Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MBIRI YA MOYO WANGA

Zimene Zatithandiza Kukhalabe Osangalala

Zimene Zatithandiza Kukhalabe Osangalala

MWANA wanga Gary atangobadwa mu 1958, ndinadziwa kuti ali ndi vuto linalake. Koma panapita miyezi 10 kuti madokotala azindikire matenda ake. Ndiyeno patadutsa zaka 5, madokotala ena a ku London anatsimikizira kuti iye alidi ndi matendawo. Kenako patapita zaka 9, mwana wathu wamkazi dzina lake Louise anabadwa. Koma zinandiwawa kwambiri kuona kuti nayenso wabadwa ndi matendawo ndipo vuto lake linali lalikulu kwambiri kuposa Gary.

Madokotala anandifotokozera mwachifundo kuti ana anga onse awiri akudwala matenda a LMBB * ndipo alibe mankhwala. Pa nthawiyo, madokotala sankadziwa zambiri za matenda amenewa. Zizindikiro zina za matendawa ndi vuto la maso, kunenepa kwambiri, kumera zala zina, kuchedwa kukula, mavuto ena a ubongo, vuto la shuga, nyamakazi ndiponso mavuto ena a impso. Choncho, ndinaona kuti kusamalira ana anga kudzakhala kovuta kwambiri. Kafukufuku wa posachedwapa akusonyeza kuti ku Britain, munthu mmodzi pa anthu 125,000 alionse ali ndi vutoli. N’kutheka kuti pali anthu ena amene ali ndi vuto limeneli koma sikuti limafika poipa kwambiri.

YEHOVA NDI MALO ATHU “OKWEZEKA NDIPONSO ACHITETEZO”

Nditangolowa m’banja, ndinacheza ndi wa Mboni za Yehova ndipo ndinazindikira nthawi yomweyo kuti akunena zoona. Koma mwamuna wanga sankafuna kumvetsera. Tinkasamukasamuka chifukwa cha ntchito ya mwamuna wangayo, choncho sindinkatha kusonkhana ndi mpingo. Komabe ndinapitiriza kuwerenga Baibulo ndiponso kupemphera kwa Yehova. Ndinalimbikitsidwa kwambiri pamene ndinawerenga kuti: “Yehova adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo kwa aliyense woponderezedwa, adzakhala malo okwezeka ndiponso achitetezo m’nthawi za masautso.” Ndinalimbikitsidwanso kudziwa kuti Yehova ‘sadzasiya ndithu anthu omufunafuna.’—Sal. 9:9, 10.

Gary anali ndi vuto la maso choncho pamene anali ndi zaka 6 tinamutumiza kusukulu yapadera kum’mwera kwa England. Zinthu zina zikamamudetsa nkhawa, ankandiimbira foni ndipo ndinkamuthandiza kudziwa mfundo zina za m’Baibulo. Patapita zaka zingapo Louise atabadwa, inenso ndinayamba kudwala matenda ena ofoola ziwalo ndiponso ena amene amachititsa kuti thupi liziphwanya kwambiri. Gary anabwera kudzakhalanso kunyumba kuchokera kusukulu kuja pamene anali ndi zaka 16. Koma vuto lake la maso linkakula ndipo mu 1975, boma linamuika m’gulu la anthu akhungu. Ndiyeno mu 1977, mwamuna wanga anatithawa.

Gary atabwera kusukulu, tinayamba kusonkhana ndi mpingo ndipo abale ndi alongowo ankatikonda. Ine ndinabatizidwa mu 1974. Ndinasangalala kwambiri pamene mkulu wina ankathandiza Gary kuti akwanitse kupirira mavuto amene ankakumana nawo pamene ankakula. Abale ndi alongo ena ankandithandizanso ndi ntchito zapakhomo ndipo kenako boma linasankha asanu mwa abale ndi alongo amenewa kuti liziwalipira pa ntchito yotisamalira. Zimenezi zatithandiza kwambiri.

Gary ankachita bwino mu mpingo ndipo anabatizidwa  mu 1982. Iye ankafunitsitsa kuchita upainiya wothandiza. Choncho ndinaganiza kuti inenso ndiuyambe ndipo tinachitira limodzi kwa zaka zambiri. Iye anasangalala kwambiri pamene woyang’anira dera wathu anamulimbikitsa kuti ayambe upainiya wokhazikika ndipo anauyambadi mu 1990.

Gary wachitidwa maopaleshoni awiri a mafupa a pafupi ndi chiuno. Yoyamba anachitidwa mu 1999 ndipo yachiwiri mu 2008. Koma Louise anabadwa ndi mavuto aakulu kwambiri. Iye anabadwa wakhungu ndipo nditaona kuti ali ndi chala china, ndinazindikira kuti matenda ake ndi omwe aja. Akuchipatala atamuunika anapeza kuti ziwalo zina zilinso ndi mavuto aakulu. Louise wapangidwa maopaleshoni ambiri akuluakulu ndipo asanu anali okhudza impso zake. Iye amadwalanso matenda a shuga.

Popeza kuti Louise amadziwa zimene zingachitike popangidwa opaleshoni, iye amauziratu madokotala ndiponso akuluakulu akuchipatala chifukwa chake salola kuikidwa magazi. Chifukwa cha zimenezi, anthuwo amamulemekeza ndiponso kumusamalira bwino.

TIMAKHALABE OSANGALALA

M’banja mwathu timatanganidwa kwambiri potumikira Yehova. Poyamba, ndinkatha maola ambiri ndikuwerengera Gary ndi Louise Baibulo ndiponso mabuku athu. Koma pano tili ndi ma CD, ma DVD ndiponso zinthu zina zomvetsera zimene timakopera pawebusaiti yathu ya www.pr418.com. Izi zimatithandiza kuti aliyense azipeza nthawi yake yomvetsera pokonzekera misonkhano kuti azikapereka ndemanga zogwira mtima.

Timayamikira kwambiri choonadi chamtengo wapatali chopezeka m’Mawu a Mulungu

Nthawi zina, Gary amafunika kuloweza mayankho ake koma akapatsidwa nkhani mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu amakamba kuchokera mumtima. Mu 1995 anaikidwa kukhala mtumiki wothandiza ndipo amathandiza kwambiri ku Nyumba ya Ufumu pa ntchito ngati kulandira abale ndi alongo komanso kusamalira zokuzira mawu.

Abale ndi alongo amapita ndi Gary mu utumiki ndipo nthawi zambiri amamuyendetsa panjinga yake. M’bale wina anamuthandiza kuchititsa phunziro la Baibulo ndi munthu wina. Gary analimbikitsanso mlongo wina amene anakhala wofooka kwa zaka 25. Panopa munthu wophunzirayo komanso mlongoyu ayamba kupita ku misonkhano.

Pamene Louise anali ndi zaka 9, agogo ake anamuphunzitsa kuluka ndipo ine ndi mlongo wina amene ankamusamalira tinamuphunzitsa kupeta nsalu. Iye amakonda kwambiri zolukaluka moti amaluka mashawelo a ana komanso mabulangete okongola oti azipatsa abale ndi alongo achikulire. Amapanganso timakadi n’kumatapo zithunzi ndipo anthu amene amawapatsa amayamikira kwambiri. Asanakwanitse zaka 15, anaphunzira kutaipa. Masiku ano, amagwiritsa ntchito kompyuta yapadera kuti azitumizirana mauthenga ndi anzake. Louise anabatizidwa ali ndi zaka 17. Ikafika nthawi yogawira timapepala tapadera mu utumiki, ine ndi Louise timachitira limodzi upainiya wothandiza. Mofanana ndi Gary, Louise amaloweza malemba oti aziuza anthu. Ena mwa malembawo ndi onena za malonjezo a Mulungu monga akuti m’dziko latsopano “maso a anthu akhungu adzatsegulidwa” ndiponso kuti “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yes. 33:24; 35:5.

Timayamikira kwambiri choonadi chamtengo wapatali chopezeka m’Mawu a Mulungu. Timayamikiranso abale ndi alongo athu chifukwa pakanapanda iwo, sitikanatha kuchita zambiri. Koposa zonse, timathokoza Yehova chifukwa chotithandiza kuti tizikhalabe osangalala.

^ ndime 5 Pali madokotala anayi amene anatulukira matendawa. Choncho amatchedwa matenda a Laurence-Moon-Bardet-Biedl potengera mayina a madokotalawo. Munthu amachita kubadwa nawo matendawa ndipo alibe mankhwala. Masiku ano anthu amangowatchula kuti matenda a Bardet-Biedl.