Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi mawu a Yesu pa Mateyu 19:10-22 amasonyeza kuti anthu amene amasankha kusakhala pa banja amalandira mphatsoyi m’njira yapadera?

Choyamba, tiyeni tione zimene zinachititsa Yesu kunena mawuwa. Afarisi anabwera kudzamufunsa nkhani yothetsa banja ndipo Yesu anawauza lamulo la Yehova pa nkhaniyi. Iye anawasonyeza kuti Chilamulo chinkalola kuti mwamuna alembe kalata yothetsera ukwati ngati wapeza kuti mkazi wake ali ndi “vuto linalake,” koma si zimene Mulungu ankafuna pa chiyambi. (Deut. 24:1, 2) Kenako Yesu anati: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”—Mat. 19:3-9.

Ophunzira ake atamva zimenezi, anati: “Ngati zili choncho kwa munthu ndi mkazi wake, ndiyetu ndi bwino kusakwatira.” Powayankha, Yesu anati: “Si onse amene angathe kuchita zimenezi, koma okhawo amene ali ndi mphatso. Pakuti ena sakwatira chifukwa chakuti anabadwa choncho kuchokera m’mimba mwa mayi awo, ndipo ena chifukwa chakuti anafulidwa ndi anthu. Koma pali ena amene safuna kukwatira chifukwa cha ufumu wakumwamba. Amene angathe kuchita zimenezi achite.”—Mat. 19:10-12.

Pali anthu ena amene sakhala pa banja chifukwa chakuti ali ndi vuto lobadwa nalo, anafulika mwangozi kapena anachita kufulidwa. Ndiye pali anthu ena amene amachita kusankha kuti asakhale pa banja. Ngakhale kuti akhoza kukhala pa banja, iwo amadziletsa kuti asakwatire kapena kukwatiwa “chifukwa cha ufumu wakumwamba.” Mofanana ndi Yesu, iwo amasankha kusakhala pa banja n’cholinga choti agwire ntchito ya Ufumu popanda zododometsa. Sikuti amabadwa ndi mphatso yosakhala pa banja kapena kupatsidwa mphatsoyi. Iwo amangoona kuti angathe kuchita zimenezi moti amasankha mwadala kuti asakwatire kapena kukwatiwa.

Mtumwi Paulo anathirira ndemanga mawu a Yesu amenewa. Iye anafotokoza kuti ngakhale kuti Akhristu apabanja ndiponso amene sali pa banja akhoza kutumikira Mulungu bwinobwino, anthu amene sali pa banja ndipo ndi ‘okhazikika mumtima’ amachita “bwino koposa.” N’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Anthu apabanja amafunikanso kugwiritsa ntchito nthawi ndiponso mphamvu zawo posamalira ndiponso kukondweretsa mwamuna kapena mkazi wawo. Koma Akhristu amene sali pa banja akhoza kugwiritsa ntchito nthawi ndiponso mphamvu zawo zonse potumikira Ambuye. Iwo amaona kuti kusakhala pa banja ndi “mphatso” yochokera kwa Mulungu.—1 Akor. 7:7, 32-38.

Choncho Malemba sanena kuti Mkhristu amalandira mphatso yokhala wosakwatira kapena wosakwatiwa m’njira yapadera. M’malomwake, munthu amasankha yekha zimenezi chifukwa chofuna kutumikira Mulungu popanda zododometsa. Anthu ambiri masiku ano amasankha kusakhala pa banja pa chifukwa chimenechi. Tingachite bwino kulimbikitsa anthu oterewa.