Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zinapangitsa Kuti Moyo wa Yesu Ukhale Waphindu

Zimene Zinapangitsa Kuti Moyo wa Yesu Ukhale Waphindu

KODI Yesu analidi ndi moyo waphindu? Iye anabadwira m’banja losauka ndipo pa moyo wake wonse analibe zinthu zambiri. Ndipotu iye ‘analibiretu poti n’kutsamira mutu wake.’ (Luka 9:57, 58) Komanso ankadedwa, kunyozedwa ndipo kenako anaphedwa ndi adani ake.

Mwina mungaganize kuti moyo woterewu sunali wosangalatsa. Koma pali zinthu zambiri zimene Yesu ankachita zimene tiyenera kuziganizira. Tiyeni tione mfundo zinayi zokhudza moyo wa Yesu.

1. YESU ANALI NDI CHOLINGA PA MOYO WAKE CHOMWE CHINALI KUCHITA CHIFUNIRO CHA MULUNGU.

“Chakudya changa ndicho kuchita chifuniro cha amene anandituma.”—Yohane 4:34.

Zolankhula komanso zochita zake zinasonyeza kuti Yesu ankafunitsitsa kuchita chifuniro cha Atate wake, Yehova. * Yesu ankasangalala kwambiri kuchita chifuniro cha Mulungu. Iye anayerekezera kuchita chifuniro cha Mulungu ndi chakudya mogwirizana ndi zimene lemba la Yohane 4:34 likunena. Taganizirani mmene zinthu zinalili pa nthawi imene Yesu ananena mawu amenewa.

Yesu ananena mawu amenewa nthawi yamasana. (Yohane 4:6) Pa nthawiyi n’kuti atayenda m’mawa wonse m’njira za m’mapiri ku Samariya, choncho ayenera kuti anali ndi njala. Ndiyeno ophunzira ake anamuuza kuti: “Rabi, idyani.” (Yohane 4:31) Apa m’pamene Yesu ananena mawu a pa Yohane 4:34. Yankho lakeli linasonyeza kuti iye ankasangalala komanso kulimbikitsidwa akamachita chifuniro cha Mulungu. Zimenezitu zikusonyeza kuti moyo wa Yesu unali waphindu.

2. YESU ANKAKONDA KWAMBIRI ATATE WAKE.

“Ndimakonda Atate.”—Yohane 14:31.

Yesu ankakondana kwambiri ndi Atate wake. Kukonda kwambiri Mulungu kunamuchititsa kuti aziuza anthu ena zolinga komanso makhalidwe a Atate wake. Iye ankauzanso anthu dzina la Mulungu. Zonena za Yesu, zochita zake komanso mmene ankaonera zinthu, zinasonyeza kuti iye anatengera kwambiri Atate wakeyo. Choncho tikamawerenga zokhudza Yesu, timakhala ngati tikuwerenga zokhudza Atate wake. N’chifukwa chake pamene Filipo anauza Yesu kuti: “Tionetseni Atatewo,” Yesu anamuyankha kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.”—Yohane 14:8, 9.

Yesu ankakonda kwambiri Atate wake mpaka kufika polola kuphedwa chifukwa chomvera Atate wakewo. (Afilipi 2:7, 8; 1 Yohane 5:3) Kukonda kwambiri  Mulungu kotereku, n’kumene kunapangitsa kuti moyo wa Yesu ukhale waphindu.

3. YESU ANKAKONDA ANTHU.

“Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.”—Yohane 15:13.

Chifukwa chopanda ungwiro, nthawi zina anthufe timaona kuti tilibe tsogolo. Baibulo limati: “Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Patokha, palibe chomwe tingachite kuti tisakumane ndi zotsatira za uchimo zomwe ndi imfa.—Aroma 6:23.

Komatu n’zosangalatsa kuti Yehova anapereka njira yotithandiza kuti timasulidwe ku uchimo ndi imfa. Iye analolera kuti Mwana wake, Yesu, yemwe anali wangwiro komanso wopanda uchimo avutike kenako n’kufa n’cholinga chotiwombola ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Chifukwa chokonda Atate wake komanso anthu, Yesu analolera kupereka moyo wake pofuna kutipulumutsa. (Aroma 5:6-8) Chikondi chotere n’chimene chinapangitsa kuti moyo wake ukhale waphindu. *

4. YESU ANKADZIWA KUTI ATATE WAKE AMAMUKONDA KOMANSO AMASANGALALA NAYE.

“Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.”—Mateyu 3:17.

Yehova ananena mawu amenewa kuchokera kumwamba pa nthawi imene Yesu ankabatizidwa. Choncho, Yehova anasonyeza kuti ankakonda Mwana wakeyu komanso ankasangalala ndi zimene ankachita. M’pake kuti Yesu ananena motsimikiza kuti Atate wake amamukonda. (Yohane 10:17) Kudziwa kuti Atate wake ankamukonda komanso ankasangalala ndi zimene ankachita, kunathandiza Yesu kukhala wolimba mtima pamene ankatsutsidwa, kuzunzidwa komanso kuphedwa. (Yohane 10:18) Kunamuthandizanso kuti aziona kuti moyo wake unali waphindu.

Apatu taona kuti moyo wa Yesu unalidi waphindu. Tingaphunzire zambiri pa moyo wake zimene zingatithandize kuti nafenso moyo wathu ukhale waphindu. Nkhani yotsatira ifotokoza malangizo amene Yesu anapatsa otsatira ake onena za mmene angakhalire ndi moyo waphindu komanso wosangalala.

^ ndime 6 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.

^ ndime 15 Kuti mudziwe zambiri zokhudza kufunika kwa imfa ya Yesu, onani mutu 5 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.