Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Ndani Anatumiza Nyenyezi Imene Inatsogolera Anthu kwa Yesu?

Kodi Ndani Anatumiza Nyenyezi Imene Inatsogolera Anthu kwa Yesu?

▪ Kodi munayamba mwaonapo zithunzi kapena masewero a kubadwa kwa Yesu akusonyeza mafumu, kapena anzeru akum’mawa atatu, akudzaona Yesu atangobadwa kumene ali modyeramo ziweto? Anthu amanena kuti Mulungu anatumiza nyenyezi kuti itsogolere amuna amenewa ku Betelehemu kukhola kumene Yesu anabadwira. M’mayiko ena, ana ambiri amafika mpaka poloweza mayina a mafumu atatu amenewa kuti ndi Melchior, Caspar ndi Baltazar. Koma ngakhale kuti nkhani imeneyi ndi yotchuka chonchi, kodi ndi yogwirizana ndi zimene Baibulo limanena? Ayi, chifukwa pali mfundo zingapo zimene zimasonyeza kuti nkhaniyi siyolondola.

Choyamba, kodi anthu amene anapita kukaona Yesuwa anali ndani? M’Malemba Achigiriki oyambirira, anthuwa satchulidwa kuti anali mafumu kapena anthu anzeru. Amatchulidwa kuti anali amagi, kapena kuti okhulupirira nyenyezi. Iwo sankalambira Yehova ndipo ankachita zamatsenga potengera kaonekedwe komanso kayendedwe ka nyenyezi. Komanso Baibulo silitchula mayina awo ndiponso kuti analipo angati.

Chachiwiri, kodi ndi nthawi iti imene iwo anapita kukaona Yesu? Iwo sanakaone Yesu ali wakhanda atagonekedwa modyeramo ziweto koma anakamuona atachokamo. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Mateyu, amene analemba nawo Uthenga Wabwino, analemba kuti: “Atalowa m’nyumbamo, anaona mwanayo ndi mayi ake Mariya.” (Mateyu 2:11) Onani kuti Baibulo likunena kuti iwo analowa m’nyumba, osati m’khola. Choncho, pa nthawiyi Yosefe ndi Mariya sankagonanso m’khola koma ankagona m’nyumba. Komanso Baibulo likusonyeza kuti mwanayo sanali modyeramo ziweto koma anali ndi mayi ake.

Chachitatu, kodi ndani anatumiza nyenyezi imene inatsogolera okhulupirira nyenyeziwa? Atsogoleri ambiri a chipembedzo amaphunzitsa kuti Mulungu ndi amene anatumiza nyenyeziyo. Koma kodi zimenezi ndi zoona? Kumbukirani kuti nyenyezi ija isanawalondolere ku Betelehemu, inawalondolera kaye kwa Mfumu Herode ku Yerusalemu. Iwo anaulula za kubadwa kwa Yesu kwa mfumu yansanje komanso yankhanza imeneyi yomwe sinasangalale itamva za kubadwa kwa mwana amene adzakhale “Mfumu ya Ayuda.” (Mateyu 2:2) Mochenjera, Herode anauza okhulupirira nyenyeziwa kuti adzamuuze malo enieni omwe am’peze mwanayo. Iye anawanamiza kuti nayenso akufuna akalambire mwanayo. Kenako nyenyezi ija inawalondolera kunyumba ya Yosefe ndi Mariya. Akanakhala kuti Mulungu sanalowererepo, zimene okhulupirira nyenyeziwa anachitazi zikanachititsa kuti mwanayo aphedwe. Mwamwayi, Mulungu analowererapo. Okhulupirira nyenyeziwo sanakamuuze Herode kumene anapeza mwanayo ndipo zimenezi zinam’kwiyitsa kwambiri moti analamula kuti ana onse a ku Betelehemu ndi madera ozungulira, kuyambira azaka ziwiri kutsika m’munsi, aphedwe.​—Mateyu 2:16.

Nthawi ina Yehova ananena kuti Yesu ndi ‘Mwana wake wokondedwa, amene amakondwera naye.’ (Mateyu 3:17) Ndiye kodi Yehova, yemwe ndi Atate wa Yesu wachilungamo komanso wachikondi, akanatuma okhulupirira nyenyezi amene sankamulambira komanso ankachita zinthu zimene zinali zoletsedwa m’Chilamulo cha Mulungu? (Deuteronomo 18:10) Kodi iye akanagwiritsa ntchito nyenyezi kuti iwatsogolere anthuwa kwa Herode, yemwe anali woopsa komanso wankhanza kwambiri, n’kukamuuza uthenga umene ungam’kwiyitse kenako n’kuwatsogoleranso pamalo amene mwana wake anali?

Tiyerekeze kuti mkulu wa asilikali watumiza msilikali amene amamukonda kwambiri kuti akagwire ntchito inayake yovuta m’dera limene muli adani awo. Kodi mkulu wa asilikaliyo angaulule kwa adaniwo malo amene msilikaliyo ali? N’zodziwikiratu kuti sangachite zimenezo. Mofanana ndi zimenezi, Yehova anatumiza Mwana wake kubwera m’dziko loopsali. Kodi Iye akanaululira Mfumu Herode komwe Mwana wake anali, akudziwa kuti pa nthawiyi Mwana wakeyo sakanatha kudziteteza? Yehova sakanachita zimenezo.

Ndiyeno kodi ndani anatumiza nyenyezi ija? Mwachidziwikire, amene anatumiza nyenyeziyi ankafunitsitsa kuti Yesu afe n’cholinga choti asakule n’kudzagwira ntchito imene anabwerera padziko lapansi. Munthu ameneyu amasocheretsanso anthu ndipo amalimbikitsa bodza, chiwawa komanso kupha anthu. Yesu anaulula kuti munthu ameneyu ndi Satana Mdyerekezi, yemwe ndi “wabodza komanso tate wake wa bodza.” Iyenso ndi “wopha anthu chiyambire kupanduka kwake.”​—Yohane 8:44.