Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Timayamikira Cholowa Chathu Chochokera kwa Mulungu?

Kodi Timayamikira Cholowa Chathu Chochokera kwa Mulungu?

“Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina . . . kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.”—MAC. 15:14.

1, 2. (a) Kodi “nyumba ya Davide” inali chiyani? Nanga inamangidwanso bwanji? (b) Kodi ndani masiku ano amene akutumikira Yehova mogwirizana?

PA MSONKHANO wosaiwalika wa bungwe lolamulira umene unachitikira ku Yerusalemu mu 49 C.E., Yakobo anati: “Sumeoni [Petulo] wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake. Ndipo zimenezi zikugwirizana ndi mawu a m’Zolemba za aneneri. Mawuwo amati, ‘Zimenezi zikadzatha ndidzabwerera ndi kumanganso nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzamanganso malo ogumuka a nyumbayo ndi kuiimikanso. Ndidzachita zimenezi kuti anthu otsalirawo afunefune Yehova ndi mtima wonse. Amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu, anthu otchedwa ndi dzina langa, watero Yehova amene akuchita zinthu zimenezi, zimene anatsimikiza kalekale kuti adzazichita.’”—Mac. 15:13-18.

2 Mawu akuti “nyumba ya Davide” akutanthauza mafumu ochokera m’banja lake. Nyumbayi inagwa pamene Mfumu Zedekiya inachotsedwa pa ufumu. (Amosi 9:11) Komabe nyumba imeneyi inali kudzamangidwanso ndi mbadwa ya Davide. Mbadwayo inali Yesu amene anadzakhala Mfumu yosatha. (Ezek. 21:27; Mac. 2:29-36) Pa msonkhanowu, Yakobo anasonyeza kuti ulosi wa Amosi unaloseranso kuti Ayuda ndiponso anthu a mitundu ina adzadzozedwa kuti adzakhale mafumu limodzi ndi Yesu kumwamba. Masiku ano, Akhristu odzozedwa amene adakali padziko lapansi ndi anthu ena mamiliyoni ambiri, omwe ndi “nkhosa zina” za Yesu, akugwira limodzi ntchito youza anthu za choonadi cha m’Baibulo.—Yoh. 10:16.

ANTHU A YEHOVA ANAKUMANA NDI MAVUTO

3, 4. Kodi n’chiyani chinathandiza anthu a Yehova kukhalabe okhulupirika pamene anali ku Babulo?

3 Ayuda atatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo, zinaonekeratu kuti “nyumba ya Davide” yagwa. Anthu a Yehova anakhala ku Babulo kwa zaka 70 kuyambira mu 607 B.C.E. mpaka mu 537 B.C.E.  Popeza anthu a ku Babulo ankalambira milungu yonyenga, kodi anthu a Yehova anakhalabe bwanji okhulupirika kwa iye pa zaka zonsezi? Iwo anachita zomwe ifenso timachita kuti tikhalebe okhulupirika m’dziko lolamulidwa ndi Satanali. (1 Yoh. 5:19) Atumiki a Yehova ali ndi cholowa chapadera chochokera kwa iye chimene chimawathandiza kukhalabe okhulupirika.

4 Mbali ina ya cholowa chimenechi ndi Mawu a Mulungu. Ayuda amene anali ku ukapolo analibe Baibulo lathunthu koma ankadziwa Chilamulo cha Mose ndiponso Malamulo Khumi. Iwo ankadziwanso “nyimbo za ku Ziyoni,” ankakumbukira miyambi yambiri ndiponso ankadziwa nkhani za atumiki a Yehova akale. Ayudawo ankalira akakumbukira Ziyoni ndipo sanaiwale Yehova. (Werengani Salimo 137:1-6.) Zinthu zimenezi zinawathandiza kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ngakhale pamene anali ku Babulo kumene kunali miyambo ndiponso ziphunzitso zambiri zonyenga.

UTATU NDI CHIPHUNZITSO CHAKALEKALE

5. Kodi ndi zitsanzo za milungu yokhala itatuitatu ziti zimene zinkapezeka ku Babulo ndi ku Iguputo?

5 Ku Babulo, anthu ankalambira milungu yokhala itatuitatu. Mwachitsanzo, mulungu mmodzi wa ku Babulo anapangidwa ndi milungu itatu yomwe inali Sini, Shamashi ndi Ishitara. Sini anali mulungu wa mwezi, Shamashi anali mulungu wa dzuwa ndipo Ishitara anali mulungu wamkazi wobereketsa ndiponso wankhondo. Ku Iguputo, anthu ankalambira mabanja a milungu yokhala itatuitatu. Pankakhala bambo, mayi ndi mwana wamwamuna. Nthawi zina mulungu wamkulu pakati pawo ankakhala mayi osati bambo. Mulungu wina wa ku Iguputo anali wopangidwa ndi mulungu Osirisi, mulungu wamkazi Isisi ndiponso mwana wawo wamwamuna Horusi.

6. Kodi chiphunzitso cha Utatu n’chiyani? Nanga anthu a Yehova atetezedwa bwanji ku bodza limeneli?

6 Nawonso matchalitchi omwe amati ndi achikhristu amalambira mulungu wopangidwa ndi milungu itatu. Atsogoleri a matchalitchi amaphunzitsa kuti Atate, Mwana ndiponso mzimu woyera amapanga Mulungu mmodzi. Koma chiphunzitso chimenechi chimachititsa Yehova kuoneka ngati alibe mphamvu chifukwa amagawana ulamuliro wake ndi milungu ina iwiri. Anthu a Yehova atetezedwa ku bodza limeneli chifukwa amakhulupirira mawu ochokera kwa Mulungu akuti: “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.” (Deut. 6:4) Yesu anabwerezanso mawu a mu lembali. Kodi alipo Mkhristu woona amene angatsutsane naye?—Maliko 12:29.

7. Kodi munthu ayenera kukhulupirira chiyani kuti abatizidwe monga Mkhristu woona?

7 Chiphunzitso cha Utatu chimatsutsana ndi zimene Yesu anauza otsatira ake. Iye anati: “Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.” (Mat. 28:19) Kuti munthu abatizidwe monga Mkhristu weniweni ndiponso monga wa Mboni za Yehova, ayenera kuzindikira kuti Atate akuimira Yehova yemwe ndi wamphamvu zonse. Ayenera kuzindikiranso udindo wa Yesu yemwe ndi Mwana wake. Munthuyo ayenera kukhulupiriranso kuti mzimu woyera ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu osati mbali ya Utatu. (Gen. 1:2) Ngati munthu akukhulupirirabe Utatu ndiye kuti sanadzipereke kwa Yehova Mulungu ndipo sangabatizidwe. Timayamikira kwambiri kuti cholowa chathu chochokera kwa Yehova chatiteteza ku chiphunzitso chonyoza Mulungu chimenechi.

KUKHULUPIRIRA MIZIMU

8. Kodi anthu ku Babulo ankakhulupirira zinthu zotani zokhudza milungu ndiponso ziwanda?

8 Chipembedzo cha ku Babulo chinali ndi ziphunzitso zambiri zonyenga ndiponso zikhulupiriro zokhudza milungu yosiyanasiyana, ziwanda ndiponso kukhulupirira mizimu. Buku lina lofotokoza za m’Baibulo limati: “Anthu a ku Babulo ankakhulupiriranso kwambiri  ziwanda. Iwo ankati ziwanda zili ndi mphamvu zodwalitsa anthu matenda osiyanasiyana kuphatikizapo a m’maganizo. Anthuwa ankakhulupirira kuti ayenera kulimbana ndi ziwandazi ndipo ankapemphera kwa milungu yawo kuti iwathandize kuthana nazo.”

9. (a) Ayuda atamasulidwa ku Babulo, kodi ambiri anayamba kukhulupirira ziphunzitso zotani? (b) Kodi timatetezedwa bwanji pa nkhani yokhulupirira mizimu?

9 Ayuda atamasulidwa ku Babulo, ambiri anayamba kukhulupirira ziphunzitso zonyenga. Zikhulupiriro zachigiriki zitayamba kufalikira, Ayuda ambiri anayambanso kukhulupirira kuti ziwanda zikhoza kuchita zinthu zabwino. Zimenezi zinachititsa kuti ziwandazo ziziwavutitsa. Koma timadziwa kuti Mulungu amadana ndi kukhulupirira mizimu kapena kuchita zinthu zokhudza ziwanda. Kudziwa zimenezi ndi mbali ina ya cholowa chathu chochokera kwa iye. (Yes. 47:1, 12-15) Cholowachi chimatiteteza chifukwa timatsatira maganizo a Mulungu pa nkhani imeneyi.—Werengani Deuteronomo 18:10-12; Chivumbulutso 21:8.

10. Kodi zikhulupiriro ndiponso zochita za Babulo Wamkulu zinayambira kuti?

10 Masiku anonso, anthu a m’zipembedzo zonyenga amachita zamizimu monga mmene ankachitira anthu a ku Babulo wakale. N’chifukwa chake Baibulo limatchula zipembedzo zonse zonyenga za padziko lapansi kuti ndi Babulo Wamkulu. (Chiv. 18:21-24) Zipembedzo zimenezi zilidi ngati Babulo wakale chifukwa chakuti ziphunzitso zawo zonyenga ndiponso zochita zawo zoipa, zinayambira kumeneko. Chifukwa chokhulupirira mizimu, kulambira mafano ndiponso kuchita zinthu zina zoipa, Babulo Wamkulu awonongedwa posachedwapa.—Werengani Chivumbulutso 18:1-5.

11. Kodi m’mabuku ndi m’magazini athu mwakhala mukupezeka chenjezo liti lokhudza kukhulupirira mizimu?

11 Baibulo limasonyeza kuti Yehova amadana ndi ‘kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga.’ (Yes. 1:13) M’zaka za m’ma 1800, anthu ambiri ankakhulupirira mizimu. Choncho Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 1885 inati: “Chikhulupiriro chakuti anthu amene anamwalira akukhalabe moyo kwinakwake si chatsopano. Zipembedzo zakale zinkaphunzitsa zimenezi ndipo nthano za pa nthawi imeneyo zinkachokera ku chikhulupiriro chimenechi.” Nkhaniyi inapitiriza kufotokoza za chiphunzitso chosemphana ndi Baibulo chakuti anthu akufa amatha kulankhula ndi amoyo. Inanena kuti chiphunzitsochi “chachititsa anthu ambiri kukhulupirira zinthu zabodza zimene ‘ziwanda’ zimachita zikamanamizira kuti ndi mizimu ya anthu akufa. Ziwanda zimachita zimenezi n’cholinga choti anthu asadziwe kuti zilipo. Choncho zimalamulira kwambiri maganizo ndiponso zochita za anthu.” Kabuku kena kakale kofotokoza zimene Malemba amanena pa nkhani yokhulupirira mizimu kanaperekanso chenjezo ngati limeneli. Nawonso mabuku ndiponso magazini athu aposachedwapa atichenjeza pa nkhaniyi.

KODI ANTHU ENA AMENE ANAMWALIRA AMAKAZUNZIKA KWINAKWAKE?

12. Kodi Solomo anauziridwa kunena chiyani zokhudza akufa?

12 Anthu “onse amene adziwa choonadi” akhoza kuyankha molondola funso limeneli. (2 Yoh. 1) Tonse timavomereza zimene Solomo analemba kuti: “Galu wamoyo ali bwino kuposa mkango wakufa. Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse . . . Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse, pakuti kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda kumene ukupitako.”—Mlal. 9:4, 5, 10.

13. Kodi Ayuda anayamba kukhulupirira chiyani chifukwa cha chipembedzo ndiponso chikhalidwe cha Agiriki?

13 Yehova anauza Ayuda zoona zokhudza akufa. Koma ufumu wa Girisi utagawidwa kwa akuluakulu anayi a asilikali a Alekizanda Wamkulu, Agirikiwo anayesetsa kugwirizanitsa Ayuda ndi Asiriya. Anachita zimenezi pogwiritsa ntchito chipembedzo ndiponso chikhalidwe chawo. Chifukwa cha zimenezi, Ayuda anayamba kukhulupirira ziphunzitso zonyenga  zakuti mzimu wa munthu sufa ndiponso kuti akufa amakazunzika kwinakwake. Komatu Agiriki si amene anayambitsa chikhulupiriro chakuti kuli malo enaake kumene mizimu ya anthu akufa imakazunzika. Tikutero chifukwa buku lina lofotokoza chipembedzo cha Ababulo limati iwo ankakhulupirira kuti “kumene anthu amapita akamwalira . . . ndi malo oopsa kwambiri, . . . ndipo malo amenewa amalamulidwa ndi milungu ndiponso ziwanda zamphamvu ndi zoopsa kwambiri.” Choncho Ababulo ankakhulupiriranso kuti mzimu wa munthu sufa.

14. Kodi Yobu ndi Abulahamu ankadziwa chiyani pa nkhani ya imfa ndi kuukitsidwa?

14 Ngakhale kuti Yobu analibe Baibulo, iye ankadziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira. Ankadziwanso kuti ngati angamwalire, Yehova Mulungu wake, yemwe ndi wachikondi, adzalakalaka kumuukitsa. (Yobu 14:13-15) Abulahamu ankakhulupiriranso kuti akufa adzaukitsidwa. (Werengani Aheberi 11:17-19.) Popeza n’zosatheka kuukitsa munthu amene sangafe, ndiye kuti atumiki a Mulungu amenewa sankakhulupirira kuti munthu ali ndi mzimu umene sufa. N’zosakayikitsa kuti mzimu wa Mulungu ndi umene unathandiza Yobu ndi Abulahamu kumvetsa zimene zimachitika munthu akamwalira komanso kukhulupirira zoti akufa adzauka. Mfundo za choonadi zimenezi ndi mbali inanso ya cholowa chathu.

TIMAFUNIKA ‘KUMASULIDWA NDI DIPO’

15, 16. Kodi zinatheka bwanji kuti timasulidwe ku uchimo ndi imfa?

15 Timayamikira kwambiri kuti Mulungu watiululiranso mmene adzatimasulire ku uchimo ndi imfa zimene tinatengera kwa Adamu. (Aroma 5:12) Timadziwa kuti Yesu “sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.” (Maliko 10:45) N’zosangalatsa kuti tili ndi mwayi ‘womasulidwa ndi dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu.’—Aroma 3:22-24.

16 Nthawi ya atumwi, Ayuda ndiponso anthu amitundu ina anafunika kulapa machimo awo  komanso kukhulupirira nsembe ya dipo imene Yesu anapereka. Kupanda kutero, sakanakhululukidwa ndipo zilinso choncho masiku ano. (Yoh. 3:16, 36) Ngati munthu amakhulupirirabe ziphunzitso zabodza monga Utatu komanso kuti munthu ali ndi mzimu umene sufa, ndiye kuti sangapindule ndi dipo. Koma ife tikhoza kupindula nalo chifukwa timadziwa choonadi chakuti “tinamasulidwa ndi dipo [la Mwana wa Mulungu wokondedwa] kutanthauza kuti machimo athu anakhululukidwa.”—Akol. 1:13, 14.

PITIRIZANI KUTUMIKIRA YEHOVA MONGA ANTHU ODZIWIKA NDI DZINA LAKE

17, 18. Kodi tingapeze kuti nkhani zokhudza mbiri yathu? Nanga kuphunzira zimenezi kungatithandize bwanji?

17 Cholowa chathu chochokera kwa Mulungu chikuphatikizaponso zinthu zimene watiphunzitsa, zinthu zina zimene takumana nazo pomutumikira ndiponso njira zimene watidalitsira. Kwa zaka zambiri, Buku Lapachaka la Mboni za Yehova lakhala likufotokoza zinthu zochititsa chidwi zimene atumiki a Yehova akuchita m’madera osiyanasiyana padzikoli. Mbiri yathu yafotokozedwanso mu mavidiyo akuti Faith in Action, Gawo 1 ndi 2, komanso m’mabuku monga lakuti, Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom. M’magazini athu mumakhalanso nkhani za Akhristu anzathu amene amafotokoza okha mbiri ya moyo wawo.

18 Aisiraeli ankapindula kwambiri akamaganizira mmene Mulungu anawamasulira ku ukapolo ku Iguputo. (Eks. 12:26, 27) Nafenso timapindula kwambiri tikamaganizira mbiri ya gulu la Yehova. Mose anaona zinthu zodabwitsa zimene Mulungu anachita ndipo atakalamba, analimbikitsa Aisiraeli kuti: “Kumbukirani masiku akale, ganizirani zaka za mibadwomibadwo ya m’mbuyomu. Funsa bambo ako ndipo akuuza, amuna achikulire pakati panu, ndipo akufotokozera.” (Deut. 32:7) Popeza ndife ‘anthu a Yehova komanso nkhosa zimene akuweta,’ tonse tiyenera kulengeza ulemerero wake ndiponso kuuza anthu ena ntchito zake zazikulu. (Sal. 79:13) Choncho ndi bwino kuganizira mbiri yathu, kuona zimene tikuphunzirapo ndiponso kuganizira zimene tidzachite m’tsogolo.

19. Popeza tikusangalala ndi kuwala kochokera kwa Mulungu, kodi tiyenera kuchita chiyani?

19 Timayamikira kwambiri kuti sitikuyenda mu mdima koma tikusangalala ndi kuwala kochokera kwa Mulungu. (Miy. 4:18, 19) Choncho tiyeni tizichita khama kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kuuza ena choonadi. Tizikhala ndi mtima ngati wa wamasalimo. Iye anatamanda Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova, ndi mawu akuti: “Ndidzanena za chilungamo chanu, osati cha wina aliyense. Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira pa unyamata wanga, ndipo mpaka pano ndikunena za ntchito zanu zodabwitsa. Ngakhale nditakalamba ndi kumera imvi, inu Mulungu musandisiye, kufikira nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatira, kufikira nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwera m’tsogolo.”—Sal. 71:16-18.

20. Kodi Satana anatsutsa nkhani ziti? Nanga inuyo mukufuna kuchita chiyani pa nkhanizi?

20 Anthu amene tadzipereka kwa Yehovafe timadziwa nkhani zomwe Satana anatsutsa zokhudza ulamuliro wa Yehova ndiponso kukhulupirika kwa anthu. Timalengeza choonadi chosatsutsika chakuti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse ndiponso kuti anthufe tiyenera kudzipereka kwa iye ndi mtima wonse. (Chiv. 4:11) Yehova watipatsanso mzimu wake kuti tilengeze uthenga wabwino kwa anthu ofatsa, timange zilonda za anthu osweka mtima ndiponso tikatonthoze anthu onse olira. (Yes. 61:1, 2 ) Panopa Satana akuyesetsa kuti azilamulira anthu onse, kuphatikizapo anthu a Mulungu, koma zimenezi sizitheka. Timayamikira kwambiri cholowa chathu chochokera kwa Mulungu ndipo sitidzasiya kukhalabe okhulupirika kwa iye. Tidzapitirizanso kutamanda Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova, mpaka kalekale.—Werengani Salimo 26:11; 86:12.