Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Cholowa Chathu Chochokera kwa Mulungu

Cholowa Chathu Chochokera kwa Mulungu

“Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova.”—YES. 54:17.

1. Kodi Yehova wateteza chiyani kuti anthu apindule?

YEHOVA, yemwe ndi “Mulungu wamoyo ndi wamuyaya,” wateteza uthenga wake wopatsa moyo kuti uthandize anthu. Uthengawo sudzatha chifukwa “mawu a Yehova amakhala kosatha.” (1 Pet. 1:23-25) Timayamikira kwambiri kuti mwachikondi, Yehova wateteza uthenga wake m’Baibulo.

2. Kodi Mulungu wateteza chiyani m’Mawu ake kuti anthu agwiritse ntchito?

2 M’Mawu ake, Mulungu wateteza dzina lake limene analisankha yekha kuti anthu ake aligwiritse ntchito. Malemba amatchula “Yehova Mulungu” koyamba m’nkhani “yofotokoza mmene kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera.” (Gen. 2:4) Dzina la Mulungu linalembedwa kambirimbiri pamiyala yomwe analembapo Malamulo Khumi. Mwachitsanzo, lamulo loyamba limayamba ndi mawu akuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wako.” (Eks. 20:1-17) Dzina la Mulungu lakhala lilipobe mpaka pano. Zili choncho chifukwa Yehova Ambuye Wamkulu Koposa anateteza Mawu ake ndiponso dzina lake ngakhale kuti Satana wakhala akuyesetsa kuti lisapezeke.—Sal. 73:28.

3. Ngakhale kuti zipembedzo zonyenga zili paliponse, kodi Mulungu wateteza chiyani?

3 Yehova watetezanso choonadi m’Baibulo lomwe ndi Mawu ake. Timayamikira kwambiri kuti Mulungu watipatsa kuwala ndiponso choonadi ngakhale kuti zipembedzo zonyenga zili paliponse m’dzikoli. (Werengani Salimo 43:3, 4.) Anthu ambirimbiri akuyenda mu mdima koma ife tikuyendabe mosangalala m’kuunika kumene Mulungu watipatsa.—1 Yoh. 1:6, 7.

TILI NDI CHOLOWA CHAMTENGO WAPATALI

4, 5. Kodi takhala ndi mwayi waukulu uti kuyambira m’chaka cha 1931?

4 Mayiko amakhala ndi zinthu zimene tinganene kuti ndi cholowa. Mwachitsanzo, amakhala ndi chikhalidwe, zikhulupiriro ndiponso miyambo zomwe m’badwo uliwonse umapatsira unzake ndipo zakhalapo kwa zaka zambirimbiri.  Akhristufenso tili ndi cholowa chamtengo wapatali kwambiri. Cholowa chathu chochokera kwa Mulungu ndi zinthu monga kukhala ndi mwayi wodziwa Mawu a Mulungu molondola komanso kumvetsa bwino choonadi chonena za iyeyo ndiponso zolinga zake. Cholowacho chimaphatikizaponso mwayi wina wapadera kwambiri.

Tinasangalala kwambiri kulandira dzina lakuti Mboni za Yehova pa msonkhano wathu mu 1931

5 Mwayi umenewu tinayamba kukhala nawo kuyambira pa msonkhano umene unachitika mu 1931 mumzinda wa Columbus ku Ohio, m’dziko la United States. Timapepala tosonyeza pulogalamu ya msonkhanowu analembapo zilembo izi “JW.” Mlongo wina anati: “Anthu ankanena mawu osiyanasiyana omwe ankaganiza kuti zilembozo zikuimira.” M’mbuyomu, tinkadziwika ndi dzina lakuti Ophunzira Baibulo. Koma Lamlungu, July 26, 1931 pa msonkhanowu, tinavomereza chigamulo chakuti tizidziwika ndi dzina lakuti Mboni za Yehova. Choncho zilembo zakuti “JW” zinkaimira dzinali m’Chingelezi. Tinali osangalala kwambiri kulandira dzina lochokera m’Malemba limeneli. (Werengani Yesaya 43:12.) M’bale wina anati: “Sindidzaiwala zimene zinachitika pa msonkhanowu. Tinavomereza dzinali mosangalala ndiponso kuwombera m’manja kwambiri.” Anthu a m’dzikoli anadana nalo kwambiri dzina limeneli. Koma ife tikuona kuti Yehova watidalitsa kwambiri chifukwa watilola kuligwiritsa ntchito kwa zaka zoposa 80 tsopano. Ndithudi, ndi mwayi waukulu zedi kukhala Mboni za Yehova.

6. Kodi mbali ina ya cholowa chathu chochokera kwa Mulungu ndi iti?

6 Mbali inanso ya cholowa chathu chochokera kwa Mulungu ndi mfundo zambiri zoona ndiponso zamtengo wapatali zochokera kwa atumiki akale. Mwachitsanzo, taganizirani za Abulahamu, Isaki ndiponso Yakobo. Anthu amenewa ayenera kuti ankakambirana ndi mabanja awo zimene angachite kuti asangalatse Yehova. M’pake kuti Yosefe anakana kuchita chiwerewere chifukwa sankafuna ‘kuchimwira Mulungu.’ (Gen. 39:7-9) Nawonso Akhristu ankaphunzitsa anzawo miyambo pochita kuwauza kapena kuwapatsa chitsanzo kuti azitsatira. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anapereka ku mipingo yachikhristu malangizo okhudza Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. (1 Akor. 11:2, 23) Masiku ano, m’Baibulo timapezamo malangizo okhudza kulambira Mulungu “motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.” (Werengani Yohane 4:23, 24.) Yehova wapereka Baibulo kuti lithandize anthu onse. Koma atumiki a Mulungufe timaliyamikira kwambiri kuposa aliyense.

7. Kodi ndi lonjezo liti lomwe ndi mbali ina ya cholowa chathu?

7 Mbali inanso ya cholowa chathu ndi nkhani za m’mabuku athu a posachedwapa zimene zimatitsimikizira kuti ‘Yehova ali kumbali yathu.’ (Sal. 118:7) Nkhanizi zimatithandiza kukhala olimba m’chikhulupiriro ngakhale pamene tikuzunzidwa. Mbali yolimbikitsa kwambiri ya cholowa chathu chochokera kwa Mulungu ndi lonjezo lakuti: “‘Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana, ndipo lilime lililonse limene lidzalimbane  nawe pamlandu udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndipo chilungamo chawo n’chochokera kwa ine,’ akutero Yehova.” (Yes. 54:17) Choncho palibe chida cha Satana chimene chingativulaze kwamuyaya.

8. Kodi tiphunzira chiyani m’nkhani ino ndiponso yotsatira?

8 Satana wakhala akuyesetsa kuwononga Mawu a Mulungu, kuthetsa dzina la Yehova ndiponso kubisa choonadi. Koma Yehova wamulepheretsa kuchita zimenezi. M’nkhani ino ndiponso yotsatira, tiphunzira (1) mmene Mulungu watetezera Mawu ake, (2) dzina lake ndiponso (3) mmene watiphunzitsira choonadi komanso kuchiteteza.

YEHOVA WATETEZA MAWU AKE

9-11. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Baibulo latetezedwa.

9 Yehova wateteza Mawu ake ngakhale kuti anthu ambiri ayesetsa kuwawononga. Buku lina limati: “Mu 1229 tchalitchi cha Katolika chinaletsa anthu wamba kugwiritsa ntchito Mabaibulo a m’zilankhulo zawo. Iwo anachita zimenezi chifukwa choopa anthu amene ankawatsutsa. . . . Pa msonkhano umene unachitikira ku Tarragona, m’dziko la Spain, m’chaka cha 1234, motsogoleredwa ndi James I kugwiritsa ntchito Mabaibulo a zilankhulo zina kunaletsedwa. . . . . Mu 1559 apapa analowerera nkhaniyi pamene Paul IV analemba kuti anthu sayenera kusindikiza kapena kukhala ndi Mabaibulo a zilankhulo zawo popanda chilolezo.”—Catholic Encyclopedia.

10 Ngakhale kuti anthu anayesetsa kuwononga Baibulo, Yehova waliteteza. Mwachitsanzo, John Wycliffe limodzi ndi anzake anatulutsa Baibulo loyamba m’Chingelezi cha m’ma 1382. Munthu winanso amene anamasulira Baibulo ndi William Tyndale, yemwe anaphedwa m’chaka cha 1536. Iye atamangiriridwa pamtengo, anthu amati anafuula kuti, “Ambuye, tsegulani maso a mfumu ya England.” Kenako anam’manga khosi ndi chingwe n’kumupha ndipo atatero, anamuwotcha.

11 N’zoona kuti Mulungu wateteza Mawu ake. Mwachitsanzo, m’chaka cha 1535, Baibulo lachingelezi lolembedwa ndi Miles Coverdale linatulutsidwa. Iye anagwiritsa ntchito Malemba Achigiriki ndiponso mabuku a Genesis mpaka 2 Mbiri a m’Malemba Achiheberi m’Baibulo lolembedwa ndi Tyndale. Koma anamasulira mbali zina za m’Malemba kuchokera ku Chilatini ndiponso pogwiritsa ntchito Baibulo lachijeremani lolembedwa ndi Martin Luther. Masiku ano, tili ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika ndipo timaliyamikira kwambiri chifukwa ndi losavuta kumva, silinasinthidwe ndiponso ndi lothandiza kwambiri mu utumiki wathu. Tikusangalala kwambiri kuti palibe chiwanda kapena munthu amene angalepheretse Yehova kuteteza Mawu ake.

YEHOVA WATETEZA DZINA LAKE

Anthu ngati Tyndale analolera kuphedwa chifukwa cha Mawu a Mulungu

12. Kodi Baibulo la Dziko Latsopano lathandiza bwanji kuteteza dzina la Mulungu?

12 Yehova Mulungu wateteza dzina lake m’Baibulo. Baibulo la Dziko Latsopano likusonyeza zimenezi. Komiti ya anthu odzipereka amene  anamasulira Baibuloli analemba m’mawu ake oyamba kuti: “Chinthu chapadera kwambiri m’Baibulo lino n’chakuti tabwezeretsa dzina la Mulungu m’malo ake oyenerera. Tachita zimenezi pogwiritsa ntchito dzina la Mulungu limene pa Chichewa limadziwika bwino kwambiri kuti ‘Yehova.’ M’Baibuloli, dzinali likupezeka maulendo 6,973 m’Malemba Achiheberi ndiponso maulendo 237 m’Malemba Achigiriki.” Baibulo la Dziko Latsopano lonse lathunthu kapena mbali zake, tsopano likupezeka m’zilankhulo zoposa 116 ndipo Mabaibulo amene asindikizidwa ndi oposa 178,545,862.

13. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu adziwa dzina la Mulungu kuyambira pamene analengedwa?

13 Anthu adziwa dzina la Mulungu kuyambira pamene analengedwa. Adamu ndi Hava ankadziwa dzinali ndipo iwo ankadziwa bwino kutchula kwake. Chigumula chitachitika, Hamu anachita zonyoza Nowa, atate ake. Atate akewo anati: “Adalitsike Yehova, Mulungu wa Semu, ndipo Kanani [mwana wa Hamu] akhale kapolo kwa iye.” (Gen. 4:1; 9:26) Mulungu ananena yekha kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli, ndipo sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense.” Iye ananenanso kuti: “Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina. Palibenso Mulungu kupatulapo ine.” (Yes. 42:8; 45:5) Yehova waonetsetsa kuti dzina lake litetezedwe ndiponso kuti lidziwike kwa anthu padziko lonse. Ndi mwayi waukulu kwambiri kugwiritsa ntchito dzina lakuti Yehova ndiponso kukhala Mboni zake. Zili ngati tikufuula kuti: “Tidzakweza mbendera zathu m’dzina la Mulungu wathu.”—Sal. 20:5.

14. Kodi dzina la Mulungu limapezekanso pa zinthu ziti?

14 Koma sikuti dzina la Mulungu limangopezeka m’Baibulo mokha. Mwachitsanzo, mwala wina wolembedwa ndi Amowabu unapezeka kutauni ya Dhiban, imene ili pa mtunda wa makilomita 21 kum’mawa kwa Nyanja Yakufa. Pamwalawo, analembapo za Mfumu Omuri ya ku Isiraeli ndipo anafotokoza zimene Mfumu Mesa inachita popandukira Isiraeli. (1 Maf. 16:28; 2 Maf. 1:1; 3:4, 5) Koma zochititsa chidwi kwambiri n’zakuti dzina la Mulungu m’Chiheberi linalembedwanso pamwalapo. Dzina la Mulungu m’Chiheberi limapezekanso m’makalata akalekale olembedwa pamapale omwe anapezeka pafupi ndi Isiraeli.

15. Kodi Baibulo la Septuagint n’chiyani? N’chifukwa chiyani linamasuliridwa?

15 Anthu oyambirira kumasulira Baibulo anathandizanso kuteteza dzina la Mulungu. Ayuda atatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo mu 607 B.C.E. n’kumasulidwa mu 537 B.C.E., ambiri sanabwerere ku Yuda ndiponso ku Isiraeli. Pofika m’zaka za m’ma 200 B.C.E., Ayuda ambiri anali kukhala mumzinda wa Alexandria ku Iguputo. Iwo ankafunitsitsa kuti Malemba Achiheberi amasuliridwe m’Chigiriki chifukwa pa nthawiyo, anthu ambiri ankalankhula Chigiriki. Anthu anamaliza kumasulira Baibulo m’Chigiriki pofika m’zaka za m’ma 100 B.C.E. ndipo Baibulo limeneli limatchedwa Septuagint. M’Mabaibulo amenewa muli dzina lakuti Yehova lolembedwa m’Chiheberi.

16. Kodi dzina la Mulungu linapezeka m’kabaibulo kati komwe kanayamba kufalitsidwa mu 1640?

16 Dzina la Mulungu limapezekanso m’kabaibulo kena kakale kamene kanali koyamba kufalitsidwa kumadera a ku America omwe ankalamulidwa ndi England. Kanali ndi buku la Masalimo lokha ndipo kanayamba kufalitsidwa m’chaka cha 1640. Anakamasulira m’Chingelezi chapanthawiyo kuchokera ku Chiheberi. M’kabaibuloka muli dzina la Mulungu pa Salimo 1:1, 2, lomwe limati “munthu wodala” sayenda m’malangizo a anthu oipa, “koma amakondwera ndi chilamulo cha Iehovah.” Kuti mudziwe zambiri zokhudza dzina la Mulungu, onani kabuku kakuti Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha.

YEHOVA AMATETEZA CHOONADI

17, 18. (a) Kodi “choonadi” chimatanthauza chiyani? (b) Kodi “choonadi cha uthenga wabwino” chimakhudza zinthu ziti?

17 Timasangalala kutumikira “Yehova, Mulungu  wachoonadi.” (Sal. 31:5) Pofotokoza tanthauzo la mawu akuti “choonadi,” dikishonale ina imati: “Choonadi ndi mfundo zenizeni zonena za nkhani inayake osati mfundo zongoganizira kapena zopeka.” M’Chiheberi cha m’Baibulo, mawu amene nthawi zambiri amawamasulira kuti “choonadi” amatanthauza mfundo yoona, yodalirika ndiponso yokhala ndi umboni. Mawu achigiriki amene amawamasulira kuti “choonadi” amatanthauza mfundo yokhala ndi umboni, yoyenera ndiponso yolondola.

18 Yehova wateteza choonadi ndiponso kuonetsetsa kuti tichidziwe bwino. (2 Yoh. 1, 2) Iye akutithandiza pang’onopang’ono kumvetsa bwino choonadi. Pajatu Baibulo limati: “Njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezereka mpaka tsiku litakhazikika.” (Miy. 4:18) Timavomereza ndi mtima wonse mawu amene Yesu anauza Mulungu m’pemphero akuti: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yoh. 17:17) M’Mawu a Mulungu muli “choonadi cha uthenga wabwino” chomwe ndi ziphunzitso zonse zachikhristu. (Agal. 2:14) Ziphunzitsozi zimakhudza zinthu monga dzina la Yehova, ulamuliro wake, nsembe ya dipo ya Yesu, kuuka kwa akufa ndiponso Ufumu. Tiyeni tsopano tikambirane mmene Mulungu watetezera choonadi ngakhale kuti Satana wayesetsa kuchibisa.

YEHOVA SANALOLE KUTI CHOONADI CHISOKONEZEDWE

19, 20. Kodi Nimurodi anali ndani? Kodi ndi ntchito iti ya m’nthawi yake imene inalephereka?

19 Chigumula chitachitika, panali munthu yemwe ankamutcha kuti Nimurodi. Iye anali “mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova.” (Gen. 10:9) Popeza Nimurodi anali wotsutsana ndi Yehova Mulungu, tinganene kuti ankalambira Satana. Iye anali ngati anthu omwe Yesu anawauza kuti: “Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo mukufuna kuchita zokhumba za atate wanu. Iyeyo . . . sanakhazikike m’choonadi.”—Yoh. 8:44.

20 Nimurodi ankalamulira mzinda wa Babele ndiponso mizinda ina ya pakati pa mtsinje wa Tigirisi ndi Firate. (Gen. 10:10) N’kutheka kuti iye ndi amene analamula kuti anthu amange mzinda wa Babele ndi nsanja yake m’chaka cha 2269 B.C.E. Ngakhale kuti Yehova anauza anthu kuti afalikire padziko lonse lapansi, anthu omwe ankamanga mzindawo anati: “Tiyeni timange mzinda wathuwathu, ndipo nsanja yake ikafike m’mwamba mwenimweni. Tikatero tidzipangira dzina loti titchuke nalo, ndipo sitibalalikana padziko lonse lapansi.” Koma iwo analephera kugwira ntchitoyi pamene Mulungu “anasokoneza chilankhulo cha anthu onse” ndipo anawabalalitsira padziko lonse lapansi. (Gen. 11:1-4, 8, 9) Ngati cholinga cha Satana chinali chakuti ayambitse chipembedzo chimodzi ndiponso kuti anthu onse azimulambira, ndiye kuti cholingacho chinalepherekeratu. Koma kuyambira kalekale, anthu olambira Yehova akhala akuchulukirachulukira.

21, 22. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti chipembedzo chonyenga sichingalepheretse kulambira koona? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

21 N’zosatheka kuti chipembedzo chonyenga chilepheretse kulambira koona. Tikutero chifukwa chakuti Mlangizi wathu Wamkulu wateteza Mawu ake, waonetsetsa kuti anthu adziwe dzina lake ndiponso wakhala akuthandiza anthu kudziwa choonadi. (Yes. 30:20, 21) Timasangalala kwambiri tikamalambira Mulungu mogwirizana ndi choonadi. Koma kuti tipitirize kuchita zimenezi, tiyenera kukhala tcheru kuti tizimudalira nthawi zonse ndiponso kuti tizitsogoleredwa ndi mzimu wake woyera.

22 M’nkhani yotsatira, tidzakambirana mmene ziphunzitso zina zonyenga zinayambira. Tidzaona kuti tikayerekezera ziphunzitsozi ndi zimene zili m’Baibulo, zimaonekeratu kuti ndi zabodza. Tidzaonanso kuti Yehova, yemwe amateteza kwambiri choonadi, watidalitsa potiphunzitsa zinthu zoona. Zinthu zimenezi ndi zamtengo wapatali kwambiri ndipo ndi mbali ina ya cholowa chathu chochokera kwa iye.