Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsanzirani Kuleza Mtima kwa Yehova ndi Yesu

Tsanzirani Kuleza Mtima kwa Yehova ndi Yesu

“Muone kuleza mtima kwa Ambuye wathu kukhala chipulumutso.”—2 PET. 3:15.

1. Kodi Akhristu ena okhulupirika amadzifunsa kuti chiyani?

MLONGO wina wokhulupirika, amene watumikira Yehova kwa zaka zambiri ndiponso kupirira mavuto ambiri, anafunsa kuti: “Koma mapeto adzafika ine ndili moyo?” Anthu ambiri amene atumikira Yehova kwa zaka zambiri amadzifunsanso funso ngati limeneli. Tonsefe timalakalaka nthawi imene Mulungu adzathetsa mavuto athu n’kupanga zinthu zonse kukhala zatsopano. (Chiv. 21:5) Ngakhale kuti tikudziwa zoti mapeto a dziko la Satanali ayandikira, kudikira moleza mtima n’kovuta.

2. Kodi tikambirana mafunso ati okhudza kuleza mtima?

2 Koma Baibulo limatilimbikitsa kukhala oleza mtima. Mofanana ndi atumiki a Mulungu akale, tidzalandira zinthu zimene Mulungu walonjeza ngati tikhala ndi chikhulupiriro champhamvu n’kumayembekezera moleza mtima. (Werengani Aheberi 6:11, 12.) Nayenso Yehova ndi woleza mtima. Bwenzi atawononga kalekale dziko loipali. Koma iye akuyembekeza nthawi yoyenera. (Aroma 9:20-24) N’chifukwa chiyani Mulungu akuleza mtima chonchi? Kodi Yesu wapereka chitsanzo chotani pa nkhani yoleza mtima ngati Mulungu? Kodi tidzapeza madalitso otani ngati nafenso tikhala oleza mtima ngati Mulungu? Mayankho a mafunso amenewa atithandiza kuti tikhale oleza mtima ndiponso achikhulupiriro champhamvu. Tidzatero ngakhale pamene tikuona ngati Yehova akuchedwa.

N’CHIFUKWA CHIYANI YEHOVA AMALEZA MTIMA?

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Yehova akuleza mtima? (b) Kodi Yehova anatani Adamu ndi Hava atamupandukira?

3 Yehova ali ndi zifukwa zomveka zokhalira woleza mtima. N’zoona kuti Yehova ndi wamphamvu m’chilengedwe chonse koma kupanduka kwa anthu mu Edeni kunayambitsa nkhani zikuluzikulu. Yehova akuleza mtima chifukwa chodziwa kuti pafunika nthawi yaitali kuti athetse bwinobwino nkhanizo. Yehova amadziwa aliyense kumwamba komanso padziko lapansi. Choncho akuchita zinthu m’njira imene ingathandize aliyense.—Aheb. 4:13.

4 Cholinga cha Yehova chinali chakuti ana a Adamu ndi Hava adzaze dziko lapansi. Satana ananyengerera Hava ndipo kenako Adamu sanamvere Mulungu. Koma izi sizinasinthe cholinga cha Yehova. Iye sanachite zinthu mwaphuma kapena mosaganiza komanso sananyanyale anthu. M’malomwake, anapeza njira yokwaniritsira cholinga chake. (Yes. 55:11) Yehova wachita zinthu modziletsa ndiponso moleza mtima. Wachita zimenezi kuti akwaniritse cholinga chake ndiponso pofuna kusonyeza kuti ndi woyenera kulamulira. Iye wadikira kwa zaka masauzande kuti mbali zina za cholinga chake zikwaniritsidwe m’njira yabwino kwambiri.

5. Kodi kuleza mtima kwa Yehova kuli ndi ubwino uti?

5 Chifukwa china chimene Yehova akulezera mtima n’chakuti iye akufuna kuti anthu ambiri apeze moyo wosatha. Panopa, iye akukonza zinthu kuti apulumutse “khamu lalikulu.” (Chiv. 7:9, 14; 14:6) Kudzera m’ntchito yolalikira, Yehova akuthandiza anthu kuphunzira za Ufumu wake ndiponso mfundo zake zolungama. Uthenga wa Ufumu ndi wabwino kwambiri ndipo umathandiza anthu. (Mat. 24:14) Munthu aliyense amene amakokedwa ndi Yehova amalowa mu mpingo wa padziko lonse wa anthu ogwirizana amene amakonda zinthu zabwino. (Yoh. 6:44-47) Mulungu wathu wachikondi amathandiza anthu amenewa kuti akhale naye pa ubwenzi wabwino. Iye wakhalanso akusankha anthu amene adzakhale m’boma lake lakumwamba. Anthuwa akadzapita kumwamba, adzathandiza anthu omvera padziko lapansi kuti akhale angwiro ndiponso kuti apeze moyo wosatha. Choncho ngakhale kuti Yehova akudikira moleza mtima, iye akukwaniritsa cholinga chake m’njira yothandiza tonsefe.

6. (a) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi woleza mtima m’masiku a Nowa? (b) Kodi Yehova akusonyeza bwanji kuti ndi woleza mtima masiku ano?

6 Yehova amaleza mtima ngakhale ataputidwa kwambiri. Mwachitsanzo, Chigumula chisanachitike dziko lonse linadzaza ndi makhalidwe oipa monga chiwerewere ndi chiwawa. Yehova “zinam’pweteka kwambiri mumtima.” (Gen. 6:2-8) Iye sanafune kulekerera zimenezi choncho anasankha kubweretsa chigumula kuti awononge anthu osamvera. Ngakhale kuti “Mulungu anali kuleza mtima m’masiku a Nowa,” iye anali kukonza zopulumutsa Nowa ndi banja lake. (1 Pet. 3:20) Pa nthawi yoyenera Yehova anauza Nowa nkhaniyi ndipo anamuuza kuti apange chingalawa. (Gen. 6:14-22) Nowa analinso “mlaliki wa chilungamo” ndipo ankauza anthu kuti Mulungu awononga dziko. (2 Pet. 2:5) Yesu ananena kuti masiku ano akufanana ndi masiku a Nowa. Yehova akudziwa nthawi imene adzawononge dziko loipali. Koma palibe munthu amene akudziwa “tsikulo ndi ola lake.” (Mat. 24:36) Panopa, Mulungu watipatsa ntchito yochenjeza anthu ndi kuwauza zimene angachite kuti apulumuke.

7. Kodi Yehova akuchedwa kukwaniritsa malonjezo ake? Fotokozani.

7 Choncho kuleza mtima kwa Yehova sikutanthauza kuti akungokhala popanda kuchita chilichonse. Tisaganize kuti kuleza mtima kwa Yehova kukutanthauza kuti sakuona zimene zikutichitikira kapena kuti alibe nazo ntchito. Koma n’zovuta kukumbukira zimenezi tikamakalamba kapena tikamakumana ndi mavuto m’dziko loipali. Tikhoza kuyamba kutaya mtima kapena kuganiza kuti Mulungu akuchedwa kukwaniritsa malonjezo ake. (Aheb. 10:36) Tisaiwale kuti Yehova ali ndi zifukwa zabwino zomuchititsa kuleza mtima ndipo akugwiritsa ntchito nthawi inoyi kuti athandize atumiki ake okhulupirika. (2 Pet. 2:3; 3:9) Tiyeni tsopano tikambirane za mmene Yesu anasonyezera kuti ndi woleza mtima ngati Mulungu.

YESU NDI CHITSANZO CHABWINO PA NKHANI YOLEZA MTIMA

8. Kodi Yesu anasonyeza kuti ndi woleza mtima pa nthawi iti?

8 Yesu akuchita chifuniro cha Mulungu ndipo wakhala akuchita zimenezi ndi mtima wonse kwa zaka masauzande ambiri. Satana atapanduka, Yehova anakonza zoti Mwana wake wobadwa yekha abwere padziko lapansi n’kukhala Mesiya. Ndiye tangoganizani. Yesu anafunika kuyembekezera zimenezi moleza mtima kwa zaka zambirimbiri. (Werengani Agalatiya 4:4.) Sikuti ankangokhala n’kumadikira koma anali wotanganidwa ndi ntchito imene Atate wake anamupatsa. Atabwera padziko lapansi, iye ankadziwa kuti malinga ndi ulosi, Satana adzachititsa kuti aphedwe. (Gen. 3:15; Mat. 16:21) Iye anachita chifuniro cha Mulungu moleza mtima ngakhale kuti ankafunika kuzunzika koopsa. Apatu anapereka chitsanzo chapamwamba kwambiri pa nkhani ya kukhulupirika. Iye anali wodzichepetsa ndipo sankadziganizira kwambiri. Tingachite bwino kutsatira chitsanzo chake.—Aheb. 5:8, 9.

9, 10. (a) Kodi Yesu wakhala akuchita chiyani poyembekezera nthawi ya Yehova? (b) Kodi tingatsanzire bwanji mtima wa Yesu?

9 Ataukitsidwa, Yesu anapatsidwa ulamuliro kumwamba ndi padziko lapansi. (Mat. 28:18) Iye amagwiritsa ntchito ulamulirowu kuti akwaniritse cholinga cha Yehova pa nthawi yake. Yesu anakhala kudzanja lamanja la Mulungu n’kumayembekezera moleza mtima mpaka mu 1914, pamene adani ake anaikidwa monga chopondapo mapazi ake. (Sal. 110:1, 2; Aheb. 10:12, 13) Posachedwapa, agwira ntchito yowononga dziko la Satanali. Panopa, Yesu akuthandiza anthu moleza mtima ndipo akuwatsogolera kuti akapeze “madzi a moyo.”—Chiv. 7:17.

10 Kodi mungatsanzire bwanji mtima wa Yesu? Yesu ankafunitsitsa kuchita zimene Atate wake anamupempha koma ankayembekezera nthawi imene Mulungu wasankha. Pamene tikuyembekezera mapeto a dziko loipali, tiyenera kukhala oleza mtima ngati Mulungu. Tiziyembekezera Mulungu ndipo tisagwe mphwayi kapena kutaya mtima. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala oleza mtima ngati Mulungu?

KODI NDINGATANI KUTI NDIZILEZA MTIMA NGATI MULUNGU?

11. (a) Kodi chikhulupiriro chimathandiza bwanji munthu kukhala woleza mtima? (b) Kodi tili ndi zifukwa zinanso ziti zotichititsa kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu?

11 Yesu asanabwere padziko lapansi, aneneri ndiponso atumiki ena okhulupirika anasonyeza kuti anthu opanda ungwiro akhoza kupirira moleza mtima. Chikhulupiriro chawo chinawathandiza kukhala oleza mtima. (Werengani Yakobo 5:10, 11.) Iwo akanakhala kuti sankakhulupirira zimene Yehova anawauza, sakanayembekezera moleza mtima kuti malonjezo ake akwaniritsidwe. Nthawi ndi nthawi ankakumana ndi zinthu zoopsa komanso zovuta koma ankakhulupirira kuti Mulungu adzachita zimene walonjeza. (Aheb. 11:13, 35-40) Panopa tili ndi zifukwa zinanso zotichititsa kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu. Yesu ndi “Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu.” (Aheb. 12:2) Iye anakwaniritsa maulosi komanso anafotokoza zolinga za Mulungu m’njira yotithandiza kukhala ndi chikhulupiriro.

12. Kodi tingalimbitse bwanji chikhulupiriro chathu?

12 Kodi tingatani kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu komanso tikhale oleza mtima? Chofunika kwambiri ndi kutsatira malangizo a Mulungu. Mwachitsanzo, pa Mateyu 6:33 timalangizidwa kuti tiyenera kufunafuna Ufumu choyamba. Kodi pali zina zimene mungachite kuti mutsatire malangizo amenewa? Mwina mungawonjezere nthawi yanu yolalikira kapena kusintha zinthu zina pa moyo wanu. Muyenera kukumbukiranso mmene Yehova wakudalitsirani chifukwa chotsatira malangizo ake. Mwina wakuthandizani kuyambitsa phunziro la Baibulo kapena wakuthandizani kupeza “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Werengani Afilipi 4:7.) Mukamaganizira madalitso amene mwapeza chifukwa chotsatira malangizo a Yehova, mudzaona ubwino wa kuleza mtima.—Sal. 34:8.

13. Perekani chitsanzo chosonyeza mmene munthu angalimbitsire chikhulupiriro ndiponso kukhala woleza mtima.

13 Taganizirani zimene mlimi amachita. Mlimi akakolola zambiri, zimamulimbikitsa kubzalanso ulendo wotsatira. Mwina amawonjezeranso minda yake. Amabzala ngakhale kuti amadziwa zoti ayenera kuyembekezera moleza mtima kuti nthawi yokolola ifike. Iye sakayikira zoti adzakolola. Ifenso tikamaphunzira malangizo a Yehova, kuwatsatira kenako n’kupeza madalitso, timakhulupirira kwambiri Yehova. Chikhulupiriro chathu chimalimba ndipo sizivuta kuyembekezera madalitso amene timadziwa kuti tidzapeza.—Werengani Yakobo 5:7, 8.

14, 15. Kodi tiyenera kuona bwanji mavuto athu?

14 Chinthu china chimene chingatithandize kukhala oleza mtima ndicho kuona dzikoli ndiponso mavuto athu m’njira yoyenera. Tiyenera kuona zinthu mmene Yehova amazionera. Mwachitsanzo, kodi Yehova amamva bwanji akamaona anthu akuvutika? Zakhala zikumupweteka kwa zaka zambirimbiri koma sikuti amamva chisoni moti n’kulephera kuchita zinthu zoyenera. Iye anatumiza Mwana wake wobadwa yekha “kuti awononge ntchito za Mdyerekezi” n’kuthetsa mavuto onse amene Satana wayambitsa padzikoli. (1 Yoh. 3:8) Mavuto a anthu ndi akanthawi koma zabwino zimene Mulungu adzachite ndi zamuyaya. Ifenso sitiyenera kuthedwa nzeru ndi mavuto a m’dziko la Satanali kapena kuona kuti mapeto akuchedwa. M’malomwake, tizikhulupirira zinthu zimene tikuyembekezera zomwe ndi zamuyaya. Yehova waikiratu nthawi yowononga dziko loipali ndipo sadzachedwa.—Yes. 46:13; Nah. 1:9.

15 M’masiku otsiriza ovutawa, tingakumane ndi mavuto aakulu amene angayese chikhulupiriro chathu. Mwina ifeyo kapena anzathu amene timawakonda kwambiri angavutike chifukwa chochitiridwa nkhanza kapena pa zifukwa zina. M’malo mokwiya nazo, tiyenera kukhulupirira Yehova ndi mtima wonse. Koma popeza kuti ndife opanda ungwiro, kuchita zimenezi si kophweka. Kumbukirani zimene Yesu anachita zomwe zili pa lemba la Mateyu 26:39.Werengani.

16. Kodi tiyenera kupewa kuchita chiyani podikira mapeto?

16 Munthu amene amakayikira kuti mapeto ayandikira sangaleze mtima. Iye angayambe kuchita zinthu zina poganiza kuti ngati zimene Yehova walonjeza sizichitika asasowe pogwira. Akhoza kuganiza kuti, ‘Ndidikire kaye ndione ngati Yehova angachitedi zimene wanena.’ Mwina angayesetse kuti atchuke kapena apeze chuma m’malo moika Ufumu wa Mulungu pa malo oyamba. Apo ayi, angaganize zopita ku yunivesite n’cholinga choti akhale ndi moyo wawofuwofu m’dzikoli. Kodi kumeneku sikungakhale kupanda chikhulupiriro? Tizikumbukira kuti Paulo anatilimbikitsa kutengera chitsanzo cha anthu okhulupirika. Anthuwa analandira zinthu zimene Yehova analonjeza chifukwa cha “chikhulupiriro ndi kuleza mtima.” (Aheb. 6:12) Yehova adzawononga dziko loipali pa nthawi yeniyeni imene wasankha. (Hab. 2:3) Pamene tikudikira zimenezi, tiyenera kupewa kutumikira Yehova mwaulesi. M’malomwake, tiyenera kukhala maso ndiponso kuchita khama polalikira uthenga wabwino. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhala osangalala kwambiri ngakhale panopa.—Luka 21:36.

MADALITSO A ANTHU OLEZA MTIMA

17, 18. (a) Kodi tili ndi mwayi wochita chiyani pamene tikuleza mtima? (b) Kodi tidzadalitsidwa bwanji chifukwa chokhala oleza mtima?

17 Enafe tatumikira Mulungu kwa miyezi yochepa pomwe ena zaka zambirimbiri. Koma tonse timafuna kutumikira Yehova kwamuyaya. Kaya kwatsala nthawi yaitali bwanji, kuleza mtima kumatithandiza kuti tipirire mpaka pamene tidzapulumuke. Yehova akutipatsa mwayi wosonyeza kuti timamukhulupirira ndi mtima wonse ndipo ndife okonzeka kuvutika chifukwa cha dzina lake. (1 Pet. 4:13, 14) Mulungu akutiphunzitsanso mmene tingakhalire oleza mtima mpaka mapeto kuti tipulumuke.—1 Pet. 5:10.

18 Yesu wapatsidwa ulamuliro wonse kumwamba ndi padziko lapansi ndipo palibe amene angatitsomphole m’manja mwake. (Yoh. 10:28, 29) Palibe chifukwa choopera zam’tsogolo kapena imfa. Anthu onse amene adzapirira moleza mtima mpaka mapeto adzapulumuka. Choncho tisalole kuti zinthu za m’dzikoli zitisokoneze kapena kutilepheretsa kudalira Yehova. M’malomwake, tiyenera kuyesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chathu ndiponso kugwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imene Mulungu akuleza mtimayi.—Mat. 24:13; werengani 2 Petulo 3:17, 18.