Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

”Musatope Kuchita Zabwino”

”Musatope Kuchita Zabwino”

“Tisaleke kuchita zabwino.”—AGAL. 6:9.

1, 2. Kodi kuganizira zimene gulu la Yehova likuchita kumatithandiza bwanji?

N’ZOSANGALATSA kudziwa kuti tili m’gulu lalikulu limene lili ndi mbali yapadziko lapansi komanso yakumwamba. Masomphenya a pa Ezekieli chaputala 1 ndi Danieli chaputala 7 amasonyeza bwino kuti Yehova akuyendetsa zinthu kuti akwaniritse cholinga chake. Yesu ndi amene akutsogolera mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova. Iye akuyang’anira ntchito yolalikira, akuphunzitsa ndi kulimbikitsa amene akugwira ntchitoyi komanso akuthandiza anthu ena kuti ayambe kulambira Yehova. Izi zimatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri gulu la Yehova.—Mat. 24:45.

2 Kodi inuyo panokha mumachita zinthu mogwirizana ndi gululi? Kodi mukutumikirabe Mulungu mwakhama kapena mwayamba kufooka? Mwina pambuyo podzifunsa mafunso amenewa, taona kuti tayamba kutopa. Zimenezi zimachitika. Mwachitsanzo, m’nthawi ya atumwi, Paulo anafunika kukumbutsa Akhristu anzake kuti aziganizira za khama la Yesu. Paulo ananena kuti izi zingawathandize kuti ‘asatope ndiponso asalefuke.’ (Aheb. 12:3) M’nkhani yapita ija, tinaona zimene gulu la Yehova likuchita. Kuganizira zimenezi kuyenera kuti kwatilimbikitsanso kwambiri kuti tikhalebe akhama komanso opirira.

3. N’chiyani chingatithandize kuti tisatope? Nanga tikambirana chiyani m’nkhani ino?

3 Koma Paulo anasonyeza kuti pamafunika zinthu zinanso kuti munthu asatope. Iye ananena kuti tiyenera kuyesetsa “kuchita zabwino.” (Agal. 6:9) Tiyeni tikambirane zinthu zisanu zimene tiyenera kuchita kuti tikhalebe olimba ndiponso tizitsatira bwino gulu la Yehova. Mwina zimenezi zitithandiza kuona zimene ifeyo kapena banja lathu liyenera kusintha.

 TIZISONKHANA KUTI TILIMBIKITSIDWE KOMANSO TILAMBIRE MULUNGU

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kusonkhana ndi mbali yofunika kwambiri pa kulambira koona?

4 Misonkhano yakhala yofunika kwambiri kwa atumiki a Yehova kuyambira kale. Kumwamba, angelo amakhala ndi nthawi yosonkhana pamaso pa Yehova. (1 Maf. 22:19; Yobu 1:6; 2:1; Dan. 7:10) Nawonso Aisiraeli ankasonkhana “kuti amvetsere ndi kuphunzira.” (Deut. 31:10-12) M’nthawi ya atumwi, Ayuda ankasonkhana kumasunagoge kuti amvetsere Malemba akamawerengedwa. (Luka 4:16; Mac. 15:21) Mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa, anthu a Yehova ankapitiriza kusonkhana limodzi. Masiku anonso, misonkhano ndi yofunika kwambiri pa kulambira kwathu. Akhristu oona ‘amaganizirana kuti alimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino.’ Tiyenera kupitiriza ‘kulimbikitsana, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene tikuona kuti tsikulo [la Yehova] likuyandikira.’—Aheb. 10:24, 25.

5. Kodi tingalimbikitsane bwanji pa misonkhano yathu?

5 Njira ina yofunika kwambiri kuti tilimbikitsane ndi kupereka ndemanga pa misonkhano. Mwachitsanzo, tingayankhe funso lolembedwa, kufotokoza lemba kapena kupereka chitsanzo chachidule chosonyeza ubwino wotsatira mfundo za m’Baibulo. (Sal. 22:22; 40:9) Kaya takhala tikusonkhana kwa nthawi yaitali bwanji, tonse timalimbikitsidwa tikamamva ndemanga zochokera pansi pa mtima za abale ndi alongo athu amisinkhu yosiyanasiyana.

6. Kodi misonkhano yathu imatithandiza bwanji?

6 Kodi Mulungu amatilimbikitsa kusonkhana pa zifukwa zina ziti? Misonkhano yathu ya mpingo ndiponso ikuluikulu imatithandiza kulankhula molimba mtima. Imatithandizanso kuti tisafooke tikakumana ndi anthu otsutsa kapena opanda chidwi mu utumiki. (Mac. 4:23, 31) Kukambirana mfundo za m’Malemba kumatipatsa mphamvu komanso kumalimbitsa chikhulupiriro chathu. (Mac. 15:32; Aroma 1:11, 12) Tikaphunzitsidwa komanso kulimbikitsana ku misonkhano, timakhala osangalala ndiponso timapeza “mtendere pa nthawi ya masoka.” (Sal. 94:12, 13) Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira ndi imene imayang’anira ntchito yokonza zimene timaphunzira ku misonkhano yathu. Timayamikira kwambiri maphunziro abwino amene timalandira mlungu uliwonse.

7, 8. (a) Kodi cholinga chachikulu cha misonkhano yathu n’chiyani? (b) Kodi inuyo misonkhano imakuthandizani bwanji?

7 Koma sikuti timangopita ku misonkhano kuti ifeyo tipindule. Cholinga chachikulu cha misonkhano yathu ndi kulambira Yehova. (Werengani Salimo 95:6.) Ndi mwayi waukulu kwambiri kutamanda Mulungu poimba pa misonkhano. (Akol. 3:16) Tiyeni tizimutamanda popezeka pa misonkhanoyi nthawi zonse komanso kupereka ndemanga. Pajatu iye ndi woyenera kulambiridwa. (Chiv. 4:11) M’pake kuti timauzidwa kuti: “Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira.”—Aheb. 10:25.

8 Kodi timaona kuti misonkhano ndi mphatso yochokera kwa Yehova yotithandiza kupirira mpaka mapeto a dziko loipali? Ngati timaona choncho, misonkhanoyi idzakhala m’gulu la “zinthu zofunika kwambiri” zimene sitingalole kuziphonya ngakhale kuti timatanganidwa. (Afil. 1:10) Sitiyenera kuphonya misonkhano pokhapokha ngati pali zifukwa zazikulu kwambiri.

FUFUZANI ANTHU OFUNA CHOONADI

9. Kodi timadziwa bwanji kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri?

9 Kulalikira mwakhama kumatithandizanso  kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi gulu la Yehova. Yesu anayambitsa ntchito imeneyi pamene anali padziko lapansi. (Mat. 28:19, 20) Kuyambira nthawi imeneyo, gulu la Yehova limaika patsogolo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Masiku ano, pali maumboni ambiri osonyeza kuti angelo amatithandiza pa ntchitoyi ndipo amatitsogolera kwa anthu ofuna choonadi. (Mac. 13:48; Chiv. 14:6, 7) Cholinga chachikulu cha mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova ndi kutsogolera ndiponso kuthandiza pa ntchito yofunikayi. Kodi ifenso timaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri pa moyo wathu?

10. (a) Kodi m’bale wina amatani kuti azikondabe choonadi? (b) Kodi utumiki wakuthandizani bwanji kuti musatope?

10 Kuchita khama mu utumiki kumatithandiza kuti tizikondabe choonadi. M’bale wina dzina lake Mitchel, yemwe wakhala mkulu komanso mpainiya wokhazikika kwa nthawi yaitali, anati: “Ndimakonda kwambiri kuuza anthu za choonadi. Ndikaganizira nkhani inayake ya m’magazini atsopano a Nsanja ya Olonda kapena Galamukani!, ndimaona kuti magazini iliyonse imalembedwa mwanzeru ndiponso moganizira kwambiri anthu. Ndiyeno ndimalakalaka kulowa mu utumiki kuti ndione zimene anthu angachite ndikamakambirana nawo za m’magaziniyo. Ndimaganiziranso mmene ndingawathandizire kuchita nayo chidwi. Utumiki umandithandiza kuti ndiziona zinthu m’njira yoyenera. Sindilola zinthu zina kundilepheretsa kulowa mu utumiki pa nthawi imene ndakonza.” Kuchita khama mu utumiki kungatithandizenso kuti tikhalebe olimba  m’masiku otsiriza ano.—Werengani 1 Akorinto 15:58.

MUZIGWIRITSA NTCHITO BWINO MABUKU AMENE GULU LIMATIPATSA

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuwerenga mabuku amene Yehova amatipatsa ndiponso kusinkhasinkha zimene timawerenga?

11 Yehova watipatsa mabuku ambiri amene amatilimbikitsa. Mwina zinakuchitikirani kuti mutawerenga buku linalake, munaganiza kuti, ‘Koma bukuli ndiye anandilembera ineyotu. Yehova waikamo zonse zimene ndimafunika.’ Sikuti zimenezi zimangochitika mwangozi. Yehova amagwiritsa ntchito mabuku ngati amenewa kuti atilangize komanso kutitsogolera. Iye ananena kuti: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.” (Sal. 32:8) Kodi timayesetsa kuwerenga mabuku onse amene timalandira ndiponso kusinkhasinkha zimene tawerengazo? Kuchita zimenezi kumatithandiza kubala zipatso ndiponso kukhalabe olimba m’masiku otsiriza ano.—Werengani Salimo 1:1-3; 35:28; 119:97.

12. N’chiyani chingatithandize kuyamikira mabuku amene timalandira?

12 Tingachite bwino kuganizira ntchito imene imakhalapo kuti mabuku ngati amenewa apezeke. Pamafunika kufufuza, kulemba, kutsimikizira kuti zimene zalembedwa n’zolondola, kuika zithunzi ndiponso kumasulira. Kenako zinthuzo zimakhala zoyenera kusindikizidwa kapena kuikidwa pa Intaneti. Komiti Yoona za Ntchito Yolemba Mabuku ya Bungwe Lolamulira ndi imene imayang’anira ntchito zonsezi. Ndiyeno pali nthambi zimene zimasindikiza mabuku ndi kuwatumiza kumipingo yonse. Cholinga cha ntchito zonsezi n’chakuti anthu a Yehova aziphunzitsidwa ndiponso kulangizidwa kuti apitirize kukhala okhulupirika. (Yes. 65:13) Tiyeni tiziyesetsa kugwiritsa ntchito bwino mabuku onse amene gulu la Yehova limatipatsa.—Sal. 119:27.

MUZITHANDIZA KUTI GULU LIZIYENDA BWINO

13, 14. Kodi ndani akuthandiza gulu la Yehova kumwamba? Kodi ife tingawatsanzire bwanji?

13 Mtumwi Yohane anaona m’masomphenya Yesu atakwera hatchi yoyera kuti akagonjetse adani a Yehova. (Chiv. 19:11-15) M’masomphenyawa, Yesu akutsatiridwa ndi angelo okhulupirika komanso odzozedwa amene alandira kale mphoto yawo kumwamba. (Chiv. 2:26, 27) Angelo ndiponso odzozedwawa akutipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yothandiza kuti gulu la Yehova liziyenda bwino.

14 Nalonso khamu lalikulu limathandiza abale a Khristu amene atsala padzikoli. (Werengani Zekariya 8:23.) Kodi aliyense payekha angathandize bwanji kuti gulu la Yehova liziyenda bwino? Choyamba, tiyenera kugonjera anthu amene akutsogolera. (Aheb. 13:7, 17) Izi zimayambira mu mpingo. Kodi zolankhula zathu zimasonyeza kuti timalemekeza akulu ndiponso udindo wawo? Kodi timalimbikitsa ana athu kuti azilemekeza abale okhulupirika amenewa ndiponso kutsatira malangizo awo ochokera m’Malemba? Nanga kodi timakambirana ndi banja lathu za ndalama zimene tingapereke pothandiza ntchito yolalikira? (Miy. 3:9; 1 Akor. 16:2; 2 Akor. 8:12) Kodi timathandiza kuyeretsa ndi kusamalira Nyumba ya Ufumu? Yehova amatipatsa mzimu wake akaona kuti tikuthandiza gulu lake m’njira zimenezi. Mzimu umenewu ndi umene umatithandiza kuti tisatope m’nthawi yamapetoyi.—Yes. 40:29-31.

TIZICHITA ZINTHU MOGWIRIZANA NDI UTHENGA WATHU

15. N’chifukwa chiyani timavutika kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Yehova?

15 Kuti tipirire komanso kuchitabe zinthu  mogwirizana ndi gulu la Yehova, khalidwe lathu liyenera kugwirizana ndi uthenga umene timalalikira. Tiyenera ‘kutsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.’ (Aef. 5:10, 11) Koma timavutika kuchita zabwino chifukwa cha kupanda ungwiro ndiponso dziko la Satana loipali. Ena mwa inu mumamenya nkhondo tsiku lililonse kuti mupitirize kukhala okhulupirika kwa Yehova. Dziwani kuti timakukondani ndipo Yehova amakukondani kwambiri chifukwa cha zimene mukuchita. Musabwerere m’mbuyo. Kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Yehova kumatithandiza kukhala osangalala ndipo sitikayikira kuti iye akusangalala nafe.—1 Akor. 9:24-27.

Yesetsani kuthandiza anthu ena kudziwa kuti nawonso akhoza kukhala m’gulu la Yehova

16, 17. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tachita tchimo lalikulu? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Anne?

16 Koma kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tachita tchimo lalikulu? Sitiyenera kubisa tchimolo koma kupempha thandizo mwamsanga. Kumbukirani mawu a Davide akuti: “Pamene ndinakhala chete osaulula machimo anga, mafupa anga anafooka, chifukwa tsiku lonse ndinali kuvutika mumtima mwanga.” (Sal. 32:3) Tikayesa kubisa machimo akuluakulu, sitisangalala ndipo ubwenzi wathu ndi Yehova umasokonekera. Koma ‘tikaulula machimo n’kuwasiya tidzachitiridwa chifundo.’—Miy. 28:13.

17 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Anne. * Iye ali wachinyamata ankachita upainiya wokhazikika koma anayamba kuchita mobisa zinthu zina zoipa. Zimenezi zinamusokoneza kwambiri. Iye anati: “Ndinangotsala ndi kachidutswa ka chikumbumtima koma kamenekoko kankandivutitsa kwambiri. Ndinkakhala wokhumudwa nthawi zonse.” Kodi iye anatani? Iye ananena kuti tsiku lina ku misonkhano, lemba la Yakobo 5:14, 15 linafotokozedwa. Anne anazindikira kuti ankafunika thandizo ndipo anapita kwa akulu. Pokumbukira zimene zinachitika, iye anati: “Mavesi amenewa ali ngati mankhwala ochokera kwa Yehova. Mankhwalawa ndi ovuta kumwa koma amachiritsa. Ndinatsatira malangizo a m’mavesiwa ndipo anandithandiza.” Panopa padutsa zaka zambiri ndipo Anne akutumikiranso Yehova mwakhama komanso chikumbumtima chake chili bwino.

18. Kodi tiziyesetsa kuchita chiyani??

18 Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala m’gulu la Yehova m’masiku otsiriza ano. Tisasiye kuyamikira zimene tili nazo. Koma tiziyesetsa limodzi ndi banja lathu kupezeka nthawi zonse pa misonkhano, kufufuza mwakhama anthu ofuna choonadi ndiponso kugwiritsa ntchito bwino mabuku amene timalandira. Tiziyesetsanso kugonjera anthu amene akutitsogolera komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi uthenga umene timalalikira. Tikamatero ndiye kuti tikuchita zinthu mogwirizana ndi gulu la Yehova komanso sitidzatopa pochita zabwino.

^ ndime 17 Dzina lasinthidwa.