Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi anthu ena amaona kuti Baibulo lili ngati chithumwa m’njira iti? Nanga Akhristu amaona bwanji zimenezi?

Anthu ena amakhulupirira kuti kungotsegula Baibulo paliponse n’kuwerenga vesi limene ayambirira kuona kukhoza kuwathandiza. Koma Akhristu oona sawombeza kapena kuchita zamatsenga. Iwo amaphunzira kwambiri Baibulo kuti adziwe zinthu zoona ndiponso kuti Mulungu awatsogolere.—12/15, tsamba 3.

Kodi “dziko” limene likupita likuimira chiyani?

“Dziko” limene likupita likuimira anthu amene zochita zawo sizigwirizana ndi zofuna za Mulungu. (1 Yoh. 2:17) Dziko lapansi lenilenili ndiponso anthu okhulupirika adzapulumuka.—1/1, tsamba 5-7.

Ngakhale kuti Abele anafa, kodi akutilankhulabe m’njira iti? (Aheb. 11:4)

Iye amalankhulabe kudzera mwa chikhulupiriro chake. Tikhoza kuphunzira za chikhulupiriro chake ndiponso kuchitsanzira. Chitsanzo cha Abele ndi chothandiza kwambiri ngakhale masiku ano.—1/1, tsamba 12.

Kodi ndi zinthu ziti zimene sitiyenera kulola kuti zisokoneze ubwenzi wathu ndi Mulungu?

Zinthu zina ndi ntchito, zosangalatsa, ubwenzi wathu ndi achibale amene achotsedwa, zipangizo zamakono, kudera nkhawa thanzi lathu, kuona ndalama molakwika ndiponso kuona kuti ndife anzeru kwambiri kapena apamwamba.—1/15, tsamba 12-21.

Kodi tikuphunzira chiyani pa kudzichepetsa kwa Mose?

Mose sankangoganizira kwambiri za udindo wake. Iye sankadzidalira koma ankadalira kwambiri Mulungu. Ifenso tisamalole udindo, mphamvu kapena luso linalake kutipangitsa kukhala odzikuza. M’malomwake tizidalira Yehova. (Miy. 3:5, 6)—2/1, tsamba 5.

Kodi anthu oukitsidwa adzakhala kuti?

Anthu 144,000 okha adzapita kumwamba. Koma ambiri adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo wosatha padziko lapansi.—3/1, tsamba 6.

Kodi mawu akuti Aisiraeli “sanachite mdulidwe wa mumtima” akutanthauza chiyani? (Yer. 9:26)

Iwo sankamvera Mulungu ndipo ankafunika kuchotsa zinthu zimene zinkawachititsa kukhala ndi mtima wosamvera. Zinthu zake ndi maganizo awo, zokonda zawo komanso zolinga zawo zimene zinali zosemphana ndi zofuna za Mulungu. (Yer. 5:23, 24)—3/15, tsamba 9-10.

Kodi Yesu anasonyeza bwanji zimene tingachite kuti tikhale ndi moyo waphindu?

Iye anali ndi cholinga pa moyo wake chomwe chinali kuchita chifuniro cha Mulungu. Iye ankakonda kwambiri Atate wake komanso ankakonda anthu. Yesu ankadziwanso kuti Atate wake amamukonda komanso amasangalala naye. Zinthu zimenezi n’zimene zingathandize munthu kukhala ndi moyo waphindu.—4/1, tsamba 4-5.

Tchulani amene ali kumbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova?

Mbaliyi ili ndi Bungwe Lolamulira, makomiti a nthambi, oyang’anira oyendayenda, mabungwe a akulu, mipingo ndi munthu wina aliyense wa Mboni payekha.—4/15, tsamba 29.

Kodi chilango chimene Mulungu anapereka kwa anthu osiyanasiyana chimasonyeza kuti iye ndi wankhanza?

Yehova sasangalala ndi imfa ya anthu oipa. (Ezek. 33:11) Zilango zimene anapereka m’mbuyomu zimasonyeza kuti iye amachenjeza kaye anthu. Zimenezi zimatipatsa chiyembekezo chakuti tidzapulumuka akamadzapereka chilango m’tsogolomu.—5/1, tsamba 5-6.

Kodi Aisiraeli ankapha anthu oipa powapachika pamtengo?

Ayi. Anthu a mitundu ina ankachita zimenezi koma osati Aisiraeli. Malemba Achiheberi amasonyeza kuti kalelo anthu oipa ankaphedwa kaye powaponya miyala asanawapachike. (Lev. 20:2, 27) Kenako ankapachika mtembowo pamtengo. Izi zinkakhala ngati chenjezo kwa anthu ena.—5/15, tsamba 13.

N’chifukwa chiyani padzikoli palibe mtendere weniweni?

Ngakhale kuti anthu achita zinthu zambirimbiri, iwo sanalengedwe kuti azitha kudzilamulira okha. (Yer. 10:23) Dziko lonseli lili m’manja mwa Satana. N’chifukwa chake anthu sangathe kubweretsa mtendere padziko lonse. (1 Yoh 5:19)—6/1, tsamba 16.