Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pomwe ananena za kumunyamulira munthu waudindo mtunda wa makilomita awiri?

Pa ulaliki wake wotchuka wa paphiri, Yesu anati: “Winawake waudindo akakulamula kuti umunyamulire katundu mtunda wa kilomita imodzi, umunyamulire mtunda wa makilomita awiri.” (Mateyu 5:41) Anthu omwe ankamvetsera Yesu ayenera kuti anazindikira kuti iye ankanena za ntchito imene anthu audindo ankakakamiza nzika kugwira.

Mu nthawi ya atumwi, Aisiraeli ankalamulidwa ndi Aroma. Aromawo ankakonda kukakamiza anthu kapena nyama kuchita zimene iwowo akuona kuti zingathandize kuti ntchito yawo iyende mwamsanga. Iwo ankathanso kutenga katundu aliyense wa munthu wina n’kugwiritsa ntchito yomwe akufunayo. Chitsanzo cha ntchito zokakamizazi ndi ntchito imene asilikali achiroma analamula Simoni, wa ku Kurene, kuchita. Iwo anamulamula kuti asenze mtengo wokapachikapo Yesu n’kupita nawo kumalo amene anakam’pachikira Yesu. (Mateyu 27:32) Ayuda ankadana kwambiri ndi ntchito zimenezi chifukwa zinkakhala zopondereza.

Sizikudziwika kuti anthu ankaumirizidwa kugwira ntchito yokakamizidwayi mpaka pati. Koma n’zokayikitsa kuti anthuwa ankagwira ntchito yoposa imene alamulidwa. Choncho, pamene Yesu anauza omvera ake kuti azinyamulira katundu munthu waudindo mtunda wa makilomita awiri, ankalimbikitsa omvera akewo kuti azigwira mosanyinyirika ntchito zimene anthu aulamuliro awauza.​—Maliko 12:17.

Kodi Anasi amene amatchulidwa m’Mauthenga Abwino anali ndani?

Baibulo limanena kuti Anasi (Ananusi) anali “wansembe wamkulu” ndipo pa nthawi imene Yesu ankazengedwa mlandu n’kuti iye ali pa udindowu. (Luka 3:2; Yohane 18:13; Machitidwe 4:6) Iye anali mpongozi wake wa Kayafa, yemwe anali mkulu wa ansembe. Kenako nayenso anakhala mkulu wa ansembe kuyambira cha m’ma 6 kapena 7 C.E. mpaka cha m’ma 15 C.E. pamene anachotsedwa pa udindowu ndi bwanamkubwa wachiroma, dzina lake Valerius Gratus. Ngakhale zinali choncho, iye anapitirizabe kukhala ndi mphamvu zambiri mu Isiraeli. Ana ake asanu komanso mpongozi wake anadzatumikiranso pa udindo wa mkulu wa ansembe.

Aisiraeli akakhala kuti akudzilamulira okha, mkulu wa ansembe ankakhala pa udindowu kwa moyo wake wonse. (Numeri 35:25) Koma pamene dziko la Isiraeli linkalamulidwa ndi Aroma, mkulu wa ansembe ankagwira ntchito yake moyang’aniridwa ndi abwanamkubwa achiroma komanso mafumu osankhidwa ndi Aroma ndipo ankatha kuchotsedwa pa udindowu ndi anthu amenewa. Mwachitsanzo, wolemba mbiri wina dzina lake Flavius Josephus analemba kuti cha m’ma 6 kapena 7 C.E. Kureniyo, yemwe anali bwanamkubwa wachiroma ku Siriya, anachotsa pa udindo wa mkulu wa ansembe munthu wina dzina lake Joazar ndipo anasankha Anasi kukhala mkulu wa ansembe. Zikuoneka kuti olamulira achiromawa akamasankha ansembe ankaonetsetsa kuti ansembewo akuchokera ku banja la ansembe.

Anthu a m’banja la Anasi anali adyera komanso olemera kwambiri. N’kutheka kuti iwo analemera chifukwa choti ankayang’anira malonda amene ankachitika m’kachisi ogulitsa zinthu zofunika popereka nsembe, monga nkhunda, nkhosa, mafuta ndiponso vinyo. Josephus ananena kuti Ananusi (Hananiya), yemwe anali mwana wa Anasi, anali ndi “antchito ake amene anali achinyengo kwambiri ndipo ankakakamiza anthu kupereka chakhumi kwa ansembe. Komanso iwo ankamenya aliyense amene wakana kuwapatsa chakhumicho.”