Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Simukudziwa Tsiku Kapena Ola Lake”

“Simukudziwa Tsiku Kapena Ola Lake”

“Chotero khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”—MAT. 25:13.

1-3. (a) Kodi mafanizo awiri a Yesu mungawayerekezere ndi zochitika ziti? (b) Kodi tiyenera kuyankha mafunso ati?

TIYEREKEZE kuti mwapemphedwa ndi nduna ya boma kuti muitenge pa galimoto kupita ku msonkhano wofunika kwambiri. Koma kutangotsala mphindi zochepa kuti munyamuke, mukuzindikira kuti mafuta ndi operewera ndipo mukuthamanga kupita kukagula ena. Ndiyeno ndunayo ikufika inu musanabwere kokagula mafutawo. Poopa kuti ichedwa, ndunayo ikupempha munthu wina kuti aitenge. Inu pofika mukupeza kuti yapita. Kodi mungamve bwanji?

2 Tiyerekezenso kuti inuyo ndinu nduna ndipo mwasankha anthu atatu kuti akugwirireni ntchito inayake yofunika kwambiri. Mutawafotokozera za ntchitoyo, onse akuvomera bwinobwino kuti agwira ndipo inu mukuchokapo. Koma pobwera mukupeza kuti awiri okha ndi amene agwira ntchitoyo. Wachitatuyo sanayese n’komwe kuchita chilichonse ndipo akupereka zifukwa zake. Kodi mungamve bwanji?

3 Yesu anapereka mafanizo awiri ofanana ndi nkhani zimene tafotokozazi. Iye ananena za anamwali ndiponso za matalente posonyeza kuti nthawi yamapeto, Akhristu odzozedwa ena adzakhala okhulupirika ndi anzeru koma ena sadzatero. * (Mat. 25:1-30) Potsindika mfundo yake iye anati: “Chotero khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.” Apa ankanena za tsiku limene Yesu adzabwere kudzawononga dziko la Satanali. (Mat. 25:13) Ifenso tiyenera kukhala maso. Kodi kutsatira malangizo a Yesu oti tikhale maso kungatithandize bwanji? Kodi ndani amene asonyeza kuti ndi okonzeka kupulumuka? Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhalebe maso?

KUKHALA MASO N’KOTHANDIZA

4. Kodi kukhala maso kumatanthauza kungokhala n’kumayang’ana nthawi? Fotokozani.

4 Pali zinthu zina zimene zimafunika kuzichita pa nthawi yake. Zinthu zake ndi monga kugwira ntchito mufakitale, kukaonana ndi dokotala kapena kukakwera basi. Koma pali zinthu zina zimene munthu safunika kuyang’ana nthawi kuti azichite chifukwa akatero, zinthu zikhoza kusokonekera kapena anthu akhoza kumwalira. Zinthu zake ndi monga kuzimitsa moto kapena kupulumutsa anthu pa ngozi. Munthu amafunika kuika maganizo ake onse pa ntchitoyo osati kuyang’ana nthawi. Panopa, mapeto ayandikira kwambiri ndipo ntchito yothandiza anthu kuti apulumuke ndi yofunika kwambiri. Akhristu afunika kukhala maso koma izi sizikutanthauza kungokhala n’kumayang’ana nthawi. Sitikudziwa kuti mapeto afika liti koma kusadziwako n’kwabwino pa zifukwa zisanu. Tiyeni tikambirane zifukwazo.

5. Kodi kusadziwa tsiku ndi ola kumathandiza bwanji kuti tisonyeze zimene zili mumtima mwathu?

5 Choyamba, kusadziwa tsikulo kumatithandiza kusonyeza zimene zili mumtima mwathu. Tingati Yehova watilemekeza posatidziwitsa tsikulo. Tikutero chifukwa zimatipatsa mpata wosonyeza kuti ndife okhulupirika kwa iye mwa kufuna kwathu. N’zoona kuti timafuna kupulumuka dzikoli likamadzawonongedwa koma timatumikira Yehova chifukwa chomukonda osati kungofuna kupulumuka. (Werengani Salimo 37:4.) Timasangalala kuchita chifuniro cha Mulungu ndipo timadziwa kuti iye amatiphunzitsa n’cholinga choti zinthu zitiyendere bwino. (Yes. 48:17) Timaonanso kuti malamulo ake si olemetsa.—1 Yoh 5:3.

6. Kodi Mulungu amamva bwanji tikamamutumikira chifukwa chomukonda? N’chifukwa chiyani amamva choncho?

6 Chifukwa chachiwiri chimene tikunenera kuti kusadziwa tsiku ndi ola n’kwabwino n’chakuti kumatipatsa mwayi wokondweretsa mtima wa Yehova. Timatumikira Yehova chifukwa chomukonda osati chifukwa chodziwa tsiku la mapeto kapena kungofuna mphoto. Zimenezi zimathandiza kuti Yehova ayankhe mabodza a Satana, amene amamunyoza. (Yobu 2:4, 5; werengani Miyambo 27:11.) Popeza tikudziwa mavuto osaneneka amene Mdyerekezi wayambitsa, timafunitsitsa kukhala ku mbali ya ulamuliro wa Yehova n’kukanitsitsa ulamuliro woipa wa Satana.

7. N’chifukwa chiyani inuyo mumafunitsitsa kutumikira Mulungu ndi kuthandiza ena?

7 Chachitatu, kusadziwa tsikulo kumatilimbikitsa kukhala odzipereka potumikira Mulungu ndiponso kuthandiza ena. Masiku ano, ngakhale anthu amene sadziwa Mulungu amakhulupirira kuti dzikoli litha posachedwapa. Chifukwa choopa zam’tsogolo, iwo amakhala ndi maganizo oti, “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.” (1 Akor. 15:32) Koma ife sitichita mantha. Timapewa mtima wodzikonda. (Miy. 18:1) M’malomwake, timadzikana n’kumagwiritsa ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu ndiponso zinthu zathu pouza anthu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Werengani Mateyu 16:24.) Kutumikira Mulungu kumatisangalatsa, makamaka tikamathandiza anthu ena kuti amudziwe.

8. Perekani chitsanzo cha m’Baibulo chosonyeza kuti timafunika kudalira kwambiri Yehova ndi Mawu ake.

8 Chachinayi, kusadziwa tsikulo kumatithandiza kudalira kwambiri Yehova ndiponso kuchita khama potsatira Mawu ake. Koma anthu opanda ungwirofe timakonda kudzidalira. Paulo analangiza Akhristu anzake kuti: “Amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.” Yoswa atangotsala pang’ono kulowetsa anthu a Mulungu m’Dziko Lolonjezedwa, anthu okwana 23,000 anaphedwa chifukwa chosamvera Yehova. Ndiyeno Paulo anati: “Zinthu zimenezi . . . zinalembedwa kuti zitichenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikira.”—1 Akor. 10:8, 11, 12.

9. Kodi mavuto amatithandiza bwanji kulimbitsa chikhulupiriro ndiponso kuyandikira Mulungu?

9 Chachisanu, kusadziwa tsikulo n’kwabwino chifukwa timatha kuphunzira pa mavuto amene tikukumana nawo ndipo chikhulupiriro chathu chimalimba. (Werengani Salimo 119:71.) N’zoona kuti masiku otsiriza a dziko loipali ndi “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Tim. 3:1-5) Anthu ambiri amatida ndipo akhoza kutizunza chifukwa cha chikhulupiriro chathu. (Yoh. 15:19; 16:2) Tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumafufuza malangizo ochokera kwa Mulungu pa nthawi imene tikuzunzika. Tikamatero, chikhulupiriro chathu chimayesedwa n’kukhala cholimba kwambiri. M’malo mobwerera m’mbuyo, timayandikira kwambiri Yehova.—Yak. 1:2-4; 4:8.

10. N’chiyani chimachititsa kuti nthawi ifulumire?

10 Nthawi imafulumira kapena kuchedwa malinga ndi zimene munthu akuchita. Munthu akamatanganidwa kwambiri, nthawi imafulumira. Nafenso tikamatanganidwa ndi ntchito yosangalatsa imene Yehova watipatsa, tidzaona kuti tsikulo lafika mwamsanga. Odzozedwa ambiri apereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Tiyeni tikambirane zimene zinachitika Yesu atangoikidwa kukhala Mfumu mu 1914. Pa nthawiyo, odzozedwa ena anasonyeza kuti anali okonzeka pomwe ena sanatero.

ODZOZEDWA ASONYEZA KUTI NDI OKONZEKA

11. Chaka cha 1914 chitakwana, kodi n’chifukwa chiyani odzozedwa ena anaganiza kuti Yesu wachedwa?

11 Kumbukirani mafanizo a Yesu okhudza anamwali ndiponso akapolo amene anapatsidwa matalente. Ngati anamwaliwa ndiponso akapolowa akanadziwa nthawi yomwe mkwati kapena Ambuye wawo afike, sakanafunikira kukhala maso. Koma iwo sankadziwa nthawi ndipo ankafunika kukhalabe maso. Odzozedwa ankadziwa kuti chaka cha 1914 n’chofunika kwambiri koma sankadziwa bwinobwino zimene zichitike m’chakacho. Popeza zinthu sizinachitike mmene iwo ankaganizira, ena anaona kuti Mkwati wachedwa. M’bale wina ananena kuti, “Ambirife tinkaganiza kuti tipita kumwamba mlungu woyamba wa mwezi wa October [mu 1914].”

12. Kodi Akhristu odzozedwa ambiri anasonyeza bwanji kuti anali okhulupirika ndi anzeru?

12 Abalewa ayenera kuti anakhumudwa kwambiri kuona kuti mapeto sanafike pa nthawi imene ankayembekezera. Vuto lina n’lakuti iwo ankazunzidwa chifukwa chosalowerera nawo nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Pa nthawiyo, ntchito yolalikira inatsala pang’ono kuimiratu. Zinali ngati odzozedwa agona koma mu 1919 anadzutsidwa. Yesu anali atabwera kudzayendera kachisi wauzimu wa Mulungu. Odzozedwa ena anapezeka kuti si oyenera kupitiriza ntchito ya Ambuye wawo, Yesu Khristu. (Mat. 25:16) Iwo anali ngati anamwali opusa amene mafuta awo anaperewera. Analinso ngati kapolo waulesi amene sanafune kudzipereka pa ntchito yokhudza Ufumu. Koma odzozedwa ambiri anasonyeza kuti anali okhulupirika ndiponso ankafunitsitsa kutumikira Ambuye wawo ngakhale pa nthawi ya nkhondoyo.

13. Kodi odzozedwa anali ndi maganizo otani chitadutsa chaka cha 1914? Nanga maganizo awo ndi otani masiku ano?

13 Chitadutsa chaka cha 1914, Nsanja ya Olonda inafotokoza kuti: “Ifeyo amene tili ndi maganizo oyenera sitikhumudwa ndi mmene Mulungu amachitira zinthu. Sitinafune kuti zofuna zathu zichitike. Titaona kuti tinali kuyembekezera zinthu zolakwika mu October 1914, tinasangalala kuti Ambuye sanasinthe cholinga chawo kuti chigwirizane ndi zofuna zathu. Sitinafune kuti achite zimenezi ayi. Chomwe timafuna n’choti timvetse zolinga zake basi.” Masiku anonso, odzozedwa ndi odzichepetsa komanso odzipereka. Iwo sanena kuti Mulungu amawauzira zochita koma amafunitsitsa kuchita ntchito ya Ambuye padzikoli. Panopa, “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” kapena kuti Akhristu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi, akutsatira chitsanzo chawo chokhala maso ndiponso kuchita khama.—Chiv. 7:9; Yoh. 10:16.

TISONYEZE KUTI NDIFE OKONZEKA

14. Kodi kumvera kwambiri kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kumatiteteza bwanji?

14 Mofanana ndi odzozedwa, Akhristu a khamu lalikulu amene ali maso amamvera kwambiri kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Iwo amadziwa kuti Mulungu akugwiritsa ntchito kapoloyu kugawira chakudya chauzimu. Choncho zili ngati Akhristuwo akuwonjezera mafuta auzimu ochokera m’Mawu a Mulungu ndiponso mzimu wake. (Werengani Salimo 119:130; Yohane 16:13.) Zimenezi zimawathandiza kukhala olimba ndiponso okonzeka podikira kubwera kwa Khristu. Iwo amachita zimenezi ngakhale pokumana ndi mayesero. Mwachitsanzo, m’ndende ina yoyang’aniridwa ndi asilikali a ku Germany, abale anali ndi Baibulo limodzi lokha. Iwo ankapemphera kuti apeze chakudya china chauzimu. Kenako anamva kuti m’bale wina, amene anali atangofika kumene kundendeyo, anabwera ndi magazini atsopano a Nsanja ya Olonda. Iye anawabisa m’mwendo wake wathabwa. M’bale Ernst Wauer, yemwe anali wodzozedwa, anali kundendeyo ndipo amakumbukira zimene zinkachitika. Iye anati: “Yehova anatithandiza kwambiri kuloweza mfundo zolimbikitsa za m’magaziniwo.” Kenako, ananenanso kuti: “Masiku ano, n’zosavuta kupeza chakudya chauzimu, koma kodi timachigwiritsa ntchito? Sindikukayika kuti Yehova adzadalitsa kwambiri anthu okhulupirika amene amamudalira ndiponso kudya chakudya patebulo lake.”

15, 16. Kodi banja lina linadalitsidwa bwanji chifukwa cha khama lawo mu utumiki? Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zitsanzo ngati zimenezi?

15 A nkhosa zina amatanganidwanso kuthandiza odzozedwa pa ntchito imene Yesu wawapatsa. (Mat. 25:40) Mosiyana ndi kapolo woipa komanso waulesi wa m’fanizo la Yesu, iwo amakhala odzipereka ndipo amaika Ufumu pa malo oyamba. Mwachitsanzo, Jon ndi Masako atapemphedwa kukatumikira m’gawo la Chitchainizi ku Kenya, anaona ngati sakwanitsa. Koma ataiganizira bwino nkhaniyi ndiponso kupemphera, anavomera kupita.

16 Iwo anadalitsidwa kwambiri chifukwa cha khama lawo. Ananena kuti, “Kunoko utumiki ukuyenda bwino kwabasi.” Iwo anayambitsa maphunziro a Baibulo okwana 7. Pali zinthu zambiri zosangalatsa zimene anakumana nazo mu utumiki. Jon ndi Masako ananenanso kuti, “Tsiku lililonse timathokoza Yehova chifukwa chotilola kubwera kuno.” Pali abale ndi alongo ambirimbiri amene asankha bwino zochita pa moyo wawo ndipo amatanganidwa potumikira Mulungu, uku akudikira mapeto. Mwachitsanzo, pali anthu masauzande ambiri amene anapita ku Sukulu ya Giliyadi ndipo panopa ndi amishonale. Mutha kumva za moyo wa amishonale mu nkhani yakuti, “Timachita Zonse Zomwe Tingathe!” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2001. Nkhaniyi ikufotokoza zimene amishonale amachita tsiku ndi tsiku. Pamene mukuwerenga nkhani yosangalatsayi, nanunso ganizirani zimene mungachite kuti muwonjezere utumiki wanu. Mukatero, mudzatamanda Mulungu ndiponso mudzakhala osangalala kwambiri.

NANUNSO KHALANI MASO

17. Kodi kusadziwa tsiku ndi ola kuli ndi ubwino wotani?

17 Taona kuti kusadziwa tsiku ndi ola kuli ndi ubwino wake choncho sitikhumudwa kapena kutaya mtima. M’malomwake, timatanganidwa pochita chifuniro cha Yehova ndipo zimenezi zimatithandiza kuyandikira kwambiri Atate wathu wachikondiyu. Timasangalala kwambiri chifukwa chakuti timagwira ntchito ya Ambuye wathu mwakhama ndiponso kupewa chilichonse chimene chingatisokoneze.—Luka 9:62.

18. N’chifukwa chiyani timafuna kutumikirabe Mulungu mokhulupirika?

18 Tsiku loti Mulungu aweruze dzikoli likuyandikira kwambiri choncho tiyenera kupitiriza kumutumikira mokhulupirika. Palibe amene akufuna kukhumudwitsa Yehova kapena Yesu. Iwo asonyeza kuti amatidalira kwambiri potipatsa ntchito yamtengo wapatali m’masiku otsiriza ano ndipo timayamikira kwambiri.—Werengani 1 Timoteyo 1:12.

19. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okonzeka?

19 Kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kukhala mu Paradaiso padziko lapansi, tiyeni tizigwira mokhulupirika ntchito yolalikira ndiponso yophunzitsa anthu. Mpaka pano, sitikudziwa kuti tsiku la Yehova lifika liti ndipo sitifunikira kudziwa zimenezi. Koma tiyeni tipitirizebe kusonyeza kuti ndife okonzeka. (Mat. 24:36, 44) Timadziwa kuti tikamadalira Yehova ndi mtima wonse ndiponso kuika Ufumu pa malo oyamba, sitidzakhumudwa.—Aroma 10:11.