Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Yesu analakwitsa ponena kuti mchere umatha mphamvu?

Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mchere watha mphamvu, kodi mphamvu yake angaibwezeretse motani? Sungagwire ntchito iliyonse koma ungafunike kuutaya kunja kumene anthu akaupondaponda.” (Mateyu 5:13) Mchere umathandiza kuti zinthu zisawonongeke. Choncho poyerekezera otsatira ake ndi mchere, Yesu ankatanthauza kuti ophunzirawo ayenera kuteteza anthu ena kuti akhalebe pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kuti apitirize kukhala ndi khalidwe labwino.

Ponena za mawu a Yesu amenewa, buku lina linanena kuti: “Mchere wa m’Nyanja Yakufa unkasakanikirana ndi zinthu zina. Choncho mcherewu ukanyowa, unkasungunuka ndipo zinkangotsala ndi zinthu zinazo zomwe zinalibe mphamvu ya mchere.” (The International Standard Bible Encyclopedia) Motero n’zomveka kuti Yesu anasonyeza kuti zotsalazo ‘sizingagwire ntchito iliyonse koma zingafunike kuzitaya kunja.’ Bukuli linanenanso kuti: “Ngakhale kuti mchere wa m’Nyanja Yakufa sunali wabwino kwenikweni poyerekeza ndi mchere umene unkapezeka m’nyanja zina, mcherewu unali wosavuta kupeza chifukwa unkapezeka m’mbali mwa nyanja ndipo n’chifukwa chake anthu a ku Palesitina ankaugwiritsa ntchito kwambiri.”

N’chifukwa chiyani kutaya ndalama ya dalakima imene Yesu anatchula m’fanizo lina inali nkhani yaikulu pa nthawiyo?

Yesu ananena fanizo la mayi amene anali ndi ndalama zokwana madalakima 10 ndipo imodzi itamutayika, anayatsa nyale n’kuyamba kusesa m’nyumba monse mpaka anapeza ndalamayo. (Luka 15:8-10) M’nthawi ya Yesu, ndalama ya dalakima inali yokwana malipiro a tsiku lonse. Choncho munthu ankaona kuti imeneyi inali ndalama yambiri yoti itatayika sangangoisiya osaifufuza. Komabe ndalama zoterezi zinali zofunikanso pa zifukwa zina.

Mabuku ena amasonyeza kuti nthawi zambiri akazi ankagwiritsa ntchito ndalamazi ngati zokongoletsera. N’kuthekanso kuti ndalama imene Yesu anatchula m’fanizo lakeli inali yomwe akazi ankaiona kuti ndi cholowa cha banja lawo kapena imene ankalandira ngati malowolo. Kaya zinalidi choncho kapena ayi, mkazi akataya ndalama yake imodzi ankada nkhawa ndipo ankayesetsa kuti aipeze.

Komanso nyumba za anthu wamba za m’nthawi ya Yesu zinkakhala zopanda mawindo okwanira ndipo zimenezi zinkapangitsa kuti muzikhala mdima. Kuwonjezera pamenepo, nthawi zambiri pansi pa nyumbazi ankayalapo mapesi. Choncho ngati ndalama yagwera m’nyumbamo, zinkakhala zovuta kuipeza. Katswiri wina wa Baibulo anati: “Motero munthu akataya chinthu chaching’ono, ngati ndalama, m’nyumba zotere, ankafunika kuyatsa nyale komanso kusesa nyumba yonse kuti apeze chinthucho.”