Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulendo Wosangalatsa Kwambiri

Ulendo Wosangalatsa Kwambiri

Kalata Yochokera ku Ireland

Ulendo Wosangalatsa Kwambiri

TSIKU lina makolo anga anandiuza kuti: “Iwetu ukufunika kuchita kanthu kena kuti usamangodandaula za mayeso. Bwanji tipite kukacheza kwa msuweni wako ku Ireland. Kumeneko tikakhalanso ndi mwayi wolalikira kwa anthu amene salalikidwa uthenga wabwino wa Ufumu kawirikawiri.”

Poyamba sindinagwirizane kwenikweni ndi maganizo amenewa. Pa nthawiyi ndinkaganizira kwambiri za mayeso amene ndinkafuna kulemba komanso ndinali ndi nkhawa chifukwa ndinali ndisanapiteko dziko lina kunja kwa England kapena kuyenda pa ndege. Pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 17 ndipo ndinkaganiza kuti poti ndakulira ku London, womwe ndi mzinda waukulu, sindingakwanitse kukhala m’tauni yaing’ono ya Skibbereen. Tauni imeneyi ili kum’mwera chakumadzulo kwa Ireland.

Koma panalibe chifukwa chodera nkhawa. Ndege yathu itangotera, ndinalikonda kwambiri dzikolo. Komabe titangoyamba ulendo wapagalimoto ndinayamba kugona chifukwa ulendowu tinanyamuka m’mawa kwambiri. Msewu umene tinadutsa unali waung’ono ndipo unali ndi khoma lomangidwa ndi miyala mbali zonse. Nthawi zina ndinkadzuka ndipo ndikaponya maso ndinkaona kuti deralo linali ndi miyala ndiponso mitengo patalipatali komabe ndinkaona kuti ndi lokongola.

Kutada, tinafika m’tauni ya Skibbereen ndipo tinasangalala kucheza komanso kulimbikitsana mwauzimu ndi msuweni wanga ndi banja lake omwe anasamukira ku Ireland kukathandiza pa ntchito yolalikira Ufumu. Tinkachita masewera okhudza nkhani zopezeka m’Baibulo. Tinalemba mayina a anthu otchulidwa m’Baibulo patimapepala n’kutiika m’jumbo. Ndiyeno aliyense ankatenga kapepala kamodzi m’jumbomo ndipo ankayesezera ndi manja nkhani zokhudza munthuyo koma osalankhula. Ndiyeno ena ankafunika kutchula dzina la munthuyo.

Tsiku lotsatira, ineyo, makolo anga, mchimwene wanga, msuwani wanga ndi mwamuna wake komanso banja lina tinanyamuka ulendo wopita pachilumba china chotchedwa Heir. Pachilumbachi pamakhala anthu osapitirira 30. Yesu ananena kuti uthenga wabwino uyenera kulalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Zimenezi n’zimene zinatichititsa kuti pa tsikuli tipite kukakambirana mfundo za m’Malemba ndi anthu a m’derali omwe ndi ochezeka komanso okonda kuchereza alendo. Tinasangalalanso kwambiri ndi malo okongola amene ali m’derali.

Pa tsikuli kunja kunalibe mitambo ndipo dzuwa linkawala kwambiri. Mphepo ikamawomba tinkamva kafungo kabwino ka maluwa owala komanso onunkhira bwino. Pakatikati pachilumbachi panali ngati dambo ndipo pa nthawiyi panali maluwa ambirimbiri. M’derali mulinso magombe amiyala momwe mumapezeka mbalame za m’madzi zooneka ngati abakha ndipo mbalamezi zinali m’zisa ndi ana ake. Kulikonse kumene ungayang’ane umaona zilumba zing’onozing’ono zomwe zili m’dera lotchedwa Roaringwater Bay ndipo zambiri mwa zilumbazi sipakhala anthu. Tinagoma kwambiri kuona zinthu zimenezi zomwe Yehova analenga.

Titabwerera ku Skibbereen, ndinasangalala kwambiri kucheza ndi anthu a mumpingo wa Mboni za Yehova wa kuderali ndipo ndinapanga mabwenzi ambiri abwino. Ndinasangalalanso kuchita zinthu zina zimene ndinali ndisanachitepo monga masewera opalasa bwato. Ndinasangalala kwambiri ndi masewera amenewa chifukwa ndinkatha kuona chilumba cha Ireland ndili m’madzi. Kenako tinapita kukapha nsomba zoti tidye pa chakudya chamadzulo, koma nthawi zina tinkapeza kuti nyama zinazake za m’madzi zagwira kale nsombazo. Tinayambitsa masewera athuathu amene tinkachita m’mbali mwa madzi komanso ndinkayeserera kuvina magule a m’dzikolo.

Tinalinso ndi nthawi yophunzirako zina ndi zina zokhudza tauni ya Skibbereen. Tinamva kuti m’chaka cha 1840, pamene ulimi wa mbatata ya kachewere sunachite bwino m’derali, anthu a m’tauniyi komanso madera ozungulira anakhudzidwa kwambiri ndi njala. Anthu ambirimbiri anafa ndi njala moti anthu pafupifupi 9,000 anaikidwa m’manda amodzi. Komabe tinalimbikitsidwa pokumbukira kuti posachedwapa, mu Ufumu wa Mulungu, sikudzakhalanso njala ndipo anthu ambiri amene anafawa adzakhalanso ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi.

Tinapita pa galimoto limodzi ndi a Mboni za Yehova a m’derali kukalalikira kwa anthu a m’gawo la mpingo wa kumaloku lomwe ndi lalikulu. Tinapita kwa anthu amene amafikiridwa mwa apo ndi apo. Tinadutsa mumsewu waung’ono komanso wotsetsereka kupita kunyumba zomwe zinamangidwa pamalo okwera kwambiri ndipo ukakhala pamalo amenewa umatha kuona bwinobwino Nyanja ya Irish. Kumenekunso tinapeza anthu ochezeka ndipo ankatilandira bwino kwambiri. Mofanana ndi mmene tinkachitira pachilumba cha Heir, tinkayamba ndi kuwafotokozera anthu kuti tangobwera kudzacheza m’derali ndipo tapatula nthawi kuti tikambirane nawo uthenga wosangalatsa wa m’Baibulo.

Amayi anga analalikira mayi wina amene anasangalala kulandira magazini athu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Patapita masiku angapo tinakumananso ndi mayiyu ndipo anatiuza kuti anasangalala kuwerenga magaziniwo.

Mayiyu anatipempha kuti: “Chonde mudzabwerenso ndipo mudzandibweretsere magazini ena.” Tinamufotokozera kuti tinangobwera kudzacheza m’derali ndipo tinali titatsala pang’ono kubwerera kwathu. Komabe tinamuuza kuti tidzamutumizira munthu woti adzapitirize kuphunzira naye.

Iye anayankha kuti: “Chabwino, koma ngati mutadzabweranso dera lino, musadzalephere kudzandiona. Ndidzakulandirani ndi manja awiri chifukwa anthu a kuno sitiiwala munthu.”

Tsiku loti tinyamuka mawa, tinapita kunyanja ndi abale ndi alongo a mumpingo wa kumaloko. Tinasanja miyala n’kuyatsa moto pogwiritsa ntchito nkhuni zokokoloka ndi madzi ndipo tinawotcha nsomba zinazake zimene tinagwira m’miyala ya m’nyanjayo. Ngakhale kuti ndinakulira mumzinda waukulu, ndinasangalala kwambiri ndi zonse zimene zinachitika pa ulendowu.

Ndikaganizira zonse zimene zinachitika mlungu umenewu, ndimaona kuti umenewu unali ulendo wosangalatsa kwambiri pa maulendo onse amene ndinayendapo. Sikuti ndinangosangalala ndi zimene tinachita, koma ndinasangalalanso chifukwa chodziwa kuti Yehova ankasangalala ndi zimene tinkachitazo komanso zinathandiza kutamanda dzina lake. Ineyo pandekha ndimakonda kutumikira Mulungu, koma ukamachita zinthu ndi mabwenzi komanso achibale amene nawonso amakonda kutumikira Mulungu, umasangalala kwambiri. Nditafika kunyumba ndinayamikira kwambiri Yehova chifukwa chondipatsa mabwenzi abwino ambiri omwenso amakonda zinthu zauzimu. Ndinayamikiranso chifukwa cha zinthu zabwino zambiri zimene ndinaona pa ulendowu zimene sindidzaiwala mpaka kalekale.

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

An Post, Ireland