Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akhristu Ayenera Kulowerera Ndale?

Kodi Akhristu Ayenera Kulowerera Ndale?

Kodi Akhristu Ayenera Kulowerera Ndale?

AKHRISTU oona salowerera nawo ndale. Iwo amachita zimenezi potsatira chitsanzo cha Yesu. Iye anati: “Ine sindili mbali ya dziko.” Ponena za otsatira ake, iye anati: “Simuli mbali ya dzikoli.” (Yohane 15:19; 17:14) Tiyeni tione zifukwa zina zimene Akhristu sayenera kulowerera ndale.

1. Ulamuliro wa anthu ndi woperewera. Baibulo limanena kuti anthu sangathe ndiponso alibe ufulu wodzilamulira. Mneneri Yeremiya anati: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”​—Yeremiya 10:23.

Mofanana ndi mmene zilili kuti anthufe sitinalengedwe mwanjira yoti tizitha kuuluka, sitinalengedwenso m’njira yoti tizidzilamulira tokha. Wolemba mbiri yakale wina, dzina lake David Fromkin, analemba zosonyeza kuti maboma a anthu ndi operewera. Iye anati: “Maboma amapangidwa ndi anthu, choncho sangakwanitse kuchita zonse bwinobwino ndipo tsogolo lawo n’losatsimikizirika. Boma la anthu likhoza kukhala ndi mphamvu zinazake, komabe mphamvu zake zimakhala zochepa.” (The Question of Government) N’chifukwa chake Baibulo limatichenjeza kuti tisamakhulupirire anthu.​—Salimo 146:3.

2. Makamu a mizimu yoipa ndi amene amayendetsa zochitika za padzikoli. Pamene Satana anam’patsa Yesu mwayi wokhala wolamulira wa dziko lonse, Yesu sanatsutse zoti Satanayo ali ndi mphamvu yopereka maulamulirowo kwa wina. Ndipotu patapita nthawi, Yesu anatchula Satana kuti ndi “wolamulira wa dziko.” Komanso nthawi ina mtumwi Paulo anatchula Satana kuti ndi “mulungu wa nthawi ino.” (Yohane 14:30; 2 Akorinto 4:4) Iye analemberanso Akhristu anzake kuti: “Sitikulimbana ndi anthu . . . koma ndi maboma, maulamuliro, olamulira dziko a mdimawu, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aefeso 6:12) Ngakhale kuti anthu ambiri samadziwa, kwenikweni mizimu yoipa ndi imene ikulamulira dziko lapansili. Kodi kudziwa mfundo imeneyi kuyenera kukhudza bwanji mmene mumaonera nkhani zandale?

Taganizirani chitsanzo ichi: Mofanana ndi mmene mabwato ang’onoang’ono amakankhidwira ndi mafunde amphamvu, maboma a anthu amayendetsedwa ndi mizimu yoipa imene ndi yamphamvu. Ndiye monga mmene okwera mabwato amene akukankhidwa ndi mafunde aja sangathe kuletsa mafunde amphamvuwo, olamulira andale sangathe kuchita zinthu motsutsana ndi zimene mizimu yoipayo ikufuna. Cholinga cha mizimu imeneyi ndi kusokonezeratu anthu onse komanso kuchititsa ‘tsoka padziko lapansi.’ (Chivumbulutso 12:12) Choncho Yehova Mulungu yekha ndi amene angathe kukonza zinthu chifukwa iyeyo ndi wamphamvu kuposa Satana ndi ziwanda zake.​—Salimo 83:18; Yeremiya 10:7, 10.

3. Akhristu oona amatumikira Ufumu wa Mulungu wokha. Yesu ndi ophunzira ake ankadziwa kuti pa nthawi yake yoyenera, Mulungu adzakhazikitsa boma lakumwamba limene lidzalamulire dziko lonse. Baibulo limatchula boma limeneli kuti ndi Ufumu wa Mulungu ndipo limanena kuti Yesu Khristu ndi amene anasankhidwa kukhala Mfumu yake. (Chivumbulutso 11:15) Popeza Ufumu umenewu udzakhudza anthu onse, mfundo yaikulu ya zimene Yesu ankaphunzitsa inali yonena za “uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Iye anaphunzitsanso ophunzira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere.” Kodi n’chifukwa chiyani anawauza kuti azipemphera kuti ufumuwo ubwere? Chifukwa Ufumu umenewu ukamadzalamulira, chifuniro cha Mulungu chidzachitika kumwamba komanso padziko lapansi.​—Mateyu 6:9, 10.

Nanga n’chiyani chidzachitikire maboma a anthu? Baibulo limayankha kuti maboma “a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzawonongedwa. (Chivumbulutso 16:14; 19:19-21) Choncho, munthu amene amakhulupirira kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uchotsa maboma onse a anthu, sangatenge nawo mbali mu zochitika zandale. Ndipotu munthu amene amachirikiza maboma a anthu amakhala akutsutsana ndi Mulungu.

Popeza Akhristu salowerera nawo ndale, kodi zikutanthauza kuti iwo alibe chidwi chothandiza anthu a m’dera lawo? Yankho la funso limeneli lili mu nkhani yotsatirayi.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Mboni za Yehova zimayesetsa kulengeza Ufumu wa Mulungu, m’malo molowerera nkhani zandale