Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu Zimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda

Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu Zimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda

YEHOVA ndi ‘Mlangizi wathu Wamkulu.’ (Yes. 30:20) Iye amaphunzitsa ena chifukwa chowakonda. Mwachitsanzo, chifukwa choti Yehova amakonda kwambiri Yesu, ‘amamuonetsa zonse zimene iye akuchita.’ (Yoh. 5:20) Iye amatikondanso ndipo n’chifukwa chake amatipatsa “lilime la anthu ophunzitsidwa bwino” pamene tikuyesetsa kumulemekeza komanso kuthandiza anthu ena.—Yes. 50:4.

Potsanzira chikondi cha Yehova, Bungwe Lolamulira lakonza sukulu zokwana 10. Lachita zimenezi kudzera m’Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa. Sukulu zimenezi zimaphunzitsa anthu ofunitsitsa kuphunzira ndiponso amene angakwanitse. Kodi inuyo mumaona kuti sukulu zimenezi ndi umboni woti Yehova amatikonda?

Tiyeni tione sukulu zimenezi ndiponso ndemanga zimene anthu amene alowa sukuluzi anena. Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ineyo ndingatani kuti ndipindule ndi maphunziro ochokera kwa Mulungu amenewa?’

PINDULANI NDI MAPHUNZIRO OCHOKERA KWA MULUNGU

Yehova ndi “Mulungu wachikondi” ndipo amatiphunzitsa kuti tizikhala ndi moyo wosangalala. Amatithandiza kuti tizithana ndi mavuto komanso kuti tizisangalala mu utumiki wathu. (2 Akor. 13:11) Mofanana ndi ophunzira oyamba a Yesu, ndife oyenera kuthandiza ena ndiponso “kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse” zimene talamulidwa.—Mat. 28:20.

Ngakhale kuti sitingalowe sukulu zonsezi, tikhoza kulowa imodzi kapena zingapo. Tikhozanso kugwiritsa ntchito mfundo zimene timaphunzira. Kulalikira limodzi ndi atumiki a Yehova amene aphunzitsidwa bwino kungatithandizenso kuti tiziphunzitsa mogwira mtima.

Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ndi sukulu iti imene ineyo ndingalowe?’

Atumiki a Yehova amaona kuti ndi mwayi kuphunzira m’sukulu zofunikazi. Tikukhulupirira kuti maphunziro amenewa akuthandizani kuyandikira kwambiri Mulungu. Akuthandizaninso kumutumikira bwino makamaka pa ntchito yofunika kwambiri yolalikira uthenga wabwino.