Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova ‘Amanyamula Katundu Wanga Tsiku ndi Tsiku’

Yehova ‘Amanyamula Katundu Wanga Tsiku ndi Tsiku’

Ngakhale kuti ndimadwaladwala, ndaona kuti Atate wathu wakumwamba wandithandiza pa moyo wanga wonse. Ndipo kwa zaka zoposa 20 zapitazi, ndasangalala kwambiri kutumikira Yehova monga mpainiya.

Ndinabadwa wolumala msana mu 1956. Vuto langali limachititsa kuti ndiziyenda movutikira komanso ndizidwaladwala.

Ndisanabadwe, amishonale ena a Mboni za Yehova anayamba kuphunzira Baibulo ndi makolo anga. Ndili mwana, m’mudzi wathu wa Usakos, ku Namibia, munali ofalitsa ochepa kwambiri. Choncho nkhani zimene tinkafunika kuziphunzira pa misonkhano ya mpingo tinkangoziphunzira patokha monga banja. Ndili ndi zaka 7, anandichita opaleshoni kuti ndizitha kutaya madzi. Nditafika zaka 14, ndinayamba kudwala matenda akugwa. Choncho sindinamalize sukulu chifukwa chakuti sukuluyo inali kutali komanso ndinkafunika kusamalidwa ndi makolo.

Komabe ndinaganiza zolimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova. Pa nthawiyi mabuku athu ambiri anali asanamasuliridwe m’chinenero chathu cha Chiafirikana. Choncho ndinaphunzira Chingelezi kuti ndizitha kuphunzira mabuku athu ambiri. Kenako ndinakhala wofalitsa ndipo ndili ndi zaka 19 ndinabatizidwa. Kwa zaka 4 zotsatira ndinkadwaladwala komanso kuvutika maganizo. Popeza tinkadziwana ndi anthu ambiri m’derali, ndinkalephera kugwira mwakhama ntchito yolalikira chifukwa cha manyazi.

Nditangopitirira zaka 20, ine ndi makolo anga tinasamukira ku South Africa. Uku n’kumene ndinayamba kusonkhana ndi mpingo ndipo zinali zosangalatsa kwambiri. Komabe anandichitanso opaleshoni ina yaikulu.

Patapita nthawi, ndinamva woyang’anira dera akunena za upainiya. Zimene ananenazo zinandikhudza kwambiri. Ndinkadziwa kuti ndine wodwaladwala, koma ndinaona mmene Yehova anandithandizira pa mavuto osiyanasiyana. Choncho ndinalemba fomu yofunsira upainiya wokhazikika. Koma popeza ndinkadwaladwala, akulu sanandivomereze chifukwa ankakayikira kuti ndingakwanitse.

Komabe ndinaganiza kuti ndizichita zonse zimene ndingathe mu utumiki. Popeza kuti amayi anga ndiponso anthu ena ankandithandiza, ndinakwanitsa maola a apainiya kwa miyezi 6. Apa ndinaona kuti ndikhoza kukhala mpainiya. Choncho ndinafunsiranso upainiya ndipo pa nthawiyi anandivomereza. Ndiyeno pa September 1, 1988, ndinakhala mpainiya wokhazikika.

Pamene ndikuchita upainiya, ndaona kuti Yehova akundithandiza nthawi zonse. M’malo moganizira kwambiri mavuto anga, ndimatanganidwa kuphunzitsa ena Baibulo. Zimenezi zandithandiza kwambiri ndiponso zalimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova. Ndine wosangalala chifukwa ndathandiza anthu ambiri kuti adzipereke kwa Mulungu n’kubatizidwa.

Panopa ndimadwaladwalabe. Koma Yehova ‘amanyamula katundu wanga tsiku ndi tsiku.’ (Sal. 68:19) Iye wandithandiza kupirira komanso kuti ndizisangalala pa moyo wanga.