Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndi Wowolowa Manja Ndiponso Wololera

Yehova Ndi Wowolowa Manja Ndiponso Wololera

“Yehova amakomera mtima aliyense, ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.”—SAL. 145:9.

1, 2. Kodi anthu amene ali pa ubwenzi ndi Yehova ali ndi mwayi wotani?

MLONGO wina dzina lake Monika anati: “Ine ndi mwamuna wanga takhala m’banja zaka pafupifupi 35 ndipo timadziwana bwino. Koma ngakhale kuti papita zaka zonsezi, tikuphunziranabe.” Mosakayikira, ndi mmene zilili ndi anthu ambiri amene ali pa banja kapena pa ubwenzi.

2 Timasangalala kudziwa bwino anthu amene timawakonda. Koma palibe munthu wabwino amene tingakhale naye pa ubwenzi kuposa Yehova. Sitingamalize kuphunzira za iye. (Aroma 11:33) Tili ndi mwayi wophunzira makhalidwe a Yehova mpaka muyaya ndipo tizidzawakonda kwambiri.—Mlal. 3:11.

3. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?

3 M’nkhani yapita ija tinaona kuti Yehova alibe tsankho ndiponso amathandiza anthu kuti azimasuka naye. Tiyeni tsopano tikambirane makhalidwe ena awiri a Yehova omwe ndi kuwolowa manja ndiponso kulolera. Tikatero, tidzafika povomereza kuti “Yehova amakomera mtima aliyense, ndipo ntchito zake zonse amazichitira chifundo.”—Sal. 145:9.

YEHOVA NDI WOWOLOWA MANJA

4. Kodi munthu wowolowa manja amatani?

4 Kodi munthu wowolowa manja amatani? Kuti tipeze yankho, tiyenera kuganizira mawu a Yesu a pa Machitidwe 20:35. Lembali limati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” Mawu achidule a Yesuwa amatithandiza kudziwa zimene munthu wowolowa manja amachita. Iye amagwiritsa ntchito nthawi yake, mphamvu zake komanso zinthu zake kuti athandize anthu ena ndipo amachita zimenezi mosangalala. Choncho tikhoza kudziwa kuti munthu ndi wowolowa manja osati poona kukula kwa mphatso yake koma ngati akupereka  mphatsoyo kuchokera pansi pa mtima. (Werengani 2 Akorinto 9:7.) Koma palibe munthu amene angafanane ndi ‘Mulungu wathu wachimwemwe’ pa nkhani yowolowa manja.—1 Tim. 1:11.

5. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wowolowa manja?

5 Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wowolowa manja? Iye amapereka zinthu zofunika kwa anthu onse, ngakhale amene sakumulambira. M’pake kuti Baibulo limati: “Yehova amakomera mtima aliyense.” Iye “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” (Mat. 5:45) N’chifukwa chake mtumwi Paulo anauza anthu ena osakhulupirira kuti: “[Yehova] anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.” (Mac. 14:17) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova ndi wowolowa manja kwa anthu onse.—Luka 6:35.

6, 7. (a) Kodi Yehova amasangalala kwambiri kupereka zinthu zofunika kwa ndani? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Mulungu amapereka zinthu zofunika kwa atumiki ake okhulupirika.

6 Yehova amasangalala kwambiri kupereka zinthu zofunika kwa atumiki ake okhulupirika. Pa nkhani imeneyi, Mfumu Davide inalemba kuti: “Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya.” (Sal. 37:25) Akhristu ambiri okhulupirika adzionera okha umboni wa mawu amenewa. Tiyeni tikambirane chitsanzo chimodzi.

7 Zaka zingapo zapitazo, mpainiya wina dzina lake Nancy anakumana ndi vuto. Iye anati: “Tsiku lina ndinkafuna ndalama zokwana madola 66 kuti ndilipire lendi mawa lake. Ndinasowa mtengo wogwira. Ndinapempherera vutoli kenako n’kunyamuka kupita kuntchito yanga yoperekera chakudya mulesitilanti. Nthawi zambiri makasitomala amandipatsa ndalama pondithokoza koma sindinkayembekezera kupatsidwa ndalama zambiri chifukwa chakuti tsiku limenelo sikunkabwera makasitomala ambiri. Koma ndinadabwa kuona kuti kunabwera anthu ambiri. Pamene ndinkaweruka, ndinawerenga ndalama zimene ndinalandira n’kupeza kuti zakwana madola 66 ndendende.” Nancy amaona kuti Yehova anayankha pemphero lake ndipo anamupatsa zimene ankafunikira.—Mat. 6:33.

8. Kodi ndi mphatso iti imene Yehova wapereka mowolowa manja kwa aliyense?

8 Koma pali mphatso ina imene Yehova wapereka mowolowa manja kwa aliyense. Mphatso yake ndi nsembe ya dipo ya Mwana wake. Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Pa lembali, mawu akuti “dziko” akutanthauza anthu. Choncho Yehova wapereka  mowolowa manja mphatso imeneyi kwa aliyense amene angafune kuilandira. Anthu amene amakhulupirira Yesu adzalandira ‘moyo wochuluka,’ kapena kuti moyo wosatha. (Yoh.10:10) Umenewutu ndi umboni waukulu kwambiri wosonyeza kuti Yehova ndi wowolowa manja.

KHALANI OWOLOWA MANJA NGATI YEHOVA

Aisiraeli ankalimbikitsidwa kukhala owolowa manja ngati Yehova (Onani  ndime 9)

9. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yowolowa manja?

 9 Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yowolowa manja? Yehova “amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.” Nafenso tiyenera kukhala “okonzeka kugawira ena” kuti nawonso azisangalala. (1 Tim. 6:17-19) Mwachitsanzo, tingachite bwino kupereka zinthu kwa anzathu komanso kwa anthu ovutika ndipo tizichita zimenezi mosangalala. (Werengani Deuteronomo 15:7.) Kodi tingatani kuti tizikumbukira kugawira ena zinthu? Abale ndi alongo ena akapatsidwa zinthu zinazake, amayesetsa kuti nawonso apereke zinthu kwa anthu ena. Mu mpingo, tili ndi abale ndi alongo ambirimbiri amene amayesetsa kukhala owolowa manja.

10. Tchulani njira ina yabwino kwambiri imene tingasonyezere kuti ndife owolowa manja.

10 Njira ina yabwino kwambiri yosonyeza kuti ndife owolowa manja ndi kulankhula mawu olimbikitsa kapena kuchita zinthu zina zothandiza anzathu. Tizigwiritsa ntchito nthawi ndiponso mphamvu zathu kuti tizichita zimenezi. (Agal. 6:10) Kuti tidziwe ngati tikuchita bwino pa nkhani imeneyi, tingadzifunse kuti: ‘Kodi anthu ena amaona kuti ndine wofunitsitsa kudzipereka kuti ndimvetsere akamafotokoza nkhawa zawo? Kodi ndimavomera munthu wina akandipempha kuti ndimuthandize zinazake? Kodi ndi liti pamene ndinathokoza kuchokera pansi pa mtima munthu wa m’banja lathu kapena Mkhristu mnzanga?’ Tikamayesetsa ‘kukhala opatsa,’ timalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova komanso anzathu.—Luka 6:38; Miy. 19:17.

11. Kodi ndi zinthu ziti zimene tingapereke mowolowa manja kwa Yehova?

  11 Anthufe tikhozanso kupereka zinthu mowolowa manja kwa Yehova. Malemba amatilimbikitsa ‘kulemekeza Yehova ndi zinthu zathu zamtengo wapatali.’ (Miy. 3:9) Pa lembali, mawu akuti ‘zinthu zamtengo wapatali’ akutanthauza nthawi yathu, mphamvu zathu komanso zinthu zathu zimene tingapereke mowolowa manja potumikira Yehova. Nawonso ana akhoza kuphunzitsidwa kupereka zinthu kwa Yehova mowolowa manja. Bambo wina dzina lake Jason anati: “Banja lathu likafuna kupereka chopereka ku Nyumba ya Ufumu, timapatsa ana athu kuti akaponye m’bokosi. Iwo amasangalala kuchita zimenezi podziwa kuti akupereka kwa Yehova.” Ana amene amaona kuti kupereka zinthu kwa Yehova n’kosangalatsa, amapitiriza kuchita zimenezi ngakhale pamene akula.—Miy. 22:6.

YEHOVA NDI WOLOLERA

12. Kodi munthu wololera amatani?

12 Kulolera ndi khalidwe lina losangalatsa limene Yehova amasonyeza. Kodi munthu wololera amatani? (Tito 3:1, 2) Iye sakhala wokakamira malamulo, kukhwimitsa zinthu kapena kuchita zinthu mwankhanza. Koma amayesetsa kukomera mtima anthu ndipo amaganizira mmene zinthu zilili pa moyo wawo. Iye amamvetsera mofunitsitsa ena akamalankhula. Amakhalanso wokonzeka kusintha, ngati n’zotheka, kuti achite zinthu zimene enawo akufuna.

13, 14. (a) Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wololera? (b) Kodi nkhani ya Loti imasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wololera?

13 Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wololera? Iye ndi wokoma mtima ndipo amaganizira zimene atumiki ake akufuna. Nthawi zambiri amachita zimene iwo apempha. Mwachitsanzo, tiyeni tione mmene Yehova anachitira zinthu ndi Loti. Pamene Yehova anafuna kuwononga mizinda ya Sodomu ndi Gomora, iye anauza Loti kuti athawire kumapiri. Koma pa zifukwa zina, Loti anapempha kuti athawire kwina. Apatu Loti anapempha Yehova kuti asinthe malangizo ake.—Werengani Genesis 19:17-20.

14 Mwina tikhoza kuganiza kuti Loti anali wofooka kapena wosamvera. Ndipotu panalibe chifukwa choopera chifukwa Yehova akanamuteteza kulikonse. Koma Loti ankaopabe ndipo Yehova analolera maganizo ake. Mulungu analolera kuti Loti athawire kumzinda umene ankafunanso kuwononga. (Werengani Genesis 19:21, 22.) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova saumirira maganizo ake kapena kukhwimitsa zinthu koma ndi wololera.

15, 16. Kodi Chilamulo cha Mose chinasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wololera? (Onani chithunzi patsamba 12.)

15 Umboni wina woti Yehova ndi wololera timaupeza m’Chilamulo cha Mose. Ngati Mwisiraeli anali wosauka moti sangathe kupereka nsembe ya nkhosa kapena mbuzi, ankaloledwa kupereka njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri. Koma bwanji ngati munthuyo anali wosauka kwambiri moti sangathenso kupereka mbalame ziwirizi? Zikatero, Yehova ankamulola kupereka ufa wochepa. Komatu ufa wake sunkayenera kukhala ufa wamba. Unkayenera kukhala “wosalala” ngati umene anthu ankagwiritsa ntchito akalandira alendo olemekezeka. (Gen. 18:6) Kodi zimenezi zinali ndi ubwino uliwonse?—Werengani Levitiko 5:7, 11.

16 Kuti timvetse ubwino wake, tiyerekeze kuti ndinu Mwisiraeli ndipo ndinu wosauka. Pamene mukufika kukachisi kuti mupereke nsembe ya ufa wanu wochepa, mukuona Aisiraeli ena opeza bwino akubweretsa ziweto zawo. Mwina poyamba mukuchita manyazi ndi nsembe yanuyo. Koma mungalimbikitsidwe mukakumbukira kuti nsembe yanu ndi yamtengo wapatali pa maso pa Yehova. Chifukwa chimodzi chimene tikunenera zimenezi  n’chakuti Yehova ankafuna kuti ufawo uzikhala wabwino kwambiri. Zinali ngati Yehova akuuza Aisiraeli osauka kuti: ‘Ndikudziwa kuti simungakwanitse kupereka zimene anzanuwo akupereka koma mukundipatsa zimene mungakwanitse ndipo ndi zabwino kwambiri.’ Kunena zoona, Yehova ndi wololera chifukwa amaganizira zimene atumiki ake angakwanitse ndiponso mmene zinthu zilili pa moyo wawo.—Sal. 103:14.

17. Kodi Yehova amasangalala tikamamutumikira motani?

 17 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova ndi wololera ndipo amasangalala ngati timamutumikira ndi moyo wathu wonse. (Akol. 3:23) Mlongo wina wachikulire wa ku Italy, dzina lake Constance, anati: “Ndimakonda kwambiri kuuza anthu za Mlengi wanga. N’chifukwa chake ndimapitiriza kulalikira ndiponso kuphunzitsa anthu Baibulo. Nthawi zina, ndimadandaula kuti sindingathe kuchita zambiri chifukwa thupi langa lafooka. Koma Yehova amadziwa zimene ndingakwanitse ndipo amandikonda. Amayamikiranso zimene ndimakwanitsa kuchita.”

KHALANI OLOLERA NGATI YEHOVA

18. Kodi makolo angatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yololera?

18 Kodi tingatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yololera? Taganizirani mmene Yehova anachitira zinthu ndi Loti. Yehova anali ndi ulamuliro wouza Loti zochita koma anamvetsera mokoma mtima pamene Lotiyo ankanena maganizo ake. Mulungu anasintha n’kulolera zimene Loti anapempha. Ngati ndinu makolo, kodi mungatsanzire bwanji Yehova? Mungachite bwino kumvetsera zimene ana anu akupempha, mwina n’kulolera maganizo awo. Pa nkhani imeneyi, Nsanja ya Olonda ya September 1, 2007 inanena kuti mwina makolo angakambirane ndi ana awo pokonza malamulo a m’banja. Mwachitsanzo, makolo ali ndi ufulu wosankha nthawi imene ana ayenera kufika pakhomo. Ngakhale zili choncho, makolo achikhristu akhoza kumvetsera maganizo a ana awo pa nkhani imeneyi. Atakambirana ndi anawo, mwina makolo angasinthe nthawiyo ngati akuona kuti sipangakhale mavuto ena. Nthawi zambiri, ana savutika kumvetsa ndiponso kutsatira malamulo ngati anakambirana ndi makolo awo pokonza malamulowo.

19. Kodi akulu angatsanzire bwanji Yehova pa nkhani yololera?

19 Nawonso akulu ayenera kutsanzira Yehova pa nkhani yololera. Iwo ayenera kuganizira mmene zinthu zilili pa moyo wa Akhristu anzawo. Kumbukirani kuti Yehova ankayamikiranso nsembe zimene Aisiraeli osauka ankapereka. Mu mpingo mumakhalanso abale ndi alongo ena amene sangachite zambiri mu utumiki chifukwa chakuti ndi odwala kapena okalamba. Kodi akulu angachite chiyani ngati Akhristu oterewa akudzimva kuti palibe chimene akuchita? Iwo angawauze mokoma mtima kuti Yehova amawakonda chifukwa chakuti akumupatsa zonse zimene angakwanitse.—Maliko 12:41-44.

20. Kodi kulolera kumatanthauza kulephera dala kuchita zinthu zina potumikira Yehova? Fotokozani.

20 Komabe tisamaganize kuti ndife ololera pamene tikulephera mwadala kuchita zinthu zina potumikira Yehova. Ena amachita zimenezi pongofuna kudzikhululukira. (Mat. 16:22) Si bwino kuchita zinthu mwaulesi poganiza kuti kumeneko n’kulolera. Tonsefe tiyenera kuchita khama kwambiri potumikira Yehova. (Luka 13:24) Nkhani ya kulolerayi tiyenera kuiona moyenera. Tiyenera kuyesetsa mwakhama potumikira Yehova koma n’kumakumbukiranso kuti Yehova safuna kuti tizichita zimene sitingakwanitse. Iye amasangalala tikamamupatsa zonse zimene tingathe. Ndi mwayitu waukulu kwambiri kutumikira Ambuye wathu yemwe ndi wololera komanso woyamikira. M’nkhani yotsatira tikambirana makhalidwe ena awiri a Yehova.—Sal. 73:28.

“Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.”—Miy. 3:9 (Onani  ndime 11)

“Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse.”—Akol. 3:23. (Onani  ndime 17)