Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mwapatulidwa

Mwapatulidwa

Mwapatulidwa

“Mwasambitsidwa kukhala oyela, mwapatulidwa.”—1 AKOR. 6:11.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

N’cifukwa ciani tiyenela kupewa mayanjano oipa?

Ndi motani mmene tingacilikizile dongosolo la gulu la Mulungu?

Kodi n’ciani cidzatithandiza kuika zinthu za kuuzimu patsogolo ndi kuteteza dzina lathu monga Akristu?

1. Kodi ndi zinthu zokhumudwitsa ziti zimene Nehemiya anapeza pamene anabwelela ku Yerusalemu? (Onani cithunzi-thunzi cimene cili kuciyambi kwa nkhani ino.)

 ANTHU a ku Yerusalemu anadabwa odabwa ndi zimene zinali kucitika. Munthu wovuta wa ku dziko lina anali kukhala mu cipinda ca m’kacisi. Alevi anasiya kugwila nchito yao. M’malo motsogolela pa nkhani za kulambila, akulu a ku Yerusalemu anali kucita malonda pa tsiku la Sabata. Aisiraeli ambili anali kukwatila anthu amitundu ina. Izi zinali zinthu zina zokhumudwitsa zimene Nehemiya anapeza zikucitika pamene anabwelela ku Yerusalemu pambuyo pa caka ca 443 B.C.E.—Neh. 13:6.

2. Kodi Aisiraeli anakhala bwanji mtundu wopatulika?

2 Aisiraeli anali mtundu wopatulika kwa Mulungu. M’caka ca 1513 B.C.E., Aisiraeli anali ofunitsitsa kucita cifunilo ca Yehova. Iwo anati: “Mau onse amene Yehova wanena tidzacita.” (Eks. 24:3) Conco, Mulungu anawapatula kukhala mtundu wake wosankhidwa. Umenewo unali mwai wamtengo wapatali. Pambuyo pa zaka 40, Mose anawakumbutsa kuti: “Ndinu anthu oyela kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani kuti mukhale anthu ake, cuma cake capadela, mwa anthu onse okhala padziko lapansi.”—Deut. 7:6.

3. Kodi mkhalidwe wa kuuzimu wa Ayuda unali wotani pamene Nehemiya anafika ku Yerusalemu kaciŵili?

3 Koma zomvetsa cisoni zinali zakuti, cisangalalo cimene Aisiraeli anali naco poyamba monga mtundu woyela sicinakhalitse. Ngakhale kuti panali anthu ena amene anali kutumikila Mulungu, kaŵili-kaŵili Ayuda ambili anali kungofuna kuoneka ngati oyela kapena opembedza m’malo mocita cifunilo ca Mulungu. Pamene Nehemiya anafika ku Yerusalemu kaciŵili, panali patapita zaka pafupi-fupi 100 kucokela pamene Ayuda okhulupilika anabwelela ku Yerusalemu kucokela ku Babulo kuti abwezeletse kulambila koona. Koma Nehemiya anapezanso kuti cangu ca mtundu umenewo pa zinthu za kuuzimu cinali kucepela-cepela.

4. Kodi tidzakambilana mfundo zotani zimene zingatithandize kukhalabe anthu opatulidwa?

4 Monga mmene zinalili ndi Aisiraeli, tinganene kuti Mboni za Yehova masiku ano zinapatulidwa ndi Mulungu. Akristu odzozedwa ndiponso a “khamu lalikulu” ndi oyela, opatulidwa kuti acite utumiki wopatulika. (Chiv. 7:9, 14, 15; 1 Akor. 6:11) Palibe amene angafune kutaya mwai wokhala wopatulika kwa Mulungu monga mmene Aisiraeli anacitila patapita nthawi. Kodi n’ciani cimene cingatithandize kuti tikhalabe oyela ndiponso kuti tikhale ndi zocita zambili mu utumiki wa Yehova? M’nkhani ino, tidzaphunzila mfundo zinai zimene zili mu Nehemiya caputala 13 zimene zingatithandize kucita zimenezo. Mfundo zimenezo ndi izi: (1) Pewani mayanjano oipa; (2) cilikizani dongosolo la gulu la Mulungu; (3) ikani zinthu za kuuzimu patsogolo ndi (4) tetezani dzina lanu monga Akristu. Tiyeni tsopano tikambilane mfundo zimenezi iliyonse payokha.

PEWANI MAYANJANO OIPA

5, 6. Kodi Eliyasibu ndi Tobia anali ndani? Nanga n’cifukwa ciani Eliyasibu anali kugwilizana ndi Tobia?

5 Ŵelengani Nehemiya 13:4-9. Si zopepuka kukhalabe oyela cifukwa cakuti makhalidwe oipa ali paliponse. Ganizilani za Eliyasibu ndi Tobia. Eliyasibu anali mkulu wa ansembe, Tobia anali waciamoni ndipo anali kugwila nchito mu ofesi ya mfumu ya Perisiya ku Yudeya. Tobia ndi anzake anali kufuna kulepheletsa Nehemiya kumanga mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 2:10) Aamoni anali kuletsedwa kulowa m’mabwalo a kacisi. (Deut. 23:3) Koma n’cifukwa ciani mkulu wa ansembe anakonzela Tobia malo m’cipinda codyelamo ca pakacisi?

6 Tobia anali wacibale wa Eliyasibu. Tobia ndi mwana wake wamwamuna Yehohanani anakwatila akazi aciyuda ndipo Ayuda ambili anali kutamanda kwambili Tobia. (Neh. 6:17-19) Manase mdzukulu wa Eliyasibu, anakwatila mwana wa Sanibalati amene anali Msamariya, mnzake kwambili wa Tobia. (Neh. 13:28) Mkulu wa ansembe Eliyasibu, analola Tobia munthu wosakhulupilila Mulungu ndi wotsutsa kumuuza zocita mwina cifukwa cakuti anthu amenewa anali pacibale. Koma Nehemiya anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova mwa kuponya katundu yense wa Tobia kunja kwa cipinda codyelamo.

7. Kodi ndi motani mmene akulu ndi anthu ena angapewele kucita zinthu zimene zingawadetse pamaso pa Yehova?

7 Monga anthu odzipeleka kwa Mulungu, cinthu cofunika kwambili kwa ife ndi kukhala okhulupilika kwa Yehova nthawi zonse. Ngati tilephela kutsatila mfundo zake zolungama, sitingakhale opatulika kwa iye. Tisalole cibale kuti citipangitse kuphwanya mfundo za m’Baibo. Akulu amatsogoleledwa ndi maganizo a Yehova osati maganizo ao kapena mmene amaonela anthu ena. (1 Tim 5:21) Akulu amayesetsa kupewa ciliconse cimene cingaononge ubwenzi wao ndi Mulungu.—1 Tim. 2:8.

8. Kodi atumiki onse odzipeleka a Yehova ayenela kukumbukila ciani pa nkhani ya mayanjano ao?

8 Tiyenela kukumbukila kuti “kugwilizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akor. 15:33) Acibale athu ena angatipangitse kucita zinthu zoipa. Eliyasibu poyamba anali citsanzo cabwino kwa anthu cifukwa cakuti anacilikiza kwambili Nehemiya pa nchito yomanga mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 3:1) Koma patapita nthawi, Eliyasibu anacita zinthu zimene zinam’pangitsa kukhala wodetsedwa pamaso pa Yehova cifukwa cosonkhezeledwa ndi Tobia ndi anthu ena. Mabwenzi abwino amatilimbikitsa kucita zinthu zabwino pa umoyo wacikristu monga kuŵelenga Baibo, kupezeka pa misonkhano yacikristu ndi kupita muutumiki wakumunda. Timakonda ndi kuyamikila kwambili acibale amene amatilimbikitsa kucita zinthu zabwino.

CILIKIZANI DONGOSOLO LA GULU LA MULUNGU

9. N’cifukwa ciani nchito za pa kacisi sizinali kuyenda bwino? Nanga Nehemiya anaimba mlandu ndani cifukwa ca zimenezi?

9 Ŵelengani Nehemiya 13:10-13. Zikuoneka kuti panthawi imene Nehemiya anabwelela ku Yerusalemu, anthu anali kupeleka zopeleka zocepa kwambili za pa kacisi. Conco, Alevi anayamba kusiya kugwila nchito zao za pa kacisi ndi kukagwila nchito ku minda yao kuti azidzicilikiza paumoyo. Nehemiya anayamba kuimba mlandu atsogoleli ao. Iwo anali kulephela kugwila nchito yao. Mwina io anali kulephela kusonkhanitsa cakhumi kucokela kwa anthu, mwinanso anali kusonkhanitsa koma sanali kupeleka ku kacisi monga mmene anali kufunikila kucitila. (Neh. 12:44) Motelo, Nehemiya anaonetsetsa kuti cakhumi cayamba kusonkhanitsidwa. Iye anaika amuna okhulupilika kuti aziyang’anila zipinda zosungilamo katundu za pa kacisi ndi kuti azigaŵila zopelekazo kwa Alevi.

10, 11. Kodi anthu a Mulungu ali ndi mwai wotani pa nkhani yocilikiza kulambila koona?

10 Kodi tikuphunzilapo ciani pamenepa? Tikukumbutsidwa kuti tili ndi mwai wolemekeza Yehova ndi cuma cathu. (Miy. 3:9) Pamene tipeleka zopeleka kuti ticilikize nchito yake, timangopatsa Yehova zinthu zimene ndi zake kale. (1 Mbiri 29:14-16) Mwina ife tingaone kuti tilibe zambili zimene tingapeleke kuti tilemekeze Yehova. Koma ngati tili ndi mtima wofunitsitsa kupeleka, iye amayamikila copeleka ciliconse cimene tingapeleke.—2 Akor. 8:12.

11 Kwa zaka zambili, banja linalake lalikulu linali kuitanila banja lina lacikulile limene linali kucita upainiya wapadela kuti likadye nao cakudya ku nyumba kwao. Anali kucita zimenezi kamodzi mlungu uliwonse. Ngakhale kuti banja lalikulu limeneli linali la ana 8, mai wa m’banjalo anali kukonda kunena kuti, “Ndimaphikila anthu 10 nthawi zonse. Conco, kuonjezela cakudya ca anthu ena aŵili si nkhani yovuta.” Kudya cakudya ndi banja lacikulile limenelo, sinali nkhani yovuta ku banja lalikulu lija. Koma apainiya aja anali kuyamikila kwambili mzimu woceleza wa banjalo. Iwo anathandiza banja lija cifukwa cakuti mau ao ndi citsanzo cao cabwino zinalimbikitsa ana a m‘banjalo kukhala ndi zolinga za kuuzimu. Ndipo m’kupita kwa nthawi ana onse a m’banja lalikulu limenelo anayamba utumiki wa nthawi zonse.

12. Kodi akulu ndi atumiki othandiza mumpingo amakhala zitsanzo m’njila yotani?

12 Phunzilo lina limene tingaphunzile pa nkhani ya Nehemiya ndi lakuti: Akulu ndi atumiki othandiza ayenela kukhala zitsanzo zabwino pa nkhani ya kulambila Yehova. Anthu ena mumpingo amapindula cifukwa ca citsanzo cao cabwino. Mwa njila imeneyi, akulu amatsatilanso citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye anacilikiza kulambila koona ndipo anali kupeleka malangizo othandiza. Mwacitsanzo, iye anapeleka malangizo othandiza pankhani yopanga zopeleka.—1 Akor. 16:1-3; 2 Akor. 9:5-7.

IKANI ZINTHU ZA KUUZIMU PATSOGOLO

13. Kodi Ayuda ena analephela bwanji kulemekeza Sabata?

13 Ŵelengani Nehemiya 13:15-21. Tikatangwanika ndi zinthu za kuthupi, tikhoza kufooka mwa kuuzimu. Mogwilizana ndi lemba la Ekisodo 31:13, Aisiraeli anauzidwa kusunga Sabata mlungu uliwonse n’colinga cowakumbutsa kuti anali anthu opatulidwa. Anali kufunikila kupatula tsiku la Sabata kuti acite kulambila kwa pabanja, kupemphela ndi kusinkha-sinkha pa Cilamulo ca Mulungu. Koma kwa anthu a m’nthawi ya Nehemiya, tsiku la Sabata linali tsiku wamba cifukwa cakuti anali kucitanso malonda patsiku limeneli. Nkhani ya kulambila anali kuikankhila pambali. Poona zimene zinali kucitika, Nehemiya analamula kuti zipata za mzinda zizitsekedwa tsiku la Sabata lisanayambe. Ndiyeno anthu onse amalonda akumaiko ena anali kuwathamangitsa tsiku la Sabata lisanayambe.

14, 15. (a) Kodi n’ciani cimene cingaticitikile ngati titangwanika ndi kufuna-funa ndalama? (b) Kodi tingalowele motani mu mpumulo wa Mulungu?

14 Kodi citsanzo ca Nehemiya cimatiphunzitsa ciani? Cimatiphunzitsa kuti sitiyenela kutangwanika ndi kufuna-funa ndalama. Ngati sitisamala tingayambe kunyalanyaza zinthu za kuuzimu cifukwa cokonda kwambili kucita malonda kapena nchito yathu yakuthupi. Tiyenela kukumbukila cenjezo la Yesu lonena za kutumikila ambuye aŵili. (Ŵelengani Mateyu 6:24) Ngakhale kuti Nehemiya anali ndi cuma, kodi iye anagwilitsila nchito bwanji nthawi yake pamene anali ku Yerusalemu? (Neh. 5:14-18) M’malo mocita malonda ndi anthu a ku Turo kapena anthu ena, iye anagwilitsila nchito nthawi yake kuthandiza abale ake ndi kucita zinthu zina zimene zinathandiza kuti dzina la Yehova liyeletsedwe. Mofananamo, akulu ndi atumiki othandiza masiku ano amaonetsetsa kuti akucita zinthu zimene zingapindulitse mpingo, ndipo abale ndi alongo amayamikila mzimu umenewo. Cifukwa ca zimenezi, pakati pa anthu a Mulungu pamakhala cikondi, mtendele ndi citetezo.—Ezek. 34:25, 28.

15 Ngakhale kuti Akristu sayenela kusunga Sabata mlungu uliwonse, Paulo anati, “mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu.” Ndipo iye anaonjezelanso kuti “Munthu amene walowa mu mpumulo wa Mulungu, ndiye kuti wapumanso pa nchito zake, monga mmene Mulungu anapumila pa nchito zake.” (Aheb. 4:9, 10) Monga Akristu, tingalowe mu mpumulo wa Mulungu ngati timamumvela ndi kugwila nchito mogwilizana ndi cifunilo cake. Kodi inuyo ndi a m’banja lanu mumaona kuti kulambila kwa pabanja, kupezeka pa misonkhano, ndi ulaliki wakumunda ndi zinthu zofunika kwambili pa umoyo wanu? Tiyenela kulankhula molimba mtima ndi amene anatilemba nchito kapena anzathu amene timacita nao malonda maka-maka ngati saona kuti zinthu za kuuzimu ndi zofunika kwambili kwa ife. M’mau ena tinganene kuti tifunikila ‘kutseka zipata za mzinda ndi kuthamangitsa anthu a ku Turo’ monga mmene Nehemiya anacitila, n’colinga cakuti tigwilitsile nchito nthawi yathu yambili pa zinthu zopatulika. Popeza kuti ndife anthu opatulidwa, tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi zocita zanga pa umoyo zimaonetsa kuti ndine wopatulidwa kucita cifunilo ca Yehova?’—Mat. 6:33.

TETEZANI DZINA LANU MONGA MKRISTU

16. Kodi mwai umene anthu anali nao wodziŵika kukhala mtundu wopatulidwa wa Mulungu unadodometsedwa bwanji m’nthawi ya Nehemiya?

16 Ŵelengani Nehemiya 13:23-27. M’nthawi ya Nehemiya, amuna aciisiraeli anali kukwatila akazi a ku maiko ena. Pa ulendo wake woyamba ku Yerusalemu, Nehemiya anauza akulu onse a kumeneko kuti alembe pa cikalata maina ao kuonetsa kuti alumbila kuti sadzakwatila akazi acikunja. (Neh. 9:38; 10:30). Koma pambuyo pa zaka zocepa, Nehemiya anapeza kuti amuna aciyuda anakwatila akazi a ku maiko ena ndiponso anali pafupi kutaya mwai wao wodziŵika monga anthu opatulidwa a Mulungu. Ana amene akazi a ku maiko ena anabeleka anali kulephela kuŵelenga kapena kukamba Ciheberi. Atakula, kodi anawo akanadzicha Aisiraeli? Kapena kodi io akanadziona kuti ndi ana aciasidodi, aciamoni ndi acimowabu? Kodi zikanatheka bwanji kuti io amvetsetse Cilamulo ca Mulungu popeza kuti io sanali kudziŵa Ciheberi? Kodi zikanatheka bwanji kuti adziŵe Yehova ndi kusankha kum’tumikila m’malo mwa milungu yonama imene amai ao anali kulambila? Vuto limenelo linafunika kuthetsedwa mwamsanga ndipo ndi zimene Nehemiya anacita.—Neh. 13:28.

17. Kodi makolo angathandize bwanji ana ao kukhala pa unansi wolimba ndi Yehova?

17 Masiku ano, tiyenela kuthandiza ana athu kuti adziŵike monga Akristu. Makolo muyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi ana anga amadziŵa kulankhula bwino lomwe “cilankhulo coyela,” cimene ndi coonadi ca m’Malemba? (Zef. 3:9) Pamene ana anga akuceza, kodi amaonetsa kuti akutsogoleledwa ndi mzimu wa Mulungu kapena wa dziko?’ Musataye mtima ngati mukuona kuti afunika kuongolela mbali zina. Zimatenga nthawi kuti munthu aphunzile cilankhulo catsopano maka-maka ngati pali zododometsa zambili. Ana anu amakumana ndi ziyeso zimene zingawapangitse kulephela kumvela Mulungu. Conco, gwilitsilani nchito nthawi imene mumacita Kulambila kwa Pabanja, ndi mipata ina kuthandiza ana anu kuumba unansi wolimba ndi Yehova. (Deut. 6:6-9) Asonyezeni mapindu amene munthu amakhala nao ngati akhala wosiyana ndi dziko la Satana. (Yoh. 17:15-17) Ndipo yesetsani kuwafika pamtima.

18. N’cifukwa ciani makolo acikristu ali pamalo abwino othandiza ana ao kudzipeleka kwa Yehova?

18 N’zoona kuti panthawi ina mwana ayenela kupanga cosankha cake pankhani yotumikila Mulungu. Komabe, pali zambili zimene makolo ayenela kucita kuti athandize anawo. Ayenela kukhala citsanzo cabwino ca ana ao. Afunikanso kuika malile pa zinthu zimene anawo angafune kucita ndiponso kukambilana nao zotulukapo za cosankha ciliconse cimene angapange. Inu makolo, ndinu amene muli pamalo abwino othandiza ana anu kuti adzipeleke kwa Yehova. Iwo amafunikila thandizo lanu kuti akhale Akristu ndi kuteteza dzinalo. Komabe, ife tonse tiyenela kusamala kuti tisataye ‘malaya athu akunja’ ophiphilitsila kutanthauza makhalidwe ndi mfundo zimene zimatidziŵikitsa kukhala otsatila a Kristu.—Chiv. 3:4, 5; 16:15.

ADZATIKUMBUKILA “PA ZABWINO” ZIMENE TIMACITA

19, 20. Kodi tiyenela kucita ciani kuti Yehova akatikumbukile “pa zabwino” zimene timacita?

19 Munthu wina amene anali ndi moyo nthawi ya Nehemiya anali Malaki. Iye ananena kuti, “buku la cikumbutso linayamba kulembedwa . . Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova ndi anthu amene anali kuganizila za dzina lake.” (Mal. 3:16, 17) Mulungu sadzaiŵala anthu onse amene amamuopa ndi amene amakonda dzina lake.—Aheb. 6:10.

20 Nehemiya anapemphela kuti, “Inu Mulungu wanga, mundikumbukile pa zabwino zimene ndinacita.” (Neh. 13:31) Monga Nehemiya, maina athu adzakhala m’buku la Mulungu la cikumbutso ngati tipitilizabe kupewa mayanjano oipa, ticilikiza dongosolo la gulu la Mulungu, tiika zinthu za kuuzimu patsogolo, ndi kuteteza dzina lathu monga Akristu. Tiyeni tipitilizebe ‘kudziyesa kuti tione ngati tikali olimba m’cikhulupililo.’ (2 Akor. 13:5) Ngati tikhalabe pa unansi wopatulika ndi Yehova, iye adzatikumbukila “pa zabwino” zimene takhala tikucita.

[Mafunso Ophunzilila]

[Cithunzi papeji 10]

Kodi Nehemiya anaonetsa bwanji kuti anali wokhulupilika kwa Yehova? (Onani ndime 5 ndi 6)

[Cithunzi papeji 12]

Thandizani ana anu kukhala ndi unansi wolimba ndi Yehova (Onani ndime 17 ndi 18)