Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musasunthike Popewa Misampha ya Satana

Musasunthike Popewa Misampha ya Satana

Musasunthike Popewa Misampha ya Satana

“Musasunthike polimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi.”—AEF. 6:11.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi atumiki a Yehova angapewe bwanji msampha wa kukonda chuma?

Kodi Mkhristu wapabanja angapewe bwanji msampha wa chigololo?

Kodi kupewa msampha wa kukonda chuma ndiponso wa chiwerewere kuli ndi ubwino wotani?

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani Satana amadana ndi odzozedwa ndiponso a “nkhosa zina”? (b) Kodi tikambirana misampha iti ya Satana m’nkhani ino?

SATANA MDYEREKEZI sakonda anthu, makamaka atumiki a Yehova. Ndipo iye akumenya nkhondo yolimbana ndi odzozedwa amene ali padziko lapansi. (Chiv. 12:17) Akhristu olimba mtimawa akhala akutsogolera ntchito yolalikira ndiponso athandiza anthu kudziwa kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli. Mdyerekezi amadananso ndi a “nkhosa zina,” amene amathandiza odzozedwa ndiponso ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yoh. 10:16) Satana alibe chiyembekezochi. M’pake kuti ndi wokwiya kwambiri. Kaya tili ndi chiyembekezo chopita kumwamba kapena chokhala padziko lapansi, Satana satifunira zabwino. Cholinga chake ndi kutikola basi.—1 Pet. 5:8.

2 Kuti zimenezi zitheke, iye amatchera misampha yosiyanasiyana. Satana “wachititsa khungu maganizo” a anthu osakhulupirira moti iwo samvetsera uthenga wabwino ndipo saona misamphayi. Koma Mdyerekezi amakolanso anthu amene akudziwa za Ufumu. (2 Akor. 4:3, 4) M’nkhani yapita ija tinakambirana mmene tingapewere misampha itatu ya Satana. Misampha yake ndi (1) kusalankhula bwino, (2) kuopa anthu kapena kufuna kuwasangalatsa ndiponso (3) kudziimba mlandu kwambiri. Tiyeni tione mmene tingapewere misampha ina iwiri. Misampha yake ndi kukonda chuma ndiponso chigololo.

MSAMPHA WA KUKONDA CHUMA

3, 4. Kodi nkhawa za moyo wa nthawi ino zingachititse bwanji anthu kuyamba kukonda chuma?

3 M’fanizo lina, Yesu ananena za mbewu zimene zinafesedwa paminga. Iye anafotokoza kuti munthu akhoza kumva mawu “koma nkhawa za moyo wa m’nthawi ino ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma zimalepheretsa mawuwo kukula, ndipo iye amakhala wosabala zipatso.” (Mat. 13:22) Choncho kukonda chuma ndi msampha umene Satana amagwiritsa ntchito.

4 Pali zinthu ziwiri zimene zimagwira ntchito limodzi polepheretsa mawu kukula. Choyamba ndi “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino.” ‘M’nthawi yovuta’ ino, pali zinthu zambiri zimene zingakudetseni nkhawa. (2 Tim. 3:1) Popeza zinthu zakwera mitengo komanso ntchito zikusowa, mukhoza kumavutika kuti mupeze zofunika pa moyo. Mukhozanso kumadera nkhawa zam’tsogolo mwina n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi zinthu zidzandiyendera bwanji ndikadzakalamba?’ Chifukwa cha zimenezi, anthu ena amayamba kufufuza chuma poganiza kuti akakhala ndi ndalama zambiri, sangadzavutike.

5. Kodi munthu angapusitsidwe bwanji ndi “chinyengo champhamvu cha chuma”?

5 Chinthu china chimene Yesu ananena ndi “chinyengo champhamvu cha chuma.” Chinyengochi limodzi ndi nkhawa zingalepheretse mawu kukula. Baibulo limanenadi kuti ‘ndalama zimateteza.’ (Mlal. 7:12) Koma kufufuza chuma n’kupanda nzeru. Ambiri azindikira kuti akamayesetsa kuti apeze chuma, amapezeka kuti akodwa mumsampha wokonda chumacho. Ena afika pokhala akapolo a chuma.—Mat. 6:24.

6, 7. (a) Kodi munthu wapantchito angakodwe bwanji mumsampha wokonda chuma? (b) Kodi Mkhristu amene wauzidwa kuti azigwira ovataimu ayenera kuganizira zinthu ziti?

6 Mtima wofuna chuma ukhoza kuyamba mosavuta. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti bwana wanu akukuuzani kuti: “Kampani yathu yapeza mwayi wa ntchito inayake. Tingofunika kugwira ovataimu kwa miyezi yochepa. Koma tidzakulipirani ndalama zambiri.” Kodi mungatani? N’zoona kuti mufunika kupezera banja lanu zinthu zofunika pa moyo koma kumbukirani kuti muli ndi udindo winanso. (1 Tim. 5:8) Pali zinthu zambiri zofunika kuziganizira. Kodi nthawi yowonjezerayo idzakhala yochuluka bwanji? Kodi sizidzakulepheretsani kutumikira bwino Mulungu, kusonkhana ndiponso kuchita Kulambira kwa Pabanja?

7 Posankha zochita, kodi mudzaganizira kwambiri za chiyani? Kodi mudzaganizira za ndalama zimene mungapeze kapena mudzaganizira mmene ntchitoyo ingakhudzire ubwenzi wanu ndi Yehova? Kodi mudzasiya kuika zinthu zokhudza Ufumu patsogolo n’cholinga choti mupeze ndalama zambiri? Apa n’zoonekeratu kuti kukonda chuma kungalepheretse munthu ndiponso banja lake kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ngati izi n’zimene zikukuchitikirani, kodi mungatani kuti muwonjoke mumsampha umenewu?—Werengani 1 Timoteyo 6:9, 10.

8. Kodi ndi nkhani za m’Baibulo ziti zimene zingatithandize kudzifufuza?

8 Kuti musakodwe mumsampha wokonda chuma, muyenera kudzifufuza nthawi ndi nthawi. Musakhale ngati Esau amene anachita zinthu zosonyeza kuti ankanyoza zinthu zauzimu. (Gen. 25:34; Aheb. 12:16) Musakhalenso ngati munthu wachuma amene Yesu anamuuza kuti: ‘Kagulitse katundu wako ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero ubwere udzakhale wotsatira wanga.’ M’malo mochita zimenezi, iye “anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.” (Mat. 19:21, 22) Chifukwa chokodwa mumsampha wokonda chuma, munthuyu anataya mwayi wotsatira munthu wofunika kwambiri kuposa wina aliyense. Samalani kuti inunso musataye mwayi wokhala wophunzira wa Yesu Khristu.

9, 10. Kodi Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziona bwanji zinthu zakuthupi?

9 Kuti tipewe msamphawu, tiyenera kutsatira malangizo a Yesu akuti: “Choncho musamade nkhawa n’kumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapena, ‘Tivala chiyani?’ Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.”—Mat. 6:31, 32; Luka 21:34, 35.

10 M’malo mokopeka ndi chinyengo champhamvu cha chuma, yesetsani kukhala ndi maganizo a Aguri amene analemba kuti: “Musandipatse umphawi kapena chuma. Ndidye chakudya chimene ndikufunika kudya.” (Miy. 30:8) Aguri ankadziwa bwino kufunika kwa ndalama komanso kuopsa kwa chinyengo champhamvu cha chuma. Dziwani kuti nkhawa za moyo uno ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma zikhoza kuwononga ubwenzi wanu ndi Yehova. Kudera nkhawa kwambiri zinthu zakuthupi kukhoza kukuwonongerani nthawi ndi mphamvu moti simungafunenso kuika zinthu za Ufumu patsogolo. Choncho yesetsani kuti musakodwe mumsampha wa Satana wa kukonda chuma.—Werengani Aheberi 13:5.

CHIGOLOLO CHILI NGATI DZENJE LOBISIKA

11, 12. Kodi n’chiyani chingachititse Mkhristu kuchita chigololo ndi munthu wa kuntchito?

11 Alenje akafuna kugwira nyama yaikulu, amakumba dzenje pampita wake. Pamwamba pake amaphimbapo ndi timitengo ndi dothi. Msampha wina wa Satana, umene wakola anthu ambiri, umafanana ndi dzenje lotereli. Msampha wake ndi chiwerewere. (Miy. 22:14; 23:27) Akhristu ambiri achita zinthu zimene zawagwetsera mosavuta m’dzenje limeneli. Akhristu amene ali pa banja achita chigololo chifukwa chocheza mosayenera ndi anthu ena n’kuyamba kukondana.

12 Zimenezi zikhoza kuchitika kuntchito. Kafukufuku wina anasonyeza kuti hafu ya akazi amene anachita chigololo komanso pafupifupi amuna onse amene anachita chigololo, anachita ndi anthu a kuntchito kwawo. Kodi mumagwira ntchito ndi anthu amene si amuna kapena akazi anzanu? Ngati ndi choncho, kodi mumacheza nawo bwanji? Kodi mumaonetsetsa kuti simukucheza nawo mopitirira malire? Mwachitsanzo, mlongo amene amakonda kucheza ndi mwamuna wina kuntchito akhoza kuyamba kumuuza zakukhosi kwake mwinanso mavuto a m’banja lake. Apo ayi, m’bale amene amakonda kucheza ndi mkazi wina kuntchito akhoza kuyamba kuganiza kuti: “Mkazi ameneyu amalemekeza maganizo anga ndipo amamvetsera ndikamalankhula. Zikuoneka kuti amandidalira. Koma mkazi wanga satero.” Kodi Akhristu oterewa sangachite chigololo?

13. Kodi anthu mu mpingo angayambe bwanji kucheza mosayenera?

13 Mu mpingo, anthu akhozanso kuyamba kucheza mosayenera. Izi ndi zimene zinachitika ku mpingo wina. Daniel ndi mkazi wake Sarah * anali apainiya okhazikika. Daniel anali mkulu yemwe sankakana ntchito iliyonse m’gulu la Yehova. Daniel ankaphunzira Baibulo ndi anyamata asanu ndipo atatu anabatizidwa. Abale atatuwa ankafunika thandizo. Daniel akatanganidwa ndi utumiki wina, Sarah ankathandiza abalewa. Iwo ankafuna munthu woti azimuuza zakukhosi kwawo ndipo ankachita zimenezi ndi Sarah. Nayenso Sarah ankafuna munthu wocheza naye ndipo ankangocheza ndi abalewo. Apa zinali ngati msampha watcheredwa. Daniel anati: “Chifukwa chothandiza anthuwa kwa nthawi yaitali, mkazi wanga anafooka moti ankafunika thandizo kuti ubwenzi wake ndi Yehova ulimbe ndiponso maganizo ake akhazikike. Vuto linanso linali loti ineyo ndinkangochita zinthu zina osaona zimenezi. Zotsatira zake zinali zomvetsa chisoni kwambiri. Mkazi wanga anachita chigololo ndi mmodzi mwa abalewo. Ndinkatanganidwa kwambiri ndi utumiki wosiyanasiyana moti sindinazindikire kuti mkazi wanga wayamba kufooka.” Kodi mungatani kuti zimenezi zisakuchitikireni?

14, 15. Kodi n’chiyani chingathandize Akhristu apabanja kupewa chigololo?

14 Kuti mupewe msampha wa chigololo, muyenera kuganizira kwambiri tanthauzo la kukhulupirika m’banja. Yesu anati: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mat. 19:6) Musamaganize kuti utumiki wanu ndi wofunika kwambiri kuposa mkazi kapena mwamuna wanu. Muyenera kukumbukiranso kuti munthu amene amakonda kusiya mkazi kapena mwamuna wake kuti akachite zinthu zina zosafunika kwenikweni, amayambitsa mavuto m’banja. Izi zingachititse kuti wina achite chigololo.

15 Koma bwanji ngati ndinu mkulu? Mtumwi Petulo analemba kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse.” (1 Pet. 5:2) Choncho ngati ndinu mkulu, muyenera kusamalira abale ndi alongo mu mpingo. Komabe simuyenera kunyalanyaza mkazi wanu n’cholinga choti musamalire mpingo. Si nzeru kutanganidwa pothandiza mpingo pamene mkazi wanu akusowa thandizo kunyumba. Zimenezi zikhoza kuwononga banja lanu. Daniel ananena kuti, “Si bwino kumangotanganidwa ndi maudindo m’gulu la Yehova n’kumanyalanyaza banja lanu.”

16, 17. (a) Kodi Akhristu apantchito angasonyeze bwanji kuti safuna kuchita chibwenzi ndi munthu wina aliyense? (b) Tchulani magazini imene ili ndi malangizo othandiza Akhristu kupewa chigololo.

16 M’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! muli malangizo ambiri othandiza Akhristu apabanja kuti asagwere mumsampha wa chigololo. Mwachitsanzo mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2006, muli malangizo akuti: “Kuntchito ndiponso kwina kulikonse, samalani ndi zinthu zimene zingachititse kuti muyambe kukondana ndi munthu winawake. Mwachitsanzo, kugwira ovataimu limodzi ndi munthu amene si mwamuna mnzanu kapena mkazi mnzanu kungathe kukulowetsani m’mayesero. Monga munthu wa pa banja, muyenera kusonyeza bwino mwa zolankhula zanu ndiponso khalidwe lanu kuti simufuna kuchita chibwenzi ndi munthu aliyense. Mosakayikira, monga munthu wodzipereka kwa Mulungu, simungachite mwadala zinthu zopatsa ena maganizo olakwika mwa kukopana ndi winawake kapena kuvala ndi kudzikongoletsa [mokopa ena]. . . . Kukhala ndi zithunzi za mwamuna kapena mkazi wanu ndiponso za ana anu kuntchito kwanu, kungathandize kuti inuyo ndiponso anthu ena azikumbukira kuti mumaona kuti banja lanu ndi lofunika. Onetsetsani kuti musalimbikitse, ngakhalenso kulekerera, zinthu zokukopani zimene wina akuchita.”

17 Nkhani yakuti “Kodi Kukhulupirika M’banja N’kutani?” mu Galamukani! ya April 2009, imanena kuti tiyenera kupewa kukhumbira ndiponso kuganizira zochita chiwerewere ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wathu. Nkhaniyi inanena kuti kuchita zimenezi kungachititse kuti muchitedi chigololo. (Yak. 1:14, 15) Ngati muli pa banja, mungachite bwino kukambirana ndi mkazi kapena mwamuna wanu nkhani ngati zimenezi nthawi ndi nthawi. Yehova ndi amene anayambitsa ukwati choncho ndi wopatulika. Mungasonyeze kuti mumayamikira zinthu zopatulika mukamakambirana ndi mkazi kapena mwamuna wanu nkhani zokhudza ukwati wanu.—Gen. 2:21-24.

18, 19. (a) Kodi zotsatira za chigololo n’zotani? (b) Kodi ubwino wa kukhala wokhulupirika m’banja ndi wotani?

18 Ngati mukuyesedwa kuti muyambe kukondana ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wanu, muyenera kuganizira mavuto amene amabwera chifukwa chochita dama kapena chigololo. (Miy. 7:22, 23; Agal. 6:7) Anthu amene achita chiwerewere amakhumudwitsa Yehova ndiponso mwamuna kapena mkazi wawo. Iwonso sasangalala. (Werengani Malaki 2:13, 14.) Muziganiziranso ubwino wokhala ndi makhalidwe oyera. Anthu amakhalidwe oyera amakhala ndi chikumbumtima choyera panopa komanso adzapeza moyo wosatha m’tsogolo.—Werengani Miyambo 3:1, 2.

19 Wamasalimo anaimba kuti: “Okonda chilamulo [cha Mulungu] amapeza mtendere wochuluka, ndipo palibe chowakhumudwitsa.” (Sal. 119:165) Choncho muzikonda kwambiri choonadi. Masiku ano ndi oipa ndiye “samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru.” (Aef. 5:15, 16) Masiku ano, Satana amagwiritsa ntchito misampha yambiri kuti akole atumiki a Mulungu. Koma Yehova watipatsa zinthu zonse zofunika kuti ‘tisasunthike’ poyesetsa ‘kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’—Aef. 6:11, 16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Mayina asinthidwa.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

Musalole kuti kukonda chuma kusokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova

[Chithunzi patsamba 29]

Kukopana kungakugwetsereni mumsampha wa chigololo