Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 PHUNZITSANI ANA ANU

Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Munthu Wachifwamba?

Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Munthu Wachifwamba?

Wachifwamba amene tikunena ndi amene Yesu akumulankhula pachithunzipa. Wachifwambayu akudzimvera chisoni chifukwa cha zimene anachita. Iye akupempha Yesu kuti: “Mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” Nde mmene ukuonera pachithunzipa, Yesu akulankhulana ndi munthu wachifwambayo. Kodi ukudziwa kuti Yesu akumuuza chiyani? * Yesu akumulonjeza kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”

Kodi ukuganiza kuti Paradaiso adzakhala kuti?— Kuti tipeze yankho lolondola, tiye tikambirane za Paradaiso amene Mulungu anapanga kuti Adamu ndi Hava azikhalamo. Kodi Paradaiso amene uja anali kuti? Anali kumwamba kapena padziko lapansi?

Ee, walondola, analidi padziko lapansi. Ndiye ngati Yesu ananena kuti wachifwamba uja adzakhala “m’Paradaiso,” ndiye kuti adzakhala padziko lapansi, likadzakhala Paradaiso. Kodi ukuganiza kuti Paradaiso ameneyu adzakhala wotani?— Tiye tione.

Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu atalenga Adamu ndi Hava, anawaika m’paradaiso padziko lapansi pompano. Paradaisoyo ankatchedwa ‘munda wa ku Edeni.’ Kodi ukuganiza kuti “munda wa ku Edeni” unali wokongola bwanji?— Wayankha bwino, mundawo uyenera kuti unali wokongola kwambiri kuposa malo ena aliwonse.

Ndiye ukuganiza kuti Yesu adzakhala padziko lapansi pano ndi wachifwamba uja?— Ayi, chifukwa nthawi imeneyo Yesu adzakhala ali kumwamba n’kumalamulira anthu amene adzakhale m’Paradaiso padziko lapansi. Ndiye pamene Yesu ankauza wachifwamba uja kuti adzakhala naye m’Paradaiso ankatanthauza kuti adzamuukitsa ndipo azidzamusamalira m’Paradaiso. Koma n’chifukwa chiyani Yesu adzalole munthuyu, amene poyamba anali wachifwamba, kuti adzakhale m’Paradaiso?— Tiye tikambirane mfundo inayake.

 N’zoona kuti munthuyu anachita zinthu zoipa kwambiri. Koma palinso anthu mabiliyoni ambiri amene anamwalira omwe ankachita zinthu zoipa. Ambiri mwa anthu amenewa ankachita zoipa chifukwa sankadziwa zimene YEHOVA amafuna kuti anthu azichita.

Ndiye anthu ngati amenewo, kuphatikizapo wachifwamba uja, adzaukitsidwa kuti akhale m’Paradaiso padziko lapansi. Iwo adzaphunzitsidwa zimene Mulungu amafuna ndipo adzakhala ndi mwayi wosonyeza ngati amakonda Yehova kapena ayi.

Kodi ukuganiza kuti anthu amenewa adzasonyeza bwanji kuti amakonda Mulungu?— Adzasonyeza kuti amakonda Mulungu akamadzachita zimene iye amafuna. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala m’Paradaiso pamodzi ndi anthu amene amakonda Yehova komanso amene amakondana.

^ ndime 3 Ngati mukuwerengera mwana nkhaniyi, mukapeza mzera muime kaye kuti anenepo maganizo ake.