Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 KALE LATHU

Mfumu Inasangalala Kwambiri

Mfumu Inasangalala Kwambiri

MU AUGUST 1936, Robert ndi George Nisbet anapita kunyumba yachifumu ku Swaziland. Iwo anapita pa galimoto yokhala ndi zipangizo zokuzira mawu ndipo anatenga galamafoni. Anagwiritsa ntchito zinthuzi kuti Mfumu Sobhuza Yachiwiri ndi anthu ake amvetsere nyimbo ndiponso nkhani za M’bale J. F. Rutherford. Mfumuyo inasangalala kwambiri. George anati: “Tinasowa choyankha pamene mfumuyo inafuna kugula galamafoniyo, malekodi ndiponso zokuzira mawu.”

Robert anapepesa n’kufotokoza kuti zinthuzo sizinali zogulitsa chifukwa sizinali zawo. Mfumuyo inafuna kudziwa mwiniwake.

Robert anayankha kuti: “Zinthuzi ndi za Mfumu ina.” Sobhuza atafunsa dzina la Mfumuyo, Robert anati: “Ndi Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.”

Sobhuza ananena kuti: “Ee! Ameneyotu ndi Mfumu yapamwamba kwambiri. Sindikufuna kutenga chinthu chake chilichonse.”

Robert analemba kuti: ‘Ndinadabwa kwambiri ndi khalidwe la mfumuyi. Iye ankalankhula Chingelezi chabwino kwambiri koma sankachita matama. Anali wochezeka ndipo sankayankha mozungulira. Ndinacheza naye mu ofesi yake kwa mphindi 45, George akuika nyimbo panja.

Robert ananenanso kuti: ‘Tsiku lomwelo, tinapita kusekondale ina ya kumeneko ndipo unali ulendo wosangalatsa. Tinalalikira mphunzitsi wamkulu ndipo anamvetsera mwatcheru. Titamuuza za galamafoni ija ndiponso malekodi a nyimbo ndi nkhani zimene onse pasukuluyo akhoza kumvetsera, anasangalala kwambiri. Kenako anaitana ophunzira pafupifupi 100 kuti adzamvetsere. Tinauzidwa kuti kusukuluyo, anyamata ankaphunzira ulimi, ukalipentala, zomangamanga, Chingelezi ndiponso masamu. Koma atsikana ankaphunzira unesi, ntchito zapakhomo ndiponso zinthu zina. Kenako tinauzidwanso kuti agogo a Mfumu Sobhuza ndi amene anayambitsa sukuluyo.’

Ophunzira a kusekondale ya ku Swaziland amene anamvetsera nkhani mu 1936

Kuyambira mu 1933, Mfumu Sobhuza ankakonda kumvetsera apainiya amene ankabwera kudzalalikira kunyumba yachifumu. Nthawi ina, anasonkhanitsa asilikali omulondera  okwana 100 kuti amvetsere malekodi a uthenga wa Ufumu. Iye analembetsanso kuti azilandira magazini athu mwezi uliwonse, komanso ankalandira mabuku athu. Pasanapite nthawi, anali ndi mabuku athu pafupifupi onse. Komanso ankasungabe bwino mabukuwo ngakhale kuti boma la atsamunda linkaletsa mabuku a Mboni pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse.

Mfumu Sobhuza Yachiwiri inapitiriza kulandira Mboni kunyumba yachifumu ku Lobamba. Nthawi zina, inkaitananso atsogoleri a matchalitchi kuti adzamvetsere nkhani za Baibulo. Nthawi ina, m’bale wina dzina lake Helvie Mashazi ankafotokoza Mateyu chaputala 23 ndipo atsogoleri a matchalitchi anapsa mtima n’kunyamuka kuti akamukhazike pansi. Koma mfumuyo inauza M’bale Mashazi kuti apitirize kukamba nkhani yake. Inauzanso anthu amene analipo kuti azilemba mavesi onse amene atchulidwa m’nkhaniyo.

Pa nthawi ina, mpainiya wina atakamba nkhani, atsogoleri 4 a matchalitchi anabisa makolala awo aubusa n’kunena kuti: “Tasiya ubusa. Tsopano ndife Mboni za Yehova.” Kenako anapempha mpainiyayo kuti awapatse mabuku ngati amene Mfumu inali nawo.

Kuchokera m’ma 1930 mpaka pamene anamwalira mu 1982, Sobhuza ankalemekeza a Mboni za Yehova ndipo sankalola kuti azunzidwe chifukwa chosachita nawo miyambo ya ku Swaziland. M’pake kuti a Mboni za Yehova ankamuyamikira ndipo anadandaula kwambiri pamene anamwalira.

Pofika m’chaka cha 2013, m’dziko la Swaziland munali ofalitsa oposa 3,000. M’dzikoli muli anthu oposa 1 miliyoni, choncho wofalitsa aliyense ayenera kulalikira anthu 384. Pa nthawiyi kunalinso apainiya oposa 260 ndiponso mipingo 90. Anthu amene anafika pa Chikumbutso m’chaka cha 2012, anali 7,496. Izi zikusonyeza kuti ambiri akhoza kukhala Mboni za Yehova. Apa tinganene kuti abale amene anapita ku Swaziland m’ma 1930 anayala maziko abwino kwambiri.—Yachokera ku South Africa.