Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi n’chifukwa chiyani kudziwa mibadwo ya makolo kunali kofunika kwambiri kwa Ayuda?

Nkhani yokhudza mibadwo inali yofunika kwambiri chifukwa inkathandiza munthu kudziwa fuko lake komanso chibale pakati pa iyeyo ndi anthu a m’fuko lakelo. Kunali kofunikanso chifukwa kunkathandiza pogawa malo komanso kudziwa woyenera kulandira cholowa. Kudziwa mibadwo ya makolo awo kunali kofunikanso kwambiri kwa Ayuda chifukwa kunawathandiza kudziwa mzere wobadwira wa Mesiya amene Mulungu analonjeza. Ayuda ankadziwa bwino kuti Mesiya adzachokera m’fuko la Yuda, ku banja la Davide.​—Yohane 7:42.

Komanso malinga ndi zimene ananena katswiri wina wamaphunziro, dzina lake Joachim Jeremias, “ntchito ya ansembe ndi Alevi inali yochokera kwa makolo . . . choncho kunali kofunika kwambiri kuti mzere wa ku banja la ansembe usadetsedwe.” Azimayi achiisiraeli amene ankakwatiwa ku mabanja a ansembe ankafunika kupereka umboni wosonyeza mbadwo wa makolo awo n’cholinga choti mzere wa ku banja la ansembe “usaipitsidwe.” M’nthawi ya Nehemiya, mabanja onse a Alevi ankawaletsa kutumikira monga ansembe akakhala kuti ‘ayang’ana mayina awo m’kaundula, kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira, koma sanawapeze.’​—Nehemiya 7:61-65.

Kuwonjezera pamenepo, Chilamulo cha Mose chinkanena kuti “mwana wapathengo” komanso “Muamoni kapena Mmowabu asalowe mumpingo wa Yehova.” (Deuteronomo 23:2, 3) Jeremias anawonjezeranso kuti pa chifukwa chimenechi, “kuti munthu akhale ndi ufulu wochita zinthu, ankafunika kupereka umboni wa mzere wake wobadwira ndipo zimenezi zikutsimikizira kuti zimene tinapeza n’zoona . . . kuti Mwisiraeli aliyense ankadziwa azigogo ake ndipo ankatha kutchula fuko limene anachokera pa mafuko 12 a Aisiraeli.”

Kodi Ayuda ankapeza kuti mbiri ya mibadwo ya makolo awo nanga ankaisunga bwanji?

Mateyu ndi Luka, omwe analemba nawo Uthenga Wabwino, anafotokoza mwatsatanetsatane za mzere wobadwira wa makolo a Yesu. (Mateyu 1:1-16; Luka 3:23-38) Palinso mabuku ena amene ali ndi mbiri ya mibadwo ya anthu akale. Mwachitsanzo, buku lina linafotokoza zokhudza rabi wina wa m’nthawi ya Yesu, dzina lake Hillel, kuti: “Mu mpukutu wina wofotokoza mibadwo umene unapezeka ku Yerusalemu munalembedwa kuti Hillel anali mbadwa ya Davide.” (Jewish midrash) Komanso katswiri wina wachiyuda wolemba mbiri yakale, dzina lake Flavius Josephus, analemba m’buku lake lina kuti makolo ake akuchimuna anali akubanja la ansembe ndipo akatengera makolo ake akuchikazi iye anali “wa m’banja lachifumu.” Josephus ananena kuti anadziwa zimenezi chifukwa cha zimene “zinalembedwa m’kaundula.”​—The Life.

Josephus analemba m’buku lake lina kuti udindo wosunga mbiri ya mabanja a ansembe unkaperekedwa kwa “anthu a mbiri yabwino.” (Against Apion) Buku lina linanena kuti: “N’kutheka kuti udindo wosunga mabuku amenewa unkaperekedwa kwa munthu wapadera komanso zikuoneka kuti ku Yerusalemu kunakhazikitsidwa khothi loti liziona nkhani zokhudza mbiri ya mibadwo ya makolo.” (The Jewish Encyclopedia) Ayuda amene sanali a m’banja la ansembe ankakalembetsa kaundula m’mizinda yomwe bambo awo anabadwira. (Luka 2:1-5) Anthu amene analemba Mauthenga Abwino ayenera kuti anapeza mfundo zina kuchokera kumalo osungirako mabuku oterewa. Zikuonekanso kuti mabanja ankasunga okha zinthu zina zokhudza mbiri ya banja lawolo.