Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kudziwa Mayankho Olondola Kuli Ndi Phindu?

Kodi Kudziwa Mayankho Olondola Kuli Ndi Phindu?

Kodi Kudziwa Mayankho Olondola Kuli Ndi Phindu?

“Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—YOHANE 8:32.

M’BAIBULO muli choonadi chimene chingatimasule ku zikhulupiriro zosamvetsetseka komanso zabodza zonena za Yesu. Koma kodi kuganizira ngati zimene timakhulupirira pa nkhani ya Yesu zili zoona n’kofunika? Inde n’kofunika chifukwa Yehova komanso Yesu amaona kuti nkhani imeneyi ndi yofunika. Choncho ifenso tiyenera kuiona kuti ndi yofunika.

N’chifukwa chiyani Yehova amaona kuti nkhani imeneyi ndi yofunika? Mwachidule, tingati ndi chifukwa chakuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Yehova amafuna kuti tikhale ndi moyo wosangalala komanso wosatha. Yesu anati: “Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko [kutanthauza anthu] mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye . . . akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mulungu anatumiza Mwana wake kuti adzatiwombole komanso kuti adzatsegule njira yoti tidzathe kukhala m’Paradaiso padziko lapansi. Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene Mulungu ankafuna pa chiyambi polenga anthu. (Genesis 1:28) Mulungu ndi wofunitsitsa kupereka mphatso ya moyo wosatha kwa anthu amene akuphunzira choonadi chonena za Mwana wake komanso amene akuchita zinthu mogwirizana ndi zimene akuphunzirazo.​—Aroma 6:23.

N’chifukwa chiyani Yesu amaona kuti nkhani imeneyi ndi yofunika? N’chifukwa chakuti Yesu nayenso amakonda anthu. Iye anasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena pamene anapereka moyo wake chifukwa cha machimo athu. (Yohane 15:13) Anachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti imeneyi ndi njira yokhayo imene ingathandize kuti anthu apulumutsidwe. (Yohane 14:6) Choncho n’zodziwikiratu kuti Yesu amafuna kuti anthu ambiri apindule ndi nsembe yake ya dipo. N’chifukwa chake iye analamula otsatira ake enieni kuti aziphunzitsa anthu padziko lonse lapansi kuti adziwe zimene Mulungu amafuna komanso cholinga chake polenga anthu.​—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

N’chifukwa chiyani nkhani imeneyi iyeneranso kukhala yofunika kwa ife? Taganizirani za zinthu zimene mumaona kuti ndi zofunika, monga thanzi lanu komanso banja lanu. Kodi mumafunitsitsa inuyo ndi anthu amene mumawakonda mutakhala ndi thanzi labwino komanso moyo wosangalala? Kudzera mwa Yesu, Yehova wapereka mwayi kwa inu komanso anthu amene mumawakonda woti mudzakhale ndi thanzi labwino komanso moyo wosatha m’dziko lapansi latsopano. M’dziko limenelo simudzakhala zopweteka kapena kuvutika kulikonse. (Salimo 37:11, 29; Chivumbulutso 21:3, 4) Kodi mungafune kudzakhala m’dziko loterolo? Ngati mungafune, pali zimene muyenera kuchita.

Onaninso vesi limene lili m’munsi mwa mutu wa nkhani ino, lomwe likuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” Choonadi ponena za Yesu komanso ponena za udindo wake pokwaniritsa cholinga cha Mulungu, chingatimasule ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Koma kuti inuyo mumasulidwe ku ukapolo umenewu, muyenera ‘kudziwa choonadi’ chimenechi. Choncho tikukupemphani kuti muphunzire zambiri zokhudza choonadichi. Muyeneranso kuphunzira zimene inuyo ndi anthu amene mumakonda mungachite kuti mupindule ndi choonadichi. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani.