Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Anatsogoleredwa ndi Mzimu Woyera’

‘Anatsogoleredwa ndi Mzimu Woyera’

‘Anatsogoleredwa ndi Mzimu Woyera’

“Ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”​—2 PET. 1:21.

MFUNDO ZOYENERA KUZIGANIZIRA

Kodi Mulungu anagwiritsa ntchito bwanji mzimu woyera pouza anthu uthenga woti alembe m’Baibulo?

Perekani umboni wosonyeza kuti Baibulo n’lochokera kwa Mulungu.

Kodi muyenera kuchita chiyani tsiku lililonse kuti muziyamikirabe Mawu a Mulungu?

1. N’chifukwa chiyani Mawu a Mulungu ndi ofunika kwambiri kwa ife?

ANTHU ambiri padzikoli amadzifunsa kuti: Kodi anthufe tinachokera kuti? N’chifukwa chiyani tili ndi moyo? Kodi tili ndi tsogolo lotani? N’chifukwa chiyani dzikoli ladzaza ndi mavuto? Kodi n’chiyani chimachitika munthu akamwalira? Popanda Mawu a Mulungu, sitikanadziwa mayankho a mafunsowa ndiponso mafunso ena ofunika. Pakanapanda Malemba Opatulika, tikanangodalira kuphunzira zinthu pa zimene timakumana nazo pa moyo. Sitikanathanso kuona “chilamulo cha Yehova” mmene wamasalimo ankachionera.​—Werengani Salimo 19:7.

2. N’chiyani chingatithandize kuonabe kuti Baibulo ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu?

2 Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ena asiya kukonda choonadi cha m’Baibulo. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 2:4.) Iwo asiya kuyenda m’njira yosangalatsa Yehova. (Yes. 30:21) Tisalole kuti zimenezi zitichitikire. M’malomwake, tiziyesetsa kupitiriza kuyamikira mfundo za m’Baibulo. Baibulo ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mlengi wathu wachikondi. (Yak. 1:17) N’chiyani chingatithandize kuyamikira kwambiri “mawu a Mulungu”? Kuganizira mfundo yakuti anthu anachita kutsogoleredwa ndi Mulungu kuti alembe Baibulo kungatithandize. Tiziganiziranso zifukwa zambiri zosonyeza kuti Malemba anauziridwa ndi Mulungu. Kuganizira zimenezi kungatilimbikitse kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse ndiponso kutsatira malangizo ake.​—Aheb. 4:12.

KODI MZIMU WOYERA UNKAWATSOGOLERA BWANJI?

3. Kodi aneneri ndiponso olemba Baibulo ena anatsogoleredwa bwanji ndi mzimu woyera?

3 Amuna okwana 40 analemba Baibulo pa zaka 1,610, kuyambira mu 1513 B.C.E. kufika mu 98 C.E. Ena anali aneneri omwe ‘ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera.’ (Werengani 2 Petulo 1:20, 21.) Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti ‘kutsogoleredwa’ amatanthauza kunyamula chinthu n’kumayenda nacho. Mawuwa “akhoza kumasuliridwa m’njira zosiyanasiyana monga kusunthidwa, kuyendetsedwa kapena kulolera kutengedwa.” * Pa Machitidwe 27:15, mawuwa anagwiritsidwa ntchito kufotokoza ngalawa imene inkatengedwa ndi mphepo n’kumayendetsedwa. Aneneri ndiponso olemba Baibulo ena ‘ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera’ m’njira yakuti Mulungu ankawalankhula, kuwalimbikitsa kulemba komanso kuwatsogolera pogwiritsa ntchito mzimu wake. Choncho iwo ankalemba maganizo a Mulungu osati awo. Nthawi zina aneneri ndiponso olemba ena sankadziwa tanthauzo la zinthu zimene ankalosera kapena kulemba. (Dan. 12:8, 9) Ndithudi, “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu” ndipo mulibe maganizo a anthu.​—2 Tim. 3:16.

4-6. Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu kuti alembe uthenga wake m’Baibulo? Perekani chitsanzo.

4 Koma kodi mzimu woyera unkathandiza bwanji anthu kuti alembe m’Baibulo uthenga wa Mulungu? Kodi iwo ankauzidwa mawu enieni kapena ankangouzidwa mfundo zoti azilembe m’mawu awoawo? Kuti timvetse, tiyeni tiyerekezere zimene bwana amachita polemba kalata. Akafuna kuti ilembedwe m’mawu enaake, amalemba yekha kapena kuuza mlembi wake mawu enieni amene akufuna kuti alembedwewo. Mlembiyo akalemba bwanayo amaisainira. Koma nthawi zina bwana amangotchula mfundo zofunika m’kalatayo ndipo mlembi amailemba pogwiritsa ntchito mawu akeake. Kenako, bwanayo amawerenga kalatayo kuti aone zinthu zoti mlembiyo akonze. Pomaliza, bwanayo amaisainira ndipo wolandira kalatayo amaona kuti yachokera kwa bwanayo.

5 N’chimodzimodzinso ndi Baibulo. Mbali zina zinalembedwa “ndi chala cha Mulungu.” (Eks. 31:18) Nthawi zina, Yehova ankatchula mawu enieni oyenera kulembedwa pamene zinali zofunika kutero. Mwachitsanzo, pa Ekisodo 34:27 timawerenga kuti: “Yehova anauza Mose kuti: ‘Dzilembere mawuwa chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe ndi Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.’” Yehova anauzanso Yeremiya kuti: “Lemba m’buku mawu onse amene ndidzalankhula nawe.”​—Yer. 30:2.

6 Koma nthawi zambiri anthu sankauzidwa mawu enieni. M’malomwake, Yehova ankangowathandiza mozizwitsa kuti adziwe mfundo zofunika kulemba ndipo iwo ankazilemba m’mawu awoawo. Lemba la Mlaliki 12:10 limati: “Wosonkhanitsayo anafufuza mawu okoma ndipo analemba mawu olondola a choonadi.” Luka, yemwe analemba Uthenga Wabwino, anati: “Ndafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pa chiyambi, ndafunitsitsa kuti ndikulembereni mwatsatanetsatane.” (Luka 1:3) Mzimu wa Mulungu unathandiza kuti uthenga wake usasinthidwe ndi anthuwo, omwe anali opanda ungwiro.

7. Kodi kugwiritsa ntchito anthu polemba Baibulo kumasonyeza bwanji kuti Mulungu ndi wanzeru?

7 Mulungu anasonyeza kuti ndi wanzeru kwambiri pogwiritsa ntchito anthu kuti alembe Baibulo. Tikutero chifukwa chakuti mawu amathandiza anthu kumva uthenga komanso angathandize kuti uthengawo uwafike pamtima. Kodi chikanachitika n’chiyani ngati Yehova akanagwiritsa ntchito angelo kuti alembe Baibulo? Kodi akanafotokoza bwino zinthu zimene zimachitikira anthu monga mantha, chisoni ndiponso kukhumudwa? Polola kuti anthu opanda ungwiro alembe uthenga wake m’mawu awoawo, Mulungu anathandiza kuti uthenga wakewo uzitifika pamtima.

UMBONI WAKUTI BAIBULO LINACHOKERA KWA MULUNGU

8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo ndi losiyana ndi mabuku ena onse achipembedzo?

8 Pali maumboni ambirimbiri osonyeza kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu. Baibulo limatithandiza kumudziwa bwino Mulungu kuposa buku lina lililonse lachipembedzo. Mwachitsanzo, mabuku achipembedzo chachihindu amafotokoza za miyambo yachipembedzo, nzeru za anthu, nthano ndiponso malamulo okhudza makhalidwe. Nawonso mabuku ena a Abuda amangofotokoza malamulo amene ansembe ndiponso masisitere ayenera kutsatira. Mabuku ena amakhala ndi ziphunzitso zachibuda komanso mawu a munthu amene anayambitsa Chibudacho, dzina lake Buddha. Komatu Buddha sankadzitcha mulungu ndipo sankanena zambiri zokhudza Mulungu. Mabuku a chipembedzo cha Chikomfyushani amanena za mbiri yakale, malamulo okhudza makhalidwe, matsenga ndiponso nyimbo. Buku loyera la Asilamu limaphunzitsa kuti kuli Mulungu mmodzi amene amadziwa zonse ngakhale zam’tsogolo ndipo amalemberatu zochitika zonse. Koma silitchula dzina la Mulungu lakuti Yehova lomwe limapezeka maulendo masauzande angapo m’Baibulo.

9, 10. Kodi Baibulo limatiphunzitsa chiyani za Mulungu?

9 Mabuku ambiri achipembedzo safotokoza zambiri za Yehova Mulungu. Koma Baibulo limatithandiza kumudziwa bwino, kudziwa zochita zake ndiponso kudziwa makhalidwe ake. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ndi wamphamvu yonse, wanzeru zonse, wachilungamo ndiponso kuti amatikonda kwambiri. (Werengani Yohane 3:16; 1 Yohane 4:19.) Baibulo limatiuzanso kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Mac. 10:34, 35) Baibulo limapezeka m’zinenero zambiri ndipo izi zimasonyeza kuti iye alibe tsankho. Akatswiri azinenero amanena kuti padziko lapansi pali zinenero zoposa 6,700. Koma ndi zinenero 100 zokha zimene zimalankhulidwa ndi anthu ambiri padziko. Ngakhale zili choncho, Baibulo lathunthu kapena mbali yake lamasuliridwa m’zinenero zoposa 2,400. Pafupifupi munthu aliyense padzikoli akhoza kupeza Baibulo lathunthu kapena mbali zake zina.

10 Yesu anati: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.” (Yoh. 5:17) Yehova ndi “Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.” Choncho tangoganizani zinthu zonse zimene iye wachita. (Sal. 90:2) Baibulo lokha limatiuza zimene Mulungu wachita m’mbuyomu, zimene akuchita panopa komanso zimene adzachite m’tsogolo. Malemba amatiphunzitsa zimene Mulungu amakonda ndi zimene amadana nazo. Amanenanso zimene tingachite kuti timuyandikire. (Yak. 4:8) Tisalole kuti chinthu china chilichonse chitilepheretse kuyandikana naye.

11. Kodi m’Baibulo timapezamo malangizo anzeru ati?

11 Baibulo lili ndi nzeru zothandiza pa nkhani zosiyanasiyana ndipo uwu ndi umboni wina wosonyeza kuti ndi lochokera kwa Mulungu osati anthu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndani akudziwa maganizo a Yehova kuti amulangize?” (1 Akor. 2:16) Lemba limeneli likuchokera pa mawu a mneneri Yesaya amene anafunsa kuti: “Ndani anayezapo mzimu wa Yehova? Ndi munthu uti amene angamupatse malangizo kapena kumuphunzitsa kanthu?” (Yes. 40:13) Yankho la mafunso onsewa n’lakuti palibe. N’chifukwa chake kutsatira malangizo a m’Baibulo n’kothandiza kwambiri kaya pa nkhani ya ukwati, kulera ana, zosangalatsa, anthu ocheza nawo, khama, kuona mtima kapena mmene tingapewere makhalidwe oipa. N’zosatheka kupeza malangizo olakwika m’Baibulo. Koma anthu alibe nzeru zokwanira zoti n’kupereka malangizo othandiza nthawi zonse. (Yer. 10:23) Malangizo awo amayenera kusinthidwa nthawi zonse chifukwa chozindikira kuti amene anapereka poyamba anali olakwika. Baibulo limati: “Maganizo a anthu ali ngati mpweya wotuluka m’mphuno.”​—Sal. 94:11.

12. Kodi anthu anachita zotani pofuna kuwononga Baibulo?

12 Anthu ambiri m’mbuyomu ankayesetsa kuti awononge uthenga wa m’Baibulo. Kulephera kwawo ndi umboni wina wotsimikizira kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu. M’chaka cha 168 B.C.E., mfumu ina ya ku Siriya, dzina lake Antiyokasi Wachinayi, inayesa kufufuza mabuku onse a Chilamulo n’cholinga choti aotchedwe. Mfumu ina yachiroma, dzina lake Diocletian, inalamula mu 303 C.E. kuti malo onse amene Akhristu ankasonkhana agwetsedwe ndiponso Mabaibulo awo aotchedwe. Anthu anawononga zinthu zimenezi kwa zaka 10. Kwa zaka mahandiredi ambiri, apapa anayesetsa kwambiri kuletsa kuti Baibulo limasuliridwe m’zinenero zina. Iwo anachita zimenezi chifukwa chakuti sankafuna kuti anthu aziphunzira Baibulo. Ngakhale kuti Satana ndi anthu ake anayesa kuwononga Baibulo, zimenezi sizinatheke ndipo lilipobe. Yehova sanalole kuti aliyense awononge mphatso imene iye anapereka kwa anthu.

UMBONI UMENE WATHANDIZA ANTHU AMBIRI KUKHULUPIRIRA

13. Perekani umboni wina wosonyeza kuti Baibulo ndi louziridwa.

13 Palinso umboni wina umene wathandiza anthu kukhulupirira kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, nkhani zake ndi zogwirizana, limanena zolondola pa nkhani zasayansi, maulosi ake anakwaniritsidwa ndipo olemba ake sankabisa zinthu. Baibulo limasintha anthu, nkhani zake zimagwirizana ndi mbiri yakale, ndiponso limapereka mayankho ogwira mtima a mafunso amene tawatchula m’ndime yoyamba. Tiyeni tikambirane zimene zinathandiza anthu ena kukhulupirira kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu.

14-16. (a) Kodi n’chiyani chinathandiza Msilamu, Mhindu ndiponso munthu wokayikira kuti kuli Mulungu kukhulupirira kuti Baibulo n’lochokera kwa Mulungu? (b) Kodi inuyo mumakonda kuuza anthu umboni uti wosonyeza kuti Baibulo n’lochokera kwa Mulungu?

14 Anwar * anabadwira m’banja lachisilamu m’dziko lina la ku Middle East. Nthawi ina atapita ku North America, a Mboni za Yehova anafika kunyumba kwake. Anwar anati: ‘Pa nthawi imeneyi, ndinkadana ndi zipembedzo zachikhristu chifukwa cha zinthu zoipa zimene zinachita m’mbuyomu. Koma ndinkakonda kuphunzira zinthu. Choncho ndinavomera kuphunzira Baibulo.’ Anwar atangoyamba kuphunzira, anabwerera kwawo ndipo sanakumanenso ndi a Mboni. Ndiyeno patapita zaka zambiri, anasamukira ku Ulaya ndipo anayambanso kuphunzira Baibulo. Iye ananena kuti: “Ndinayamba kukhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu nditaona kuti maulosi a m’Baibulo amakwaniritsidwa, nkhani za m’Malemba Opatulika zimagwirizana, mfundo zake sizisemphana ndiponso atumiki a Yehova amakondana.” Anwar anabatizidwa mu 1998.

15 Mtsikana wina wa zaka 16, dzina lake Asha, anakulira m’banja lachihindu. Iye anati: “Ndinkapemphera pokhapokha pamene ndinkapita kukachisi kapena pamene ndinkakumana ndi mavuto. Koma sindinkaganiza n’komwe za Mulungu pamene zinthu zinkandiyendera bwino.” Iye ananenanso kuti: “Tsiku lina a Mboni za Yehova atabwera kunyumba, moyo wanga unasinthiratu.” Asha anaphunzira Baibulo ndipo anayamba kudziwa Mulungu n’kukhala naye pa ubwenzi. N’chiyani chinamuthandiza kukhulupirira kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu? Iye anafotokoza kuti: “Baibulo linayankha mafunso anga onse. Linandithandiza kukhulupirira Mulungu popanda kumuona, kapena kuti popanda kupita kukachisi kukagwadira fano.”

16 Mtsikana wina dzina lake Paula anabadwira m’banja lachikatolika. Koma atakula, anayamba kukayikira zoti kuli Mulungu. Kenako chinthu china chinamuchitikira. Iye anati: “Ndinakumana ndi mnzanga wina yemwe ndinali ndisanaonane naye kwa miyezi yambiri. Nthawi imeneyi, anthu ambiri sankameta tsitsi ndipo ankakonda kusuta chamba. Koma mnyamatayo anali atasinthiratu moti anali atameta tsitsi lake bwinobwino ndipo anali wosangalala. Nditaona zimenezi, ndinamufunsa kuti: ‘Kodi watani? Unali kuti?’ Iye ananena kuti anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anayamba kundilalikira.” Paula ataona kuti choonadi cha m’Malemba ndi champhamvu moti chikhoza kuthandiza munthu wotereyu, anayamba kukhulupirira kuti Baibulo n’lochokeradi kwa Mulungu.

“MAWU ANU NDI NYALE YOUNIKIRA KUMAPAZI ANGA”

17. Kodi kuwerenga ndiponso kusinkhasinkha Mawu a Mulungu tsiku lililonse kungakuthandizeni bwanji?

17 Baibulo ndi mphatso yabwino kwambiri imene Yehova wapereka pogwiritsa ntchito mzimu woyera. Khalani ndi chizolowezi choliwerenga tsiku lililonse ndipo mudzayamba kulikonda kwambiri ndiponso kukonda Wolemba wake wamkulu. (Sal. 1:1, 2) Musanayambe kuliwerenga, muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimu wake ndiponso kukuthandizani kumvetsa zimene mukuwerenga. (Luka 11:13) M’Baibulo muli maganizo a Mulungu choncho mukamasinkhasinkha zimene mumawerenga, mumayamba kuona zinthu mmene Mulungu amazionera.

18. N’chifukwa chiyani mungakonde kuphunzirabe Baibulo?

18 Pitirizani kuphunzira choonadi ndipo muzitsatira zimene mukuphunzira. (Werengani Salimo 119:105.) Muziyang’ana m’Malemba mmene mungayang’anire pa galasi loonera nkhope. Mukaona zinthu zoyenera kusintha, muyenera kuzisintha. (Yak. 1:23-25) Muzigwiritsa ntchito Mawu a Mulungu monga lupanga kuti muteteze zimene mumakhulupirira ndiponso kuchotsa zikhulupiriro zonama mumtima mwa anthu ofatsa. (Aef. 6:17) Mukamachita zimenezi, muziyamikira kuti aneneri ndiponso anthu ena amene anagwiritsidwa ntchito kuti alembe Baibulo ‘anatsogoleredwa ndi mzimu woyera.’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Buku lakuti A Greek-English Lexicon of the New Testament and Other Early Christian Literature.

^ ndime 14 Mayina ena asinthidwa.

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 29]

Muziwerenga Baibulo tsiku lililonse ndipo mudzayamba kukonda kwambiri Wolemba wake wamkulu

[Chithunzi patsamba 26]

Anthu amaona kuti kalata yachokera kwa munthu amene waisainira