Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusakhulupirika Ndi Chizindikiro cha Masiku Otsiriza

Kusakhulupirika Ndi Chizindikiro cha Masiku Otsiriza

Kusakhulupirika Ndi Chizindikiro cha Masiku Otsiriza

‘Tinakhala okhulupirika, olungama, ndi opanda chifukwa chotinenezera.’​—1 ATES. 2:10.

PEZANI MFUNDO ZIKULUZIKULU IZI:

Kodi tikuphunzira chiyani pa kusakhulupirika kwa Delila, Abisalomu ndi Yudasi Isikariyoti?

Kodi tingatsanzire bwanji kukhulupirika kwa Yonatani ndi Petulo?

Kodi tingatani kuti tikhalebe okhulupirika mu ukwati komanso kwa Yehova?

1-3. (a) Kodi chizindikiro china choopsa cha masiku otsiriza n’chiyani? (b) Kodi tikambirana mafunso atatu ati?

KODI Delila, Abisalomu ndiponso Yudasi Isikariyoti amafanana pa nkhani iti? Onse anali osakhulupirika. Woweruza Samisoni ankakonda Delila koma iye sanakhulupirike kwa Samisoni. Abisalomu sanakhulupirike kwa Mfumu Davide yemwe anali abambo ake. Yudasi sanakhulupirike kwa Ambuye wake, Khristu Yesu. Zochita za anthu onsewa zinabweretsa mavuto aakulu kwa anzawo. Koma n’chifukwa chiyani tiyenera kukambirana nkhani imeneyi?

2 Wolemba mabuku wina ananena kuti kusakhulupirika ndi limodzi mwa mavuto ofala kwambiri masiku ano. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa popereka chizindikiro cha “mapeto a nthawi ino,” Yesu ananena kuti: “Anthu ambiri . . . adzaperekana.” (Mat. 24:3, 10) Pa lembali mawu oti ‘kupereka’ akunena za “kupereka munthu wina m’manja mwa adani m’njira yachinyengo.” Kufala kwa kusakhulupirika kumeneko kukusonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’ Paulo ananeneratu kuti m’masiku otsiriza anthu adzakhala “osakhulupirika” ndiponso “achiwembu.” (2 Tim. 3:1, 2, 4) Ngakhale kuti olemba mabuku ndi mafilimu amaonetsa zochita za anthu osakhulupirika ngati zosangalatsa, zinthu zoterezi zikachitikadi zimapweteka ena ndiponso kubweretsa mavuto. Kunena zoona, kusakhulupirika ndi chizindikiro choopsa cha masiku otsiriza.

3 Kodi tingaphunzire chiyani kwa anthu a m’Baibulo omwe anakhala osakhulupirika? Kodi ndi zitsanzo ziti za anthu amene anakhala okhulupirika kwa anzawo zimene tiyenera kutengera? Nanga tiyenera kukhalabe okhulupirika kwa ndani? Tiyeni tikambirane.

ZITSANZO ZAKALE ZOTICHENJEZA

4. Kodi Delila anapereka bwanji Samisoni ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zinali zoipa kwambiri?

4 Chitsanzo choyamba ndi cha Delila, mzimayi wachinyengo amene Woweruza Samisoni ankamukonda. Samisoni ankafunitsitsa kutsogolera anthu a Mulungu pa nkhondo yomenyana ndi Afilisiti. Olamulira asanu a Afilisiti ayenera kuti ankadziwa zoti Delila sankakonda kwenikweni Samisoni choncho anamulonjeza kuti amupatsa ndalama zambiri akawauza chinsinsi cha mphamvu zake zapadera. Iwo anachita zimenezi kuti aphe Samisoni. Chifukwa cha dyera, Delila anavomera koma analephera maulendo atatu kudziwa chinsinsi cha mphamvu zake. Choncho anapitiriza kumupanikiza “ndi mawu ake mosalekeza, ndi kum’chonderera” mpaka Samisoni anafika “potopa nazo kwambiri.” Ndiyeno anamuuza kuti sanametepo tsitsi lake moti atangometa, mphamvu zake zikhoza kuthera pomwepo. * Delila atadziwa zimenezi, anaitana munthu wina kuti amumete tsitsilo pamene ankagona pamiyendo pake. Kenako anam’pereka kwa adani ake kuti athane naye. (Ower. 16:4, 5, 15-21) Zimene iye anachitazi zinali zoipa kwambiri. Chifukwa cha dyera, Delila anapereka Samisoni yemwe ankamukonda.

5. (a) Kodi Abisalomu anasonyeza bwanji kusakhulupirika kwa Davide ndipo izi zikusonyeza kuti anali munthu wotani? (b) Kodi Davide anamva bwanji Ahitofeli atalowa nawo m’chiwembucho?

5 Tsopano tikambirane chitsanzo cha Abisalomu yemwe analinso wosakhulupirika. Chifukwa chofuna kwambiri kukhala wolamulira, iye anafunitsitsa kulanda ufumu wa Davide, yemwe anali abambo ake. Choyamba Abisalomu ‘anakopa mitima ya anthu a mu Isiraeli.’ Iye ankanamizira kuti ankawakonda n’kumawalonjeza zinthu zabodza. Ankawakumbatira ndi kuwapsompsona ngati kuti amawakonda. (2 Sam. 15:2-6) Abisalomu anakopa ngakhale Ahitofeli, amene Davide ankamudalira kwambiri, n’kukhala naye m’chiwembucho. (2 Sam. 15:31) Pa Salimo 3 ndi 55, Davide anafotokoza mmene izi zinamupwetekera. (Sal. 3:1-8; werengani Salimo 55:12-14.) Abisalomu anakonzera chiwembu mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Zimenezi zinasonyeza kuti sankalemekeza Mulungu ndipo sankaona kuti Yehova ndi woyenera kusankha mfumu. (1 Mbiri 28:5) Koma chiwembu chake chinalephereka ndipo Davide anapitiriza kulamulira monga wodzozedwa wa Yehova.

6. Kodi Yudasi anapereka bwanji Yesu ndipo anthu akamva dzina loti Yudasi amaganizira za chiyani?

6 Ndiyeno tikambirane zimene Yudasi Isikariyoti anachitira Khristu. Pa Pasika womaliza amene Yesu anachita limodzi ndi atumwi ake 12, iye anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Mmodzi wa inu andipereka.” (Mat. 26:21) Nthawi ina usiku womwewo, Yesu ali m’munda wa Getsemane anauza Petulo, Yakobo, ndi Yohane kuti: “Onani! Wondipereka uja ali pafupi.” Nthawi yomweyo, Yudasi anafika limodzi ndi achiwembu anzake ndipo “analunjika kwa Yesu n’kunena kuti: ‘Mtendere ukhale nanu Rabi!’ Ndipo anam’psompsona.” (Mat. 26:46-50; Luka 22:47, 52) Yudasi ‘anapereka munthu wolungama’ kwa adani ake. Kodi Yudasi wadyerayo anachita zimenezi kuti alandire ndalama zingati? Eti ndalama 30 zasiliva. (Mat. 27:3-5) Kuyambira nthawi imeneyi, anthu akamva dzina loti Yudasi amangoganizira za munthu wosakhulupirika, makamaka amene amanamizira kuti amakonda mnzake koma n’kumupereka.

7. Kodi taphunzira chiyani pa zimene anachita (a) Abisalomu ndi Yudasi? (b) Delila?

7 Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo zotichenjeza zimenezi? Abisalomu ndi Yudasi anafa mochititsa manyazi chifukwa chokonzera chiwembu odzozedwa a Yehova. (2 Sam. 18:9, 14-17; Mac. 1:18-20) Anthu akamvanso dzina loti Delila amangoganizira za munthu wosakhulupirika ndiponso wonamizira kukonda wina. (Sal. 119:158) Tiyeni tipeweretu mtima wofuna kutchuka komanso dyera chifukwa zidzasokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Zitsanzo zimenezi zatichenjeza mwamphamvu kuopsa kwa kusakhulupirika.

TENGERANI CHITSANZO CHA ANTHU OKHULUPIRIKA

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani Yonatani analonjeza kukhala wokhulupirika kwa Davide? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yonatani?

8 Koma Baibulo limafotokozanso za anthu ambiri amene anakhala okhulupirika. Tiyeni tikambirane zitsanzo ziwiri n’kuona zimene tikuphunzirapo. Tiyamba ndi munthu amene anakhala wokhulupirika kwa Davide. Yonatani anali mwana wamwamuna woyamba kubadwa wa Mfumu Sauli. Choncho iye ndi amene ankayembekezera kulowa ufumu wa Isiraeli. Koma Yehova anasankha Davide kuti adzakhale mfumu yotsatira. Yonatani analemekeza zimene Mulungu anasankha ndipo sankachitira nsanje Davide. M’malomwake Yonatani anayamba ‘kugwirizana kwambiri ndi Davide’ ndipo anamulonjeza kuti adzakhalabe wokhulupirika kwa iye. Iye ankalemekeza Davide monga wodzozedwa wa Mulungu mpaka anamupatsa zovala zake, lupanga lake, uta ndiponso lamba wake. (1 Sam. 18:1-4) Yonatani anachita zonse zimene akanatha kuti alimbikitse Davide. Iye anaika moyo wake pa ngozi pofuna kuteteza Davide kuti Sauli asamuphe. Mokhulupirika, Yonatani anauza Davide kuti: “Iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli, ndipo ine ndidzakhala wachiwiri kwa iwe.” (1 Sam. 20:30-34; 23:16, 17) M’pake kuti Yonatani atamwalira, Davide anaimba nyimbo yosonyeza kuti ankakonda Yonatani ndipo akumva chisoni chachikulu.​—2 Sam. 1:17, 26.

9 Yonatani ankadziwiratu woyenera kumumvera. Iye ankagonjera Yehova monga Wolamulira ndipo anakhala wokhulupirika kwa Davide monga wodzozedwa wa Mulungu. Masiku anonso, zikhoza kutheka kuti ife sitinapatsidwe udindo wapadera mu mpingo koma tiyenera kukhala okhulupirika kwa abale amene aikidwa kuti azitsogolera pakati pathu.​—1 Ates. 5:12, 13; Aheb. 13:17, 24.

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani Petulo anakhalabe wokhulupirika kwa Yesu? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Petulo?

10 Mtumwi Petulo ndi chitsanzo china chabwino pa nkhani ya kukhulupirika. Iye analumbira kuti sadzasiya Yesu. Pa nthawi ina Khristu anagwiritsa ntchito fanizo potsindika kufunika kokhulupirira nsembe ya thupi ndi magazi ake yomwe anali atangotsala pang’ono kupereka. Ophunzira ake ambiri anaona kuti mawu amenewa ndi ozunguza ndipo anamusiya. (Yoh. 6:53-60, 66) Ndiyeno Yesu anafunsa atumwi ake 12 aja kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” Apa Petulo anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha. Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera wa Mulungu.” (Yoh. 6:67-69) Kodi pa nthawiyi Petulo anali atamvetsa zonse zimene Yesu anafotokoza zokhudza nsembe imene ankafuna kupereka? Zikuoneka kuti ayi. Ngakhale zinali choncho, Petulo anatsimikiza mtima kukhalabe wokhulupirika kwa Mwana wodzozedwa wa Mulungu.

11 Petulo sanaganize kuti mwina Yesu sakuona zinthu moyenera ndipo pakapita nthawi, adzasintha zimene wanena. M’malomwake anali wodzichepetsa ndipo anadziwa kuti Yesu ali ndi “mawu a moyo wosatha.” Nanga ifeyo timatani tikamva mfundo inayake imene “mtumiki woyang’anira nyumba wokhulupirika” wafalitsa m’mabuku athu yomwe sitikuimvetsa kapena sikugwirizana ndi zimene timaganiza? Tiyenera kuyesetsa kuti tiimvetse mfundoyo osati kumangoyembekezera kuti zinthu zisinthe mogwirizana ndi maganizo athu.​—Werengani Luka 12:42.

KHALANIBE WOKHULUPIRIKA KWA MWAMUNA KAPENA MKAZI WANU

12, 13. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu asakhulupirike m’banja ndipo n’chifukwa chiyani sitinganene kuti n’zosapeweka ngati anthu afika pa uchikulire?

12 Kusakhulupirika kwa mtundu uliwonse n’koipa kwambiri. Choncho sitiyenera kulola kuti khalidwe limeneli lisokoneze mtendere ndi umodzi wa Akhristu m’banja ndiponso mu mpingo. Tiyeni tikambirane mmene tingakhalire okhulupirika mu ukwati komanso kwa Mulungu.

13 Zimakhala zopweteka kwambiri ngati munthu wakhala wosakhulupirika n’kuchita chigololo. Munthu akachita chigololo ndiye kuti sanakhulupirike kwa mwamuna kapena mkazi wake. Munthu wosiyidwayo amavutika kwambiri mumtima. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu amene ankakondana asiyane? Choyamba n’chakuti anthuwo amasiya kukondana ngati poyamba. Katswiri wina wa maphunziro a zachikhalidwe, dzina lake Gabriella Turnaturi, ananena kuti izi zimachitika ngati anthu asiya kuchita zonse zimene angathe kuti alimbitse ubwenzi wawo. Izi zikhoza kuchitikira ngakhale anthu achikulire amene akhala m’banja kwa zaka zambiri. Mwachitsanzo, mwamuna wina wazaka 50 anasiya mkazi amene anakhala naye m’banja zaka 25 n’cholinga choti akhale ndi mkazi wina amene anakopeka naye. Ena amanena kuti izi n’zimene zimachitika munthu akafika zaka zimenezi. Koma zoona zake n’zakuti uku n’kusakhulupirika basi ndipo palibe chifukwa chonenera kuti n’zosapeweka. *

14. (a) Kodi Yehova amamva bwanji akaona anthu osakhulupirika m’banja? (b) Kodi Yesu ananena chiyani pa nkhani ya kukhulupirika mu ukwati?

14 Kodi Yehova amamva bwanji akaona anthu akuthetsa banja pa zifukwa zosagwirizana ndi Malemba? Mulungu wathu ‘amadana ndi zoti anthu azithetsa mabanja.’ Iye ananena mawu amphamvu kwambiri otsutsa anthu amene amazunza ndiponso kusiya mwamuna kapena mkazi wawo. (Werengani Malaki 2:13-16.) Maganizo a Yesu ndi ofanana kwambiri ndi a Atate ake pa nkhani imeneyi. Iye anaphunzitsa kuti munthu sangasiye mwamuna kapena mkazi wake wosalakwa n’kumaganiza kuti palibe vuto.​—Werengani Mateyu 19:3-6, 9.

15. Kodi anthu amene ali m’banja angatani kuti akhalebe okhulupirika?

15 Kodi anthu amene ali m’banja angatani kuti akhalebe okhulupirika? Mawu a Mulungu amati: “Usangalale ndi mkazi [kapena mwamuna] wapaunyamata wako.” Amanenanso kuti: “Sangalala ndi moyo limodzi ndi mkazi [kapena mwamuna] wako amene umamukonda.” (Miy. 5:18; Mlal. 9:9) Pamene akukula, anthu okwatirana ayenera kuchita zonse zimene angathe kuti azikondana ndiponso kusamalirana kwambiri. Izi zikutanthauza kuti aziderana nkhawa, kukomerana mtima ndiponso azipeza nthawi yocheza limodzi. Ayenera kuganizira mmene angatetezere ukwati wawo ndiponso ubwenzi wawo ndi Yehova. Kuti izi zitheke, iwo ayenera kuphunzira Baibulo limodzi, kuyendera limodzi mu utumiki ndiponso kupemphera limodzi kuti Yehova awadalitse.

KHALANIBE OKHULUPIRIKA KWA YEHOVA

16, 17. (a) Kodi kukhala okhulupirika kwa Mulungu kungayesedwe bwanji m’banja ndiponso mu mpingo? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza ubwino womvera lamulo la Mulungu lakuti tisamayanjane ndi achibale amene achotsedwa.

16 Pali Akhristu ena amene anachita machimo akuluakulu ndipo anadzudzulidwa “mwamphamvu, kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba.” (Tito 1:13) Koma anthu ena amachita zinthu zoyenera kuchotsedwa nazo mu mpingo. “Anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilango” choterechi amadzakhalanso olimba mwauzimu. (Aheb. 12:11) Bwanji ngati wachibale wathu kapena mnzathu wapamtima wachotsedwa? Apa tiyenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu osati munthuyo. Yehova amachita nafe chidwi kuti aone ngati tikumvera lamulo lake lakuti tisamayanjane ndi munthu aliyense amene wachotsedwa.​—Werengani 1 Akorinto 5:11-13.

17 Tiyeni tione chitsanzo chimodzi chosonyeza ubwino wotsatira lamulo la Yehova lakuti tisamayanjane ndi achibale amene achotsedwa. Mnyamata wina anachotsedwa n’kukhala kunja kwa zaka zoposa 10. Pa nthawi yonseyi, bambo ake, mayi ake ndiponso azichimwene ake anayi ‘analeka kuyanjana’ naye. Nthawi zina, iye ankayesetsa kuti azichita nawo zinthu zina koma chosangalatsa n’chakuti palibe ngakhale mmodzi amene analolera zimenezo. Atabwezeretsedwa, iye ananena kuti nthawi zonse ankalakalaka kucheza ndi azibale akewo makamaka usiku akakhala yekha. Koma ananena kuti iwo akanayesa kucheza naye, ngakhale pang’ono pokha, iye sakanadandaula. Koma poti iwo sanayerekeze n’komwe kulankhula naye, iye ankalakalaka kwambiri kucheza nawo ndipo ichi ndi chimodzi mwa zinthu zimene zinamulimbikitsa kuti akonze ubwenzi wake ndi Yehova. Muyenera kuganizira zimenezi pa nthawi iliyonse imene mukuyesedwa kuti muyambe kucheza ndi wachibale amene wachotsedwa.

18. Popeza takambirana kuopsa kwa kusakhulupirika ndiponso ubwino wa kukhulupirika, inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani?

18 Kusakhulupirika n’kofala kwambiri m’dzikoli. Koma mu mpingo wachikhristu muli zitsanzo za anthu okhulupirika zofunika kutengera. Moyo wawo umasonyeza kuti iwo ndi ‘okhulupirika, olungama, ndi opanda chifukwa chowanenezera.’ (1 Ates. 2:10) Tiyeni tonse tikhalebe okhulupirika kwa Mulungu ndiponso kwa anzathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Sikuti mphamvu zake zinkachokera m’tsitsi lenilenilo koma tsitsilo linkaimira ubwenzi wake wapadera ndi Yehova monga Mnaziri. Ubwenziwu ndi umene unachititsa kuti Samisoni akhale ndi mphamvu.

^ ndime 13 Kuti mumve zambiri pa nkhani imeneyi, onani nkhani yakuti “Zimene Mungachite Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Ali Wosakhulupirika,” mu Nsanja ya Olonda ya June  15, 2010, tsamba 29 mpaka 32.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Ngakhale kuti ena anakana Mwana wodzozedwa wa Mulungu, Petulo anakhala wokhulupirika kwa iye