunika kulandira thandizo lauzimu. Thandizo limeneli lilipo mu mpingo chifukwa Baibulo limati: “Ngati munthu wapatuka n’kuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu oyenerera mwauzimu, yesani kumuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa. Pamene mukutero, aliyense wa inu asamale.” (Agal. 6:1) Mkulu mmodzi kapena awiri angamuthandize ndipo ‘pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo ndipo machimo ake adzakhululukidwa.’ (Yak. 5:13-15) Anthu amene athandizidwa kuthetsa vuto loonera zolaula, aona kuti kuyandikira kwa Mulungu ndi kumene kwawathandiza mofanana ndi mmene kunamuthandizira Asafu.​—Sal. 73:28.

Koma mtumwi Paulo ananena kuti anthu ena amene anachita machimo “sanalape pa zonyansa zawo, dama lawo, ndi khalidwe lawo lotayirira limene akhala akuchita.” * (2 Akor. 12:21) Ponena za mawu amene anawamasulira kuti “zonyansa” pulofesa wina dzina lake Marvin R. Vincenta ananena kuti mawuwa amanena “za zonyansa zokhudzana ndi chiwerewere.” N’zomvetsa chisoni kuti zolaula zina zimasonyeza zinthu zonyansitsitsa kupitirira pongoonetsa anthu amaliseche kapena anthu akuchita chiwerewere. Pamakhala zinthu zonyansa kwambiri monga kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, kugonana kwa anthu ambirimbiri pamalo amodzi, kugonana ndi nyama, kugona ana, anthu angapo kugwiririra munthu mmodzi, kuchitira nkhanza azimayi ndiponso kumangirira munthu n’cholinga chofuna kugonana naye. M’nthawi ya Paulo anthu ena omwe anali “mu mdima wa maganizo” anafika posathanso ‘kuzindikira makhalidwe abwino, ndipo anadzipereka okha ku khalidwe lotayirira kuti achite chonyansa chamtundu uliwonse mwadyera.’​Aef. 4:18, 19.

Paulo ananenanso za “zinthu zodetsa” pa Agalatiya 5:19. Katswiri wina wa ku Britain ananena kuti “pa lembali mawuwa amanena za zilakolako zosakhala zachibadwa.” Palibe Mkhristu amene angatsutse zoti zinthu zimene tatchula pamwambapa ndi “zilakolako zosakhala zachibadwa” ndipo n’zonyansa kwambiri. Pa Agalatiya 5:19-21, Paulo anamaliza ndi mawu akuti anthu amene amachita zonyansa zimenezi “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” Choncho ngati munthu atakhala ndi chizolowezi choonera zolaula zonyansa kwambiri zimenezi kwa nthawi yaitali ndipo sakulapa n’kutembenuka, akhoza kuchotsedwa mu mpingo wachikhristu. Munthu wotereyu ayenera kuchotsedwa n’cholinga choti mpingo ukhale woyera.​—1 Akor. 5:5, 11.

Tiyenera kudziwa kuti anthu ena amene anaonera zolaula zonyansazi amapita kwa akulu n’kuthandizidwa kuti asinthe. Yesu anauza Akhristu mu mpingo wa Sade kuti: “Limbikitsa otsala amene atsala pang’ono kufa, . . . pitiriza kukumbukira zimene unalandira ndi zimene unamva. Pitiriza kuzitsatira, ndipo ulape. Ndithudi, ukapanda kudzuka, . . . sudzadziwa ngakhale pang’ono ola limene ndidzafike kwa iwe.” (Chiv. 3:2, 3) N’zotheka ndithu kulapa n’kukwatulidwa pamoto.​—Yuda 22, 23.

Ndi bwino kuti aliyense ayesetse kupewa chilichonse chimene chingamuchititse kukhala pa ngozi mwauzimu. Choncho tiyeni titsimikize mu mtima mwathu kuti tisadzaonere zolaula za mtundu uliwonse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Kuti mudziwe kusiyana kwa mawu akuti “chonyansa chamtundu uliwonse, dama ndiponso khalidwe lotayirira,” onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2006, tsamba 29 mpaka 31.

[Mawu Otsindika patsamba 30]

Mkhristu amene wakhala akuonera zolaula ayenera kudzuka mwauzimu n’kuyesetsa kuti apeze thandizo lauzimu