Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yandikirani Mulungu

‘Mudzandiweramira Kuti Mundithandize’

‘Mudzandiweramira Kuti Mundithandize’

KUDZICHEPETSA ndi khalidwe losiririka. Nthawi zonse timasangalala kukhala pa ubwenzi ndi anthu omwe ndi odzichepetsa. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti masiku ano n’zovuta kupeza anthu amene ndi odzichepetsadi, makamaka ngati anthuwo ali ndi udindo winawake. Nanga bwanji Yehova Mulungu, yemwe ndi wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse? Kodi iye ndi wodzichepetsa? Tiyeni tikambirane mawu a mneneri Yeremiya opezeka palemba la Maliro 3:20, 21.​—Werengani.

Yeremiya ndi amene analemba buku la Maliro ndipo pa nthawiyi n’kuti zinthu zisali bwino pakati pa Aisiraeli. Mneneriyu anali ali ndi chisoni chachikulu chifukwa choona kuti mzinda wa Yerusalemu umene ankaukonda kwambiri wawonongedwa ndi Ababulo. Ngakhale kuti iye anali ndi chisoni, ankadziwa kuti chilango chimene Yehova anapereka kwa Aisiraeli chinali choyenera chifukwa cha zoipa zimene iwo anachita. Koma kodi Yeremiya analibe chiyembekezo? Kodi iye ankaona kuti Yehova ndi wouma mtima moti sangaone anthu amene alapa n’kuwapulumutsa? Onani zimene Yeremiya analankhula m’malo mwa Aisiraeli anzake.

Ngakhale kuti pa nthawiyi Aisiraeli ambiri anali ndi chisoni, Yeremiya anali ndi chiyembekezo. Iye anafuulira Yehova kuti: “Ndithu mudzandikumbukira ndi kundiweramira kuti mundithandize.” (Vesi 20) Yeremiya sankakayikira kuti Yehova amuthandiza chifukwa ankadziwa kuti iye sangamuiwale komanso sangaiwale anthu ake amene alapa. Ndiyeno kodi Mulungu wamphamvuyonse anachita chiyani?​—Chivumbulutso 15:3.

Yeremiya ankakhulupirira kuti Yehova ‘adzawerama’ kuti athandize anthu amene alapadi kuchokera pansi pa mtima. Baibulo lina linamasulira vesi limeneli kuti: “Mundikumbukire ndipo munyonyomale kuti mundithandize.” Mawu amenewa akutithandiza kuona kuti Yehova ndi Mulungu wokoma mtima komanso wachikondi. Pamenepa Yeremiya ankayembekezera kuti Yehova, yemwe ndi “Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi,” anyonyomala kuti athandize anthu ake kusiya njira zawo zoipa ndi kukhalanso naye pa ubwenzi. (Salimo 83:18) Chifukwa cha chiyembekezo chimenechi, Yeremiya anapeza chitonthozo pa ululu womwe ankamva mu mtima mwake. Mneneri wokhulupirikayu anatsimikiza mtima kuyembekezera mpaka nthawi ya Yehova yoti apulumutse anthu ake itakwana.​—Vesi 21.

Mawu amene Yeremiya analembawa akutiphunzitsa zinthu ziwiri zokhudza Yehova. Choyamba, tikuphunzira kuti Yehova ndi wodzichepetsa. (Salimo 18:35) Ngakhale kuti iye ali ndi “mphamvu zambiri,” amadzichepetsa n’cholinga chakuti atithandize tikakumana ndi mavuto. (Yobu 37:23; Salimo 113:5-7) Kodi mfundo imeneyi siyolimbikitsa? Chachiwiri, Yehova ndi wachifundo moti ndi ‘wokonzeka kukhululukira’ anthu ochimwa amene alapa ndipo iye amayambiranso kuwakonda. (Salimo 86:5) Makhalidwe awiri amenewa, kudzichepetsa ndi chifundo, amayendera limodzi.

Ndifetu oyamikira kwambiri kuti Yehova ndi wosiyana ndi anthu ambiri audindo, omwe chifukwa cha kunyada amakhala ouma mtima komanso sakhudzidwa n’komwe anthu akamavutika. Kodi mukufuna kuphunzira za Mulungu wodzichepetsa ameneyu, yemwe ndi wokonzeka ‘kunyonyomala’ kuti athandize anthu ake akakumana ndi mavuto?

Mavesi amene mungawerenge mu June:

Yeremiya 51-52; Maliro 1-5Ezekieli 1-5

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Yehova ndi wofunitsitsa kuwerama kuti atithandize tikakhala pa mavuto