Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kale Lathu

‘Anthu Anali Asanamvepo Uthenga Wabwino Chonchi’

‘Anthu Anali Asanamvepo Uthenga Wabwino Chonchi’

M’BALE GEORGE NAISH anaona mulu wa mitengo yaitali mamita 18 pamalo amene ankasunga zida zankhondo mumzinda wa Saskatoon ku Saskatchewan m’dziko la Canada. Iye anafunsa kuti, “Kodi zonsezi n’zachiyani?” Anauzidwa kuti zinali zomangira nsanja pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Pa nthawi inayake, m’baleyo ananena kuti, “Nditangoona, ndinaganiza zozigwiritsa ntchito kukonza nsanja za siteshoni ya wailesi.” Ananenanso kuti, “Aka kanali koyamba kuganiza zogwiritsa ntchito wailesi polalikira.” Patangopita chaka chimodzi chokha, tinatsegula siteshoni ya wailesi yotchedwa CHUC mu 1924. Siteshoni imeneyi inali imodzi mwa masiteshoni oyambirira kuulutsa nkhani zachipembedzo ku Canada.

Canada ndi dziko lalikulu moti lingafanane ndi Ulaya. Choncho zinali zothandiza kwambiri kugwiritsa ntchito wailesi polalikira. Mlongo Florence Johnson amene ankagwira ntchito ku siteshoniyi anati, “Kulalikira pa wailesi kunathandiza kwambiri kuti anthu amene sitikanatha kuwapeza amve choonadi. Popeza kuti mawailesi anali atangoyamba kumene, anthu ankachita chidwi kwambiri ndi nkhani ina iliyonse imene inkaulutsidwa.” Pofika mu 1926, Mboni za Yehova, zomwe pa nthawiyo zinkatchedwa Ophunzira Baibulo, zinali ndi masiteshoni a wailesi m’mizinda inayi ku Canada. *

Kodi ndi zinthu ziti zimene zinkaulutsidwa pa wailesi? Abale ndi alongo ochokera ku mipingo yapafupi ankaimba nyimbo ndipo ena ankagwiritsa ntchito zida zoimbira. Abale ankakamba nkhani ndiponso ena ankakambirana za Baibulo. Mlongo Amy Jones amene ankachita nawo zimenezi anati, “Nthawi zina mu utumiki ndikakumana ndi anthu n’kuwauza dzina langa, ankanena kuti, ‘Ndakukumbukirani, ndinakumvani pa wailesi.’”

Ophunzira Baibulo mumzinda wa Halifax ku Nova Scotia anayamba njira yatsopano youlutsira uthenga pa wailesi. Ankalola anthu kuimba foni n’kufunsa mafunso okhudza Baibulo. M’bale wina anati, “Anthu ambirimbiri ankaimba foni moti zinkavuta kuyankha onse.”

Mofanana ndi zimene zinkachitikira mtumwi Paulo, anthu ena ankamvetsera uthenga wa Ophunzira Baibulo koma ena ayi. (Mac. 17:1-5) Mwachitsanzo, Hector Marshall atamva Ophunzira Baibulo akunena za buku lakuti Studies in the Scriptures, anaitanitsa mavoliyumu 6. Pa nthawi ina, iye analemba kuti, “Ndinkaganiza kuti mabukuwo azindithandiza kukaphunzitsa ku Sande Sukulu.” Koma Hector atangomaliza kuwerenga voliyumu yoyamba, anasiya tchalitchi chake. Iye ankalalikira mwakhama ndipo anatumikira Yehova mokhulupirika mpaka pamene anamwalira mu 1998. Tsiku lina pa wailesi, anaulutsa nkhani yakuti “Ufumu Ndi Umene Udzakonze Zinthu Padzikoli.” Tsiku lotsatira kum’mawa kwa Nova Scotia, munthu wina yemwe anali mkulu wa asilikali, dzina lake J. A. MacDonald, anauza m’bale wina kuti: “Anthu a kuno kuchilumba cha Cape Breton anamva dzulo uthenga wanu. Anali asanamvepo uthenga wabwino chonchi.”

Koma atsogoleri a matchalitchi anakwiya. Akatolika ena ku Halifax anaopseza kuti aphulitsa siteshoni imene Ophunzira Baibulo amaulutsira mapulogalamu awo. Chifukwa cholimbikitsidwa ndi atsogoleri a zipembedzo, mu 1928 boma linalengeza mwadzidzidzi kuti silidzaperekanso malaisensi kwa Ophunzira Baibulo kuti azipitiriza kuulutsa zinthu pa wailesi yawo. Chifukwa cha zimenezi, abale anayamba kufalitsa kapepala ka mutu wakuti Kodi Mwini Mphepo Ndi Ndani? Komabe akuluakulu a boma anakanabe kuwapatsa malaisensi.

Kodi zimenezi zinabweza m’mbuyo kagulu ka atumiki a Yehova ku Canada? Mlongo Isabel Wainwright anati: “Poyamba, zinkaoneka ngati adani amenewa apambana. Koma ndinadziwa kuti Yehova akanafuna akanatha kulepheretsa zofuna zawo. Choncho tinangoona kuti Yehova akufuna kuti tisinthe n’kuyamba njira ina yabwino kwambiri yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu.” M’malo modalira kwambiri kulalikira pa wailesi, Ophunzira Baibulo ku Canada anayamba kudalira kwambiri njira yopita kunyumba za anthu kukawalalikira. Koma pa nthawi imene wailesi inkagwiritsidwa ntchito, inathandiza kwambiri poulutsa uthenga wabwino.—Nkhaniyi yachokera ku Canada.

^ ndime 4 Abale ankalipiranso ndalama ku masiteshoni ena a wailesi ku Canada kuti aziwapatsa nthawi yoti alalikire.