Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzifufuza “Nzeru Zoyendetsera Moyo” Wanu

Muzifufuza “Nzeru Zoyendetsera Moyo” Wanu

Muzifufuza “Nzeru Zoyendetsera Moyo” Wanu

Moyo wathu uli ngati ulendo wapanyanja. Ndipo nzeru za anthu n’zoperewera pothandiza munthu kuyenda bwino pa moyo wake. Anthu ambiri amakumana ndi mavuto pa moyo wawo ndipo amakhala ngati boti limene lasweka ndi mphepo yamkuntho. (Sal. 107:23, 27) N’chifukwa chiyani fanizo limeneli lili loyenera?

Kale, ulendo wapanyanja unkakhala woopsa kwambiri moti pankafunika munthu wodziwa bwino kuyendetsa boti. Munthu ankaphunzira luso limeneli kwa anthu odziwa bwino kuyendetsa maboti monga kwa munthu amene ankatsogolera pa ntchito yoyendetsa. (Mac. 27:9-11) M’zithunzi zakale, munthu wotsogolera pa ntchito yoyendetsa boti ankajambulidwa wamkulu kuposa ena pofuna kusonyeza kuti ntchito yake inali yofunika kwambiri. Kuti athe kuyenda bwino panyanja, anthu oyendetsa maboti ankaphunzitsidwa za nyenyezi, mphepo ndiponso zinthu zina zimene zikanawathandiza kuti asasochere. Pofotokoza za anthu ena oyendetsa boti, Baibulo limati anali “aluso” ndipo mawu amene anagwiritsidwa ntchito amatanthauza anzeru.​—Ezek. 27:8.

Masiku ano, moyo ungakhale wovuta kwambiri ndipo ungafanane ndi ulendo wapanyanja wakale. N’chiyani chingatithandize kuti tiyende bwino?

KODI TINGAPEZE BWANJI “NZERU ZOYENDETSERA MOYO” WATHU?

Popeza moyo uli ngati ulendo wapanyanja, mfundo ina ya m’Baibulo ingakhale yothandiza. Mfundo yake ndi yakuti: “Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka, ndipo munthu womvetsa zinthu ndi amene amapeza nzeru zoyendetsera moyo wake.” (Miy. 1:5, 6) Mawu achiheberi amene anamasuliridwa kuti “nzeru zoyendetsera moyo,” angagwiritsidwe ntchito pofotokoza zimene munthu wopereka malangizo pa ntchito yoyendetsa sitima yapanyanja ankachita. Mawuwa amanena za kutsogolera mwaluso.

Ngakhale kuti pamafunika khama, n’zotheka ndithu kupeza “nzeru zoyendetsera moyo” wathu bwinobwino. Buku la Miyambo limasonyeza kuti tiyenera kukhala anzeru, omvetsa zinthu ndiponso ozindikira. (Miy. 1:2-6; 2:1-9) Tisasiye kufufuza malangizo a Mulungu chifukwa nawonso anthu oipa amatha kupereka malangizo amene angativulaze.​—Miy. 12:5.

Choncho m’pofunika kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama. Tikatero, tidzadziwa mfundo zamtengo wapatali zokhudza Yehova komanso Yesu Khristu, amene anatengera Atate wake ndendende. (Yoh. 14:9) Timalandira malangizo anzeru ambirimbiri pa misonkhano yampingo. Anthu ena, monga makolo athu, akhoza kutithandizanso kupeza nzeru.​—Miy. 23:22.

MUZIONERATU ZINTHU N’KUKONZEKERA

Tikakumana ndi mavuto, timafunika kwambiri kupeza “nzeru zoyendetsera moyo” wathu. Munthu amene wakumana ndi vuto lalikulu koma osadziwa zoyenera kuchita akhoza kusokoneza kwambiri moyo wake.​—Yak. 1:5, 6.

Mawu akuti “nzeru zoyendetsera moyo” ndi ofanana ndi amene anamasuliridwa kuti “malangizo anzeru” ndipo chochititsa chidwi n’chakuti amagwiritsidwa ntchito ponena za nkhondo. Baibulo limati: “Zolinga zimakhazikika anthu akakambirana, ndipo uzitsatira malangizo anzeru pomenya nkhondo yako.”​—Miy. 20:18; 24:6.

Katswiri wa zankhondo amakonzeratu pulani ya mmene asilikali adzamenyere nkhondo. Ifenso tingachite bwino kuoneratu zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. (Miy. 22:3) Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mwapatsidwa mwayi wantchito kapena ngati akufuna kukukwezani kuntchito? Mwina mungaganizire zinthu monga malipiro, nthawi imene muziwononga popita ndi pobwera kuntchitoko ndiponso zinthu zina. Koma muyenera kuganiziranso zinthu izi: Kodi ntchitoyi ndi yogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo? Kodi izidzandipatsa mpata wopezeka pa misonkhano ndiponso wolowa mu utumiki mokwanira?​—Luka 14:28-30.

Mlongo wina dzina lake Loretta anali pa ntchito yabwino pakampani ina. Pa nthawi imene kampaniyo inkasamutsidwa, Loretta anapatsidwa mwayi wokwezedwa. Mabwana ake anamuuza kuti: “Mwayi umenewu sudzaupezanso moyo wako wonse.” Iwo anamuuzanso kuti: “Tafufuza kale n’kupeza kuti pali Nyumba ya Ufumu pafupi ndi malo amenewa.” Koma Loretta ankafuna kuyamba moyo wosalira zambiri n’cholinga choti awonjezere zochita potumikira Mlengi. Iye anaona kuti ntchito yatsopanoyo sidzamupatsa mpata wokwanira wotumikira Mulungu. Choncho, iye anapereka kwa bwana wamkulu kalata yosiya ntchito. Bwanayo anauza Loretta kuti anali munthu mmodzi yekha amene ankafunitsitsa kuti azigwirabe ntchito pakampaniyo. Panopa Loretta wakhala akuchita upainiya kwa zaka 20 ndipo amaona kuti zinthu zamuyendera bwino chifukwa chakuti malangizo a m’Mawu a Mulungu anamuthandiza kupeza “nzeru zoyendetsera moyo” wake. Iye analimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova ndipo wathandiza anthu ambiri kuphunzira choonadi cha m’Baibulo.

Munthu amene ali pa banja amafunikanso “nzeru zoyendetsera moyo” wake. Kulera ana ndi ntchito yotenga zaka zambiri ndipo zimene munthu angasankhe pa zinthu zauzimu kapena zakuthupi, zikhoza kukhudza tsogolo la banja lonse. (Miy. 22:6) Makolo achikhristu angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi zolankhula komanso zochita zathu zikuthandiza ana athu kukonda Mulungu moti angathe kudzachita zinthu mwanzeru akadzakula? Kodi tikuwapatsa chitsanzo chabwino pa nkhani yokhala moyo wosalira zambiri komanso kuika maganizo onse potumikira Mulungu?’​—1 Tim. 6:6-10, 18, 19.

Sikuti munthu amakhala ndi moyo wabwino ngati ali ndi zinthu kapena ngati amachita zinthu zimene anthu m’dzikoli amaona kuti ndi zofunika kwambiri. Mfumu Solomo inazindikira mfundo imeneyi ndipo inauziridwa kulemba kuti: “Anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendera bwino, chifukwa chakuti anali kumuopa.” (Mlal. 8:12) Choncho ndi bwino ndithu kufufuza m’Mawu a Mulungu “nzeru zoyendetsera moyo” wathu.​—2 Tim. 3:16, 17.

[Chithunzi patsamba 30]

Munthu wotsogolera pa ntchito yoyendetsa boti ankajambulidwa wamkulu pofuna kusonyeza kuti ankagwira ntchito yofunika kwambiri

[Mawu a Chithunzi]

Su concessione del Ministero per i Beni e le Attività Culturali. N’zoletsedwa kukopera chithunzichi m’njira iliyonse.