Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Ena Amachita pa Khirisimasi Pofuna Kusangalala

Zimene Ena Amachita pa Khirisimasi Pofuna Kusangalala

“N’zosavuta kutengeka ndi zimene anthu amachita pa nthawi ya Khirisimasi. Komabe pa nthawi ya holide ngati imeneyi pamakhala zambiri zochita moti anthu sakhalanso ndi nthawi yokwanira yocheza ndi achibale komanso anzawo. Choncho m’malo moti tisangalale pa nthawiyi, timakhala otanganidwa kwambiri ndipo zimangotiwonjezera mavuto.”—BRAD HENRY, BWANAMKUBWA WAKALE WA KU OKLAHOMA [U.S.A.] ANANENA ZIMENEZI PA DECEMBER 23, 2008.

NTHAWI ya Khirisimasi ikamayandikira pamakhala nyimbo, mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV zimene zimapangitsa anthu kuona kuti nthawiyi ndi yosangalatsa. Kodi mukuganiza kuti chinthu chofunika kwambiri kuchita pa Khirisimasi n’chiyani? Kapena kodi ndi

  • Kukumbukira Yesu Khristu?

  • Kupatsana mphatso?

  • Kuthandiza osowa?

  • Kukachezera achibale?

  • Kukhala mwamtendere?

Monga mmene mawu a bwanamkubwa amene ali kumanzerewa akusonyezera, anthu ambiri amalephera kuchita zimene ankafuna pa nthawi ya Khirisimasi. Pa nthawiyi anthu ambiri amakhala otanganidwa kwambiri, ankhawa komanso amawononga ndalama zambiri kugula zinthu. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti anthu sangapeze zochita zina mkati mwa chaka zimene zingachititse kuti azikhala osangalala?

Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyenera kukumbukira Yesu Khristu, kukhala owolowa manja, kuthandiza osowa komanso kuchezera achibale. Komanso limatiphunzitsa kuti tiyenera kukhala amtendere. Choncho m’malo mokambirana chifukwa chimene anthu ena sakondwerera Khirisimasi, * m’nkhanizi tikambirana mafunso otsatirawa:

  • Kodi n’chifukwa chiyani anthu ambiri amaona kuti n’koyenera kukondwerera Khirisimasi?

  • Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu asamasangalale pa nthawi ya Khirisimasi ngati mmene amafunira?

  • Ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene zathandiza anthu ambiri kukhala osangalala ngakhale kuti sakondwerera Khirisimasi?

^ ndime 10 Kuti mudziwe mfundo za m’Malemba zimene zimapangitsa anthu ena kuti asamachite Khirisimasi, onani nkhani yakuti, “Zimene Owerenga Amafunsa—N’chifukwa Chiyani Anthu Ena Sachita Nawo Khirisimasi?”