Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzitsani Ana Anu

Gehazi Anapeza Mavuto Chifukwa cha Dyera

Gehazi Anapeza Mavuto Chifukwa cha Dyera

KODI nthawi ina unalakalakapo chinthu chinachake kwambiri? * Ngati unachitapo zimenezi, dziwa kuti si iwe woyamba. Anthu ambiri amachita zimenezi akafuna kukhala ndi chinthu chimene amachilakalaka pa moyo wawo. Koma kodi uyenera kunama kuti upeze chinthucho?— Ayi, suyenera kuchita zimenezo. Munthu amene amanama kuti apeze chinthu chinachake ndiye kuti ndi wadyera. Tiye tione zimene zinachititsa kuti munthu wina, dzina lake Gehazi, apeze mavuto chifukwa cha dyera. Gehazi ankatumikira Elisa, yemwe anali mneneri wa Mulungu woona, Yehova.

Elisa ndi Gehazi anakhalapo kalekale zaka pafupifupi 1,000 mwana wa Mulungu, Yesu, asanabadwe padziko lapansili. Yehova ankagwiritsira ntchito Elisa pochita zodabwitsa. Iyetu ankachita zozizwitsa. Mwachitsanzo, m’Baibulo muli nkhani ya munthu wina amene anali mkulu wa gulu la asilikali a Siriya yemwe ankadwala matenda akhate. Palibe munthu amene akanam’chiritsa, koma Elisa yekha basi.

Mulungu akamamugwiritsira ntchito pochiritsa anthu, Elisayo sankalandira ndalama. Kodi ukudziwa chifukwa chake?— Chifukwa chakuti ankadziwa kuti Yehova ndiye ankachiritsa anthuwo osati iyeyo. Namani atachiritsidwa anasangalala kwambiri moti anafuna kupatsa Elisa mphatso za golide, siliva ndi zovala zabwino kwambiri. Elisa anakana mphatsozi, koma Gehazi ankazifuna kwambiri.

Namani atangochoka, Gehazi anamuthamangira, koma sanauze Elisa kuti akupita kwa Namani. Atam’peza Namani, kodi ukudziwa zimene anamuuza?— Iye anamuuza kuti: ‘Elisa wandituma kuti ndikuuzeni kuti kwabwera alendo awiri posachedwapa. Choncho akufuna kuti mum’patseko zovala ziwiri kuti akapatse alendowa.’

Koma iye ankanama. Sizinali zoona kuti kunali kutabwera alendo. Iye ananena zimenezi chifukwa ankafuna kwambiri zovala zimene Namani ankafuna kupatsa Elisa zija. Namanitu sanadziwe kuti zimene Gehazi ananenazi zinali zabodza. Choncho, iye anapereka mphatsozi kwa Gehazi. Komanso Namani anapatsa Gehazi zinthu zoposa zimene anapempha. Kodi ukudziwa zimene zinachitika pambuyo pake?

Pamene Gehazi anafika kwa Elisa, Elisayo anamufunsa kuti: “Kodi unapita kuti?”

Iye anayankha kuti: ‘Sindinapite kulikonse.’ Komabe, Yehova anauza Elisa zimene Gehazi anali atachita. Choncho, Elisa anauza Gehazi kuti: ‘Ino si nthawi yolandira ndalama ndi zovala.’

Gehazi analandira ndalama komanso zovala zomwe sizinali zoyenera kukhala zake. Choncho, Mulungu anachititsa kuti khate la Namani lija lipite kwa Gehazi. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa?—Tikuphunzirapo kuti ifeyo sitiyenera kunama.

N’chifukwa chiyani Gehazi anangopeka nkhani yomwe sinali yoona?— Iye anachita zimenezi chifukwa cha dyera. Ankafuna kukhala ndi zinthu zimene sizinali zake, choncho anaganiza zongonama kuti apeze zinthuzo. Chifukwa cha zimenezi, iye anadwala khate kwa moyo wake wonse.

Koma Gehazi anapezanso mavuto ena oposa khate limene ankadwala. Kodi ukudziwa mavuto amene anawapeza?— Iye sanalinso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu chifukwa Mulungu anasiya kumukonda. Ife tisalole kuti chinthu chilichonse chisokoneze ubwenzi wathu ndi Mulungu. Koma tiyenera kukhala okoma mtima komanso tizigawira ena zimene tili nazo.

^ ndime 3 Ngati mukuwerengera mwana nkhaniyi, mukapeza mzera muime kaye ndi kumulimbikitsa kuti anenepo maganizo ake.