Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo

Ankateteza ndi Kusamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika

Ankateteza ndi Kusamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika

TAYEREKEZERANI kuti mukuona Yosefe akukweza katundu pabulu. Kenako akusisita bulu wakeyo uku akuyang’anitsitsa mudzi wa Betelehemu. Iye ankaganizira za ulendo wautali umene ayende wopita ku Iguputo. Kodi iye ndi banja lake akakwanitsa kusintha zinthu pa moyo wawo kuti akagwirizane ndi anthu akumeneko omwe ali ndi chilankhulo komanso miyambo yosiyana ndi yawo?

Zinali zovuta kuti Yosefe auze mkazi wake wokondedwa, Mariya, nkhani yomvetsa chisoni. Komabe iye analimba mtima n’kumuuza. Anamuuza zimene mngelo wa Mulungu anamufotokozera m’maloto zoti Mfumu Herode akufuna kupha mwana wawo ndipo iwo akufunika kusamuka mwamsanga. (Mateyu 2:13, 14) Mariya anamva chisoni kwambiri ndi zimenezi. Iye anadabwa kuti munthu wina angafune kupha mwana wake wosalakwayo chifukwa chiyani? Uthenga umene anauzidwawo unali wovuta kumvetsa komabe iwo anakhulupirira Yehova ndipo anayamba kukonzekera zosamuka.

Usiku, anthu a ku Betelehemu ali m’tulo, Yosefe, Mariya ndi Yesu anatuluka m’mudziwo. Iwo analowera chakummwera ndipo pamene kumacha, Yosefe ayenera kuti anayamba kuda nkhawa kuti ziwathera bwanji. Popeza kuti iye anali kalipentala wamba, kodi akanakwanitsa bwanji kuteteza banja lake kwa asilikali amphamvu? Kodi akanakwanitsa kupezera banja lake zosowa? Kodi iye akanakwanitsa udindo waukulu umene Yehova Mulungu anamupatsa wosamalira ndi kulera Yesu, yemwe anali mwana wapadera? Yosefe anakwanitsa kuchita zinthu zonsezi. Nkhaniyi ikusonyeza mmene iye anachitira zimenezi. Kuphunzira zimene iye anachita kuthandiza abambo komanso ena tonsefe kutsanzira chikhulupiriro chake.

Yosefe Anateteza Banja Lake

Miyezi yambiri izi zisanachitike, m’tawuni ya Nazareti, komwe kunali kwawo kwa Yosefe, munachitika zinthu zimene zinasintha kwambiri moyo wa Yosefeyo. Pa nthawiyi n’kuti iye ali pa chibwenzi ndi Mariya, mwana wa Heli. Yosefe ankaona kuti Mariya anali mtsikana wokhulupirika koma kenako anangomva kuti Mariyayo ali ndi pakati. Atamva zimenezi anakonza zoti amusudzule mwamseri n’cholinga choti asamuchititse manyazi. * Koma asanachite zimenezi mngelo wa Mulungu analankhula naye kudzera m’maloto ndipo anamuuza kuti Mariya anali ndi pakati mwa mphamvu ya mzimu woyera wa Yehova. Mngeloyo ananenanso kuti mwana amene adzabadweyo “adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.” Komanso anauza Yosefe kuti: “Usaope kutengera Mariya mkazi wako kunyumba.”​—Mateyu 1:18-21.

Popeza Yosefe anali munthu wolungama komanso ankamvera Mulungu, anachita zimene mngelo anamuuzazo. Iye anavomera udindo waukulu kwambiri wolera mwana wosakhala wake koma amene anali wofunika kwambiri kwa Mulungu. Kenako, Yosefe anatenga mkazi wake, yemwe pa nthawiyi anali ndi pakati, n’kupita ku Betelehemu kuti akalembetse m’kaundula. Iye anachita zimenezi pomvera lamulo la boma ndipo kumeneko n’kumene mwana wa Mariya anabadwira. *

Yosefe sanabwererenso ndi banja lake ku Nazareti. Iye anakhazikika ku Betelehemu, kufupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Ngakhale kuti anali wosauka, Yosefe ankayesetsa kuteteza ndi kupezera anthu a m’banja lake zosowa zawo. Kwa kanthawi, iwo ankakhala m’kanyumba kenakake. Kenako, Yesu atakwanitsa chaka chimodzi, moyo wa banja lawo unasinthanso mwadzidzidzi.

Kunyumba kwa Yosefe ndi Mariya kunabwera amuna okhulupirira nyenyezi ochokera Kum’mawa, omwe mwina ankachokera ku Babulo. Iwo anatsatira nyenyezi inayake mpaka kukafika kunyumbako ndipo cholinga chawo chinali kukaona mwana amene adzakhale mfumu ya Ayuda. Amunawa anali aulemu kwambiri.

Kaya ankadziwa kapena ayi, zimene okhulupirira nyenyeziwa anachita zinamuika Yesu m’mavuto oopsa. M’malo mowatsogolera ku Betelehemu, nyenyezi ija inawalondolera kaye ku Yerusalemu. Kumeneko amunawa anauza Mfumu Herode, yemwe anali woipa kwambiri, kuti akufufuza mwana amene adzakhale mfumu ya Ayuda. Herode atamva zimenezi anachita nsanje ndipo anakwiya kwambiri.​—Onani nkhani yakuti “Zimene Owerenga Amafunsa . . . Kodi Ndani Anatumiza Nyenyezi Imene Inatsogolera Anthu Kwa Yesu?” patsamba 29.

Koma mwamwayi, Yehova yemwe ndi wamphamvu kuposa Herode anateteza mwanayo. Kodi iye anachita zimenezi motani? Amuna aja anabweretsa mphatso zamtengo wapatali zoti banjali silinkayembekezera kuti lingakhale nazo. Iwo anabweretsa “golide, lubani ndi mule.” Amuna okhulupirira nyenyeziwa anali ndi cholinga choti pobwerera kwawo, adzerenso kwa Mfumu Herode kuti akamufotokozere kumene kuli mwanayo. Koma Yehova analowererapo. Kudzera m’maloto anawauza kuti adutse njira ina.​—Mateyu 2:1-12.

Okhulupirira nyenyezi aja atangochoka, mngelo wa Yehova anachenjeza Yosefe kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo uthawire ku Iguputo. Ukakhale kumeneko kufikira nthawi imene ndidzakuuze, chifukwa Herode akukonza zoyamba kufunafuna mwanayu kuti amuphe.” (Mateyu 2:13) Monga taonera koyambirira kwa nkhani ino, Yosefe sanazengereze kutsatira chenjezolo ndipo anasamukira ku Iguputo. Iye anachita zimenezi chifukwa anaona kuti kuteteza mwanayo kunali kofunika kuposa chilichonse. Chifukwa chakuti okhulupirira nyenyezi aja anali atawapatsa mphatso zamtengo wapatali, iwo anali ndi zinthu zoti angakagwiritse ntchito kumalo kumene anasamukirako.

Ulendowu unali wautali, wovuta komanso wotopetsa. Koma m’mabuku ena amene anawonjezeredwa pa mabuku amene ali m’Baibulo muli nkhani zopeka komanso nthano zina zomwe zimanena mokometsera ulendo wa banjali wopita ku Iguputo. Nkhanizi zimati ulendowo unali wosapweteka chifukwa chakuti Yesu mozizwitsa anafupikitsa ulendowu, anachititsa kuti anthu achifwamba asawavulaze komanso anachititsa kuti mitengo ya kanjedza iziweramira pansi kuti mayi ake athyole zipatso zake. *

Makolo angaphunzire zambiri kwa Yosefe. Iye anasiya kaye ntchito yake ndi zinthu zina n’cholinga chakuti ateteze banja lake. N’zachidziwikire kuti iye ankaona kuti anali ndi udindo wopatsidwa ndi Yehova wosamalira banja lake. Masiku anonso makolo ali ndi udindo waukulu wolera ana chifukwa m’dzikoli muli zinthu zambiri zimene zingathe kuwononga khalidwe la ana, mwinanso kuwaphetsa kumene. Komabe n’zosangalatsa kuti makolo ambiri amayesetsa kugwira ntchito mwakhama kuti asamalire komanso ateteze ana awo ngati mmene Yosefe anachitira.

Yosefe Ankapezera Banja Lake Zosowa

Zikuoneka kuti banjali silinakhale ku Iguputo nthawi yaitali chifukwa pasanapite nthawi mngelo anauza Yosefe kuti Herode wafa. Choncho Yosefe anatenga banja lake n’kuyamba ulendo wobwerera kudziko lakwawo. Ulosi wina unaneneratu kuti Yehova adzaitana mwana wake “kuti atuluke mu Iguputo.” (Mateyu 2:15) Yosefe anathandizira nawo kuti ulosi umenewu ukwaniritsidwe. Koma kodi tsopano iye ndi banja lake akakhala kuti?

Ngakhale kuti Herode anali atafa, Yosefe anachita zinthu mosamala chifukwa anadziwa kuti Arikelao, amene analowa m’malo mwa Herode, nayenso anali wankhanza. Mulungu anatsogolera Yosefe ndi banja lake kuti apite chakumpoto, kutali ndi mzinda wa Yerusalemu, mpaka anafika kwawo ku Nazareti mumzinda wa Galileya. Kumeneko Yosefe ndi Mariya anaberekanso ana ena.​—Mateyu 2:19-23.

Iwo ankakhala moyo wosalira zambiri komabe ankafunika kugwira ntchito mwakhama kuti apeze zofunika pa moyo. Baibulo limanena kuti Yosefe anali mmisiri wamatabwa. Mawu amenewa akusonyeza kuti ntchito yake inkaphatikizapo kugwetsa mitengo, kuinyamula komanso kuiumitsa kuti akamangire nyumba ndi milatho ing’onoing’ono. Mitengoyi ankaigwiritsanso ntchito popanga maboti, ngolo, mateyala, magoli ndi zipangizo zosiyanasiyana zaulimi. (Mateyu 13:55) Imeneyi sinali ntchito yamasewera. Nthawi zambiri mmisiri wamatabwa ankagwirira ntchito pakhonde pa nyumba yake kapena m’kanyumba komwe ankakamanga moyandikana ndi nyumba yakeyo.

Yosefe anali ndi zipangizo zosiyanasiyana zogwirira ntchito yake ndipo n’kutheka kuti zina mwa zimenezi anapatsidwa ndi bambo ake. Ankagwiritsa ntchito zipangizo monga sikweya, chingwe chowongolera, kankhwangwa, sowo, kasemasema, hamala, tchizulo, zomatira zosiyanasiyana, choboolera komanso mwina ankakhala ndi misomali ngakhale kuti inali yokwera mtengo.

Yesu ali wamng’ono ayenera kuti ankakonda kuonerera bambo ake akamagwira ntchito. Ankayang’anitsitsa mwachidwi chilichonse chimene iwo ankachita. Iye ayenera kuti ankachita chidwi ndi mphamvu komanso luso la bambo akewo. N’kutheka kuti Yosefe ankaphunzitsa mwana wakeyo ntchito zing’onozing’ono monga kusalaza thabwa pogwiritsa ntchito chikopa chouma cha nsomba. Mwinanso anamuphunzitsa kusiyanitsa matabwa a mitengo imene ankagwiritsa ntchito monga matabwa a mtengo wa mkuyu, wa maolivi ndi mitengo ina.

Yesu ankadziwa kuti ngakhale kuti bambo ake anali ndi manja okhakhala chifukwa cha ntchito imene ankagwira, monga kugwetsa mitengo, kuiwaza komanso kulumikiza matabwa, iwo ankamusisita mwachikondi ndiponso ankamulimbikitsa. Ankachitanso chimodzimodzi ndi mayi ake komanso abale ake. Yosefe ndi Mariya anali ndi banja lalikulu chifukwa m’kupita kwa nthawi anali ndi ana ena osachepera 6 kuwonjezera pa Yesu. (Mateyu 13:55, 56) Yosefe ankafunika kugwira ntchito mwakhama kuti asamalire ndiponso kudyetsa banja lake lonse.

Komabe iye ankadziwa kuti chofunika kwambiri ndi kusamalira banja lake mwauzimu. Choncho ankayesetsa kupeza nthawi yophunzitsa ana ake za Yehova Mulungu ndi malamulo Ake. Nthawi zonse Yosefe ndi Mariya ankatenga ana awo kupita kusunagoge kumene Chilamulo chinkawerengedwa ndiponso kufotokozeredwa. N’kutheka kuti Yesu ankakhala ndi mafunso pa zimene wamva kusunagogeko ndipo Yosefe ankayesetsa kumuyankha mafunso akewo. Yosefe ankatenganso banja lake kupita ku zikondwerero zomwe zinkachitika ku Yerusalemu. Kuti akapezeke ku mwambo wa Pasika umene unkachitika chaka chilichonse, iye ndi banja lake ankayenera kuyenda ulendo wa makilomita oposa 112. Ulendo wonsewu unkatenga milungu iwiri.

Masiku ano, Akhristu omwe ndi mitu ya mabanja amachitanso chimodzimodzi. Amadzipereka kuthandiza ana awo ndipo amaona kuti kuphunzitsa ana awo zinthu zauzimu n’kofunika kwambiri kuposa zinthu zakuthupi. Iwo amayesetsa kupita ndi ana awo ku misonkhano yonse yachikhristu, ya mpingo ngakhalenso yaikuluikulu. Mofanana ndi Yosefe, iwo amadziwa kuti palibe chabwino chimene angapatse ana awo kuposa kuwaphunzitsa zinthu zauzimu.

“Tinada Nkhawa Kwambiri”

Yesu ali ndi zaka 12, Yosefe anatenganso banja lake kupita ku Yerusalemu. Inali nthawi ya chikondwerero cha Pasika ndipo mabanja akuluakulu anayendera limodzi. Iwo ankayenda ndi nyama zonyamula katundu ndipo anadutsa m’njira zomwe zinali ndi msipu wobiriwira m’mbali mwake. Akuyandikira mzinda wa Yerusalemu, womwe unali pamalo okwera, n’kutheka kuti ambiri anayamba kuimba masalimo a nyimbo zokwerera kumzinda. (Salimo 120–134) Pa nthawi ya chikondwererochi, mumzindawo munali anthu piringupiringu. Chikondwererocho chitatha, mabanja onse anayamba ulendo wobwerera kwawo. Mwina chifukwa chotanganidwa, Yosefe ndi Mariya ankangoona ngati Yesu ali naye limodzi pa ulendowo ndipo mwina ankaganiza kuti ali ndi achibale ena. Koma atayenda mtunda wa tsiku lathunthu, anazindikira kuti pagululo palibe Yesu.​—Luka 2:41-44.

Nthawi yomweyo anayambanso ulendo wobwerera ku Yerusalemu ndipo anam’fufuza m’malo onse amene anadutsa. Taganizirani mmene mzindawo unkaonekera pa nthawiyi, anthu onse atapita, pamene iwo ankayenda kwinaku akuitana Yesu. Kodi iye anali ali kuti? Atafufuza kwa masiku atatu, mwina Yosefe anayamba kuda nkhawa kuti walephera udindo wake umene Yehova anamupatsa. Kenako anapita kukam’fufuza m’kachisi. Iwo anafufuza paliponse mpaka anafika m’chipinda chimene munali aphunzitsi odziwa bwino Chilamulo ndipo mmenemo ndi mmene anam’peza Yesu. Apa n’zoonekeratu kuti mtima wa Yosefe ndi Mariya unakhala m’malo.​—Luka 2:45, 46.

Yesu ankamvetsera zimene aphunzitsiwo ankanena ndipo ankawafunsa mafunso. Aphunzitsiwo anachita chidwi kwambiri ndi nzeru za mwanayo komanso mayankho amene ankapereka. Koma Mariya ndi Yosefe anadabwa kum’peza ali kumeneko. Baibulo limasonyeza kuti Yosefe sanalankhule kanthu. Koma mawu amene Mariya analankhula akusonyeza maganizo amene makolo onsewo anali nawo. Iye anati: “Mwanawe, n’chifukwa chiyani wativutitsa chonchi? Ine ndi bambo akowa tinada nkhawa kwambiri ndipo timakufunafuna.”​—Luka 2:47, 48.

Pamenepatu Mawu a Mulungu akusonyeza kuti kulera mwana si ntchito yamasewera, ngakhale mwanayo atakhala wangwiro. Zimene zikuchitika m’dzikoli masiku ano zikuchititsa kuti kulera ana kuzipangitsa makolo kukhala ndi ‘nkhawa kwambiri.’ Komabe iwo ayenera kudziwa kuti Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amazindikira mavuto amene makolo akukumana nawo.

N’zosangalatsa kuti Yesu anali pamalo amene ankaona kuti amuthandiza kuyandikira kwa Atate wake wakumwamba, Yehova. Iye anali wofunitsitsa kuphunzira zambiri za Atate wake. N’chifukwa chake anayankha makolo ake kuti: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kodi simunadziwe kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?”​—Luka 2:49.

Yosefe ayenera kuti anaganizira mawu amenewa kambirimbiri. N’kutheka kuti nthawi zina akakumbukira mawuwa ankanyadira popeza anali atayesetsa kumuphunzitsa mwanayu kuti aziona kuti Yehova Mulungu ndi Atate wake. Ngakhale kuti Yesu anali adakali mwana, ankakonda kwambiri Yehova ndipo ankamuona kuti ndi “Atate” wake. Iye anakhala ndi maganizo amenewa chifukwa cha zimene Yosefe ankam’phunzitsa.

Ngati ndinu bambo, kodi mumazindikira udindo umene muli nawo wothandiza ana anu kuti aziona kuti Yehova ndi Atate wachikondi komanso amateteza anthu ake? N’chimodzimodzinso ngati mumalera ana oti si anu. Muyenera kutengera chitsanzo cha Yosefe ndipo muziona kuti mwana aliyense ndi wofunika. Athandizeni kuyandikira kwa Atate wawo wakumwamba, Yehova Mulungu.

Yosefe Anakhalabe Wokhulupirika

M’Baibulo muli nkhani zochepa zokhudza Yosefe komabe nkhani zake ndi zothandiza kwambiri. Baibulo limanena kuti Yesu “anapitiriza kuwamvera” makolo ake. Komanso limanena kuti “Yesu anali kukulabe m’nzeru ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiriza kukondwera naye.” (Luka 2:51, 52) Mawu amenewa akutiphunzitsa zambiri zokhudza Yosefe. Choyamba, tikuphunzira kuti Yosefe anapitirizabe kutsogolera banja lake. Tikutero chifukwa Yesu, yemwe anali mwana wangwiro, ankalemekeza komanso kumvera bambo akewo.

Chachiwiri, tikuphunzira kuti Yesu anapitiriza kukula mu nzeru. N’zosakayikitsa kuti Yosefe ndi amene anathandiza kwambiri mwana wakeyu. Pa nthawi imeneyo, panali mwambi umene Ayuda ankakonda kunena. Iwo ankanena kuti anthu ongokhala osagwira ntchito ndi amene amakhala anzeru koma anthu amene amagwira ntchito mwakhama monga akalipentala, alimi komanso osula zitsulo “sangaphunzitse ena nzeru ndi chilungamo ndipo anthu oterewa sayenera kupezeka pamene akuluakulu akukamba mawu okuluwika.” Koma nkhani ya Yesu inasonyeza kuti mawu amenewa ndi abodza. Iye ali mnyamata, bambo ake omwe anali kalipentala wamba, anamuphunzitsa “nzeru ndi chilungamo” cha Yehova. Yosefe ayenera kuti anaphunzitsa Yesu zimenezi kambirimbiri.

Chinanso chimene chikusonyeza kuti Yosefe ankalera bwino Yesu ndi mmene Yesuyo ankakulira. Yesu anali mwana wosamalidwa bwino ndipo anali wamphamvu komanso wathanzi. Yosefe anaphunzitsanso mwana wakeyu ntchito yamanja imene iye ankagwira. Yesu sankangodziwika kuti anali mwana wa mmisiri wamatabwa koma nayenso ankadziwika kuti anali “mmisiri wamatabwa.” (Maliko 6:3) Izi zikusonyeza kuti Yosefe anamuphunzitsa bwino ntchitoyi. Abambo ambiri amatsatira chitsanzo cha Yosefe ndipo amaganizira za tsogolo la ana awo, choncho amaonetsetsa kuti akuwaphunzitsa ntchito kuti adzadziimire paokha akadzakula.

Kungoyambira pamene Yesu anabatizidwa ali ndi zaka 30, Baibulo silitchulanso za Yosefe. N’kutheka kuti pamene Yesu ankayamba utumiki wake n’kuti Mariya ali mayi wamasiye. (Onani bokosi lakuti “Kodi Yosefe Anamwalira Liti?” patsamba 27.) Komabe zimene Yosefe anachita zinasonyeza kuti iye anali bambo wabwino yemwe ankateteza ndi kusamalira banja lake. Komanso iye anakhalabe wokhulupirika mpaka imfa yake. Zimene Yosefe anachita ndi chitsanzo chabwino kwa abambo, amuna okwatira komanso Akhristu onse.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 M’masiku amenewo, chibwenzi chinkaonedwa mosasiyana kwenikweni ndi ukwati.

^ ndime 8 Onani nkhani yakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo​—‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2008.

^ ndime 14 Baibulo limasonyeza momveka bwino kuti Yesu sanachite chozizwitsa chilichonse mpaka pamene anabatizidwa. (Yohane 2:1-11) Kuti mudziwe zambiri za mabuku owonjezera amene anthu ena amati ali m’gulu la Mauthenga Abwino a m’Baibulo, werengani nkhani imene ili patsamba 18 yakuti, “Kodi Pali Mabuku Ena a Uthenga Wabwino Amene Amafotokoza Nkhani za Yesu Zimene M’Baibulo Mulibe?

[Bokosi patsamba 27]

Kodi Yosefe Anamwalira Liti?

Taona kuti Yosefe anali adakali moyo mpaka pamene Yesu anali ndi zaka 12. Pa msinkhu umenewu ana ambiri achiyuda ankayamba kuphunzira ntchito imene bambo awo ankagwira moti pofika zaka 15 ankakhala ataidziwa ntchitoyo. Zikuoneka kuti Yosefe anakhala ndi moyo mpaka anaphunzitsa Yesu kukhala kalipentala. Koma kodi Yosefe anali adakali moyo pamene Yesu ankayamba utumiki wake ali ndi zaka 30? N’zokayikitsa ngati anali moyo chifukwa pa nthawiyi amene amatchulidwa ndi amayi ake a Yesu, azichimwene ake ndi azilongo ake basi. Ndiponso pa nthawi ina Yesu ankatchedwa kuti “mwana wa Mariya,” osati mwana wa Yosefe. (Maliko 6:3) Zikuonekanso kuti pa nthawi ina Mariya ndi amene ankatsogolera zochitika za m’banjali popanda kufunsa mwamuna wake. (Yohane 2:1-5) Zimenezi zinali zosatheka pa nthawi imeneyo pokhapokha ngati mkazi ali wamasiye. Ndipo Yesu atatsala pang’ono kufa, anapempha mtumwi Yohane kuti azisamalira amayi ake. (Yohane 19:26, 27) Zikanakhala kuti Yosefe anali moyo, Yesu sakanachita zimenezi. Choncho zikuoneka kuti Yosefe anamwalira Yesu adakali mnyamata. Popeza kuti Yesu ndiye anali mwana wamkulu m’banjamo, ndi amene anapitiriza ntchito ya ukalipentala ija, n’kumasamalira banja lawo mpaka pamene anabatizidwa.

[Chithunzi patsamba 24]

Pofuna kuteteza mwana wake, Yosefe anachita zinthu mosazengereza komanso mosonyeza kuganizira ena

[Chithunzi patsamba 25]

Yosefe ankagwira ntchito mwakhama kuti apezere banja lake zosowa

[Chithunzi patsamba 26]

Nthawi zonse Yosefe ankapita ndi banja lake kukachisi ku Yerusalemu kuti akalambire Mulungu

[Chithunzi patsamba 28]

Yosefe anaphunzitsa mwana wake ntchito ya ukalipentala