Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Limbani Mtima Pokumana ndi Mavuto

Limbani Mtima Pokumana ndi Mavuto

“Mulungu ndiye pothawira pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.”—SAL. 46:1.

1, 2. Kodi ndi mavuto ati amene anthu ambiri akukumana nawo? Kodi Akhristufe timafunitsitsa kuchita chiyani?

MASIKU ano, mavuto ali ponseponse. Masoka achilengedwe amangoti achitika achitikanso. Anthufe tikuvutika kwambiri chifukwa cha zinthu monga zivomezi, tsunami, moto wolusa, kusefukira kwa madzi, kuphulika kwa mapiri ndiponso mphepo kapena mvula yamkuntho. Mavuto a m’banja komanso a munthu aliyense payekha amachititsa kuti anthu ambiri azikhala amantha komanso achisoni. N’zoona kuti “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera” tonsefe.—Mlal. 9:11.

2 Anthu a Mulungu amapitiriza kumutumikira mosangalala ngakhale kuti amakumana ndi mavuto ngati amenewa. Komabe timafunitsitsa kukhala okonzeka kuti tipirire vuto lililonse limene tingakumane nalo pamene mapeto a dzikoli akuyandikira. N’chiyani chingatithandize kupirira mavuto amenewa popanda kutaya mtima? Nanga n’chiyani chingatithandize kukhala olimba mtima pokumana ndi mavutowo?

TSANZIRANI ANTHU AMENE ANALIMBA MTIMA POKUMANA NDI MAVUTO

3. Mogwirizana ndi lemba la Aroma 15:4, kodi tingalimbikitsidwe bwanji tikakumana ndi mavuto aakulu?

3 N’zoona kuti anthu ambiri amakumana ndi mavuto kuposa m’mbuyomu, koma mavuto anayamba kalekale. Tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa anthu a Mulungu akale amene analimba mtima pokumana ndi mavuto.—Aroma 15:4.

4. Kodi Davide anakumana ndi mavuto ati? Nanga n’chiyani chimene chinamuthandiza?

4 Tiyeni tione chitsanzo cha Davide. Iye anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Pa nthawi ina, Mfumu Sauli ankafuna kumupha. Adani ankamenyana naye ndipo nthawi ina anagwira akazi ake. Anzake ena, ngakhalenso anthu am’banja mwake, anamupandukira. Komanso nthawi zina ankavutika kwambiri maganizo. (1 Sam. 18:8, 9; 30:1-5; 2 Sam. 17:1-3; 24:15, 17; Sal. 38:4-8) Baibulo limasonyeza kuti Davide anazunzika kwambiri chifukwa cha mavutowa. Koma sanamuchititse kuti asiye kukhulupirira Yehova. Iye ananena mosakayika kuti: “Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga. Ndingachitenso mantha ndi ndani?”—Sal. 27:1; werengani Salimo 27:5, 10.

5. N’chiyani chinathandiza Abulahamu ndi Sara kupirira mavuto?

5 Abulahamu ndi Sara ankakhala m’mahema kwa zaka zambirimbiri. Iwo anali alendo m’mayiko ena ndipo moyo wawo sunali wofewa. Mwachitsanzo, anavutika chifukwa cha njala ndiponso kuchitiridwa chiwawa ndi mitundu yowazungulira. (Gen. 12:10; 14:14-16) Koma kodi n’chiyani chinawathandiza kupirira zimenezi? Baibulo limanena kuti Abulahamu “anali kuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.” (Aheb. 11:8-10) Abulahamu ndi Sara ankaika maganizo awo pa zimene anali kuyembekezera osati pa mavuto awo.

6. Kodi tingatsanzire bwanji Yobu?

6 Nayenso Yobu anakumana ndi mavuto aakulu. Tangoganizirani mmene iye anamvera pamene chilichonse pa moyo wake chinasokonekera. (Yobu 3:3, 11) Yobu sankadziwa bwinobwino zimene zinachititsa mavutowo koma sanasiye kukhulupirira Mulungu. Iye anakhalabe ndi mtima wosagawanika. (Werengani Yobu 27:5.) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife.

7. Kodi Paulo anakumana ndi zinthu ziti potumikira Mulungu? Nanga n’chiyani chinamuthandiza kukhalabe wolimba mtima?

7 Nayenso Paulo ndi chitsanzo chabwino. Iye anakumana ndi ‘zoopsa mumzinda, m’chipululu ndiponso panyanja.’ Anafotokoza kuti anavutika ndi ‘njala, ludzu, kuzizidwa ndi kukhala wosavala.’ Ananenanso kuti anakhala “pamadzi akuya usiku ndi usana wonse.” Zikuoneka kuti izi zinachitika nthawi ina pamene chombo chimene anakwera chinasweka. (2 Akor. 11:23-27) Koma onani zimene Paulo ananena pambuyo poti anatsala pang’ono kufa chifukwa chotumikira Mulungu. Anati: “Zinatero kuti tisakhale ndi chikhulupiriro mwa ife tokha, koma mwa Mulungu amene amaukitsa akufa. Iye anatipulumutsadi ku chinthu choopsa, ndicho imfa, ndipo adzatipulumutsabe.” (2 Akor. 1:8-10) Si anthu ambiri amene akumana ndi mavuto ambiri ngati Paulo. Komabe ambirife tingamvetse mmene iye ankamvera ndipo tingalimbikitsidwe ndi chitsanzo chake cha kulimba mtima.

MUSATAYE MTIMA MUKAKUMANA NDI MAVUTO

8. Kodi tingamve bwanji ngati takumana ndi mavuto? Perekani chitsanzo.

8 Chifukwa cha kuchuluka kwa mavuto, anthu ambiri amataya mtima. Izi zimatha kuchitikiranso Akhristu. Mlongo wina dzina lake Lani, * yemwe ankachita utumiki wa nthawi zonse limodzi ndi mwamuna wake ku Australia, anapezeka ndi khansa ya m’mawere. Atauzidwa zimenezi, sanakhulupirire. Iye anati: “Chithandizo chimene ankandipatsa chinkandidwalitsa koopsa ndipo ndinkangodziona ngati wachabechabe.” Tsoka ndi ilo, ankafunikanso kusamalira mwamuna wake amene anali atachitidwa opaleshoni ya msana. Kodi zinthu ngati zimenezi zitakuchitikirani, mungatani?

9, 10. (a) Kodi sitiyenera kulola Satana kuchita chiyani? (b) Kodi ndi maganizo ati amene angatithandize kupirira “masautso ambiri” otchulidwa pa Machitidwe 14:22?

9 Tiyenera kukumbukira kuti Satana amafuna kugwiritsa ntchito mavuto amene takumana nawo kuti afooketse chikhulupiriro chathu. Koma tisamulole kuchita zimenezi. Lemba la Miyambo 24:10 limati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” Kusinkhasinkha zitsanzo za m’Baibulo za anthu ngati amene takambiranawa kungatithandize kulimba mtima pokumana ndi mavuto.

10 Tiyeneranso kukumbukira kuti sitingachotse mavuto athu onse panopa. M’malomwake, tiziyembekezera kukumana nawo. (2 Tim. 3:12) Pajatu, lemba la Machitidwe 14:22 limati: “Tiyenera kukumana ndi masautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.” Choncho tisamakhumudwe kwambiri tikakumana ndi mavuto. Koma tiziona kuti mavutowo akutipatsa mwayi wosonyeza kulimba mtima chifukwa chokhulupirira kuti Mulungu atithandiza.

11. Kodi tingatani kuti mavuto athu asatifooketse?

11 Tiyenera kumaganizira zinthu zolimbikitsa osati zofooketsa. Mawu a Mulungu amanena kuti: “Mtima wachimwemwe umapangitsa nkhope kusangalala, koma chifukwa cha kupweteka kwa mtima munthu sasangalala.” (Miy. 15:13) Nawonso azachipatala amanena kuti kuganizira zinthu zolimbikitsa kumathandiza kuti tikhale athanzi. Mwachitsanzo, odwala ena amapatsidwa mankhwala oti si enieni koma amayamba kuchira chifukwa chongoganiza kuti alandira thandizo. Koma ngati atauzidwa kuti mankhwala amene akulandira amudwalitsa, amayambadi kudwala kwambiri. Choncho, kuganizira kwambiri mavuto amene sitingawathetse kukhoza kutifooketsa. Koma Yehova sapereka mankhwala abodza. Pakagwa tsoka, iye amatithandizadi potilimbikitsa ndi Mawu ake, Akhristu anzathu komanso mzimu woyera. Kuganizira zinthu zimenezi n’kumene kungatilimbikitse. M’malo moganizira mavuto athu, tiziona zimene tingachite kuti tithane nawo n’kumaganizira zinthu zabwino zimene zikuchitika pa moyo wathu.—Miy. 17:22.

12, 13. (a) N’chiyani chathandiza atumiki a Mulungu kupirira masoka? Perekani chitsanzo. (b) Kodi nthawi ya masoka imathandiza bwanji anthu kudziwa chinthu chofunika kwambiri pa moyo?

12 Chaposachedwapa, m’mayiko ambiri mwachitika masoka achilengedwe. Koma abale ambiri m’mayiko oterewa sanafooke. Komatu sizinali zophweka. Chakumayambiriro kwa chaka cha 2010, ku Chile kunachitika chivomezi champhamvu ndipo madzi ambirimbiri anasefukira. Nyumba ndi katundu za abale ambiri zinawonongedwa ndipo njira zimene ena ankapezera ndalama zinasokonekera. Koma abale athu anapitirizabe kutumikira Yehova. M’bale wina dzina lake Samuel, yemwe nyumba yake inawonongedwa, anati: “Ngakhale kuti zinthu zinali zitavuta kwambiri, ine ndi mkazi wanga sitinasiye kupita ku misonkhano ndiponso kulalikira. Ndikuona kuti zimenezi n’zimene zinatithandiza kuti tisataye mtima.” Mofanana ndi anthu ena ambiri, iwo anangoiwala za mavutowo n’kumapitiriza kutumikira Yehova.

13 Mu September 2009, ku Philippines kunagwa mvula yamkuntho ndipo madzi anasefukira m’madera ambiri a mumzinda wa Manila. Munthu wina wachuma, amene katundu wake wambiri anawonongeka, anati: “Madzi osefukira anachititsa kuti olemera ndi osauka afanane chifukwa onse ankavutika.” Apa n’zoonekeratu kuti malangizo a Yesu ndi othandiza. Iye anati: “Unjikani chuma chanu kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge, ndiponso kumene mbala sizingathyole n’kuba.” (Mat. 6:20) Ndalama ndi katundu zikhoza kutha mosavuta. Choncho munthu akamadalira zinthu zimenezi, adzangogwiritsidwa fuwa la moto basi. Koma ndi nzeru kuika kutumikira Yehova pamalo oyamba chifukwa sangatisiye ngakhale titakumana ndi mavuto.—Werengani Aheberi 13:5, 6.

ZIFUKWA ZOTICHITITSA KUKHALA OLIMBA MTIMA

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala olimba mtima?

14 Yesu anauza ophunzira ake kuti pa nthawi ya kukhalapo kwake padzakhala mavuto koma anati: “Musadzachite mantha.” (Luka 21:9) Tiyenera kukhala olimba mtima chifukwa Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu yathu, komanso Yehova, amene analenga zinthu zonse, akutithandiza. Paulo analimbikitsa Timoteyo pomuuza kuti: “Mulungu sanatipatse mzimu wamantha, koma wamphamvu, wachikondi, ndi woti tiziganiza bwino.”—2 Tim. 1:7.

15. Kodi atumiki ena a Mulungu ananena zinthu ziti zosonyeza kuti ankamudalira? Nanga tingawatsanzire bwanji?

15 Tiyeni tione zinthu zina zimene atumiki a Mulungu olimba mtima ananena. Davide anati: “Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa. Mtima wanga umam’khulupirira. Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwera.” (Sal. 28:7) Paulo anasonyeza kulimba mtima ponena kuti: “Tikugonjetsa zinthu zonsezi kudzera mwa iye amene anatikonda.” (Aroma 8:37) Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anasonyeza kuti anali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Iye anati: “Sindikhala ndekha, chifukwa Atate ali ndi ine.” (Yoh. 16:32) Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo zimenezi? Anthu onsewa anasonyeza kuti ankadalira Yehova. Ifenso tikamadalira kwambiri Mulungu tingakhale olimba mtima pokumana ndi vuto lililonse.—Werengani Salimo 46:1-3.

ZINTHU ZOTITHANDIZA KUKHALABE OLIMBA MTIMA

16. Kodi kuphunzira Mawu a Mulungu kungatithandize bwanji?

16 Sikuti Akhristufe timakhala olimba mtima chifukwa chodzidalira. Koma timalimba mtima chifukwa chakuti timadziwa Mulungu ndiponso kumudalira. Kuphunzira Baibulo kumatithandiza kuchita zimenezi. Mlongo wina amene amavutika maganizo anafotokoza zimene zimamuthandiza. Iye anati, “Ndimakonda kuwerenga mobwerezabwereza malemba amene amandilimbikitsa kwambiri.” Tiyeneranso kutsatira malangizo oti tizichita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse. Kodi inu mukuchita zimenezi? Kuphunzira patokha komanso monga banja kungatithandize kukhala ndi maganizo amene wamasalimo anali nawo. Iye anati: “Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu! Ndimasinkhasinkha chilamulocho tsiku lonse.”—Sal. 119:97.

17. (a) N’chiyani chingatithandize kukhalabe olimba mtima? (b) Tchulani nkhani ya mbiri ya moyo imene inakuthandizani.

17 Tilinso ndi mabuku ofotokoza Baibulo amene amatithandiza kudalira Yehova. Mwachitsanzo, nkhani zofotokoza mbiri ya moyo wa anthu zimalimbikitsa abale ambiri. Mlongo wina wa ku Asia, amene amadwala matenda ena a maganizo, anasangalala kwambiri atawerenga mbiri ya m’bale wina. M’baleyo pa nthawi ina anali mmishonale ndipo anapeza njira yomuthandiza kupirira matenda omwewa. Mlongoyu analemba kuti, “Nkhaniyi inandithandiza kumvetsa vuto langa komanso inandipatsa chiyembekezo.”

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera pafupipafupi?

18 Chinthu china chimene chingatithandize ndi pemphero. Pemphero limathandiza pa vuto lililonse. Pofotokoza mmene limathandizira, mtumwi Paulo anati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Kodi timapemphera pafupipafupi kuti tipeze mphamvu pa nthawi imene tapanikizika ndi mavuto? M’bale wina wa ku Britain dzina lake Alex, amene wakhala akuvutika maganizo kwa nthawi yaitali, anati: “Kulankhula ndi Yehova m’pemphero ndiponso kuwerenga Baibulo kuti ndimve mawu ake n’zimene zandithandiza kwambiri pa vuto langali.”

19. Kodi tiyenera kuona bwanji misonkhano yathu?

19 Kusonkhana ndi Akhristu anzathu kungatithandizenso kupirira. Wamasalimo wina analemba kuti: “Ndimalakalaka mabwalo a Yehova ndipo ndafookeratu chifukwa cholakalaka mabwalowo.” (Sal. 84:2) Kodi ifenso timalakalaka kusonkhana? Lani amene tamutchula kale uja ananena mmene ankaonera misonkhano. Iye anati: “Ndinkadziwa kuti ndiyenera kupita ku misonkhano basi. Yehova sangandithandize kupirira ngati ndimajomba ku misonkhano.”

20. Kodi kulalikira kungatithandize bwanji?

20 Chinthu chinanso chimene chingatithandize ndi kulalikira mwakhama. (1 Tim. 4:16) Mlongo wina ku Australia, amene anali ndi mavuto ambirimbiri, anati: “Sindinkafuna kulalikira ngakhale pang’ono. Koma mkulu wina mu mpingo anandipempha kuti ndipite naye mu utumiki ndipo ndinapita. Yehova ayenera kuti anali kundithandiza. Nthawi iliyonse imene ndinkalowa mu utumiki, ndinkasangalala kwambiri.” (Miy. 16:20) Anthu ambiri azindikira kuti akamathandiza anthu ena kukhulupirira Yehova, amalimbitsanso chikhulupiriro chawo. Izi zimawathandiza kuiwala mavuto awo n’kumaganizira zinthu zofunika kwambiri.—Afil. 1:10, 11.

21. Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani tikamakumana ndi mavuto?

21 Yehova wapereka zinthu zambiri zotithandiza kulimba mtima. Tiyenera kugwiritsa ntchito zinthu zimene watipatsazi. Tizisinkhasinkhanso zitsanzo za atumiki a Mulungu olimba mtima n’kumawatsanzira. Tikamachita zimenezi, sitidzataya mtima pokumana ndi mavuto. Pamene mapeto akuyandikira, tidzakumana ndi mavuto ambiri. Koma tingakhale ndi maganizo a Paulo amene anati: “Timagwetsedwa pansi, koma sitiwonongedwa. . . . Sitikubwerera m’mbuyo.” (2 Akor. 4:9, 16) Yehova angatithandize kukhala olimba mtima pokumana ndi mavuto.—Werengani 2 Akorinto 4:17, 18.

^ ndime 8 Mayina ena asinthidwa.