Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ziphuphu—Zili Ponseponse

Ziphuphu—Zili Ponseponse

“Boma limapatsa kampani yathu ntchito yoti tigwire. Koma nthawi zambiri timayembekezera kwa miyezi iwiri kapena itatu kuti atipatse malipiro a ntchito imene tagwira. Komabe posachedwapa ndinalandira foni kuchokera kwa munthu wina wogwira ntchito m’boma. Iye anandiuza kuti akhoza kutithandiza kuti tizilandira mofulumira malipiro athu ngati titam’patsa ndalama.”—JOHN. *

KODI anthu ena anayamba akuuzani kuti mupereke ziphuphu? Mwina zimene tatchulazi sizinakuchitikireni, komabe n’kutheka kuti munavutikapo chifukwa cha ziphuphu zimene ena anachita.

Malinga ndi lipoti limene bungwe lina loona za katangale linatulutsa m’chaka cha 2011 (Transparency International *) “pa mayiko komanso madera okwana 183, mayiko ambiri anaonetsa kuti sanachite bwino pa nkhani yolimbana ndi katangale.” Komanso lipoti limene bungweli linatulutsa m’chaka cha 2009, linasonyeza kuti katangale sanasiye malo. Lipotilo linati: “Zikuonekeratu kuti palibe dziko limene simuchitika zakatangale.”

“Kuchita ziphuphu n’kugwiritsa ntchito mphamvu molakwa n’cholinga chofuna kupeza kenakake. Ziphuphu zimachititsa kuti anthu azivutika chifukwa choti anthu ena audindo sakuchita zinthu mwachilungamo.”​TRANSPARENCY INTERNATIONAL

Nthawi zina kuchita katangale kapena ziphuphu kumabweretsa mavuto aakulu. Mwachitsanzo, magazini ina inanena kuti “ziphuphu komanso kuchita zinthu mosasamala” ndi zina mwa zimene zinachititsa kuti anthu ambiri afe pa chivomezi chachikulu chimene chinachitika ku Haiti m’chaka cha 2010. Magaziniyi inanenanso kuti: “Nyumba zambiri m’dzikoli sizinamangidwe bwino chifukwa anthu amene ankayang’anira ntchitoyo ankalandira ziphuphu.”—Time.

Kodi ziphuphu zidzatha? Kuti tiyankhe funso limeneli tiyenera kudziwa kaye zimene zimachititsa anthu kuti azichita ziphuphu. Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.

^ ndime 2 Dzina lasinthidwa.

^ ndime 4 Bungweli limandandalika mmene mayiko achitira pa nkhani ya katangale potengera zakatangale zimene zimachitika m’mabungwe a boma.